Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Pa Genesis 6:3 timawerenga kuti: “Mzimu wanga supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu, popeza alinso athupi. Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.” Kodi apa Yehova anaika malire a moyo wa anthu kuti azingokhala zaka 120? Nanga kodi Nowa analalikira za Chigumula kwa nthawi yaitali chonchi?

Yankho la mafunso onsewa ndi lakuti ayi.

Chigumula chisanachitike, anthu ankakhala ndi moyo zaka zambiri. Pa nthawi imene Chigumula chinkachitika Nowa anali ndi zaka 600 ndipo anakhala ndi moyo zaka 950. (Gen. 7:6; 9:29) Anthu ena amene anabadwa Chigumula chitachitika anakhalanso ndi moyo zaka zoposa 120. Mwachitsanzo, Aripakisadi anamwalira ali ndi zaka 438 ndipo Shela anamwalira ali ndi zaka 433. (Gen. 11:10-15) Koma pofika nthawi ya Mose anthu ankangokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80. (Sal. 90:10) Choncho lemba la Genesis 6:3 silinaike malire kuti anthu azikhala zaka 120.

Kodi pamenepa ndiye kuti lemba limeneli limasonyeza kuti Mulungu anauza Nowa kuti achenjeze anthu ena kuti pakatha zaka 120 adzawononga dziko? Ayi. Mulungu analankhula ndi Nowa maulendo angapo. Pa vesi 13 la chaputala chomwechi timawerenga kuti: “Mulungu anauza Nowa kuti: ‘Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse, popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa.’” Zaka zotsatira, Nowa anamaliza ntchito yaikulu yomanga chingalawa ndipo pa nthawi imeneyi “Yehova anauza Nowa kuti: ‘Lowa m’chingalawacho, iwe ndi banja lako.’” (Gen. 6:13; 7:1) Ndiyeno pali nthawi zina pamene Yehova ankauza Nowa zinthu zina.​—Gen. 8:15; 9:1, 8, 17.

Komabe, mawu a pa Genesis 6:3 amamveka mosiyanako chifukwa satchula za Nowa kapena kusonyeza kuti Mulungu ankalankhula ndi Nowa. Zikuoneka kuti mawu a palembali anali mawu amene Mulungu ananena okhudza cholinga chake kapena kuti zimene ankafuna kuchita. (Yerekezerani ndi Genesis 8:21.) Chochititsa chidwi n’chakuti, pofotokoza zinthu zimene zinachitika Adamu asanalengedwe, timamva mawu monga akuti: “Mulungu anati.” (Gen. 1:6, 9, 14, 20, 24) Apa n’zodziwikiratu kuti Mulungu sankalankhula ndi munthu wina aliyense padziko lapansi chifukwa chakuti pa nthawiyi anthu anali asanalengedwe.

Choncho tikhoza kunena kuti mawu a pa Genesis 6:3 amangofotokoza cholinga cha Mulungu chowononga dongosolo loipa padziko lapansi. Yehova anapereka chiweruzo chakuti adzawononga dongosololi pambuyo pa zaka 120 ngakhale kuti Nowa sankadziwa zimenezi. Koma n’chifukwa chiyani anaika malire? Nanga n’chifukwa chiyani anadikira kwa nthawi yonseyi?

Mtumwi Petulo ananena zifukwa zake. Iye anati: “Mulungu anali kuleza mtima m’masiku a Nowa, pamene chingalawa chinali kupangidwa, chimene chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, miyoyo 8 yokha.” (1 Pet. 3:20) Pamene Mulungu anatsimikiza zoti awononga dziko pakapita zaka 120 panali zinthu zina zimene zinayenera kuchitika. Patapita zaka 20 Nowa ndi mkazi wake anayamba kubereka ana. (Gen. 5:32; 7:6) Ana awo atatu anakula n’kukwatira ndipo izi zinachititsa kuti m’banja lawo mukhale “miyoyo 8.” Kenako iwo anafunika kumanga chingalawa. Tikaganizira za kukula kwa chingalawachi, ndiponso chiwerengero cha anthu m’banja la Nowa titha kuona kuti ntchitoyi inali yaikulu kwambiri. Chifukwa chakuti Mulungu analeza mtima kwa zaka 120, zinthu zonsezi zinatheka ndipo panakonzedwa njira yopulumutsira zinthu zamoyo. Izi zinathandiza kuti anthu 8 okhulupirika ‘apulumutsidwe pamadzi.’

Baibulo silitchula chaka chimene Yehova anauza Nowa kuti adzawononga dziko ndi Chigumula. N’kutheka kuti ana ake anabadwa, kukula ndiponso kukwatira kutatsalabe zaka 40 kapena 50 kuti Chigumula chichitike. Kenako Yehova anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse.” Iye anauzanso Nowa kuti amange chingalawa chachikulu kuti iye ndi banja lake alowemo. (Gen. 6:13-18) Pa zaka zotsatira, sikuti Nowa ankangopereka chitsanzo pa nkhani ya kuchita chilungamo. Iye analinso “mlaliki wa chilungamo” ndipo ankalalikira uthenga wosapita m’mbali wakuti Mulungu akufuna kuwononga anthu osaopa Mulungu a pa nthawiyo. Nowa sanadziwiretu chaka chimene Chigumulacho chidzachitika koma ankadziwa zoti chidzachitika. Inunso mukudziwa kuti chinachitikadi.​—2 Pet. 2:5.