Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika

Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika

Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika

“Koma ine ndidzayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.”​—SAL. 26:11.

1, 2. Kodi Yobu ananena chiyani pa nkhani ya kukhala ndi mtima wosagawanika ndipo kodi mawu ake a mu chaputala 31 amasonyeza chiyani?

KALE anthu ankagwiritsa ntchito sikelo ngati imene anthu masiku ano amagwiritsa ntchito pogulitsa nyama pamsika. Sikeloyi inkakhala ndi kandodo ndipo ankapachika mbale kumbali zonse ziwiri. M’mbale ina ankaikamo kamwala ndipo m’mbale ya mbali inayo ankaikamo zinthu zimene akuyeza. Anthu a Mulungu ankafunika kugwiritsa ntchito sikelo yolondola.​—Miy. 11:1.

2 Pamene munthu wokhulupirika Yobu ankavutitsidwa ndi Satana, ananena kuti: “[Yehova] adzandiyeza pasikelo zolondola, ndipo Mulungu adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 31:6) Pa nkhani imeneyi, Yobu anatchula zinthu zingapo zimene zingayese munthu wa mtima wosagawanika. Mawu a Yobu m’chaputala 31 amasonyeza kuti iye anapambana mayeserowo. Chitsanzo chake chabwino chingatithandize kuchitanso chimodzimodzi ndiponso kulankhula molimba mtima ngati wamasalimo Davide amene ananena kuti: “Koma ine ndidzayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.”​—Sal. 26:11.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale pa zinthu zazing’ono?

3 Ngakhale kuti Yobu anayesedwa koopsa iye anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Ena amanena kuti Yobu ndi chitsanzo chapamwamba kwambiri pa nkhani yokhalabe ndi mtima wosagawanika atayesedwa modetsa nkhawa. Ife sitikumana ndi mavuto ofanana ndendende ndi amene Yobu anakumana nawo. Koma kuti tikhalebe ndi mtima wosagawanika ndiponso kuti tikhale kumbali ya ulamuliro wa Mulungu, tiyenera kukhala okhulupirika ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono.​—Werengani Luka 16:10.

Tiyenera Kupewa Chiwerewere

4, 5. Kuti akhalebe ndi mtima wosagawanika, kodi Yobu anapewa khalidwe liti?

4 Kuti titumikire Mulungu ndi mtima wosagawanika tiyenera kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino ngati mmene Yobu anachitira. Iye anati: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali? Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ndipo ndinali kudikirira pakhomo lolowera kunyumba kwa mnzanga, mkazi wanga aperere ufa mwamuna wina, ndipo amuna ena agone naye.”​—Yobu 31:1, 9, 10.

5 Pofuna kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, Yobu anapewa kuyang’anitsitsa mkazi mpaka kufika pofuna kugona naye. Yobu anali wokwatira ndipo sankakopa akazi osakwatiwa kapena kukhala ndi mtima wosirira mkazi wa mwini. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anafotokoza mfundo yamphamvu kwambiri pa nkhani ya chiwerewere. Anthu onse amene akufuna kukhala ndi mtima wosagawanika sayenera kuiwala mfundo imeneyi.​—Werengani Mateyu 5:27, 28.

Pewani Kuchita Chinyengo

6, 7. (a) Kodi nkhani ya Yobu ikusonyeza kuti Mulungu amagwiritsa ntchito chiyani potiyeza ngati tili ndi mtima wosagawanika? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa chinyengo?

6 Ngati tikufuna kukhala anthu a mtima wosagawanika tiyenera kupewa kuchita zinthu zachinyengo. (Werengani Miyambo 3:31-33.) Yobu anati: “Ngati ndayenda ndi anthu osanena zoona, ndipo phazi langa lathamangira ku chinyengo, iye [Yehova] adzandiyeza pasikelo zolondola, ndipo Mulungu adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 31:5, 6) Yehova amayeza anthu “pasikelo zolondola.” Monga mmene anachitira ndi Yobu, Mulungu amatiyeza mwachilungamo kuona ngati tikumutumikira ndi mtima wosagawanika.

7 Ngati titachita zinthu zachinyengo ndiye kuti sitingatumikire Mulungu ndi mtima wosagawanika. Anthu a mtima wosagawanika ‘amasiya zinthu zochititsa manyazi zochitikira mseri, ndipo sayenda mwachinyengo.’ (2 Akor. 4:1, 2) Koma bwanji ngati timalankhula kapena kuchitira Mkhristu mnzathu zinthu zachinyengo zomwe zingamuchititse kupempha Mulungu kuti amuthandize? Zotsatira zake zingakhale zoopsa kwambiri. Wamasalimo anaimba kuti: “Ndinafuulira Yehova m’masautso anga, ndipo iye anandiyankha. Inu Yehova, ndilanditseni ku milomo yonama, ndi ku lilime lachinyengo.” (Sal. 120:1, 2) Tiyenera kukumbukira kuti Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu ndipo “amayesa mtima ndi impso” kuti aone ngati tilidi ndi mtima wosagawanika.​—Sal. 7:8, 9.

Perekani Chitsanzo Chabwino Pochita Zinthu ndi Ena

8. Kodi Yobu ankachita bwanji zinthu ndi ena?

8 Kuti tikhalebe ndi mtima wosagawanika, tiyenera kukhala achilungamo, odzichepetsa komanso achifundo ngati mmene Yobu analili. Iye anati: “Ngati ndinkalepheretsa chiweruzo cha kapolo wanga wamwamuna, kapena cha kapolo wanga wamkazi pa mlandu ndi ine, ndiye ndingatani Mulungu akaimirira, ndipo akandifunsa ndingamuyankhe chiyani? Kodi amene anandipanga m’mimba si amene anapanganso iyeyo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe m’mimba?”​—Yobu 31:13-15.

9. Kodi Yobu ankasonyeza akapolo ake makhalidwe ati ndipo kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimenezi?

9 Pa nthawi ya Yobu panali njira zosavuta kutsatira poweruza milandu. Milandu inkaweruzidwa bwino ndipo panalinso makhoti a akapolo. Pochita zinthu ndi akapolo Yobu anali wachilungamo komanso wachifundo. Ngati tikufuna kukhala ndi mtima wosagawanika tiyenera kusonyeza makhalidwe amenewa. Makhalidwewa ndi ofunika kwambiri makamaka kwa akulu mumpingo.

Khalani ndi Mtima Wopatsa Osati Wansanje

10, 11. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yobu anali wopatsa ndiponso wokonda kuthandiza ena? (b) Kodi lemba la Yobu 31:16-25 likutikumbutsa malangizo ati a m’Malemba amene anadzaperekedwa pambuyo pake?

10 Yobu anali ndi mtima wopatsa ndiponso wofuna kuthandiza ena. Iye sanali wodzikonda kapena wansanje. Yobu anati: “Ngati ndinkachititsa chisoni maso a mkazi wamasiye, ngati ndinkanyema chakudya changa n’kumadya ndekha, mwana wamasiye osadya nawo . . . ngati ndinkaona munthu akuzunzika chifukwa chosowa chovala, . . . ngati ndili pachipata ndinaonapo mwana wamasiye akufunika thandizo langa, koma ine n’kumuopseza ndi dzanja langa fupa la paphewa langa ligwe kuchoka m’malo mwake, ndipo fupa la kumtunda la dzanja langa lithyoke.” Apa zikuoneka kuti Yobu akanakhala ndi mtima wogawanika akananena kwa golide kuti “ndimadalira iwe.”​—Yobu 31:16-25.

11 Mawu a ndakatulo amenewa akutikumbutsa mawu a Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu akuti: “Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo, ndi kukhala wopanda banga la dzikoli.” (Yak. 1:27) Ndi bwinonso kukumbukira chenjezo la Yesu lakuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” Kenako Yesu anapereka fanizo la munthu wachuma amene anali ndi khalidwe la kusirira kwa nsanje koma ‘sanali wolemera kwa Mulungu’ pamene ankafa. (Luka 12:15-21) Kuti tipitirize kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika tiyenera kupewa dyera ndiponso kusirira kwa nsanje. Kusirira kwa nsanje n’kofanana ndi kulambira mafano. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene amasirira chinthu mwansanje amachikonda ndiponso kuchiganizira kwambiri kuposa Yehova. Choncho chinthucho chimakhala ngati fano limene akulilambira. (Akol. 3:5) Mtima wosagawanika suyendera limodzi ndi mtima wadyera.

Musasiye Kulambira Koona

12, 13. Kodi Yobu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yopewa mafano?

12 Anthu a mtima wosagawanika sasiya kulambira koyera. Yobu sanachite zimenezi chifukwa ananena kuti: “Ngati ndinkaona kuwala kukamanyezimira, kapena mwezi wamtengo wapatali ukuyenda, ndipo mtima wanga unayamba kukopeka mobisa, komanso dzanja langa linapsompsona pakamwa panga chimenechonso chikanakhala cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza, chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba.”​—Yobu 31:26-28.

13 Yobu sankalambira zinthu zopanda moyo. Ngati mtima wake ukanayamba kukopeka mobisa ataona zinthu zakumwamba monga mwezi kapena ngati ‘dzanja lake likanapsompsona pakamwa pake,’ mwina posonyeza kulambira chinachake, akanakhala wolambira mafano amene anakana Mulungu. (Deut. 4:15, 19) Kuti titumikire Mulungu ndi mtima wosagawanika, tiyenera kupewa mafano a mtundu uliwonse.​—Werengani 1 Yohane 5:21.

Pewani Mtima Wobwezera Kapena Wachiphamaso

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yobu sankafunira ena zoipa?

14 Yobu sankafunira ena zoipa ndipo sanali wankhanza. Iye ankadziwa kuti munthu amene ali ndi mtima wosagawanika amapewa makhalidwe amenewa. Iye anati: “Ngati ndinkasangalala ndi kutha kwa munthu amene ankadana nane kwambiri, kapena ngati ndinkakondwera chifukwa chakuti zoipa zam’gwera . . . ine sindinalole m’kamwa mwanga kuchimwa, popempha lumbiro loipira moyo wake.”​—Yobu 31:29, 30.

15. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusangalala munthu amene amatida akakumana ndi tsoka?

15 Yobu anali wolungama ndipo sankasangalala munthu amene ankamuda akakumana ndi tsoka. Mwambi wina wa m’Baibulo umanena kuti: “Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere, kuti Yehova angaone ndipo zingamuipire m’maso mwake n’kuchotsa mkwiyo wake pa mdani wakoyo.” (Miy. 24:17, 18) Popeza Yehova amaona mumtima, amadziwa ngati tikusangalala chifukwa cha tsoka limene lagwera munthu wina ndipo iye sangasangalale ndi mtima umenewo. (Miy. 17:5) Zikatero, Mulungu akhoza kutilanga chifukwa amati: “Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.”​—Deut. 32:35.

16. Kodi tingakhale bwanji ochereza ngakhale titakhala kuti sindife olemera?

16 Yobu anali ndi mtima wochereza. (Yobu 31:31, 32) Ngakhale kuti sindife olemera, tikhoza ‘kukhala ochereza.’ (Aroma 12:13) Tikhoza kugawana ndi ena zinthu zochepa zimene tili nazo podziwa kuti, “ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.” (Miy. 15:17) Kudya chakudya chosalira zambiri koma pali mtendere ndi mtumiki mnzathu wokhulupirika kumakhala kosangalatsa ndiponso kopindulitsa mwauzimu.

17. Ngati tachita tchimo lalikulu n’chifukwa chiyani sitiyenera kubisa?

17 Anthu ayenera kuti ankalimbikitsidwa mwauzimu akamacherezedwa ndi Yobu chifukwa chakuti iye sanali munthu wachinyengo. Iye sanali ngati anthu osaopa Mulungu amene ‘ankatamandanso anthu ena n’cholinga choti apezepo phindu.’ (Yuda 3, 4, 16) Yobu ‘sankabisanso machimo ake m’thumba la malaya’ poopa kuti anthu sangamulemekeze ngati atadziwa za tchimolo. Iye ankafunitsitsa kuyezedwa ndi Mulungu amene akanatha kumupempha kuti amukhululukire machimo ake. (Yobu 31:33-37) Ngati titachita tchimo lalikulu sitiyenera kubisa chifukwa choopa kuchita manyazi. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufuna kukhalabe ndi mtima wosagawanika? Tingatero mwa kuvomereza machimo athu, kulapa, kupempha thandizo lauzimu ndiponso kuchita zonse zimene tingathe kuti tikonze zimene zinalakwikazo.​—Miy. 28:13; Yak. 5:13-15.

Munthu Wokhulupirika Anapempha Kuimbidwa Mlandu

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yobu sankadyera anthu masuku pamutu? (b) Kodi Yobu anali wokonzeka kutani ngati akanapezeka wolakwa?

18 Yobu anali woona mtima ndiponso wachilungamo. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ngati nthaka yanga ikanandilirira popempha thandizo, ndipo ngati mizere yake ikanalirira pamodzi, ngati ndadya zipatso zake osapereka ndalama, ndipo ndachititsa moyo wa olima ake kupumira m’mwamba, m’malo mwa tirigu, pamere chitsamba chaminga, ndipo m’malo mwa balere, pamere zitsamba zonunkha.” (Yobu 31:38-40) Yobu sankalanda minda ya anthu ndipo antchito ake sankawadyera masuku pamutu. Mofanana ndi Yobu tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova pa zinthu zikuluzikulu ngakhalenso zing’onozing’ono.

19 Yobu anafotokozera anzake atatu komanso Elihu amene anali wachinyamata, zimene ankachita pa moyo wake. Yobu anapempha kuti munthu wina amuimbe mlandu mwa kulemba mfundo zotsutsa mbiri ya moyo wake, yomwe inali ngati chikalata chosainidwa ndi Yobuyo. Yobu anali wokonzeka kulandira chilango ngati atapezeka kuti ndi wolakwa. Choncho anafotokoza mbali yake pa mlanduwu n’kumayembekeza kuti Mulungu amuweruze ndipo ‘mawu a Yobu anathera pamenepa.’​—Yobu 31:35, 40.

Mukhoza Kukhala Wokhulupirika

20, 21. (a) N’chiyani chinathandiza Yobu kukhalabe ndi mtima wosagawanika? (b) Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri Mulungu?

20 Yobu anakhalabe wokhulupirika chifukwa chakuti ankakonda Mulungu ndipo Yehova ankamukonda komanso kumuthandiza. Yobu anati: “Mwandipatsa moyo ndi kundisonyeza kukoma mtima kosatha [Yehova], ndipo mwa kundisamalira mumateteza moyo wanga.” (Yobu 10:12) Yobu ankakondanso anthu chifukwa chozindikira kuti munthu amene sakomera mtima anzake ndiye kuti saopa Wamphamvuyonse. (Yobu 6:14) Anthu amene ali ndi mtima wosagawanika amakonda Mulungu ndiponso anzawo.​—Mat. 22:37-40.

21 Tingakulitse chikondi chathu kwa Mulungu mwa kuwerenga Mawu ake tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha mfundo zokhudza Mulungu zimene timamva m’Mawu akewo. Tiyenera kutamanda Yehova ndiponso kumuthokoza m’pemphero lochokera pansi pa mtima chifukwa cha zabwino zimene amatichitira. (Afil. 4:6, 7) Tikhoza kuimbira Yehova nyimbo ndiponso kupindula kwambiri chifukwa chosonkhana ndi anthu ake. (Aheb. 10:23-25) Tikhoza kuyamba kukonda kwambiri Mulungu ngati tikugwira nawo ntchito yolengeza “uthenga wabwino wa chipulumutso chake.” (Sal. 96:1-3) Tikamatero tidzakhalabe ndi mtima wosagawanika ndipo tidzalankhula ngati wamasalimo amene anaimba kuti: “Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.”​—Sal. 73:28.

22, 23. Popeza tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova, kodi zochita zathu zikufanana bwanji ndi za anthu okhulupirika a m’mbuyomu?

22 Kwa zaka zambiri zimene zapitazi, Yehova wakhala akupereka ntchito zosiyanasiyana kwa anthu ake okhulupirika. Nowa anamanga chingalawa ndipo anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5) Yoswa anatsogolera Aisiraeli polowa m’Dziko Lolonjezedwa ndipo izi zinatheka chifukwa chakuti iye ankawerenga “buku la malamulo . . . usana ndi usiku” ndiponso kutsatira zonse zolembedwamo. (Yos. 1:7, 8) Akhristu oyambirira ankapanga ophunzira ndiponso kusonkhana nthawi zonse kuti aphunzire Malemba.​—Mat. 28:19, 20.

23 Ifenso timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova komanso kuti tili ndi mtima wosagawanika tikamalalikira chilungamo, kupanga ophunzira, kutsatira malangizo a m’Malemba, kusonkhana ndi Akhristu anzathu pamisonkhano ya mpingo, yadera ndiponso yachigawo. Zinthu zimenezi zimatithandiza kukhala olimba mtima, olimba mwauzimu ndiponso kuti tizikwanitsa kuchita chifuniro cha Mulungu bwinobwino. N’zotheka kuchita zimenezi chifukwa chakuti Atate wathu wakumwamba ndiponso Mwana wake amatithandiza. (Deut. 30:11-14; 1 Maf. 8:57) Kuwonjezera pamenepo, timalimbikitsidwa ndi gulu lonse la abale amene ali ndi mtima wosagawanika komanso amalemekeza Yehova yemwe ndi Ambuye Wamkulu.​—1 Pet. 2:17.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tiyenera kuona bwanji mfundo za Yehova za makhalidwe abwino?

• Kodi ndi makhalidwe ati a Yobu amene amakusangalatsani?

• Malinga ndi Yobu 31:29-37, kodi Yobu anali munthu wotani?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Tikhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika ngati Yobu

[Chithunzi patsamba 32]

N’zotheka kukhalabe ndi mtima wosagawanika