Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Amakhala Kumwamba?

Kodi Ndani Amakhala Kumwamba?

Kodi Ndani Amakhala Kumwamba?

Yerekezerani kuti mukuona zochitika izi: Ku Ulaya, mayi wina wachikulire akulowa mutchalitchi atanyamula kolona m’manja. Kenako akugwada pansi modzichepetsa pafupi ndi chifaniziro cha Mariya. Ku Africa banja lina likuthira mowa pamanda a wachibale wawo amene ankamulemeza kwambiri. Ku America, mnyamata wina amakhulupirira kuti ali ndi mngelo wakewake amene amamuteteza. Choncho akusala kudya ndipo akukhala phee, kuganiza mozama ndi cholinga choti alankhulane ndi mngeloyo. Ndipo ku Asia, wansembe wina akuwotcha mapepala ena ake amitundu yosiyanasiyana ngati nsembe kwa mizimu ya makolo.

ANTHU onsewa akufanana pa chinthu chimodzi. Onse akukhulupirira kuti kwinakwake kuli mizimu imene angathe kulankhula nayo ndipo imakhudza zochitika pa moyo wa munthu. Chikhulupiriro chimenechi sichinayambe lero komanso sichodabwitsa. Koma chimene chimadabwitsa ndi choti pali maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mizimu imeneyi.

Mwachitsanzo, Asilamu amakhulupirira kuti pali Mulungu mmodzi, Allah. * M’Matchalitchi Achikhristu anthu amakhulupirira kuti Mulungu ndi Utatu, kutanthauza kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera. Pomwe Ahindu amakhulupirira kuti pali milungu yaimuna ndi yaikazi yoposa 1,000. Anthu ena amakhulupiriranso kuti mizimu imakhala mu nyama zinazake, m’mitengo, m’miyala ndi m’mitsinje. Palinso anthu ena amene amakhulupirira mabuku, mafilimu, ndiponso mapologalamu a pa TV amene amafalitsa nkhani zokhudza angelo, ziwanda, mizukwa ndiponso milungu yaimuna ndi yaikazi.

Anthu amasiyana maganizo pa nkhani ya milungu ndipo amasiyananso maganizo pa zimene ayenera kuchita kuti alankhule ndi milunguyo. Koma ndi zachidziwikire kuti si njira zonse zolankhulira ndi milungu zimene zingakhale zoyenera. Kuti mumvetse zimenezi, taganizirani zimene timachita tikafuna kuimba foni. Choyamba, timasankha munthu amene tikufuna kumuimbirayo ndipo timakhala ndi chikhulupiriro kuti munthuyo ndi weniweni ndipo foniyo imufikadi. Kungakhale kupanda nzeru kuimbira foni munthu amene tikungoganiza kuti mwina aliko. Ndipo choopsa kwambiri ndi chakuti tingathe kuimbira munthu wina wake wachinyengo.

Ndiyeno kodi kumwamba kuli ndani? Baibulo limayankha funso limeneli komanso limafotokoza amene ali woyenera kulankhula naye komanso zimene tingayembekezere kwa iye. Tikukupemphani kuti mupitirize kuwerenga nkhani zotsatirazi. Mudabwa kumva zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mawu akuti “Allah” si dzina, koma ndi chimodzimodzi kunena kuti “Mulungu.”