Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anakana Mesiya?

N’chifukwa Chiyani Anakana Mesiya?

N’chifukwa Chiyani Anakana Mesiya?

PAMENE Yesu anali padziko lapansi, anthu ambiri anasangalala ndi zimene ankaphunzitsa komanso anadabwa ndi zozizwitsa zimene iye anachita. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri ‘akhulupirire mwa iye’ komanso avomereze kuti iye ndi Mesiya kapena Khristu amene analonjezedwa. Iwo anati: “Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka kuposa zimene munthu uyu wachita?”​—Yohane 7:31.

Komabe ngakhale kuti panali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya, anthu ambiri amene anaona ndiponso kumva zonena zake sanamukhulupirire. Ndi zomvetsa chisoni kuti ngakhalenso ena amene poyamba anamukhulupirira anasiya kumukhulupirira. Kodi ndi chifukwa chiyani ambiri anakana kuti Yesu ndi Mesiya ngakhale kuti panali umboni wokwanira? Tiyeni tikambirane zifukwa zake, ndipo dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zingandichitikirenso ineyo?’

Sanachite Zimene Anthu Ankayembekezera

Pa nthawi imene Yesu anabadwa, Ayuda ambiri ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. Yesu ali wakhanda, pamene makolo ake anapita naye kukachisi, anakumana ndi anthu amene “anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu” kudzera mwa Mesiya wolonjezedwa. (Luka 2:38) Kenako anthu amene anaona zochita za Yohane M’batizi anadabwa ndipo anati: “Kodi Khristu uja si ameneyu?” (Luka 3:15) Kodi Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankayembekezera kuti Mesiya adzachita chiyani?

Nthawi imeneyo Ayuda ankakhulupirira kuti Mesiya akadzabwera, adzawapulumutsa ku ulamuliro wopondereza wa Aroma ndipo adzabwezera ufumu kwa Aisiraeli. Yesu asanayambe utumiki wake panali atsogoleri ena amene ankauza anthu kuti azichita ziwawa posonyeza kusagwirizana ndi ulamuliro umene unalipo. Mwina zimene atsogoleriwa anachita ndi zimene zinachititsa kuti anthu akhale ndi maganizo olakwika okhudza zimene Mesiya adzachite.

Yesu anali wosiyana kwambiri ndi Amesiya abodza amenewa. Iye sanalimbikitse anthu kuti azichita chiwawa koma anawaphunzitsa kuti azikonda adani awo ndiponso azimvera olamulira. (Mateyu 5:41-44) Yesu anakanitsitsa zimene anthu ankafuna kuti iye akhale mfumu. Ndipo anawauza kuti ufumu wake sunali “mbali ya dziko lino.” (Yohane 6:15; 18:36) Koma ngakhale zinali choncho, zinaoneka kuti anthu ankachita zinthu mogwirizana ndi zimene iwowo ankayembekezera kuti Mesiya adzachita akadzabwera.

Yohane M’batizi anaona ndi kumva umboni wa zozizwitsa zimene Yesu anachita zosonyeza kuti anali Mwana wa Mulungu. Koma pamene Yohane anali m’ndende anatumiza ophunzira ake kuti akafunse Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?” (Mateyu 11:3) Mwina Yohane ankafuna kutsimikizira ngatidi Yesu anali Mpulumutsi wolonjezedwa amene anali kudzachita zimene Ayuda ankayembekezera.

Nawonso atumwi a Yesu zinawavuta kumvetsa mfundo yakuti iye anayenera kuphedwa kenako n’kuukitsidwa. Tsiku lina Yesu anawafotokozera kuti kunali koyenera kuti Mesiya azunzike ndi kufa. Koma Petulo “anam’tengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula.” (Maliko 8:31, 32) Petulo anachita zimenezi chifukwa anali asanadziwe kuti Yesu anayenera kufa n’cholinga choti akwaniritse udindo wake monga Mesiya.

Pa nthawi imene Yesu ankalowa mu Yerusalemu, kutangotsala pang’ono kuti Pasika wa 33 C.E. achitike, anthu ambiri anayimba nyimbo zomutamanda monga Mfumu. (Yohane 12:12, 13) Koma zinthu zinasintha mofulumira kwambiri. Pasanathe mlungu umodzi Yesu anamangidwa ndi kuphedwa. Izi zitachitika, ophunzira ake awiri anadandaula kuti: “Ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.” (Luka 24:21) Ngakhale Yesu ataukitsidwa ndi kuonekera kwa ophunzira ake, iwo anali adakali ndi maganizo akuti Mesiya akhazikitsa ufumu padziko lapansi. Anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Apa n’zoonekeratu kuti maganizo olakwika amene anthu a m’nthawi ya Yesu anali nawo okhudza Mesiya anakhazikika kwambiri mumtima mwawo.​—Machitidwe 1:6.

Koma Yesu atapita kumwamba ndiponso ophunzira ake atalandira mzimu woyera, ophunzira akewo anamvetsa bwinobwino kuti Mesiya adzalamulira dziko lapansi monga Mfumu yakumwamba. (Machitidwe 2:1-4, 32-36) Mtumwi Petulo ndi Yohane analalikira molimba mtima za kuuka kwa Yesu ndipo iwo anachita zozizwitsa posonyeza umboni wakuti Mulungu anali kuwathandiza. (Machitidwe 3:1-9, 13-15) Anthu ambiri a ku Yerusalemu anamvetsera uthenga wawo ndipo anakhala okhulupirira. Koma atsogoleri achiyuda sanasangalale nazo zimenezi. Iwo anatsutsa kwambiri atumwi ndi ophunzira a Yesu ngati mmenenso anachitira ndi iyeyo. Kodi n’chifukwa chiyani atsogoleri achiyuda amenewo anakana Yesu kwa mtuwagalu?

Anakanidwa ndi Atsogoleri Achipembedzo

Pa nthawi imene Yesu ankabwera padziko lapansi, zochita ndiponso zoganiza za atsogoleri achiyuda zinali zosiyaniranatu ndi zimene Malemba amaphunzitsa. Asaduki, Afarisi ndi alembi, omwe anali atsogoleri achipembedzo nthawi imeneyo ankakhulupirira kwambiri ziphunzitso zamakolo awo kuposa Mawu a Mulungu olembedwa. Kawirikawiri iwo ankaimba Yesu mlandu wophwanya Chilamulo chifukwa chochiritsa anthu pa tsiku la Sabata. Yesu anasonyeza kuti iwo sanayenere kukhala atsogoleri ndiponso ananena kuti si zoona kuti Mulungu amakondwera nawo. Iye anachita zimenezi mwa kutsutsa mwamphamvu ziphunzitso zawo zosachokera m’Malemba. Yesu anachokera m’banja losauka ndipo sanapite ku masukulu awo achipembedzo. N’chifukwa chake ndi zosadabwitsa kuti anthu onyada amenewa zinawavuta kuvomereza kuti Yesu ndi Mesiya. Atsogoleri achipembedzowa anakwiya kwambiri chifukwa choti Yesu anawadzudzula moti ‘anakonza chiwembu choti amuphe.’​—Mateyu 12:1-8, 14; 15:1-9.

Kodi atsogoleri achipembedzowa ananena chiyani pa nkhani ya zozizwitsa zimene Yesu ankachita? Iwo sanatsutse kuti Yesu ankachitadi zozizwitsa. Koma anachitira Mulungu mwano mwa kuyesetsa kuchititsa anthu kuti asamakhulupirire Yesu. Anachita zimenezi ponena kuti Yesu ankachita zozizwitsa mothandizidwa ndi mphamvu ya Satana. Iwo anati: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi. Amatero ndi mphamvu ya Belezebule, wolamulira ziwanda.”​—Mateyu 12:24.

Komanso panali chifukwa china chachikulu chimene chinawachititsa kuti asavomereze kuti Yesu ndi Mesiya. Yesu ataukitsa Lazaro, atsogoleri a magulu osiyanasiyana a zipembedzo anaitanitsa msonkhano ndipo anati: “Kodi tichite chiyani pamenepa, chifukwa munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka? Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye, ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” Chifukwa choopa kulandidwa maudindo awo, atsogoleri achipembedzo amenewa anakonza chiwembu choti aphe Yesu ndi Lazaro.​—Yohane 11:45-53; 12:9-11.

Ayuda Ankasala Ndiponso Kuzunza Ophunzira a Yesu

Zochita za atsogoleri achipembedzo achiyuda a m’nthawi ya atumwi zinachititsa kuti anthu azidana ndi munthu aliyense amene ankakhulupirira kuti Yesu anali Mesiya. Atsogoleri achipembedzowa anali onyada chifukwa cha maudindo apamwamba amene anali nawo ndipo ankanyoza aliyense amene ankakhulupirira Yesu. Iwo ankati: “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene wakhulupirira mwa iye, alipo ngati?” (Yohane 7:13, 48) Atsogoleri ena achiyuda monga Nikodemo ndi Yosefe wa ku Arimateya anadzakhala ophunzira a Yesu. Koma ankachita zimenezi mobisa chifukwa cha mantha. (Yohane 3:1, 2; 12:42; 19:38, 39) Atsogoleri achiyuda anali atalengeza kuti “Ngati wina angavomereze kuti Yesu alidi Khristu, adzamuchotsa musunagoge.” (Yohane 9:22) Munthu wotere ankamusala ndipo ankamuona kuti ndi munthu wamba, wosafunika.

Kudana ndi atumwi ndiponso ophunzira a Yesu kunafika poipa kwambiri moti kenako anayamba kuwazunza. Atumwi anazunzidwa m’Khoti Lalikulu la Ayuda chifukwa cholalikira molimba mtima. (Machitidwe 5:40) Anthu otsutsa ananamizira wophunzira wina wa Yesu dzina lake Sitefano kuti anachitira Mulungu mwano. Khoti Lalikulu la Ayuda linamuweruza kuti ndi wolakwa ndipo anam’ponya miyala mpaka kumupha. Kenako “panabuka chizunzo chachikulu choukira mpingo umene unali mu Yerusalemu. Onse anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya, kupatulapo atumwi okha.” (Machitidwe 6:8-14; 7:54–8:1) Saulo, yemwe kenako anakhala mtumwi Paulo, anazunza Akhristu. Mkulu wa ansembe ndiponso “bungwe lonse la akulu” ankathandizira zimenezi.​—Machitidwe 9:1, 2; 22:4, 5.

Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, Chikhristu chinafalikira mwansanga zaka zingapo kuchokera pamene Yesu anamwalira. Koma ngakhale kuti anthu ambiri anakhala okhulupirira, Akhristu anali kagulu kochepa poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu a ku Palesitina. Munthu aliyense amene ankadzidziwikitsa kuti ndi wotsatira wa Khristu ankasalidwa mwinanso kuchitiridwa zachiwawa.

Zimene Tikuphunzira Kwa Anthu Amene Anakana Yesu

Monga taonera, maganizo olakwika, kuopa anthu komanso kuopa kuzunzidwa zinalepheretsa anthu ambiri m’nthawi ya atumwi kukhulupirira Yesu. Masiku anonso maganizo olakwika onena za Yesu komanso za zimene ankaphunzitsa angalepheretse anthu kumukhulupirira. Mwachitsanzo, anthu ambiri anaphunzitsidwa kuti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima yawo kapena anaphunzitsidwa kuti anthu ndi amene angabweretse Ufumu wa Mulungu. Ena amakhulupirira kuti asayansi kapena zipangizo zamakono zingathetse mavuto a anthu. Zimenezi zachititsa kuti anthu asamakhulupirire Mesiya. Masiku ano, olemba mabuku, mafilimu ndiponso nyimbo amalimbikira kunena kuti nkhani za m’Baibulo zonena za utumiki wa Yesu sizinachitikedi. Choncho anthu amenewa amachititsa kuti anthu asamakhulupirire kuti Yesu ndi Mesiya.

Chifukwa cha maganizo ndi ziphunzitso zimenezi, anthu ambiri sadziwa udindo wa Mesiya kapena amaona kuti nkhani imeneyi ilibe ntchito. Komabe kwa anthu amene akufunitsitsa kufufuza umboni wakuti Yesu ndi Mesiya, pali umboni wambiri masiku ano kusiyana ndi umene unalipo m’nthawi ya atumwi. Tikutero chifukwa tili ndi Malemba Achiheberi onse omwe ali ndi ulosi wosiyanasiyana wonena zimene Mesiya anali kudzachita. Komanso tili ndi Mauthenga Abwino onena zimene Yesu anachita pokwaniritsa ulosi umenewo. *

Kunena zoona, aliyense angapeze umboni wokwanira womuthandiza kusankha bwino pa nkhani imeneyi. Ndiponso tifunika kuiganizira mwamsanga nkhaniyi. N’chifukwa chiyani tikunena choncho? Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti posachedwapa Yesu, yemwe ndi Mesiya komanso Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzachotsa onse amene akuononga dzikoli ndipo adzabweretsa ulamuliro wolungama. Ulamuliro umenewo udzachititsa kuti dziko lapansili likhale Paradaiso ndipo anthu omvera adzakhalapo kosatha. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15, 18; 21:3-5) Inunso mungakhale ndi tsogolo labwino lotereli ngati mutayesetsa kuphunzira za Yesu panopa ndi kusonyeza kuti mumamukhulupirira. Kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 Onani tchati chakuti “Maulosi Onena za Mesiya” chomwe chili patsamba 201 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni. Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Kodi inuyo mukanakhala kuti munalipo m’nthawi ya Yesu, mukanavomereza kuti iye ndi Mesiya?

[Chithunzi patsamba 21]

Musalole maganizo olakwika kukulepheretsani kuphunzira zoona zokhudza Yesu