Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wakumva Pemphero”

“Wakumva Pemphero”

Yandikirani Mulungu

“Wakumva Pemphero”

1 MBIRI 4:9, 10

KODI Yehova Mulungu amayankhadi mapemphero ochokera pansi pa mtima a anthu amene amadzipereka ndi mtima wonse pomulambira? Nkhani ya m’Baibulo ya munthu wina wosadziwika kwenikweni dzina lake Yabezi imasonyeza kuti Yehova ‘amamvadi pemphero’ (Salimo 65:2) Nkhani yachidule imeneyi imapezeka pa mndandanda wa mayina ofotokoza mibadwo ya anthu chakumayambiriro kwa buku la 1 Mbiri. Tiyeni tione 1 Mbiri 4:9, 10.

Nkhani yonse ya Yabezi imangopezeka m’mavesi awiri amenewa basi. Malinga ndi vesi 9, ‘mayi ake ndiwo anamutcha dzina lakuti Yabezi, chifukwa anati: “Ndam’bereka ndikumva ululu.”’ * N’chifukwa chiyani anasankha dzina limeneli? Kodi iye anamva ululu kwambiri kuposa umene akazi amamva nthawi zonse pobereka? Kodi kapena anali wamasiye ndipo ankadandaula kuti mwamuna wake sanaone mwana wakeyu atabadwa? Baibulo silinena kalikonse pa nkhani imeneyi. Koma mayiyu sankadziwa kuti tsiku lina adzanyadira za mwana wakeyu. N’kutheka kuti abale ake a Yabezi anali anthu abwino koma ‘Yabezi anali wolemekezeka kwambiri kuposa abale akewo.’

Yabezi anali munthu wokonda kupemphera. Iye anayamba pemphero lake ndi kupempha madalitso kwa Mulungu. Kenako anapempha zinthu zitatu zimene zikusonyeza kuti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba.

Poyamba, Yabezi anapempha Mulungu kuti: ‘Mukulitse dziko langa.’ (Vesi 10) Munthu wolemekezekayu sankalanda malo a anthu kapena kusirira zinthu za eni. N’kutheka kuti iye ankaganizira za anthu osati malo. Mwina ankapempha kuti dera lake likule mwamtendere n’cholinga choti mukhale anthu ambiri olambira Mulungu woona. *

Chachiwiri, Yabezi anapempha kuti “dzanja” la Mulungu likhale naye. Mawu ophiphiritsa akuti dzanja la Mulungu amatanthauza mphamvu zimene Mulungu amagwiritsa ntchito pothandiza anthu amene amamulambira. (1 Mbiri 29:12) Kuti alandire zimene anapempha kuchokera pansi pa mtima, Yabezi anadalira Mulungu yemwe dzanja lake silifupika kwa anthu amene amamukhulupirira.​—Yesaya 59:1.

Chachitatu, Yabezi anapemphera kuti: ‘Munditeteze ku tsoka, kuti lisandivulaze.’ Mawu akuti, ‘kuti lisandivulaze’ akusonyeza kuti Yabezi sanapemphe kuti asakumane ndi tsoka koma kuti asade nkhawa kwambiri ndi tsokalo kapena kugonja pokumana ndi zoipa.

Pemphero la Yabezi limasonyeza kuti iye ankaganizira kwambiri za kulambira koona ndipo ankakhulupirira ndi kudalira Wakumva pemphero. Kodi Yehova anamuyankha bwanji? Nkhani yachiduleyi imatha ndi mawu akuti: “Choncho Mulungu anakwaniritsa zimene iye anapempha.”

Wakumva pempheroyu sanasinthe. Iye amasangalala ndi mapemphero a anthu amene amamulambira. Anthu amene amamukhulupirira ndiponso kumudalira sakayikira mawu awa: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.”​—1 Yohane 5:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Dzina lakuti Yabezi ndi lochokera ku mawu amene amatanthauza “ululu.”

^ ndime 4 M’mabuku achiyuda ofotokozera Malemba Opatulika mawu a Yabeziwa analembedwa kuti: “Ndidalitseni ndi ana ndipo mukuze malire a malo anga kuti mukhale ophunzira.”