Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Inoyo Ndiyo Nthawi Yeniyeni Yovomerezeka’

‘Inoyo Ndiyo Nthawi Yeniyeni Yovomerezeka’

‘Inoyo Ndiyo Nthawi Yeniyeni Yovomerezeka’

“Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.”​—2 AKOR. 6:2.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuzindikira zoyenera kuchita nthawi ina iliyonse?

“CHILICHONSE chili ndi nthawi yake, ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake.” (Mlal. 3:1) Solomo ankalemba za ubwino wozindikira nthawi yoyenera kuchita zinthu zina zofunika kwambiri monga kulima, kuyenda ulendo, kuchita bizinezi kapena kulankhulana ndi anthu ena. Komabe, tiyeneranso kudziwa ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kuigwira pa nthawi ina iliyonse. M’mawu ena, tingati tiyenera kudziwa zinthu zofunika kuziika pamalo oyamba.

2. Tikudziwa bwanji kuti Yesu ankalalikira akudziwa bwino za nthawi imene iye ankakhala?

2 Yesu ali padziko lapansi ankadziwa bwino za nthawi imene ankakhala ndiponso zoyenera kuchita. Iye ankadziwa zinthu zoyenera kukhala pamalo oyamba ndipo ankadziwanso kuti nthawi yoti maulosi ambiri okhudza Mesiya akwaniritsidwe yayandikira. (1 Pet. 1:11; Chiv. 19:10) Yesu anali ndi ntchito yoyenera kugwira yosonyeza kuti analidi Mesiya wolonjezedwa. Iye anafunika kuchitira umboni choonadi cha Ufumu ndiponso kusonkhanitsa anthu oti adzalamulire naye mu Ufumuwo. Yesu anafunikanso kuyala maziko a mpingo wachikhristu umene unali kudzagwira ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira mpaka kumalekezero a dziko lapansi.​—Maliko 1:15.

3. Kodi kudziwa bwino za nthawi kunathandiza bwanji Yesu pa ntchito yake?

3 Kudziwa zimenezi kunali kothandiza kwambiri pa moyo wa Yesu. Kunamulimbikitsa kukhala wodzipereka kwambiri pochita chifuniro cha Atate wake. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokololazo kuti atumize antchito okam’kololera.” (Luka 10:2; Mal. 4:5, 6) Yesu atasankha ophunzira 12 kenako 70, anawapatsa malangizo omveka bwino ndipo anawatumiza kukalalikira uthenga wakuti: “Ufumu wakumwamba wayandikira.” Ponena za Yesu timawerenga kuti: “Tsopano atamaliza kupereka malangizo kwa ophunzira ake 12 aja, anachoka kumeneko n’kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.”​—Mat. 10:5-7; 11:1; Luka 10:1.

4. Kodi Paulo ankatsanzira Yesu Khristu m’njira iti?

4 Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri kwa otsatira ake onse pa nkhani ya kudzipereka. Izi ndi zimene mtumwi Paulo ankatanthauza polimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Muzitsanzira ine, monga mmene inenso ndimatsanzirira Khristu.” (1 Akor. 11:1) Kodi Paulo ankatsanzira Khristu m’njira iti? Iye ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene angapeze kuti alalikire uthenga wabwino. M’makalata amene Paulo analembera mipingo muli mawu monga akuti “musakhale aulesi pa ntchito yanu,” “tumikirani Yehova monga akapolo,” ‘khalani ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye,’ ndiponso akuti “chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova.” (Aroma 12:11; 1 Akor. 15:58; Akol. 3:23) Paulo sanaiwale zimene zinachitika pamene Ambuye Yesu Khristu anaonekera kwa iye panjira ya ku Damasiko. Sanaiwalenso mawu a Yesu amene Hananiya, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anamuuza. Iye anati: “Munthu ameneyu ndi chiwiya changa chochita kusankhidwa chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.”​—Mac. 9:15; Aroma 1:1, 5; Agal. 1:16.

‘Inoyo Ndiyo Nthawi Yeniyeni Yovomerezeka’

5. Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Paulo kuchita utumiki wake modzipereka?

5 Tikawerenga buku la Machitidwe timaona kuti Paulo anali wolimba mtima komanso wodzipereka pa utumiki wake. (Mac. 13:9, 10; 17:16, 17; 18:5) Paulo ankadziwa bwino za nthawi imene ankakhala. Iye anati: “Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.” (2 Akor. 6:2) M’mbuyomo, chaka cha 537 B.C.E., inali nthawi yovomerezeka yoti anthu amene anagwidwa n’kutengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo abwerere kwawo. (Yes. 49:8, 9) Koma kodi Paulo ankatanthauza chiyani pa lembali? Tikhoza kudziwa zimene ankatanthauza tikaona bwino nkhani yonse.

6, 7. Kodi ndi mwayi wamtengo wapatali uti umene Akhristu odzozedwa apatsidwa masiku ano, nanga kodi ndani akugwira nawo ntchitoyi?

6 Chakumayambiriro kwa kalata yake, Paulo ananena za mwayi wamtengo wapatali umene iye ndi Akhristu anzake odzozedwa anapatsidwa. (Werengani 2 Akorinto 5:18-20.) Iye ananena kuti anaitanidwa ndi Mulungu kuti achite “utumiki wokhazikitsanso mtendere” n’kupempha anthu kuti ‘agwirizanenso ndi Mulungu.’ Izi zinatanthauza kuthandiza anthu kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

7 Kuyambira pamene makolo anthu oyamba anapandukira Mulungu m’munda wa Edene, anthu onse salinso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo ndi otalikirana naye. (Aroma 3:10, 23) Zimenezi zachititsa kuti anthu onse akhale mumdima wauzimu ndipo ichi n’chifukwa chake tonse timavutika ndiponso kufa. Paulo analemba kuti: “Tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Koma Mulungu wayesetsa kuthandiza anthu ndipo ‘akuwapempha’ kuti abwerere kwa iye kapena kuti agwirizane nayenso. Uwu ndi utumiki umene Paulo ndi Akhristu anzake odzozedwa anapatsidwa. ‘Nthawi yovomerezeka imeneyi’ ndi “tsiku la chipulumutso” kwa anthu amene amakhulupirira Yesu. Akhristu odzozedwa onse limodzi ndi anzawo a “nkhosa zina,” amene akugwira nawo ntchito, akupitiriza kuitana anthu kuti apindule ndi ‘nthawi yovomerezekayi.’​—Yoh. 10:16.

8. Kodi chochititsa chidwi kwambiri pa nkhani yogwirizananso ndi Mulungu n’chiyani?

8 Chochititsa chidwi kwambiri pa nkhani yogwirizananso ndi Mulunguyi n’chakuti anthu ndi amene analakwitsa zinthu m’munda wa Edene koma Mulungu ndi amene anachita zinthu zothandiza kuti akonze zolakwikazo. (1 Yoh. 4:10, 19) Kodi iye anachita chiyani? Paulo anayankha kuti: “Mulungu anali kugwirizanitsa dziko ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, moti sanawawerengere anthuwo machimo awo, ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga umenewu wokhazikitsanso mtendere.”​—2 Akor. 5:19; Yes. 55:6.

9. Kodi Paulo anachita chiyani posonyeza kuti ankayamikira chifundo cha Mulungu?

9 Popereka nsembe ya dipo, Yehova wapereka mwayi woti anthu amene amamukhulupirira akhululukidwe machimo ndiponso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kuwonjezera pamenepo iye watuma anthu omuimira kuti apemphe anthu kulikonse kuti akhale pa mtendere ndi Mulungu nthawi ikadalipo. (Werengani 1 Timoteyo 2:3-6.) Paulo ankayesetsa mwakhama kuchita “utumiki wokhazikitsanso mtendere” chifukwa choti ankadziwa cholinga cha Mulungu ndiponso za nthawi imene iye ankakhala. Cholinga cha Yehova sichinasinthe. Iye akulandirabe anthu masiku ano. Mawu a Paulo onena kuti ‘inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezeka’ ndiponso akuti “linolo ndilo tsiku lachipulumutso” akugwirabe ntchito. Uwutu ndi umboni wakuti Yehova ndi Mulungu wachifundo ndiponso wokoma mtima.​—Eks. 34:6, 7.

‘Musaphonye Cholinga Chake’

10. Kodi Akhristu odzozedwa akale komanso a masiku ano amaona bwanji ‘tsiku la chipulumutso’?

10 Anthu oyamba kupindula ndi kukoma mtima kwa Mulungu ndi amene anali ‘ogwirizana ndi Khristu.’ (2 Akor. 5:17, 18) ‘Tsiku lawo la chipulumutso’ linayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Kungoyambira nthawi imeneyo, anthu a m’gulu limeneli apatsidwa ntchito yolengeza ‘uthenga wokhazikitsanso mtendere.’ Masiku ano, otsalira a Akhristu odzozedwa akuchitabe “utumiki wokhazikitsanso mtendere.” Iwo amazindikira kuti angelo anayi amene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya ‘akugwira mwamphamvu mphepo zinayi za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi.’ Choncho tikukhalabe ‘m’tsiku la chipulumutso’ komanso ‘nthawi yeniyeni yovomerezeka.’ (Chiv. 7:1-3) Chifukwa cha zimenezi, kuyambira m’ma 1900, otsalira a Akhristu odzozedwa akhala akuyesetsa mwakhama kuchita “utumiki wokhazikitsanso mtendere” mpaka kumalekezero a dziko lapansi.

11, 12. Kodi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, Akhristu odzozedwa anasonyeza bwanji kuti ankadziwa bwino za nthawi imene ankakhala? (Onani chithunzi patsamba 15.)

11 Mwachitsanzo, buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom limanena kuti pamene zaka za m’ma 1900 zinkayamba, “C. T. Russell ndi anzake ankakhulupirira kwambiri kuti anali kukhala mu nthawi yokolola ndipo anthu ankafunika kumva choonadi chimene chimamasula anthu.” Kodi iwo anachita chiyani atadziwa zimenezi? Podziwa kuti anali kukhala mu nthawi yokolola, ndiponso ‘nthawi yeniyeni yovomerezeka,’ abalewa sanangokhutira ndi kuitana anthu kuti adzakhale nawo pa misonkhano yawo. Izi n’zimene atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ankachita. Koma Akhristu odzozedwawa anayamba kufufuza njira zina zolalikirira uthenga wabwino. Chinthu china chimene anachita chinali kugwiritsa ntchito zipangizo zimene zinali zamakono pa nthawiyo kuti apititse patsogolo ntchito yawo.

12 Kuti afalitse uthenga wabwino wa Ufumu, kagulu ka atumiki kameneka kanagwiritsa ntchito timapepala, magazini ndi mabuku. Iwo ankalembanso ulaliki ndi nkhani zina m’manyuzipepala osiyanasiyana. Ankaulutsanso mapulogalamu awo a nkhani za m’Malemba pa wailesi zosiyanasiyana. Abalewa ankakonzanso mafilimu okhala ndi mawu pa nthawi imene anthu anali asanayambe kukonza mafilimu oterewa. Kodi zotsatira za khama lawoli ndi zotani? Masiku ano, anthu oposa 7 miliyoni amva uthenga wakuti: “Gwirizananinso ndi Mulungu,” ndipo nawonso akulengeza uthenga umenewu. Atumiki a Yehova oyambirirawa ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzipereka ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ena.

13. Kodi sitiyenera kuiwala cholinga cha Mulungu chiti?

13 Mawu a Paulo akuti ‘inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezeka’ akugwirabe ntchito masiku ano. Ife amene talawa kukoma mtima kwa Yehova timayamikira kwambiri kuti tapatsidwa mwayi wakumva ndi kulandira uthenga wotigwirizanitsa ndi Mulungu. M’malo mongokhala phee, timatsatira mawu amene Paulo ananena akuti: “Tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.” (2 Akor. 6:1) Cholinga cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndi “kugwirizanitsa dziko ndi iyeyo” kudzera mwa Khristu.​—2 Akor. 5:19.

14. Kodi masiku ano anthu ali ndi mwayi wotani m’mayiko ambiri?

14 Anthu ambiri amene Satana wawachititsa khungu ndi otalikirana ndi Mulungu ndipo sadziwa cholinga cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulunguyo. (2 Akor. 4:3, 4; 1 Yoh. 5:19) Chifukwa chakuti zinthu zikuipiraipira padzikoli, anthu ambiri amachita chidwi kwambiri akathandizidwa kuzindikira kuti mavuto onsewa alipo chifukwa chakuti anthu ndi otalikirana ndi Mulungu. Ngakhale m’mayiko amene anthu sankachita chidwi ndi ntchito yathu yolalikira, anthu ambiri tsopano akumvetsera uthenga wabwino ndipo akuchitapo kanthu kuti agwirizanenso ndi Mulungu. Kodi timadziwa kuti ino ndi nthawi yofunika kudzipereka kwambiri polengeza pempho lakuti: “Gwirizananinso ndi Mulungu”?

15. M’malo mongowauza anthu kuti zinthu ziwayendera bwino akagwirizana ndi Mulungu, kodi tiyenera kuwathandiza kudziwa chiyani?

15 Ntchito yathu si yongouza anthu kuti akagwirizana ndi Mulungu, Iye adzawathandiza pa mavuto awo onse ndipo adzakhala osangalala. Anthu ambiri amene amapita kutchalitchi amakhala ndi maganizo amenewa ndipo matchalitchi amawauzanso zimenezi. (2 Tim. 4:3, 4) Koma cholinga cha utumiki wathu si chimenechi. Uthenga wabwino umene timalalikira ndi wakuti chifukwa cha chikondi, Yehova ndi wokonzeka kukhululukira anthu kudzera mwa Khristu. Choncho anthu akhoza kuyandikana ndi Mulungu ndiponso kugwirizana naye. (Aroma 5:10; 8:32) Ndipotu ‘nthawi yeniyeni yovomerezeka’ yatsala pang’ono kutha.

“Yakani ndi Mzimu”

16. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kukhala wolimba mtima ndiponso wodzipereka?

16 Ndiyeno kodi tingatani kuti tikhale odziperekabe pa kulambira koona? Anthu ena mwachibadwa ndi amanyazi ndipo sakhala omasuka kucheza ndi anthu. Komabe tiyenera kudziwa kuti kudzipereka sikutanthauza kuti munthu akhale wopanda manyazi ndipo sikudalira chibadwa cha munthu ayi. Paulo ananena chimene chingathandize munthu kukhala wodzipereka. Iye anauza Akhristu anzake kuti: “Yakani ndi mzimu.” (Aroma 12:11) Mzimu woyera wa Yehova ndi umene unathandiza kwambiri mtumwiyu kukhala wolimba mtima komanso kulalikira mogwira mtima. Kuchokera pamene anaitanidwa ndi Yesu mpaka pamene anamangidwa komaliza n’kuphedwa ku Roma, panadutsa zaka zoposa 30 ndipo pa zaka zonsezi sanafooke. Paulo nthawi zonse ankadalira Mulungu amene ankamupatsa mphamvu kudzera mwa mzimu woyera. Iye anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Kodi chitsanzo chakechi chingatithandize bwanji?

17. Kodi tingatani kuti ‘tiyake ndi mzimu’?

17 Mawu amene anawamasulira kuti “yakani” amatanthauza kuwira. (Kingdom Interlinear) Kuti madzi amene ali pamoto aziwirabe pamafunika kuti motowo usazirale. Mofanana ndi zimenezi, kuti ‘tiyake ndi mzimu’ pamafunika kuti mzimu wa Mulungu uzigwirabe ntchito pa ife. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova watipatsa kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tizikhala ndi phunziro laumwini, kulambira kwa pabanja, kusonkhana ndi Akhristu anzathu mu mpingo ndiponso kupemphera. Tikatero tidzakhala ndi “moto” wotithandiza kuwirabe kapena kuti ‘kuyakabe ndi mzimu.’​—Werengani Machitidwe 4:20; 18:25.

18. Popeza ndife Akhristu odzipereka kodi tiyenera kuika maganizo athu onse pa cholinga chiti?

18 Munthu wodzipereka ndi amene amaika maganizo ake onse pa cholinga chake ndipo salola kusokonezedwa kapena kugwetsedwa mphwayi. Popeza ndife Akhristu odzipereka kwa Mulungu, cholinga chathu ndi kuchita zinthu zonse zimene Yehova amafuna kuti tichite ngati mmene Yesu anachitira. (Aheb. 10:7) Masiku ano, cholinga cha Yehova ndi chakuti anthu ambiri agwirizanenso naye. Ntchito imene tapatsidwayi ndi yofunika kwambiri ndipo iyenera kuchitika mwamsanga. Motero tiyeni tiyesetse mmene tingathere kukhala odzipereka kwambiri ngati mmene Yesu ndi Paulo anachitira.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi “utumiki wokhazikitsanso mtendere” umene Paulo ndi Akhristu odzozedwa ena apatsidwa n’chiyani?

• Kodi otsalira a odzozedwa agwiritsa ntchito motani ‘nthawi yeniyeni yovomerezeka’?

• Kodi atumiki achikhristu angatani kuti ‘ayake ndi mzimu’?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Paulo sanaiwale zimene zinachitika Ambuye Yesu Khristu ataonekera kwa iye