Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Musamangokhala Wankhawa Ndiponso Wachisoni?

Kodi Mungatani Kuti Musamangokhala Wankhawa Ndiponso Wachisoni?

Kodi Mungatani Kuti Musamangokhala Wankhawa Ndiponso Wachisoni?

KODI nthawi zina mumavutika maganizo chifukwa cha nkhawa ndiponso chisoni? Zoona n’zakuti, aliyense nthawi zina zimenezi zimamuchitikira. M’dzikoli masiku ano tikukumana ndi mavuto azachuma, mukuchitika zachiwawa komanso zinthu zambiri zopanda chilungamo. Chifukwa cha zinthu zimenezi, anthu ambiri amakhala osasangalala, amadziimba mlandu kwambiri, ndipo amadziona kuti ndi osafunika.

Koma maganizo amenewa ndi oopsa chifukwa angatichititse kuti tisamadzidalire. Angachititsenso kuti tisamaganize bwino komanso kuti tizikhala osasangalala. Baibulo limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24: 10) Kuti zinthu zitiyendere bwino m’dziko lamavutoli, tifunika kukhalabe ndi mphamvu. Choncho m’pofunika tiziyesetsa kuti tisamangokhala a nkhawa ndiponso achisoni. *

Baibulo limatipatsa malangizo othandiza kwambiri kuti tisamangokhala ndi nkhawa ndiponso chisoni. Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi ndiponso ndi amene amatipatsa zofunika pa moyo, samafuna kuti tizivutika ndi nkhawa kapena kusowa chiyembekezo. (Salimo 36:9) Choncho, tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Mawu ake angatithandizire kuti tisamangokhala ankhawa ndiponso achisoni.

Dziwani Kuti Mulungu Amakukondani Kwambiri

Anthu ena amaganiza kuti Mulungu alibe nthawi yoti azikhala ndi chidwi ndi zimene zikumuchitikira munthu aliyense payekha. Kodi nanunso mumaganiza choncho? Baibulo limatitsimikizira kuti Mlengi wathu amachita chidwi ndi mmene tikumvera mumtima mwathu. Wamasalimo anati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Wolamulira Wamkulu ndiponso wamphamvu yonse amakhala wokonzeka kutithandiza tikakhala m’mavuto.

Mulungu ndi wachikondi ndipo amatidera nkhawa. Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Iye amakonda anthu ndipo amamvera chisoni amene akuvutika. Mwachitsanzo, pamene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, iye anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo. Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse.”​—Ekisodo 3:7, 8.

Mulungu amadziwa kwambiri mmene timamvera. Pajatu, “iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.” (Salimo 100:3) Choncho ngakhale pamene tikuona kuti anthu sakumvetsa mavuto athu, tizikhala otsimikiza kuti Mulungu akumvetsa. Mawu a Mulungu amati: “Mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Mulungu amadziwa ngakhale mmene tikumvera mumtima mwathu.

N’zoona kuti Yehova amadziwanso zolakwa zathu. Koma timayamikira kwambiri kuti Mlengi wathu wachikondi amatikhululukira. Mulungu anauzira Davide kulemba kuti: “Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake, Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:13,14) Mulungu amaona zabwino mwa ifeyo zimene mwina eni akefe sitingathe kuziona. Tikalapa machimo athu iye amaona zabwino mwa ife ndipo amaiwala zoipa zathu.​—Salimo 139:1-3, 23, 24.

Choncho tikayamba kudziona kuti ndife osafunika, tiyenera kuyesetsa kuthetsa maganizo amenewo. Tiyenera kukumbukira mmene Mulungu amationera.​—1 Yohane 3:20.

Khalani pa Ubwenzi Wolimba ndi Mulungu

Kodi pali phindu lotani tikamadziona ngati mmene Mulungu amationera? Zingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo imeneyi ndi njira ina yothandiza kuti tisamangokhala achisoni ndi ankhawa. Koma kodi n’zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

Monga Atate wachikondi, Yehova Mulungu ndi wofunitsitsa kwambiri kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4: 8) Taganizirani mfundo yochititsa chidwi kwambiri imeneyi: Ngakhale kuti ndife ofooka ndiponso ochimwa, Mfumu ya chilengedwe chonse ingakhale bwenzi lathu lapamtima.

Mulungu watiuza zonse zokhudza iyeyo m’Baibulo n’cholinga chakuti timudziwe bwinobwino. Tikamawerenga Baibulo nthawi zonse, tingaphunzire za makhalidwe osangalatsa amene Mulungu ali nawo. * Tikamasinkhasinkha zimene tawerengazo, ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba. Tidzamudziwadi kuti ndi Atate wachikondi komanso wachifundo kwambiri.

Kuganizira kwambiri zimene timaphunzira m’Baibulo kumatithandizanso m’njira ina. Timayandikira Atate wathu wakumwamba mwa kuphunzira mfundo zake, kuzilola kuti zititonthoze, zititsogolere ndiponso zitithandize kukonza zimene timalakwitsa. Tiyenera kuchita zimenezi makamaka ngati zinthu zinazake zikutivutitsa maganizo kwambiri. Wamasalimo analemba kuti: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” (Salimo 94:19) Mawu a Mulungu amatonthoza mtima kwambiri. Tikadzichepetsa n’kumvera mawu ake a choonadi tidzaona kuti maganizo odziona kuti ndife osafunika akutha pang’onopang’ono. M’malo mwake tidzayamba kupeza mtendere wamumtima umene ndi Mulungu yekha amene amaupereka. Choncho, Yehova amatitonthoza ngati mmene kholo lachikondi limatonthozera mwana wake amene wakhumudwa.

Kulankhula ndi Mulungu kawirikawiri m’pemphero ndi njira inanso yothandiza kwambiri kuti tikhale naye pa ubwenzi. Baibulo limatitsimikizira kuti “chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Kaya pali zinthu zinazake zimene zikutichititsa mantha kapena tili ndi nkhawa inayake, tizipemphera kwa Mulungu kuti atithandize. Tikamuuza Mulungu zakukhosi kwathu, timapeza mtendere wamumtima. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7.

Mukamawerenga Baibulo nthawi zonse, kusinkhasinkha ndiponso kupemphera, n’zosakayikitsa kuti ubwenzi wanu ndi Atate wanu wakumwamba udzakula. Ubwenzi wolimba umenewu ndi chida champhamvu chokuthandizani kuti musamangokhala achisoni ndiponso ankhawa. Kodi chinanso chimene chingatithandize n’chiyani?

Nthawi Zonse Muziganizira za Chiyembekezo cha Moyo Wabwino

N’zotheka kumaganizirabe zinthu zabwino ngakhale tikukumana ndi mavuto aakulu zedi. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Mulungu watilonjeza zinthu zabwino zomwe zidzachitikadi. Mtumwi Paulo analemba mwachidule za zinthu zimenezi kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo [la Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Mawu akuti “kumwamba kwatsopano” akutanthauza boma, lomwe ndi Ufumu wakumwamba wa Mulungu womwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu. Mawu akuti “dziko lapansi latsopano” akutanthauza anthu onse amene adzakhale padziko lapansili omwe Mulungu azidzasangalala nawo. “Kumwamba kwatsopano” kukamadzalamulira, anthu okhala pa dziko lapansi sadzavutikanso ndi zinthu zimene zimachititsa anthu kukhala ankhawa ndiponso achisoni. Ponena za anthu okhulupirika amene adzakhalepo pa nthawiyo, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:4.

Sitikukayikira kuti inunso mukuona kuti zimenezi ndi zosangalatsa ndiponso zolimbikitsa kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti zinthu zabwino zam’tsogolo zimene Mulungu wasungira Akhristu oona ndi “chiyembekezo chosangalatsa.” (Tito 2:13) Sitingamakhale ankhawa ndiponso achisoni ngati timaganizira kwambiri zinthu zimene Mulungu watilonjeza komanso zifukwa zimene tiyenera kukhulupirira malonjezowo.​—Afilipi 4:8.

Baibulo limayerekezera chiyembekezo chachipulumutso chimene tili nacho ndi chisoti. (1 Atesalonika 5:8) Kale msilikali sankayesa dala kupita kunkhondo osavala chisoti. Iye ankadziwa kuti chisoti chimenechi chimamuteteza ku zida zosiyanasiyana zimene adani angamuponyere. Chiyembekezo chimateteza maganizo athu ngati mmene chisoti chinali kutetezera mutu wa msilikali. Tikamaganizira kwambiri zinthu zimene zimatipatsa chiyembekezo, sitingamakhale odandaula, amantha kapena kuganiza kuti palibe chimene chingatiyendere bwino.

Choncho n’zotheka kupewa kukhala ankhawa ndiponso achisoni. Inunso mungathe kupewa zimenezi. Ganizirani mmene Mulungu amakuonerani, yesetsani kukhala naye pa ubwenzi ndipo muziganizira kwambiri za chiyembekezo cha m’tsogolo. Mukatero mungakhale otsimikiza kuti inunso mudzakhalapo pamene anthu onse sadzakhalanso ankhawa kapena achisoni.​—Salimo 37:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Anthu amene akuvutika maganizo kwambiri kapena akhala ndi vuto limeneli kwa nthawi yaitali, angafunike kukaonana ndi dokotala.​—Mateyu 9:12.

^ ndime 14 Nsanja ya Olonda ya August 1, 2009 muli ndandanda yabwino kwambiri yothandiza kuwerenga Baibulo.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

“Ndikudziwa bwino zowawa zawo.”​—EKISODO 3:7, 8

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​—SALIMO 94:19

[Mawu Otsindika patsamba 21]

“Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”​—AFILIPI 4:7

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 20, 21]

Mavesi Olimbikitsa Onena za Yehova Mulungu

“Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.”​—EKISODO 34:6.

“Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 MBIRI 16:9.

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—SALIMO 34:18.

“Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”​—SALIMO 86:5.

“Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.”​—SALIMO 145:9.

“Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”​—YESAYA 41:13.

“Atamandike . . . Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.”​—2 AKORINTO 1:3.

“Tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.”​—1 YOHANE 3:19, 20.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 22]

Akuyesetsa Kuthana ndi Vuto Lomangokhala Ankhawa ndi Achisoni

“Bambo anga ndi chidakwa ndipo zimenezi zimandibweretsera mavuto ambirimbiri. Kuyambira kale ndakhala ndikudziona kuti ndine wosafunika. Koma munthu wina wa Mboni za Yehova atayamba kundiphunzitsa Baibulo, ndinadziwa kuti Mulungu analonjeza kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Zimenezi zinachititsa kuti ndizikhala wosangalala kwambiri. Ndinayamba kuwerenga Baibulo kawirikawiri ndipo nthawi zonse ndimaonetsetsa kuti ndizikhala nalo pafupi. Ndikayamba kuvutika maganizo, ndimalitenga n’kuyamba kuwerenga mavesi olimbikitsa. Ndikawerenga za makhalidwe abwino a Mulungu, ndimalimba mtima ndipo ndimaona kuti ndine wofunika kwambiri kwa iye.”​—Kátia, mayi wazaka 33. *

“Ndinali chidakwa, ndinkasuta chamba kwambiri, kumwa mankhwala osiyanasiyana osokoneza bongo komanso ndinkafwenkha guluu. Zinthu zanga zonse zitandithera, ndinayamba moyo wopemphapempha. Koma moyo wanga unasintha kwambiri munthu wina wa Mboni za Yehova atayamba kundiphunzitsa Baibulo. Ndinakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Ngakhale kuti nthawi zina ndimalimbanabe ndi maganizo odziimba mlandu ndiponso kudziona ngati wosafunika, ndimadalira Mulungu chifukwa ndi wachifundo ndiponso wokoma mtima. Sindikukayika kuti Mulungu apitirizabe kundipatsa mphamvu zondithandiza kuti ndisamadzione ngati wosafunikira. Ndimaona kuti kudziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa, ndi chinthu chachikulu kwambiri chimene chachitika pamoyo wanga.”​—Renato, bambo wazaka 37.

“Kuyambira ndili mwana, ndinkakonda kudziyerekezera ndi m’bale wanga wamwamuna. Ndinkaona kuti amandiposa pa chilichonse. Mpaka pano ndimadzikayikirabe kwambiri ndipo ndimaona kuti palibe chabwino chimene ndingachite. Koma ndatsimikiza mtima kuthana ndi vuto limeneli. Ndimapemphera kwa Yehova kawirikawiri ndipo maganizo amenewa akandibwerera, Yehova amandithandiza kuthana nawo. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amandikonda ndiponso amandiganizira.”​—Roberta, mayi wazaka 45.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 45 Tasintha mayina ena.