Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kufunafuna Choyamba “Chilungamo Chake”

Pitirizani Kufunafuna Choyamba “Chilungamo Chake”

Pitirizani Kufunafuna Choyamba “Chilungamo Chake”

“Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”​—MAT. 6:33.

1, 2. Kodi chilungamo cha Mulungu chimatanthauza chiyani, nanga n’chogwirizana ndi chiyani?

“PITIRIZANI kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Yesu Khristu ananena malangizo amenewa pa ulaliki wake wa paphiri ndipo ndi odziwika bwino kwa Mboni za Yehova masiku ano. Timafunitsitsa kusonyeza kuti timakonda boma la Ufumu umenewu ndiponso kukhala okhulupirika ku Ufumuwo pa zochita zathu zonse. Koma sitiyenera kuiwala mbali yachiwiri ya malangizowa yakuti, “ndi chilungamo chake.” Kodi chilungamo cha Mulungu n’chiyani, nanga tingatani kuti tichifunefune choyamba?

2 Mawu amene anawamasulira kuti “chilungamo” angamasuliridwenso kuti “kukhala woongoka.” Choncho chilungamo cha Mulungu chimatanthauza kukhala woongoka mogwirizana ndi mfundo zake. Popeza ndi Mlengi, Yehova ali ndi ufulu wokonza mfundo zosonyeza zinthu zoyenera ndi zolakwika, zabwino ndi zoipa. (Chiv. 4:11) Koma chilungamo cha Mulungu si cha malamulo ambirimbiri okhwimitsa zinthu. Chilungamo chake n’chogwirizana ndi makhalidwe ake akuluakulu omwe ndi chikondi, nzeru ndi mphamvu. Choncho chilungamo cha Mulungu n’chogwirizana ndi chifuniro chake. Chimaphatikizaponso zimene amafuna kuti anthu om’tumikira azichita.

3. (a) Kodi kufuna chilungamo cha Mulungu poyamba kumatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mfundo zolungama za Yehova?

3 Kodi kufuna choyamba chilungamo cha Mulungu kumatanthauza chiyani? Mwachidule tingati kumatanthauza kuchita chifuniro cha Mulungu kuti timusangalatse. Kufunafuna chilungamo chake kumaphatikizapo kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama osati mfundo zathu. (Werengani Aroma 12:2.) Zimene timachita pa moyo wathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Si nkhani yongomvera malamulo ake chifukwa choopa chilango. Chifukwa chokonda Mulungu, timayesetsa kumusangalatsa mwa kutsatira mfundo zake osati kukhazikitsa mfundo zathuzathu. Timadziwa kuti kuchita zimenezi n’koyenera ndipo tinalengedwa kuti tizichita zinthu mwa njira imeneyi. Mofanana ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, tiyenera kukonda chilungamo.​—Aheb. 1:8, 9.

4. Kodi kufunafuna chilungamo cha Mulungu n’kofunika bwanji?

4 Kodi kufunafuna chilungamo cha Yehova n’kofunika bwanji? Taganizirani mfundo iyi: M’munda wa Edene Adamu ndi Hava anayesedwa ngati angavomereze kuti Yehova ndi woyenera kuwapatsa mfundo zoti aziyendera kapena ayi. (Gen. 2:17; 3:5) Iwo analephera kuchita zimenezi ndipo zotsatira zake ndi zakuti anthufe timavutika komanso timafa. (Aroma 5:12) Komabe Mawu a Mulungu amanena kuti: “Amene akufunafuna chilungamo ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.” (Miy. 21:21) Motero, zotsatira za kufunafuna chilungamo cha Mulungu n’zakuti munthu amakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo izi zingathandize kuti munthuyo apulumuke.​—Aroma 3:23, 24.

Msampha wa Kudzilungamitsa

5. Kodi tiyenera kupewa msampha uti?

5 M’kalata yake yopita kwa Akhristu ku Roma, mtumwi Paulo anatsindika za msampha umene tiyenera kuupewa ngati tikufuna kuti tifunefune chilungamo cha Mulungu. Polankhula za Ayuda anzake Paulo anati: “Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola. Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu, iwo sanagonjere chilungamocho koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.” (Aroma 10:2, 3) Malinga ndi zimene Paulo ananena, anthu amenewa sankamvetsa chilungamo cha Mulungu chifukwa chakuti ankatanganidwa ndi kukhazikitsa chilungamo chawochawo. *

6. Kodi tiyenera kupewa khalidwe liti, ndipo chifukwa chiyani?

6 Njira imodzi imene ingatigwetsere mu msampha umenewu ndi kutumikira Mulungu mwa mpikisano, n’kumadziyerekezera ndi anthu ena. Mtima umenewu ungachititse kudziona ngati ndife anzeru kwambiri komanso a khalidwe labwino. Koma kuchita zinthu mwa njira imeneyi, kungakhale kuiwala chilungamo cha Yehova. (Agal. 6:3, 4) Tiyenera kuchita zinthu zabwino chifukwa chokonda Yehova. Kuchita zinthu pongofuna kusonyeza kuti ndife olungama ndi umboni wakuti sitimukonda.​—Werengani Luka 16:15.

7. Kodi Yesu anachita chiyani pofuna kuthandiza anthu kuti apewe kudzilungamitsa?

7 Yesu sankasangalala ndi anthu “odziona ngati olungama amenenso amaona ena onse ngati opanda pake.” Pofuna kuthandiza anthu kuti apewe khalidweli ananena fanizo ili: “Anthu awiri anapita m’kachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi, winayo anali wokhometsa msonkho. Mfarisi uja anaimirira ndi kuyamba kupemphera mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’ Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’” Yesu anamaliza ndi mawu akuti: “Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”​—Luka 18:9-14.

Msampha wa Kukhala “Wolungama Mopitirira Muyezo”

8, 9. Kodi kukhala “wolungama mopitirira muyezo” kumatanthauza chiyani, ndipo kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

8 Msampha wina umene tiyenera kuupewa watchulidwa pa Mlaliki 7:16. Lembali limati: “Usakhale wolungama mopitirira muyezo kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri, kuopera kuti ungadzibweretsere chiwonongeko.” Wolemba Baibulo ameneyu anafotokoza chifukwa chimene tiyenera kupewa khalidwe limeneli mu vesi 20. Iye anati: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” Munthu “wolungama mopitirira muyezo” amakhazikitsa mfundo zake za chilungamo ndipo amaweruza ena malinga ndi mfundo zakezo. Koma sadziwa kuti pochita zimenezi amaika mfundo zake pamwamba pa mfundo za Mulungu ndipo izi zimachititsa kuti akhale wosalungama pamaso pa Mulungu.

9 Kukhala “wolungama mopitirira muyezo” kungachititse munthu kukayikira mmene Yehova amachitira zinthu zina. Tiyenera kukumbukira kuti tikamakayikira zoti Yehova amachita zinthu mwachilungamo timakhala tikunena kuti mfundo zathu ndi zapamwamba kuposa mfundo zolungama za Yehova. Zili ngati kuti tikumuzenga mlandu Yehova n’kumuweruza malinga ndi mfundo zathu pa nkhani ya chabwino ndi choipa. Koma Yehova ndi amene ali ndi udindo wokhazikitsa mfundo zolungama osati ifeyo.​—Aroma 14:10.

10. Mofanana ndi Yobu, kodi n’chiyani chingatichititse kuweruza Mulungu?

10 Ngakhale kuti palibe aliyense wa ife amene angafune kuweruza Mulungu, kupanda ungwiro kwathu kungachititse kuti tiyambe khalidwe limeneli. Tikhoza kuyamba khalidweli ngati zinthu zinazake zachitika ndipo tikuona kuti sizinachitike mwachilungamo, kapena ngati takumana ndi vuto linalake. Ngakhale Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika anayamba khalidwe limeneli. Poyamba Yobu anafotokozedwa kuti anali munthu “wopanda cholakwa, wowongoka mtima, woopa Mulungu ndiponso wopewa zoipa.” (Yobu 1:1) Koma kenako Yobu anakumana ndi mavuto motsatizanatsatizana amene anamuchititsa kuganiza kuti panalibe chilungamo. Izi zinachititsa Yobu kudziona kuti “anali wolungama, osati Mulungu.” (Yobu 32:1, 2) Yobu anayenera kuthandizidwa kuti aziona zinthu moyenera. Choncho sitiyenera kudabwa ngati nthawi zina tingakhale ndi maganizo ngati amenewa. Ngati zimenezi zitachitika, kodi n’chiyani chingatithandize kusintha maganizo athu?

Sitidziwa Zonse

11, 12. (a) Ngati tikuona kuti zinthu zina sizinachitike mwachilungamo, kodi tiyenera kukumbukira chiyani? (b) N’chifukwa chiyani munthu wina angaganize kuti fanizo la Yesu la anthu ogwira ntchito kumunda wa mpesa limasonyeza kupanda chilungamo?

11 Poyamba tiyenera kukumbukira kuti sitidziwa zonse. Ndi mmenenso zinthu zinalili ndi Yobu. Iye sankadziwa za misonkhano ya angelo a Mulungu kumwamba pamene Satana ankamuneneza. (Yobu 1:7-12; 2:1-6) Yobu sankadziwa kuti Satana ndiye ankachititsa mavuto ake. Ndipotu sitikudziwa ngati Yobu ankadziwa n’komwe zoona zake za Satana. Choncho ankaganiza kuti Mulungu ndiye ankachititsa mavuto ake. Ndiyetu n’zosavuta kukhala ndi maganizo olakwika ngati sitikudziwa zinthu zonse.

12 Taganizirani za chitsanzo cha Yesu cha anthu ogwira ntchito m’munda wa mpesa. (Werengani Mateyu 20:8-16.) M’fanizoli, Yesu anafotokoza za mwinimunda amene anapereka ndalama zofanana kwa antchito ake, kaya anali atagwira ntchito tsiku la thunthu kapena ola limodzi. Kodi inu mukuganiza bwanji pa nkhani imeneyi? Kodi pamenepa panachitika chilungamo? Mwina mukumvera chisoni anthu amene anagwira ntchito tsiku lonse kunja kukutentha kwambiri. N’zoona kuti iwo anafunika kupatsidwa ndalama zambiri. Tikaona nkhaniyi mwa njira imeneyi, tikhoza kunena kuti mwinimundayu ndi wopanda chikondi ndipo sanachite chilungamo. Ngakhalenso mawu amene anayankha antchito amene anadandaula angasonyeze kuti anali wamwano komanso wopondereza. Koma kodi tikudziwa zonse pa nkhaniyi?

13. Kodi tiyenera kuganiziranso zinthu ziti pa fanizo la Yesu la ogwira ntchito m’munda wa mpesa?

13 Tiyeni tionenso fanizoli. N’zosakayikitsa kuti mwinimunda wa m’fanizoli ankadziwa kuti anthu ogwira ntchitowo anafunika kupeza chakudya cha mabanja awo. M’nthawi ya Yesu, anthu ogwira ntchito kumunda ankapatsidwa malipiro tsiku ndi tsiku. Mabanja awo ankadalira malipiro a tsiku lililonse. Zimenezi zili m’maganizo, tiyeni tiganizire za anthu amene mwinimundayu anawapeza mochedwa omwe anagwira ntchitoyi kwa ola limodzi lokha. N’kutheka kuti iwo sakanatha kudyetsa banja lawo ndi malipiro a ola limodzi koma ankafunitsitsa kugwira ntchito ndipo anali atafufuza ntchito tsiku lonse. (Mat. 20:1-7) Iwo sanalephere mwadala kugwira ntchito tsiku lonse. Palibe umboni wosonyeza kuti ankazemba ntchito mwadala. Tayerekezerani kuti inuyo mukufufuza ntchito tsiku lonse ndipo anthu ambiri akudalira malipiro amene inuyo mulandire tsikulo. Kodi simungayamikire kwambiri ngati mutapeza ntchito? Nanga mungamve bwanji ngati mutalandira malipiro okwanira okuthandizani kudyetsa banja lanu?

14. Kodi fanizo la munda wa mpesa likutiphunzitsa mfundo yofunika iti?

14 Ndiyeno tiyeni tionenso zimene mwinimundayu anachita. Iye sanapereke ndalama zoperewera kwa munthu aliyense. Iye anaona kuti munthu aliyense ali ndi udindo wopeza ndalama zothandizira banja lake. Ngakhale kuti panali antchito ambirimbiri, mwinimundayu sanapezerepo mwayi woti agwiritse ntchito anthu n’kuwapatsa ndalama zochepa. Anthu onsewa anapita kwawo ali ndi ndalama zokwanira kugula chakudya cha mabanja awo. Kuganizira mfundo zimenezi kungatithandize kusintha maganizo athu pa zimene mwinimundayu anachita. Zimene anachitazi, zinasonyeza kuti anali wachikondi ndipo sanapondereze antchito ake. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzirapo kuti kungoganizira mfundo zochepa chabe kungatichititse kuganiza kuti zinthu sizinayende bwino. Fanizo limeneli likusonyeza kuti chilungamo cha Mulungu ndi chapamwamba kwambiri ndipo sichiyendera malamulo kapena mfundo zimene anthu amaona kuti n’zoyenera.

Tingaone Zinthu Molakwika Kapena Moperewera

15. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti tiziona zinthu molakwika kapena moperewera?

15 Ngati tikuona kuti nkhani inayake sinayende bwino, chinthu chachiwiri chimene tiyenera kukumbukira ndi chakuti, tingaone zinthu molakwika kapena moperewera. Zinthu monga kupanda ungwiro, tsankho, kapena chikhalidwe chathu zingachititse kuti tiziona zinthu molakwika. Tikhozanso kuona zinthu moperewera chifukwa chakuti sitidziwa bwinobwino zolinga za anthu ena ndiponso zimene zili mumtima mwawo. Koma Yehova ndi Yesu saona zinthu molakwika ndipo amadziwa zonse.​—Miy. 24:12; Mat. 9:4; Luka 5:22.

16, 17. Pa nthawi imene Davide anachita chigololo ndi Bati-seba, n’chifukwa chiyani Yehova sanaumirire lamulo lake?

16 Tiyeni tikambirane nkhani yokhudza tchimo la Davide ndi Bati-seba. (2 Sam. 11:2-5) Malinga ndi Chilamulo cha Mose, iwo anafunika kuphedwa. (Lev. 20:10; Deut. 22:22) Ngakhale kuti Yehova anawalanga, sanaumirire kuti lamulo lake litsatiridwe. Kodi pamenepa Yehova anachita chilungamo? Kodi anakondera Davide, n’kuphwanya mfundo Zake zolungama? Anthu ena akawerenga Baibulo amaganiza choncho.

17 Koma Yehova anapereka lamulo limeneli lokhudza chigololo kwa oweruza opanda ungwiro amene sankadziwa za mumtima mwa munthu. Ngakhale kuti anali opanda ungwiro, lamulo limeneli linawathandiza kuti nthawi zonse azipereka chiweruzo chofanana. Koma Yehova amadziwa zimene zili mumtima wa munthu. (Gen. 18:25; 1 Mbiri 29:17) Sitiyenera kuganiza kuti Yehova ayenera kutsatira ndendende malamulo amene anaikira oweruza opanda ungwiro. Kuchita zimenezi, kungafanane ndi kukakamiza munthu amene maso ake ali bwinobwino kuti azivala magalasi a anthu amene ali ndi vuto la maso. Yehova anaona bwinobwino zimene zinali mumtima wa Davide ndi Bati-seba ndipo anaonanso kuti iwo alapa zenizeni. Choncho, iye anawaweruza mogwirizana ndi zimenezo, mwachifundo ndiponso mwachikondi.

Pitirizani Kufunafuna Chilungamo cha Yehova

18, 19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamaweruze Yehova malinga ndi mfundo zimene ifeyo tikuona kuti ndi za chilungamo?

18 Nthawi zina zimene timawerenga m’Baibulo kapena zochitika pamoyo wathu zingatichititse kuganiza kuti Yehova sanachite chilungamo. Koma tisamaweruze Mulungu malinga ndi mfundo zimene ifeyo tikuona kuti ndi za chilungamo. Nthawi zonse tiyenera kukumbukira kuti sitidziwa zonse ndipo timaona zinthu molakwika kapena moperewera. Tisaiwale kuti “mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:19, 20) Tikamatero, mtima wathu ‘sudzakwiyira Yehova.’​—Miy. 19:3.

19 Mofanana ndi Yesu, tiyeni nthawi zonse tizivomereza kuti Yehova yekha ndiye woyenera kukhazikitsa mfundo za chilungamo ndiponso zabwino. (Maliko 10:17, 18) Yesetsani ‘kudziwa molondola’ mfundo zake. (Aroma 10:2; 2 Tim. 3:7) Tikamachita zimenezi ndiponso kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi chifuniro cha Yehova, timasonyeza kuti tikufunafuna choyamba “chilungamo chake.”​—Mat. 6:33.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Malinga ndi zimene katswiri wina analemba, mawu amene anawamasulira kuti “kukhazikitsa” angatanthauzenso ‘kuimiritsa chipilala.’ Choncho mophiphiritsira, Ayuda amenewa ankaimiritsa chipilala kuti anthu aziwatamanda m’malo motamanda Mulungu.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kufunafuna chilungamo cha Yehova?

• Kodi tiyenera kupewa misampha iwiri iti?

• Kodi tingafunefune bwanji chilungamo cha Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi fanizo la Yesu la anthu awiri amene anapemphera m’kachisi, likutiphunzitsa chiyani?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi kunali kupanda chilungamo kupereka malipiro ofanana kwa anthu amene anagwira ntchito tsiku lonse ndi amene anangogwira ola limodzi?