Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza munthu wina amene kale anali msilikali woukira boma komanso amene anali wakuba kuti asinthe khalidwe lake? N’chiyani chinathandiza mayi wina amene anali katswiri wa masewera a karate kuti asinthe zolinga zake pa moyo? Nanga kodi bambo wina anapindula bwanji chifukwa chokhulupirira kuti mwana wake adzasintha? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa.

“Ndikusangalala ngakhale kuti kale zinthu sizinkayenda bwino pa moyo wanga.”​—GARRY P. AMBROCIO

ZAKA: 47

DZIKO: PHILIPPINES

POYAMBA: NDINALI MSILIKALI WOUKIRA BOMA

KALE LANGA: Ndinakulira m’tauni ina yaing’ono yotchedwa Vintar. Tauni imeneyi inali m’chigwa chozunguliridwa ndi mapiri obiriwira ndiponso mitsinje ya madzi oyera. Komanso m’chigwachi munkawomba kamphepo kayaziyazi. Ngakhale kuti derali linali lokongola chonchi, tinkakhala movutika kwambiri. Anthu ankakonda kuba ziweto zathu komanso katundu wathu wa m’nyumba.

Ndili wachinyamata ndinkakonda kumwa kwambiri ndiponso kusuta ndi azinzanga. Pofuna kupeza ndalama zoti ndikamwere ndiponso kugulira fodya, ndinkaba ndalama za anthu ena. Ndinafika mpaka pobera agogo anga aakazi zinthu zodzikongoletsera zamtengo wapatali monga ndolo, zibangiri ndi zina zotere. Asilikali a boma anayamba kundikayikira kuti ndikugwirizana ndi gulu lina la asilikali oukira boma amene ankadziwika kuti New People’s Army (NPA). Chifukwa cha zimenezi sindinkati ndamenyedwa liti ndi asilikali a bomawa. Poona zimenezi, ndinaganiza zolowadi gulu loukira bomalo. Kwa zaka zisanu, ndinakhala ndili m’tchire, kudera lamapiri ndi gulu la NPA. Kumeneko moyo unali wovuta. Sitinkakhala malo amodzi chifukwa choopa asilikali a boma. Nditatopa ndi moyo umenewu, ndinapita kukadzipereka kwa gavanala wa chigawo cha Ilocos Norte. Gavanalayu anandilandira bwino ndipo anandithandiza kwambiri mpaka anandipezera ntchito yabwino. Koma ndinapitirizabe khalidwe langa loipa lija. Ndinkathyola nyumba za anthu ndiponso kuopseza anthu.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Kuntchito kwathu kunali mayi wina, dzina lake Loida, ndipo anali wa Mboni za Yehova. Mayi ameneyu ndi amene anachititsa kuti ndikumane ndi munthu wina dzina lake Jovencio amene anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Koma zinali zovuta kwambiri kuti ndisinthe khalidwe langa. Ndinkasuta fodya Jovencio asanafike kuti tiphunzire Baibulo komanso ndinkapitirizabe kuchita zinthu zophwanya malamulo. Kenako apolisi anandigwira ndipo ndinakhala m’ndende miyezi 11. Pa nthawi imeneyi, ndinapemphera kwa Yehova, kumuchonderera kuti andithandize. Ndinamupempha kuti andikhululukire ndiponso kuti andipatse mzimu wake woyera kuti unditsogolere komanso kundilimbikitsa.

Patapita nthawi munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera kudzandiona kundendeko ndipo anandipatsa Baibulo. Ndinaliwerenga ndipo ndinaphunzira kuti Yehova ndi wachifundo, wachikondi komanso amatikhululukira machimo. Ndinazindikira kuti Yehova wandichitira chifundo ndipo wandipatsa mwayi woti ndimudziwe. Ndinamupempha kuti andipatse mphamvu yondithandiza kusiya makhalidwe anga oipa. Zimene ndinawerenga pa Miyambo 27:11 zinandikhudza kwambiri. Ndinangomva ngati Yehova akulankhula ndi ineyo. Lemba limeneli limati: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”

Nditatuluka kundende ndinayambiranso kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, kupita ku misonkhano yawo komanso kutsatira zimene ndinkaphunzira m’Baibulo. Pa mapeto pake, mothandizidwa ndi Yehova, ndinasiya makhalidwe anga oipa aja. Kenako ndinadzipereka kwa Yehova Mulungu.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ngakhale kuti kale zinthu sizinkayenda bwino pa moyo wanga, tsopano ndikusangalala. Komanso ngakhale kuti poyamba ndinali kapolo wa makhalidwe oipa, tsopano ndasinthiratu ndipo ndine munthu watsopano. (Akolose 3:9, 10) Panopa ndimaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuti ndimasonkhana ndi anthu oyera a Yehova. Ndikuonanso kuti ndimwayi kuthandiza anthu ena kuphunzira za Mulungu wathu wamphamvu zonse, Yehova.

“Cholinga changa chinali kukaimira dziko la Brazil.”​—JULIANA APARECIDA SANTANA ESCUDEIRO

ZAKA: 31

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: NDINALI KATSWIRI WA MASEWERA A KARATE

KALE LANGA: Ndinakulira m’tauni ya Londrina. Ngakhale kuti anthu ambiri m’tauniyi anali osauka, dera lonseli linali laukhondo komanso anthu ankakhala mwamtendere. Nditakwanitsa zaka 10, m’bale wanga wamwamuna, yemwe anali wamkulu kwa ineyo anandilimbikitsa kuti ndiyambe kuphunzira masewera ena a karate otchedwa tae kwon do. Dzina limeneli limatanthauza “kumenyana ndi manja ndi mapazi.” Poyamba bambo anga sankasangalala kuti ndizichita masewera amenewa koma kenako anangondisiya.

Ndinkachita pulakatesi kwambiri, zimene zinachititsa kuti ndiwine mipikisano yambiri m’dera la Parana. Kenako ndinawina mipikisano yambiri m’dziko lonse la Brazil ndipo mu 1993, ndinakhala nambala wani pa akatswiri onse a tae kwon do m’dziko lonse la Brazil. Tsopano ndinkafunitsitsa kukapikisana ndi akatswiri a masewerawa a m’mayiko ena. Koma makolo anga anali osauka moti sakanatha kundilipirira ulendo wokachita nawo masewerawa kunja.

Ndinkakhulupirira kuti tsiku lina masewera amenewa azidzachitikanso pa masewera a Olimpiki, ndipo ndi zimene zinachitikadi pa mapeto pake. Ndinkafuna kukaimira Brazil ku masewera a Olimpiki, moti ndinalimbikira kwambiri pulakatesi. Chifukwa cha zimenezi anthu ena anandilipirira ulendo wanga wokachita nawo mipikisano ya tae kwon do ku France, Vietnam, South Korea, Japan ndiponso kumayiko ena a ku South America. Cholinga changa china chinali kukachita nawo tae kwon do pa mpikisano wotchedwa Pan American Games. Ndinakonzekera bwino kwambiri moti mu 2003, ndinakhala mmodzi mwa anthu atatu amene anasankhidwa kupita ku mpikisano umenewo ku Santo Domingo, m’dziko la Dominican Republic.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: M’chaka cha 2001 ine ndi mnyamata amene ndinali naye pa chibwenzi tinakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kutiphunzitsa Baibulo. Poyamba ndinalibe chidwi kwenikweni. Nthawi zonse ndinkakhala wotopa ndipo tikamaphunzira zinkandivuta kuika maganizo anga onse pa phunzirolo moti nthawi zambiri ndinkasinza. Koma ngakhale zinali choncho, zimene ndinkaphunzirazo zinandikhudza kwambiri ndipo zimenezi zinaonekera pa mpikisano wotsatira.

Popeza kuti ndinasankhidwa kukachita nawo mpikisano wa Pan American Games, aphunzitsi athu anakonza zoti ndikachite nawo masewera okonzekera mpikisano waukuluwo. Nthawi yanga yoti ndimenyane ndi munthu wina itakwana, ndinangoima chilili osachita chilichonse chifukwa ndinkaona kuti panalibe chifukwa chilichonse choti ndimenyane naye. Ndinakumbukira kuti Mkhristu sayenera kumenyana ndi anthu ena ngakhale pa masewera. Ndinakumbukiranso lamulo la m’Baibulo lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 19:19) Nthawi yomweyo ndinangochoka pamalo omenyaniranawo ndipo sindinaganizenso zobwerera. Anthu anangondiyang’anitsitsa chifukwa chosakhulupirira zimene ndinachitazo.

Nditafika kunyumba, ndinakhala pansi n’kuganiziranso zimene ndinayenera kuchita ndi moyo wanga. Ndinatenga kabuku kena ka Mboni za Yehova kamene kamafotokoza zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. M’kabukuka ndinapezamo lemba la Salimo 11:5 limene limanena kuti Yehova “amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” Mawu a wamasalimo amenewa anandikhudza mtima kwambiri moti ndinaganiza zosiyiratu masewera a tae kwon do.

Aphunzitsi anga sanasangalale nazo zimenezi. Iwo anayesetsa kundinyengerera kuti ndisinthe maganizo pondiuza kuti ndine nambala wani m’dziko lonse la Brazil. Ankandiuzanso kuti ndatsala pang’ono kukapikisana nawo ku masewera a Olimpiki. Koma ine ndinali nditasankha kale zochita.

Pa nthawi imeneyi n’kuti ineyo ndi mnyamata amene ndinali naye pa chibwenzi uja titakwatirana. Iye anali atayamba kale kulalikira limodzi ndi a Mboni. Ankabwera kunyumba ali wosangalala ndipo ankandiuza zinthu zonse zosangalatsa zimene wakambirana ndi anthu. Ndinkadziwa kuti ngati nanenso ndikufuna kugwira nawo ntchito imeneyi, ndiyenera kusintha moyo wanga. Choncho ndinatsanzika ku chipembedzo chimene ndinali ndipo kenako ndinabatizidwa, n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ine ndi mwamuna wanga ndife osangalala ndiponso ogwirizana chifukwa tikuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo m’banja mwathu. Ndimamuthandiza kuti agwire bwino ntchito yake yosamalira mpingo. Zinali zotheka kupata mendulo yagolide ndiponso kutchuka kwambiri. Koma ndikuona kuti palibe chimene dziko lopanda chilungamoli lingandipatse, chimene chingapose mwayi wotumikira Yehova Mulungu.

“Bambo anga sanataye chikhulupiriro choti ndidzasintha.”​—INGO ZIMMERMANN

ZAKA: 44

DZIKO: GERMANY

POYAMBA: NDINALI BAUNSA PAMALO ENA ACHISANGALALO

KALE LANGA: Ndinabadwira m’tauni yokhala ndi mgodi wa malasha [coal] ya Gelsenkirchen. Makolo anga anali mu zipembedzo zosiyana. M’banja mwathu tinalipo ana anayi, ineyo, m’bale wanga ndi alongo anga awiri. Bambo anga anali a Mboni za Yehova ndipo amayi ankadana ndi zoti iwo azitiphunzitsa zimene bambowo ankakhulupirira. Bambowo ankayendetsa mathiraki, ndipo tsiku lililonse ankagwira ntchito maola 10 kapena kuposa. Nthawi zambiri ankayamba ntchito 2 kapena 3 koloko m’mawa. Ngakhale zinali choncho, nthawi zonse iwo ankatiphunzitsa zinthu zauzimu. Koma ine ndinalibe nazo chidwi.

Nditakwanitsa zaka 15 ndinayamba kunyansidwa ndi misonkhano ya chipembedzo yomwe bambo anga ankandiuza kuti ndizipitako moti ndinasiya kuwamvera. Patatha chaka ndinalowa kalabu ya masewera a nkhonya. Pa zaka ziwiri zotsatira ndinkachita zinthu zimene bambo anga ankakhumudwa nazo kwambiri. Kenako nditakwanitsa zaka 18 ndinachoka panyumba.

Ndinkakonda kwambiri masewera moti ndinkachita pulakatisi maulendo 6 mlungu uliwonse. Choyamba ndinkachita pulakatisi masewera a nkhonya kenako ndinkanyamula zitsulo. Kumapeto kwa mlungu uliwonse ndinkapita ndi azinzanga m’malo osiyanasiyana achisangalalo. Tsiku lina tili ku malo ena achisangalalo, ndinamenyana ndi munthu wina wooneka woopsa, koma ndinamugwetsa mosavuta. Mwini wake wa malowo anaona zimenezi ndipo nthawi yomweyo anandilemba ntchito yoti ndizisungitsa chitetezo pamalopa. Popeza kuti malipiro ake anali abwino, ndinalola kuyamba ntchitoyi.

Ku mapeto kwa mlungu uliwonse ndinkaima pakhomo ndipo ndinali ndi mphamvu zolola kapena kuletsa munthu kulowa m’malo achisangalalowo. Ndinkakhala wotanganidwa kwambiri chifukwa pamalo amenewa pankafika anthu pafupifupi 1,000. Anthu sankati amenyana liti. Nthawi zambiri anthu ena ankandiopseza ndi mfuti kapena mabotolo osweka. Ena mwa amene ndinawakaniza kulowa kapena amene ndinawatulutsa ankandidikirira panja kuti abwezere. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 20 ndipo ndinkaona kuti palibe angandimenye. Koma kwenikweni ndinali wopulupudza chifukwa ndinali waukali, wonyada, wongofuna kutchuka ndiponso wouma mtima.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ngakhale kuti ndinkachita zimenezi, bambo anga sanataye chikhulupiriro choti ndidzasintha. Anakonza zoti kumene ndinkakhalako ndizilandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! * Koma ankangounjikika m’chipinda changa chifukwa sindinkawawerenga. Koma tsiku lina ndinaganiza zowerenga ena mwa magaziniwa. Ndinawerenga nkhani zonena za kutha kwa maboma, dongosolo la zamalonda komanso zipembedzo zimene zilipozi ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndiimbire foni mlongo wanga. Iyeyo ndi mwamuna wake anali a Mboni za Yehova. Iwo anadzipereka kuti aziphunzira nane Baibulo ndipo ndinavomera.

Mfundo imene ili pa Agalatiya 6:7 inandithandiza kwambiri kusintha. Malinga ndi zimene ndinakumana nazo pa moyo wanga, ndinadziwa kuti chilichonse chimene ndingachite, kunena kapena kusankha panopa, chidzakhala ndi zotsatira zake m’tsogolo. Komanso mfundo ya pa lemba la Yesaya 1:18 inandilimbikitsa kwambiri. Lembali limati: “Yehova akuti, ‘Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine. Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri. Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.’” Kungoyambira pamene ndinayamba kuphunzira, lemba limeneli linandithandiza kuti ndisamadzione kuti ndine wosafunika kapena kuganiza kuti sindingabwererenso kwa Yehova.

Mmene inkatha miyezi 6 n’kuti nditasintha kwambiri ngakhale kuti ndinafunika kuyesetsa kwambiri kuti ndichite zimenezi. Ndinafunika kusiya zoipa zonse zimene ndinkachita komanso kusiya kucheza ndi anthu amene ndinkacheza nawo poyamba. Choncho ndinayamba kuuza azinzanga kuti ndikuphunzira Baibulo komanso ndinkawauza zimene ndinkaphunzirazo. Chifukwa cha zimenezi iwo anasiya kucheza nane ndipo ankandinena kuti ndine wansembe. Mlongo wanga anandithandiza kupeza ntchito ina yabwino.

Ndinayamba kusonkhana ku Nyumba ya Ufumu kumene mlongo wangayo ndi mwamuna wake ankasonkhana ngakhale kuti unali ulendo wa makolomita 30 kuchokera kumene ndinkakhala. Pafupi ndi kwathu panali Nyumba ya Ufumu, koma sindinkapita kumeneko chifukwa ndinkaopa kukumana ndi anthu amene ankandidziwa kuyambira ndili mwana. Ndinkaopanso kulalikira nyumba ndi nyumba kudera lakwathu. Ndinkachita mantha kuti mwina ndingakumane ndi munthu amene ndinamutulutsa m’malo achisangalalo aja, kapena munthu amene ndinamupatsa mankhwala osokoneza bongo. Koma ndinagwiritsa ntchito mfundo imene ndinaphunzira pa masewera onyamula zitsulo yonena kuti, njira yovuta kwambiri yonyamulira zitsulo ndi imenenso imakhala yothandiza kwambiri. Choncho nditangoyenerera kugwira nawo ntchito imeneyi ndinayamba kulalikira.

Vuto linanso limene ndinafunika kulimbana nalo linali lakuti sindinkakonda kuwerenga ndiponso kuphunzira. Ndinkafuna kuti ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba koma ndinkadziwa kuti zimenezi zingatheke pokhapokha nditachita khama kuwerenga Baibulo. Ndinazindikiranso kuti mofanana ndi kunyamula zitsulo, pamafunika khama kuti munthu akhale wolimba mwauzimu.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Phindu loyamba ndi lakuti panopo ndidakali moyo. Koma nthawi ndi nthawi ndimafunika kusamala kuti ndisayambirenso makhalidwe oipa. Panopa ndili ndi banja labwino ndipo mkazi wanga ali ndi makhalidwe abwino kwambiri achikhristu. M’gulu la Mboni za Yehova, ndili ndi mabwenzi enieni ambiri amene ndimawakhulupirira. Bambo anga anamwalira zaka zisanu zapitazo koma asanamwalire anasangalala kundiona nditabwerera kwa Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 34 Magaziniwa amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.