Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Ufumu Umene Udzasintha Dziko Lonse Lapansi

Ufumu Umene Udzasintha Dziko Lonse Lapansi

KODI ukuganiza kuti Ufumu umenewu ndi uti?​— * Ndi Ufumu umene Yesu ananena kuti tizipempha kuti ubwere. Iye anatiphunzitsa kuti zipempha Mulungu kuti: “Ufumu wanu ubwere.” (Mateyu 6:9, 10) Kwa zaka pafupifupi 2,000 tsopano, otsatira a Yesu akhala akupempha Mulungu kuti Ufumu umenewu ubwere. Kodi iweyo unapemphapo Ufumu umenewu?​—

Kuti umvetse tanthauzo la ufumu, uyenera udziwe kaye tanthauzo la mawu akuti mfumu. Mfumu ndi munthu amene akulamulira dziko kapena dera linalake. Ufumu wa Mulungu udzalamulira padziko lonse lapansi. Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, aliyense padziko lapansi adzasangalala ndi madalitso amene Ufumuwo udzabweretse.

Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba. Lemba Yesaya 9:6 limanena za Wolamulira wa boma limeneli. Taona zimene Baibulo likunena za wolamulira ameneyu. Lemba limeneli limati: “Kwa ife kwabadwa mwana . . . , ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro. Iye adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere.”

Kodi ukudziwa kuti mawu akuti kalonga palembali akutanthauza chiyani?​— Inde, akutanthauza mwana wa mfumu. Kodi Mfumu yaikulu kumwamba ndani?​— Walondola ngati wayankha kuti Yehova. Baibulo limamutchula Yehova kuti “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) M’Baibulo, kawirikawiri Yesu amatchedwa “Mwana wa Mulungu.” Chifukwa chimodzi ndi chakuti Yehova ndi amene anapatsa Yesu moyo. Choncho, Yehova ndi Atate ake enieni a Yesu.​—Luka 1:34, 35; Yohane 1:34, 49; 3:17; 11:27; 20:31; Machitidwe 9:20.

Ufumu wa Mulungu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tidziupempherera ndi boma lapadera, losiyana ndi maboma onse. Ufumu umenewu ndi wa Kalonga chifukwa Yehova anapatsa Mwana wake, Yesu, mphamvu zolamulira mu Ufumu umenewu. Koma kodi ukudziwa kuti palinso ena amene anasankhidwa kuti adzalamulire ndi Yesu mu Ufumu wa Atate wake?​— Tiye tikambirane za anthu amenewa.

Kutatsala nthawi yochepa kuti Yesu aphedwe, iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti akupita kumwamba, ku “nyumba” ya Atate wake. Iye anati: “Ndikupita kukakukonzerani malo . . . , kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.” (Yohane 14:1-3) Kodi ukudziwa kuti atumwi ndiponso anthu ena amene anasankhidwa akachita chiyani kumwamba ndi Yesu?​— “Adzalamulira monga mafumu limodzi naye.” Baibulo limatiuzanso chiwerengero cha anthu amenewa, amene adzalamulire ndi Yesu. Anthu amenewa adzakhalapo 144,000.​—Chivumbulutso 14:1, 3; 20:6.

Kodi ukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padziko lapansi, Kalonga Wamtendere pamodzi ndi olamulira osankhidwa okwanira 144,000 akadzayamba kulamulira?​— Zidzakhala zosangalatsa kwambiri. Sikudzakhala nkhondo. Nyama sizizidzadyana komanso zidzakhala pamodzi ndi anthu mwamtendere. Anthu sadzadwalanso kapena kufa. Anthu osaona adzayamba kuona. Anthu ogontha adzayamba kumva. Anthu olumala adzakhala bwinobwino ndipo azidzathamanga ndi kudumpha ngati gwape. M’dzikoli mudzakhala chakudya chokwanira aliyense. Ndipo anthu onse azidzakondana ngati mmene Yesu anaphunzitsira ophunzira ake. (Yohane 13:34, 35) Tiye tiwerenge mavesi a m’buku la Yesaya, onena za zinthu zabwino zimene zidzakhalepo pa nthawiyo.​—Yesaya 2:4; 11:6-11; 25:8; 33:24; 35:5, 6; 65:21-24.

Kungoyambira pamene Yesu anaphunzitsa anthu kupemphera kuti, “ufumu wanu ubwere,” anthu ambiri aphunzira zambiri za Ufumu umenewo. Zimene aphunzirazo zachititsa kuti asinthe moyo wawo. Posachedwapa, Ufumu umenewo udzabwera ndi kuchotsa maboma onse padziko lapansi. Zikadzatero, aliyense amene amatumikira Yehova Mulungu ndi Wolamulira wake wosankhidwa, Yesu Khristu, adzakhala pa mtendere. Adzakhala ndi thanzi labwino, komanso azidzakhala wosangalala nthawi zonse.​—Yohane 17:3.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.