Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Baibulo m’buku la 1 Akorinto limanena za nyama yoperekedwa nsembe ku mafano?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muzidya popanda kufunsa mafunso, poopera chikumbumtima chanu.” (1 Akorinto 10:25) Kodi nyama imeneyi inkachokera kuti?

Kupereka nsembe ziweto unali mwambo waukulu mu akachisi a Agiriki ndiponso Aroma, komabe sikuti nyama yonse yoperekedwa nsembe inkadyedwa pa mwambowu. Nyama imene yatsala mu akachisi achikunja amenewo ankaigulitsa m’misika. Komanso buku lina linanena kuti: “Atsogoleri achipembedzo . . . ankadziwikanso kuti ndi ophika kapena opha nyama. Nyama imene ankapatsidwa chifukwa chogwira ntchito yopha ziweto ankaigulitsa kumsika.”​—Idol Meat in Corinth [Nyama Yoperekedwa Nsembe ku Mafano ku Korinto].

Choncho sikuti nyama yonse imene inali kugulitsidwa m’misika inali yotsala pa miyambo yachipembedzo. Atafukula bwinja la mzinda wakale wa Pompeii, anapeza kuti mumsika wake wa nyama munali mafupa a nkhosa zathunthu. Katswiri wina wamaphunziro, dzina lake Henry J. Cadbury, ananena kuti zimenezi zikusonyeza kuti “mwina nthawi zina ankagulitsa ziweto zamoyo, kapena ankaziphera pamsika pomwepo, kapenanso anali kuzipereka nsembe m’kachisi.”

Mfundo ya Paulo palembali inali yakuti, ngakhale kuti Akhristu sankayenera kuchita nawo miyambo yachikunja yachipembedzo, sikunali kulakwa kugula nyama yoti yatsala popereka nsembe m’kachisi. Zimenezi zinali choncho chifukwa, nyamayi singakhale yodetsedwa chabe chifukwa chakuti yatsala kopereka nsembe.

M’nthawi ya Yesu, kodi n’chifukwa chiyani Ayuda ndi Asamariya ankadana kwambiri?

Lemba la Yohane 4:9 limanena kuti: “Ayuda ndi Asamariya sayanjana.” Zikuoneka kuti udani umenewu unayamba pamene Yerobowamu anayambitsa kulambira mafano mu ufumu wakumpoto wa mafuko 10 a Aisiraeli. (1 Mafumu 12:26-30) Kwawo kwa Asamariya kunali ku Samariya, mzinda umene unali likulu la ufumu wakumpotowo. Mafuko 10 amenewo atagonjetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E, Asuriwo anayamba kutumiza ku Samariyako anthu amitundu ina osalambira Yehova, kuti azikakhala kumeneko. Anthu obwerawa anayamba kukwatirana ndi Asamariya ndipo zikuoneka kuti zimenezi zinachititsa kuti kulambira kwa Asamariya kupitirire kusokonezeka.

Patapita zaka zambiri, Asamariya anatsutsa Ayuda amene anachokera ku ukapolo ku Babulo kuti asamangenso kachisi wa Yehova komanso mpanda wa mzinda wa Yerusalemu. (Ezara 4:1-23; Nehemiya 4:1-8) Mkangano pa nkhani ya chipembedzo unakula pamene Asamariya anamanga kachisi wawowawo pa phiri la Gerizimu, mwina cha m’ma 300 B.C.E.

M’nthawi ya Yesu, mawu akuti “Msamariya” ankatanthauza munthu wa chipembedzo cha ku Samariya, osati kwenikweni munthu wokhala ku Samariya. Pa nthawiyi, Asamariya ankalambirabe ku phiri la Gerizimu ndipo Ayuda ankanyoza kwambiri komanso kunyansidwa ndi Asamariya.​—Yohane 4:20-22; 8:48.

[Chithunzi patsamba 12]

Mbale yadothi ya m’zaka za m’ma 500 b.c.e. yosonyeza anthu akupereka nsembe

[Mawu a Chithunzi]

Musée du Louvre, Paris

[Chithunzi patsamba 12]

Yerobowamu anayambitsa kulambira mafano