Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndani Akudziwa Maganizo a Yehova?”

“Ndani Akudziwa Maganizo a Yehova?”

“Ndani Akudziwa Maganizo a Yehova?”

“‘Ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti am’langize?’ Koma ifeyo tili ndi maganizo a Khristu.”​—1 AKOR. 2:16.

1, 2. (a) Kodi anthu amakumana ndi vuto lotani? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya mmene anthufe timaganizira ndi mmene Yehova amaganizira?

KODI zimakuvutani kudziwa mmene munthu wina amaganizira? Mwina mwangokwatira kapena kukwatiwa kumene ndipo mukuona kuti n’zovuta kudziwa mmene mwamuna kapena mkazi wanu amaganizira. Amuna ndi akazi amaganiza ndiponso kulankhula mosiyana. M’zikhalidwe zina amuna ndi akazi, ngakhale olankhula chinenero chimodzi, amaphunzitsidwa kuti azilankhula mosiyana kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, kusiyana chikhalidwe ndi chinenero kumachititsa kuti anthu aziganiza ndiponso kuchita zinthu m’njira zosiyanasiyana. Komabe, tikamayesetsa kuwadziwa bwino anthu ena m’pamenenso timakhala ndi mwayi womvetsa mmene amaganizira.

2 Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti mmene anthufe timaganizira ndi zosiyana kwambiri ndi mmene Yehova amaganizira. Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Maganizo a anthu inu si maganizo anga, ndipo njira zanga si njira zanu.” Ndiyeno pofotokoza mfundo imeneyi Yehova ananena kuti: “Pakuti monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.”​—Yes. 55:8, 9.

3. Tchulani njira ziwiri zimene zingatithandize kukhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova.”

3 Kodi izi zikutanthauza kuti sitiyenera kuyesa n’komwe kudziwa mmene Yehova amaganizira? Ayi. Ngakhale kuti sitingadziwe bwinobwino maganizo onse a Yehova, Baibulo limatilimbikitsa kukhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova.” (Werengani Masalimo 25:14; Miyambo 3:32.) Njira imodzi imene ingatithandize kuyandikira Yehova ndi kuganizira ndiponso kuphunzira zochita zake zomwe zinalembedwa m’Mawu ake Baibulo. (Sal. 28:5) Njira ina ndi kudziwa “maganizo a Khristu” yemwe ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (1 Akor. 2:16; Akol. 1:15) Tikhoza kudziwa makhalidwe a Yehova ndiponso mmene iye amaganizira mwa kuphunzira komanso kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo.

Pewani Chizolowezi Choipa

4, 5. (a) Kodi tiyenera kupewa chizolowezi choipa chiti? Fotokozani. (b) Kodi Aisiraeli anali ndi maganizo olakwika ati?

4 Tikamasinkhasinkha zochita za Yehova tiyenera kupewa chizolowezi chomuweruza poyerekezera ndi mfundo zimene anthu amayendera. Chizolowezi chimenechi chatchulidwa m’mawu a Yehova opezeka pa Masalimo 50:21. Lembali limati: “Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.” Izi n’zofanana ndi zimene katswiri wina wa Baibulo ananena zaka 175 zapitazo. Iye anati: “Anthu amakonda kuweruza Mulungu malinga ndi mmene iwo amaonera zinthu ndipo amaganiza kuti iye ndi womangika ndi malamulo amene anthuwo amaona kuti ndi oyenera kuwatsatira.”

5 Tiyenera kusamala kwambiri kuti tisamaganize zoti Yehova ayenera kumachita zinthu mogwirizana ndi mfundo kapena zofuna zathu. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Tikamaphunzira nkhani zina za m’Baibulo, tingamaganize kuti Yehova sanachite bwino pa nkhaniyo. Tingakhale ndi maganizo amenewa chifukwa chakuti sitidziwa zambiri ndiponso ndife opanda ungwiro. Aisiraeli anali ndi maganizo olakwikawa ndipo ankaona kuti Yehova sakuyendetsa bwino zinthu pakati pawo. Taonani zimene Yehova anawauza: “Anthu inu mudzanena kuti: ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo? Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?”​—Ezek. 18:25.

6. Kodi Yobu anaphunzira chiyani ndipo kodi tingapindule bwanji ndi zimene zinamuchitikira?

6 Chinthu chofunika kwambiri kuti tisakhale ndi maganizo oweruza Yehova malinga ndi mfundo zimene timayendera, ndi kuzindikira kuti ife sitidziwa zambiri ndipo nthawi zina timakhala ndi maganizo olakwika kwambiri. Izi n’zimene Yobu anafunika kudziwa. Pa nthawi imene ankavutika, Yobu anathedwa nzeru n’kuyamba kumangodziganizira yekha. Iye sankaonanso zinthu zikuluzikulu zofunika, koma Yehova anamuthandiza kuti aziona zinthu moyenera. Iye anamufunsa mafunso oposa 70 amene sanathe kuwayankha. Pochita zimenezi, Yehova anathandiza Yobu kuzindikira kuti sankadziwa zinthu zambiri. Zitatero Yobu anadzichepetsa n’kusintha mmene ankaonera zinthu.​—Werengani Yobu 42:1-6.

Kukhala ndi “Maganizo a Khristu”

7. Kodi kuphunzira zimene Yesu anachita kungatithandize bwanji kudziwa mmene Yehova amaganizira?

7 Yesu anatsanzira bwinobwino Atate wake pa zolankhula zake komanso zochita zake. (Yoh. 14:9) Choncho, kuphunzira zimene Yesu ankachita kungatithandize kudziwa bwino mmene Yehova amaganizira. (Aroma 15:5; Afil. 2:5) Tiyeni tione nkhani ziwiri za m’Mauthenga Abwino.

8, 9. Malinga ndi lemba la Yohane 6:1-5, kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu afunse Filipo funso ndipo n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa funso limeneli?

8 Taganizirani zimene zinachitika Pasika wa 32 C.E. atangotsala pang’ono kuchitika. Atumwi a Yesu anali atangofika kumene kuchokera ku ulendo wolalikira m’Galileya monse. Popeza anali atatopa, Yesu anawatenga kupita kumalo a kwaokha kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya. Koma anthu masauzande ambiri anawatsatira. Yesu atachiritsa anthu ambiri ndiponso kuwaphunzitsa zinthu zambiri panali vuto limodzi. Gulu la anthulo linali ndi njala ndipo panalibe kulikonse kumene likanapeza chakudya. Yesu atadziwa za vutoli anafunsa Filipo amene anachokera m’deralo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tikaigula kuti?”​—Yoh. 6:1-5.

9 N’chifukwa chiyani Yesu anafunsa Filipo funso limeneli? Kodi Yesu sankadziwa zoyenera kuchita? Ayi. Nanga kodi maganizo ake anali otani? Mtumwi Yohane amene analipo pa nthawiyo anati: “[Yesu] ananena izi mongomuyesa, popeza anali atadziwa kale chimene ati achite.” (Yoh. 6:6) Pamenepatu Yesu ankafuna kudziwa ngati ophunzira ake anali ndi chikhulupiriro cholimba. Pofunsa funso limeneli iye anakopa chidwi cha ophunzirawo ndipo anawapatsa mwayi wosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro chakuti Yesu akhoza kuwapatsa chakudya. Koma iwo sanachite zimenezi, m’malomwake anasonyeza kuti sankaona zinthu moyenera. (Werengani Yohane 6:7-9.) Kenako Yesu anawasonyeza kuti akhoza kuchita zinthu zimene iwo sanaziganizirepo. Iye anadyetsa masauzande a anthuwa m’njira yozizwitsa.​—Yoh. 6:10-13.

10-12. (a) N’chifukwa chiyani poyamba Yesu ankakana pempho la mayi wachigiriki? Fotokozani. (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

10 Nkhani imeneyi ingatithandizenso kudziwa mmene Yesu ankaganizira pa nthawi inanso. Atangodyetsa kumene gulu la anthuli, Yesu ndi atumwi ake analowera chakumpoto kupitirira malire a Isiraeli, pafupi ndi Turo ndi Sidoni. Ali kumeneku, mkazi wina wachigiriki anapempha Yesu kuti achiritse mwana wake wamkazi. Poyamba, Yesu sanayankhe. Koma mkaziyo atalimbikira kupempha, Yesu anamuuza kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera tiagalu.”​—Maliko 7:24-27.

11 N’chifukwa chiyani poyamba Yesu anakana kuthandiza mayiyu? Kodi mwina Yesu ankangofuna kumuyesa ngati mmene anachitira ndi Filipo, kuti aone ngati angasonyeze chikhulupiriro? Ngakhale kuti Malemba sasonyeza mmene mawu a Yesu ankamvekera, mawu akewo sanachititse mayiyo kutaya mtima. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “tiagalu” iye sananyoze mayiyo. Mwina Yesu anachita zinthu ngati mmene kholo lingachitire ndi mwana wake amene akupempha kanthu. Nthawi zina kholo silisonyeza kuti limupatsa mwanayo zimene akufuna n’cholinga choti aone ngati mwanayo watsimikizadi. Kaya zinalidi choncho, mayiyu atasonyeza chikhulupiriro Yesu anachiritsa mwana wakeyo.​—Werengani Maliko 7:28-30.

12 N’khani ziwiri za m’Mauthenga Abwino zimenezi zatithandiza kudziwa bwino “maganizo a Khristu.” Tsopano tiyeni tikambirane mmene nkhani zimenezi zingatithandizire kudziwa bwino maganizo a Yehova.

Mmene Yehova Analankhulira ndi Mose

13. Kodi kudziwa maganizo a Yesu kungatithandize bwanji?

13 Kudziwa mmene Yesu ankaganizira kungatithandize kumvetsa zigawo za m’Malemba zimene ndi zovuta kuzimvetsa. Mwachitsanzo, taganizirani mawu amene Yehova analankhula ndi Mose, Aisiraeli atapanga mwana wa ng’ombe kuti azimulambira. Mulungu anati: “Ndawayang’ana anthu amenewa, ndipo ndaona kuti ndi anthu ouma khosi. Ndileke tsopano kuti mkwiyo wanga uwayakire ndipo ndiwafafanize, koma iwe ndikupange kukhala mtundu waukulu.”​—Eks. 32:9, 10.

14. Kodi Mose anayankha bwanji zimene Yehova ananena?

14 Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake. Iye anati: ‘N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu? Aiguputo anenerenji kuti, “Anawatulutsa m’dziko lino kuti akawaphe kumapiri ndi kuwafafaniza padziko lapansi”? Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo, ndipo mverani chisoni anthu anu kuti musawagwetsere tsoka. Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira pa inu mwini, powauza kuti, “Ndidzachulukitsa mbewu yanu ngati nyenyezi zakumwamba, ndipo dziko lonseli limene ndalipatula ndidzalipereka kwa mbewu yanu, kuti likhale lawo mpaka kalekale.”’ Pamenepo, Yehova anayamba kumva chisoni chifukwa cha tsoka limene ananena kuti agwetsera anthu ake.”​—Eks. 32:11-14. *

15, 16. (a) Kodi mawu a Yehova anapatsa Mose mwayi wochita chiyani? (b) Kodi mawu akuti Yehova “anayamba kumva chisoni” akutanthauza chiyani?

15 Kodi Mose anafunikadi kuthandiza Yehova kuti asinthe maganizo ake? Ayi. Ngakhale kuti Yehova ananena zimene ankafuna kuchita, sikuti anali atasankhiratu zoti achite. Apa Yehova ankangoyesa Mose, ngati mmene Yesu anachitira ndi Filipo komanso mayi wachigiriki uja. Mose anapatsidwa mwayi wofotokoza maganizo ake. * Yehova anapatsa Mose udindo wokhala mkhalapakati wa Aisiraeli ndi Yehova ndipo Yehova ankachita zinthu moganizira udindo wa Mose. Kodi Mose akanasokonezeka chifukwa chokhumudwa ndi zochita za Aisiraeli? Kodi iye akanapezerapo mwayi wolimbikitsa Yehova kuti asiye mtundu wa Isiraeli n’kuchititsa kuti mbadwa zake zikhale mtundu wamphamvu?

16 Mawu a Mose anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi wachilungamo. Zolankhula zake zinasonyeza kuti sanali wodzikonda, koma ankadera nkhawa dzina la Yehova. Iye sankafuna kuti dzinali linyozedwe. Apatu Mose anasonyeza kuti ankadziwa “maganizo a Yehova” pa nkhani imeneyi. (1 Akor. 2:16) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Popeza Yehova anali asanatsimikize kuchita zimene ananena, nkhani ya m’Baibuloyi imati iye “anayamba kumva chisoni.” M’Chiheberi mawu amenewa amangotanthauza kuti Yehova sanapereke chilango chimene ankafuna kupereka ku mtundu wonsewu.

Mmene Yehova Analankhulira ndi Abulahamu

17. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi woleza mtima kwambiri pamene Abulahamu ankafotokoza maganizo ake?

17 Chitsanzo china chosonyeza kuti Yehova amalola atumiki ake kusonyeza chikhulupiriro chawo ndi zimene Abulahamu anapempha zokhudza mzinda wa Sodomu. Pa nkhani imeneyi, Yehova anasonyeza kuti ndi woleza mtima kwambiri chifukwa analola Abulahamu kufunsa mafunso maulendo 8. Ulendo wina Abulahamu anachonderera kuti: “Simungachite zimenezo, kupha munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama aone zofanana ndi woipa. Simungachite zimenezo ayi. Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?”​—Gen. 18:22-33.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa zokambirana za pakati pa Yehova ndi Abulahamu?

18 Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani za mmene Yehova amaganizira? Kodi Yehova anafunika kukambirana ndi Abulahamu kuti adziwe zoyenera kuchita? Ayi. Yehova akanatha kungouziratu Abulahamu zifukwa zimene akanawonongera mzindawu. Koma kudzera m’zokambirana zimenezi, Yehova anathandiza Abulahamu kumvetsa zimene anasankha ndiponso mmene Iye amaganizira. Zinathandizanso kuti Abulahamu azindikire kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri ndiponso wachilungamo. Pamenepatu Yehova anakambirana ndi Abulahamu ngati mnzake weniweni.​—Yes. 41:8; Yak. 2:23.

Zimene Tikuphunzirapo

19. Kodi tingatsanzire bwanji Yobu?

19 Kodi taphunzira chiyani pa nkhani ya “maganizo a Yehova”? Tiyenera kulola kuti Mawu a Mulungu azitithandiza kudziwa bwino maganizo a Yehova. Popeza kuti anthufe sitidziwa zambiri, tisamaweruze Yehova malinga ndi mfundo ndiponso maganizo amene timayendera. Yobu anati: “[Mulungu] si munthu ngati ine kuti ndimuyankhe, kapena kuti tizengane mlandu.” (Yobu 9:32) Mofanana ndi Yobu tikayamba kudziwa bwino maganizo a Yehova tidzafuula kuti: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake, ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake. Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”​—Yobu 26:14.

20. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati sitikumvetsa nkhani inayake m’Baibulo?

20 Tikamawerenga Malemba, kodi tiyenera kutani ngati tapeza nkhani yovuta kuimvetsa makamaka yokhudza mmene Yehova amaganizira? Ngati tafufuza nkhaniyo koma osapeza yankho lomveka bwino, tiyenera kuona kuti umenewu ndi mwayi wathu wosonyeza kuti timakhulupirira kwambiri Yehova. Tisaiwale kuti mfundo zina zimatithandiza kusonyeza kuti timakhulupirira kuti Yehova ali ndi makhalidwe abwino. Tiyeni tikhale odzichepetsa n’kuvomereza kuti sitingamvetse zochita zake zonse. (Mlal. 11:5) Izi zidzatithandiza kuvomereza mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake? Pakuti ‘ndani akudziwa maganizo a Yehova, kapena ndani angakhale phungu wake?’ Kapenanso, ‘Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?’ Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemerero ukhale wake kwamuyaya. Ame.”​—Aroma 11:33-36.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Pa Numeri 14:11-20 palinso nkhani yofanana ndi imeneyi.

^ ndime 15 Akatswiri ena amanena kuti mawu achiheberi okuluwika, amene anawamasulira kuti “ndileke” pa Eksodo 32:10 ndi opempha Mose kuti akhale mkhalapakati kapena kuti aime pakati pa Yehova ndi mtundu wa Isiraeli. (Sal. 106:23; Ezek. 22:30) N’zoonekeratu kuti Mose anali womasuka kufotokoza maganizo ake kwa Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kupewa chizolowezi choweruza Yehova malinga ndi mfundo zimene timayendera?

• Kodi kudziwa bwino zochita za Yesu kungatithandize bwanji kukhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova”?

• Kodi mwaphunzira chiyani pa zokambirana za pakati pa Yehova ndi Mose komanso Abulahamu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 5]

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya maganizo a Yehova tikaona mmene analankhulira ndi Mose komanso Abulahamu?