Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

5 Kodi Tiyenela Kupemphela Pamalo Ati, Nanga Nthawi Yanji?

5 Kodi Tiyenela Kupemphela Pamalo Ati, Nanga Nthawi Yanji?

MWINA mwaonapo kuti anthu a m’zipembedzo zambili amamanga nyumba zikulu-zikulu zopemphelelamo ndipo amakhazikitsa nthawi imene anthu ayenela kukapemphela. Kodi Baibo imanena kuti tiyenela kupemphela tili pamalo ena ake komanso pa nthawi inayake?

Baibo imasonyeza kuti pali nthawi zina zimene tiyenela kupemphela. Mwacitsanzo, Yesu asanadye na otsatila ake anapemphela kwa Mulungu, kumuyamikila cifukwa ca cakudyaco. (Luka 22:17) Ndipo pamene ophunzila ake anasonkhana kuti alambile Mulungu, anapemphela limodzi. Pamenepa iwo anacita zimene zinali kucitika kuyambila kale m’masunagoge a Ayuda ndiponso m’kacisi ku Yerusalemu. Mulungu anafuna kuti kacisi akhale “nyumba yopemphelelamo mitundu yonse.”—Maliko 11:17.

Atumiki a Mulungu akasonkhana pamodzi n’kupemphela, Mulungu angayankhe mapemphelo amenewo. Ngati iwo ali ogwilizana mwauzimu ndiponso zimene akunena m’mapemphelo awowo zikugwilizana na Malemba, Mulungu amakondwela. Ndipo pemphelo lingacititse kuti Mulungu acite zinthu zimene mwina sakanacita. (Aheberi 13:18, 19) Nthawi zonse, Mboni za Yehova zimapemphela pamisonkhano yawo imene imacitikila pa Nyumba ya Ufumu. Tikukuitanilani kumisonkhano imeneyi kuti mudzamve mapemphelo amenewa.

Komabe Baibo silinenelatu nthawi imene tiyenela kupemphela kapena malo opemphelelapo. M’Baibo muli nkhani za atumiki a Mulungu amene anapemphela nthawi zosiyana-siyana ndiponso pamalo osiyana-siyana. Yesu anati: “Popemphela, lowa m’cipinda cako pawekha ndi kutseka citseko, ndipo pemphela kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatelo Atate wako amene amaona kucokela kosaonekako adzakubwezela.”—Mateyu 6:6.

Tingapemphele nthawi iliyonse ndiponso kulikonse

Kodi mfundo imeneyi si yolimbikitsa? Mukhoza kupemphela kwa Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse pa nthawi iliyonse komanso muli nokha-nokha, ndipo dziŵani kuti Mulungu adzamva mapemphelo anu. N’cifukwa cake Yesu nthawi zambili anali kupita kwayekha kukapemphela. Pa nthawi ina, iye anacezela usiku wonse kupemphela kwa Mulungu kuti amuthandize kusankha bwino cocita pa nkhani ina yofunika kwambili.—Luka 6:12, 13.

Baibo imanenanso za amuna na akazi ena amene anapemphela kwa Mulungu pofuna kuti asankhe bwino zocita pa nkhani zofunika kwambili kapena pofuna kuti awathandize pa mavuto awo. Nthawi zina anapemphela mokweza mawu koma nthawi zina anapemphela camumtima. Anapemphela pagulu komanso anapemphela ali pa okha. Komabe cofunika kwambili n’coti anapemphela. Ndipotu Mulungu amauza atumiki ake kuti: “Muzipemphela mosalekeza.” (1 Atesalonika 5:17) Iye ni wofunitsitsa kumvetsela mapemphelo a anthu amene amacita cifunilo cake ngakhale atapemphela kambili bwanji. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambili?

Komabe, cifukwa ca mmene zinthu zilili m’dzikoli, anthu ena amafuna kudziwa ngati pemphelo lili lothandizadi. Mwina inuyo mungafunse kuti, ‘Kodi kupemphela kungandithandizedi?’