Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu

Achinyamata, Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu

Achinyamata, Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu

“Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.”​—MIY. 4:5.

1, 2. (a) N’chiyani chinathandiza mtumwi Paulo kuthana ndi mavuto amene anakumana nawo? (b) Kodi mungatani kuti mupeze nzeru ndi luso lomvetsa zinthu?

“PAMENE ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” Kodi mukudziwa amene ananena mawu amenewa? Anali mtumwi Paulo. Ngakhale kuti Paulo ankakonda Yehova, nthawi zina ankavutika kuti achite zabwino. Kodi iye ankamva bwanji chifukwa cha mavuto amenewa? Iye analemba kuti: “Munthu wovutika ine!” (Aroma 7:21-24) Kodi mukumvetsa mmene Paulo anamvera? Kodi nanunso nthawi zina mumavutika kuti muchite zabwino? Zikatero, kodi mumakhumudwa ngati mmene Paulo anachitira? Ngati zili choncho musataye mtima. Paulo anathana ndi mavuto amene anakumana nawowa ndipo inunso mukhoza kuthana nawo.

2 Paulo anathana ndi mavutowa chifukwa chakuti analola kutsogoleredwa ndi “mawu olondola.” (2 Tim. 1:13, 14) Zotsatira zake zinali zakuti anapeza nzeru ndiponso luso lomvetsa zinthu. Izi zinamuthandiza kupirira mavuto amene anakumana nawo komanso kusankha zochita mwanzeru. Yehova Mulungu angakuthandizeni kupeza nzeru ndiponso luso lomvetsa zinthu. (Miy. 4:5) Iye wapereka malangizo abwino kwambiri m’Mawu ake, Baibulo. (Werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.) Tiyeni tione mmene mungapindulire ndi mfundo za m’Malemba pochita zinthu ndi makolo anu, pogwiritsa ntchito ndalama ndiponso mukakhala nokha.

Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu

3, 4. N’chifukwa chiyani mumavutika kutsatira malamulo a makolo anu, nanga n’chifukwa chiyani makolo amapereka malamulo?

3 Kodi zimakuvutani kutsatira malamulo a makolo anu? N’chifukwa chiyani zimakuvutani? Chifukwa china chingakhale chakuti mumafuna kuti nthawi zina muzisankha nokha zinthu. Maganizo amenewa si olakwika ayi. Ndi umboni wakuti mukukula. Koma pamene mukukhalabe panyumba ya makolo anu muyenera kuwamvera.​—Aef. 6:1-3.

4 Kumvetsa bwino malamulo a makolo anu komanso zimene amafuna kuti muzichita kungathandize kuti musamavutike kuwamvera. N’zoona kuti nthawi zina mungakhale ndi maganizo amene mtsikana wina dzina lake Brielle * wa zaka 18 anali nawo. Pofotokoza za makolo ake iye anati: “Iwo amachita zinthu ngati kuti sanakhalepo pa msinkhu wangawu. Safuna kuti ndizinena maganizo anga pa nkhani zina, ndizisankha ndekha zochita kapena ndizichita zinthu ngati munthu wamkulu.” Mofanana ndi Brielle, mwina inunso mumaona kuti makolo anu sakupatsani ufulu umene mumafuna. Komabe makolo anu amapereka malamulo chifukwa chakuti amakuderani nkhawa. Kuwonjezera pamenepo, makolo achikhristu amadziwa kuti adzayankha mlandu kwa Yehova ngati sakusamalirani bwino.​—1 Tim. 5:8.

5. Kodi mungapindule bwanji chifukwa chomvera makolo anu?

5 Kumvera malamulo a makolo anu kuli ngati kubweza ngongole ku bungwe lokongoza ndalama. Mukamabweza ngongoleyo mokhulupirika bungwelo limakukhulupirirani ndipo lingakubwerekeninso zina. Mofanana ndi zimenezi muyenera kulemekeza ndiponso kumvera makolo anu. (Werengani Miyambo 1:8.) Mukamawamvera kwambiri, iwonso azikukhulupirirani ndipo azikupatsani ufulu waukulu. (Luka 16:10) Koma ngati nthawi zambiri simuwamvera, iwo sangakupatseni ufulu umene mumafuna.

6. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale omvera?

6 Chinthu china chimene chingathandize ana kumvera malamulo a makolo awo ndi chitsanzo chimene makolowo amasonyeza. Makolo akamamvera malamulo a Yehova mochokera pansi pa mtima, amasonyeza kuti malamulo ake ndi abwino. Izi zingathandize anawo kuonanso kuti malamulo a makolo awo ndi abwino. (1 Yoh. 5:3) Ndipotu Baibulo limafotokoza nkhani zina pamene Yehova anapatsa atumiki ake mwayi wofotokoza maganizo awo. (Gen. 18:22-32; 1 Maf. 22:19-22) Zimenezi zikusonyeza kuti makolo nawonso ayenera kupatsa mwayi ana awo wofotokoza maganizo awo pa nkhani zina.

7, 8. (a) Kodi achinyamata ena amakhumudwa ndi zinthu ziti? (b) Fotokozani chinthu chofunika kuchizindikira kuti muzitsatira malangizo.

7 Ana amakhumudwanso chifukwa choona kuti amadzudzulidwa ndi makolo awo popanda zifukwa zomveka. Nthawi zina mungakhale ndi maganizo ngati amene mnyamata wina dzina lake Craig anali nawo. Iye anati: “Amayi anga ankangokhala ngati wapolisi wofufuza milandu, nthawi zonse ankangofuna kundipezera zifukwa.”

8 Nthawi zambiri makolo akamawongolera kapena kulangiza ana awo zimakhala ngati akuwadzudzula. Baibulo limavomereza kuti chilango chimakhala chowawa ngakhale chitakhala choyenerera. (Aheb. 12:11) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzitsatira malangizo amene mwapatsidwa? Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti makolo anuwo amapereka malangizo chifukwa chokukondani. (Miy. 3:12) Iwo amafuna kukuthandizani kuti musakhale ndi makhalidwe oipa koma kuti mukhale ndi makhalidwe abwino. Makolo anu amadziwa kuti ngati sakulangizani ndiye kuti sakukondani. (Werengani Miyambo 13:24.) Muyenera kudziwanso kuti nthawi zina timaphunzira zambiri pamene talakwitsa n’kupatsidwa malangizo. Ndiye ngati mukupatsidwa malangizo ndi bwino kusankhapo mfundo zanzeru m’malangizowo. Baibulo limati: “Kupeza nzeru monga phindu n’kwabwino kuposa kupeza siliva monga phindu, ndipo kukhala nazo monga zokolola n’kwabwino kuposa kukhala ndi golide.”​—Miy. 3:13, 14.

9. M’malo mongoganizira zinthu zimene zikuoneka kuti si zachilungamo, kodi achinyamata ayenera kuchita chiyani?

9 Koma nthawi zina makolo amalakwitsa zinthu. (Yak. 3:2) Mwina nthawi zina angalankhule mosaganizira pokulangizani. (Miy. 12:18) Kodi n’chiyani chingachititse makolo anu kulankhula m’njira imeneyi? Mwina angakhale atapanikizika ndi zinthu zina kapena angamaganize kuti inu mwalakwitsa chifukwa chakuti iwo alephera kukuthandizani. M’malo mongoganizira zinthu zimene mukuona ngati sanachite mwachilungamo, muyenera kuyamikira kuti iwo akuyesetsa kukuthandizani. Kukhala ndi mtima wolandira malangizo kudzakuthandizani mukadzakula.

10. Kodi mungatani kuti musamavutike kutsatira malamulo ndi malangizo a makolo anu?

10 Kodi mumafuna kuti musamavutike kutsatira malamulo ndi malangizo a makolo anu? Ngati ndi choncho muyenera kuphunzira kulankhulana bwino. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Poyamba muyenera kumvetsera mwatcheru zimene makolo anu akunena. Baibulo limati: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yak. 1:19) M’malo modziikira kumbuyo, yesetsani kukhala chete ndi kumvetsera zimene makolo anu akunena. Maganizo anu azikhala pa zimene akulankhula osati mmene akulankhulira. Kenako ayankheni mwaulemu ndi kuwatsimikizira kuti mwamva zimene anenazo. Koma bwanji ngati mukufuna kufotokoza chifukwa chimene mwanenera kapena kuchita zinazake? Nthawi zambiri ndi bwino ‘kulamulira milomo yanu’ kapena kuti kukhala chete mpaka mutasonyeza kuti mutsatira zimene makolo anu akufuna. (Miy. 10:19) Makolo anu akaona kuti mwawamvetsera iwonso adzakumvetserani mukamalankhula. Kuchita zinthu mwa njira imeneyi kudzasonyeza kuti mukutsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu.

Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu Pogwiritsa Ntchito Ndalama

11, 12. (a) Kodi Mawu a Mulungu amapereka malangizo otani pa nkhani ya ndalama ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi makolo anu angakuthandizeni bwanji kugwiritsa ntchito bwino ndalama?

11 Baibulo limanena kuti, ‘ndalama zimateteza.’ Koma vesi lomweli limanenanso kuti nzeru ndi yofunika kwambiri kuposa ndalama. (Mlal. 7:12) Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiziona ndalama kuti n’zofunika koma tisamazikonde. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kukonda ndalama? Taganizirani chitsanzo ichi. Mpeni ndi chipangizo chothandiza kwambiri kukhitchini. Koma mpeni womwewo ungavulaze munthu amene sakuugwiritsa ntchito bwino. N’chimodzimodzinso ndi ndalama. Ngati mukudziwa kuzigwiritsa ntchito bwino zingakuthandizeni kwambiri. Koma anthu “ofunitsitsa kulemera” nthawi zambiri amawononga ubwenzi wawo ndi anthu ena, ndi banja lawo ndiponso ndi Mulungu. Zotsatira zake n’zakuti amadzibweretsera “zopweteka zambiri pathupi lawo.”​—Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.

12 Kodi mungaphunzire bwanji kugwiritsa ntchito bwino ndalama? Mwina mungafunse makolo anu mmene mungachitire zimenezi. Solomo analemba kuti: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka, ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake.” (Miy. 1:5) Mtsikana wina dzina lake Anna anapempha malangizo kwa makolo ake ndipo iye anati: “Bambo anga anandiphunzitsa kupanga bajeti komanso anandiuza kufunika kogwiritsa ntchito ndalama mwanzeru m’banja.” Mayi ake anamuphunzitsanso zinthu zina zofunika kwambiri. Ponena za mayi ake iye anati: “Anandiphunzitsa kuti ndisanagule chinthu, ndizifufuza kaye m’malo osiyanasiyana kuti ndiyerekezere mitengo yake.” Kodi zimenezi zamuthandiza bwanji Anna? Iye anati: “Panopa ndaphunzira kusawononga ndalama ndipo zimenezi zandithandiza kukhala ndi mtendere wa m’maganizo chifukwa sindikhala ndi ngongole zosafunikira.”

13. Kodi mungatani kuti musamawononge ndalama?

13 Mukamangogula zinthu zilizonse zimene mwaona kapena kugula zinthu kuti mugometse anzanu, mudzakhala ndi ngongole zambiri. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupewa zimenezi? Muyenera kukhala odziletsa pa nkhani yogwiritsa ntchito ndalama. Izi n’zimene mtsikana wina wa zaka za m’ma 20, dzina lake Ellena amachita. Iye anati: “Ndisanapite koyenda ndi anzanga, ndimawerengetseratu ndalama zimene ndikufuna kukagwiritsa ntchito. . . . Ndinaonanso kuti ndi bwino kupita kogula zinthu ndi anzanga amene amagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru, ndipo amandilimbikitsa kuyerekezera kaye mitengo ndisanagule chinthu.”

14. N’chifukwa chiyani muyenera kusamala kwambiri ndi “chinyengo champhamvu cha chuma”?

14 Kupeza ndalama ndi kuzigwiritsa ntchito bwino n’kofunika kwambiri. Koma Yesu ananena kuti anthu “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” ndi amene amakhala osangalala. (Mat. 5:3) Iye anachenjeza kuti zinthu monga “chinyengo champhamvu cha chuma” zingalepheretse munthu kukhala ndi chidwi chochita zinthu zauzimu. (Maliko 4:19) Choncho ndibwino kuti Mawu a Mulungu azikutsogolerani kuti muziona ndalama m’njira yoyenera.

Mawu a Mulungu Azikutsogolerani Mukakhala Nokha

15. Kodi ndi nthawi iti pamene mungayesedwe kwambiri pa nkhani yokhala okhulupirika kwa Mulungu?

15 Kodi inu mumaona kuti mungayesedwe kwambiri pa nkhani yokhala wokhulupirika pamaso pa Mulungu pa nthawi imene muli ndi anthu ena kapena mukakhala nokha? Mukakhala kusukulu kapena kuntchito mosakayikira mumakhala wosamala ndi zinthu zimene zingawononge ubwenzi wanu ndi Mulungu. Koma pa nthawi imene mukupumula panokha ndiponso pamene simuli tcheru kwambiri ndi pamene mungagonje mosavuta poyesedwa.

16. N’chifukwa chiyani muyenera kumvera Yehova ngakhale pamene muli nokha?

16 N’chifukwa chiyani muyenera kumvera Yehova ngakhale pamene muli nokha? Kumbukirani izi: Zochita zanu zingachititse kuti mukondweretse mtima wa Yehova kapena kumumvetsa chisoni. (Gen. 6:5, 6; Miy. 27:11) Zochita zanu zimakhudza Yehova chifukwa chakuti iye “amakuderani nkhawa.” (1 Pet. 5:7) Iye amafuna kuti muzimumvera n’cholinga choti zinthu zikuyendereni bwino. (Yes. 48:17, 18) Atumiki a Yehova m’nthawi ya Aisiraeli akanyalanyaza malangizo ake, Yehova ankamva chisoni. (Sal. 78:40, 41) Koma Yehova ankakonda kwambiri mneneri Danieli moti mngelo anamuuza kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 10:11) N’chifukwa chiyani zinali choncho? Danieli anali wokhulupirika kwa Mulungu akakhala pagulu komanso akakhala payekha.​—Werengani Danieli 6:10.

17. Kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati posankha zosangalatsa?

17 Kuti mukhale wokhulupirika kwa Mulungu pamene muli nokha muyenera kuphunzitsa “mphamvu zanu za kuzindikira . . . kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” Muyeneranso kuphunzitsa mphamvuzo mwa ‘kuzigwiritsa ntchito’ n’kumachita zimene mukudziwa kuti n’zolondola. (Aheb. 5:14) Mwachitsanzo, posankha nyimbo, mafilimu kapena malo ena pa Intaneti, mafunso otsatirawa ndi amene angakuthandizeni kusankha zoyenera ndi kupewa zolakwika. Dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi zingandithandize kukhala ndi chifundo chachikulu kapena zingandichititse kusangalala ndi “tsoka la wina”?’ (Miy. 17:5) ‘Kodi zingandithandize “kukonda chabwino” kapena zingandilepheretse “kudana ndi choipa”?’ (Amosi 5:15) Zimene mumachita mukakhala nokha n’zimene zimasonyeza zinthu zimene mumaona kuti n’zofunika.​—Luka 6:45.

18. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwakhala mukuchita tchimo mwamseri, ndipo n’chifukwa chiyani?

18 Kodi muyenera kutani ngati mukudziwa kuti mwakhala mukuchita zinthu zina zolakwika mwamseri? Kumbukirani kuti “wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.” (Miy. 28:13) Kungakhale kupanda nzeru ngati tingapitirize kuchita machimo ‘n’kumamvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu.’ (Aef. 4:30) Ndi udindo wanu kuvomereza ndiponso kuulula machimo anu kwa Mulungu ndiponso kwa makolo anu. Pa nkhani imeneyi “akulu a mpingo” angakuthandizeni kwambiri. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu anati: “Iwo amupempherere [munthu wochimwayo] ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14, 15) N’zoona kuti zotsatira zake zingakhale zochititsa manyazi mwinanso zokhumudwitsa. Koma ngati mungalimbe mtima n’kupempha thandizo mudzachita bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti mudzapewa mavuto ena amene angabwere ndipo mudzakhalanso ndi mtendere wa mumtima umene munthu amakhala nawo chifukwa cha chikumbumtima choyera.​—Sal. 32:1-5.

Muzikondweretsa Mtima wa Yehova

19, 20. Kodi Yehova amakufunirani zotani, nanga kodi muyenera kuchita chiyani?

19 Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” ndipo amafuna kuti inunso mukhale achimwemwe. (1 Tim. 1:11) Iye amakufunirani zabwino. Ngakhale anthu ena asaone khama lanu pochita zinthu zabwino, iye amaona. Palibe chimene Yehova saona. Iye amakuyang’anani osati n’cholinga chokupezerani zifukwa koma kuti akuthandizeni kuchita zinthu zabwino. Baibulo limati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.

20 Motero, lolani kuti Mawu a Mulungu azikutsogolerani ndipo muzitsatira malangizo ake. Mukatero mudzapeza nzeru ndi luso lomvetsa zinthu. Zimenezi zidzakuthandizani kuthana ndi mavuto akuluakulu ndiponso kusankha zinthu mwanzeru pa nkhani zikuluzikulu. Izi zidzachititsa kuti musangalatse makolo anu ndiponso Yehova komanso kuti mukhale osangalala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mayina tawasintha.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi achinyamata angatani kuti asamavutike kutsatira malamulo ndi malangizo a makolo awo komanso kuti apindule nawo?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuona ndalama moyenera?

• Kodi mungatani kuti mukhalebe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene muli nokha?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi mudzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu pamene muli nokha?