Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

KODI nkhani ya Adamu na Hava, omwe anali kukhala m’munda wa Edeni, mumaidziŵa? Nkhani imeneyi ni yodziŵika kwa anthu ambili padziko lonse lapansi. Tikukupemphani kuti muŵelenge nkhani imeneyi. Nkhaniyi imapezeka pa Genesis 1:26–3:24. Mwacidule, nkhaniyi imanena kuti:

Yehova Mulungu a anapanga munthu pogwilitsa nchito fumbi lapansi ndipo anam’patsa dzina lakuti Adamu. Mulungu anaika munthuyu m’munda umene unali m’dela lina lochedwa Edeni. Mulungu ni amene anapanga munda umenewu. Unali na madzi okwanila ndipo munali mitengo yobiliwila ndiponso ya zipatso zambili zokoma. Pakati pamundawu panali “mtengo wodziwitsa cabwino ndi coipa.” Mulungu analetsa anthu kudya zipatso za mtengo umenewu ndipo anawauza kuti adzafa ngati sadzamvela zimenezi. Patapita nthawi, Yehova anagwilitsa nchito nthiti ya Adamu n’kumupangila mnzake. Ameneyu anali mkazi ndipo dzina lake anali Hava. Mulungu anapatsa Adamu na Hava nchito yoti azisamalila munda wa Edeni ndipo anawauzanso kuti abelekane aculuke adzaze dziko lapansi.

Tsiku lina Hava ali yekha, njoka inamuuza kuti adye zipatso za mtengo umene Mulungu anawaletsa. Inacita zimenezi pomuuza kuti Mulungu anamunamiza ndipo anamubisila zinthu zabwino zimene zikanacititsa kuti afanane na Mulungu. Iye anakopeka n’kudya cipatso coletsedwa cija. Adamu nayenso anagwilizana naye posonyeza kusamvela Mulungu ndipo anadya cipatsoco. Zitatelo, Yehova anaweluza Adamu, Hava ndiponso njoka. Kenako anthuwo anathamangitsidwa m’munda wa Edeni ndipo Mulungu anaika angelo kuti azilondela mundawo n’colinga cakuti anthuwo asabwelelenso.

Kale, akatswili ena amaphunzilo ndiponso a mbili yakale anali kuvomeleza kuti zocitika zochulidwa m’buku la m’Baibo la Genesis zinacitikadi. Koma masiku ano pali anthu ambili amene amatsutsa kuti zimenezi zinacitikadi. Kodi n’ciani cimacititsa anthuwa kutsutsa kuti nkhani ya m’buku la Genesis yonena za Adamu, Hava ndiponso munda wa Edeni inacitikadi? Tiyeni tikambilane mfundo zinayi zimene otsutsa amanena.

1. Sikunakhalepo munda wa Edeni.

Kodi n’cifukwa ciani anthu amakayikila mfundo imeneyi? N’kutheka kuti amatengela zimene akatswili ena amanena. Kwa zaka zambili, akatswili a maphunzilo a zaumulungu anali kunena kuti munda wa Mulungu umenewu unali udakalipo kwinakwake. Koma iwo anali kunena zimenezi cifukwa cotengela nzelu za akatswili acigiriki monga Plato na Aristotle, amene anali kuphunzitsa kuti padziko lapansi pano sipangakhale ciliconse cangwilo, kapena kuti copanda vuto lililonse. Iwo anali kunena kuti zinthu zotelozo zimangopezeka kumwamba kokha. Pomva zimenezi, akatswili a maphunzilo a zaumulungu anayamba kuganiza kuti ndiye kuti Paradaiso woyambililayo anali kumwamba. Ena anali kunena kuti munda umenewo unali pamwamba paphili lalitali kwambili, zomwe zinacititsa kuti mundawo usakhudzidwe na zoipa zimene zimacitika padziko lapansi. Masiku ano akatswili ena amanena kuti munda umenewu uli kumpoto kapena kum’mwela kwa malekezelo a dziko lapansi ndipo ena amanena kuti uli pamwezi kapena pamalo ena pafupi na mwezi. b Cifukwa ca mfundo ngati zimenezi, anthu anayamba kuona kuti nkhani ya munda wa Edeni ni nthano cabe yongofuna kusangalatsa anthu. Akatswili ena amaphunzilo masiku ano amatsutsa zimene Baibo imanena zokhudza kumene kunali munda wa Edeni ndipo amati kunalibe malo ngati amenewo.

Komano Baibo ikamanena za munda wa Edeni silinena mfundo ngati zimenezo. Lemba la Genesis 2:8-14 limatiuza zinthu zingapo zomveka bwino zokhudza munda umenewu. Limatiuza kuti mundawu unali cakum’mawa kwa dela lochedwa Edeni. M’munda umenewu munadutsa mtsinje wina umene kutsogolo kwake unagawikana n’kukhala mitsinje inayi. Baibo imatchula mayina a mitsinje inayi yonseyi ndipo imafotokozanso mwacidule kumene mtsinje uliwonse unalowela. Kwa nthawi yaitali, akatswili ena akhala akucita cidwi kwambili na mfundo zimenezi ndipo ambili a iwo akhala akufufuza mwakhama nkhani ya m’Baibo imeneyi kuti mwina ingawathandize kupeza malo enieni kumene kunali munda wa Edeni. Komabe zimene apeza zacititsa kuti akhale na maganizo osiyana-siyana komanso otsutsana pa nkhaniyi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nkhani zokhudza dela lochedwa Edeni komanso munda wokongola ndiponso mitsinje imene inali m’delali ni zabodza, mwinanso nthano cabe?

Taganizilani izi: Nkhani za m’munda wa Edeni zinacitika zaka zoposa 6,000 zapitazo. Mose ni amene analemba zocitika zimenezi ndipo mwina anauzidwa zimenezi na anthu ena kapena anagwilitsa nchito zolembedwa zimene zinalipo kale. Koma Mose analemba nkhanizi patapita zaka pafupifupi 2,500 kucokela pamene zinacitika. Conco pa nthawiyo imene Mose anali kulemba zimenezi, munda wa Edeni unali kale mbili yakale. N’kutheka kuti palipano, popeza patha zaka zambili-mbili, zinthu zothandiza anthu kuzindikila malo, monga mitsinje, zimene zinachulidwa m’nkhaniyi zinasintha. Tikutelo cifukwa nthaka ya dziko lapansili imayenda-yenda. Ndiponso kudela kumene kukuoneka kuti kunali Edeni kumacitika zivomezi kaŵili-kaŵili, moti zina mwa zivomezi zazikulu kwambili zimene zacitikapo padziko lonse lapansi zinacitika m’dela limeneli. M’madela otelewa, zinthu zacilengedwe zimasintha nthawi zonse. Kuwonjezela pamenepa, Cigumula ca Nowa ciyenela kuti cinasinthilatu mmene delali linali kuonekela moti sitingathenso kudziŵa kuti poyamba linali kuoneka bwanji. c

Komabe pali mfundo zoŵelengeka zimene tikudziŵa. Mwacitsanzo, nkhani ya m’buku la Genesis imasonyeza kuti munda wa Edeni unalidi malo enieni. Mtsinje wa Firate na wa Tigirisi kapena kuti Hidekeli, yomwe ni iŵili mwa mitsinje inayi imene imachulidwa m’nkhaniyi, ilipobe mpaka pano ndipo mitsinjeyi inayambila pamalo oyandikana. Nkhaniyi imachula madela amene mitsinje imeneyi inadutsa ndipo imachulanso zinthu zacilengedwe zimene ni zodziŵika kwambili m’madela amenewa. Anthu a ku Isiraeli ni amene anali oyambilila kuŵelenga nkhani imeneyi ndipo mfundo zimenezi zinawathandiza kudziŵa zambili.

Ndiyeno kodi nthano komanso nkhani zopeka zimafotokozedwa conci? Ayi. Kaŵili-kaŵili, nkhani zotelozo sizichula mwacindunji zinthu zimene aliyense angafufuze n’kupeza umboni wake mosavuta. Nthawi zambili zimayamba na mawu akuti: “Panangokhala.” Koma nkhani zonena za zinthu zimene zinacitikadi zimakhala na mfundo zonse zofunikila kuti munthu amvetse bwino nkhaniyo ngati mmene nkhani yonena za munda wa Edeni ilili.

2. Sizoona kuti Mulungu anapanga Adamu kucokela ku fumbi ndiponso Hava kucokela ku nthiti ya Adamu.

Masiku ano asayansi apeza umboni wosonyeza kuti thupi la munthu linapangidwa na zinthu zosiyana-siyana monga hayidirojeni, okisijini na kaboni, zimene zimapezekanso munthaka. Koma kodi zinatheka bwanji kuti apange cinthu camoyo kucokela ku zinthu zimenezi?

Asayansi ambili amanena kuti zinthu zamoyo zinakhalapo zokha. Iwo amati poyamba kunali tamoyo tating’ono kwambili tokhala na thupi lopanda zinthu zambili ndiponso losacolowana. Ndiyeno amati tamoyo timeneti tinali kusintha pang’ono-pang’ono pa zaka mamiliyoni ambili n’kukhala na matupi ocolowana kwambili. Koma si zoona kuti pangakhale camoyo ca “thupi lopanda zinthu zambili ndiponso losacolowana” cifukwa cakuti zamoyo zonse, kuphatikizapo tizilombo tating’ono kwambili tosaoneka na maso, tokhala na selo imodzi yokha, tili ndi thupi locholowana kwambili lovuta kumvetsa. Palibe umboni wosonyeza kuti pali camoyo ciliconse cimene cinalakhapo cokha. Ndiponso palibe umboni wosonyeza kuti zimenezi zingacitike. M’malo mwake, zolengedwa zonse zimasonyeza umboni wosatsutsika wakuti zinacita kulengedwa na winawake wanzelu kwambili kuposa anthufe. dAroma 1:20.

Tiyelekeze kuti mukumvetsela nyimbo inayake yoimbidwa mwaluso kwambili kapena mukuyang’ana cithunzi cojambulidwa bwino zedi kapenanso mukucita cidwi na makina ena ocita zinthu modabwitsa. Kodi munganene kuti zinthu zimenezi zinangokhalapo zokha? N’zodziŵikilatu kuti simunganene zimenezi. Ngakhale zili conco, zinthu zopangidwa mwaluso zimenezi sitingaziyelekezele n’komwe na thupi la munthu limene linapangidwa mogometsa komanso mokongola kwambili. Ndiyeno kodi n’zomveka kunena kuti palibe Mlengi amene anapanga munthu? Ndipotu nkhani ya m’buku la Genesis imanena kuti pa zamoyo zonse zimene zili padziko lapansili, ndi anthu okha amene analengedwa m’cifanizo ca Mulungu. (Genesis 1:26) N’cifukwa cake anthu okha ni amene amatha kusonyezako luso lopanga zinthu limene Mulungu ali nalo, moti nthawi zina amatha kuyimba nyimbo mwaluso kwambili, kujambula zithunzi zokongola komanso kupanga makina odabwitsa. Conco kodi ziyenela kutidabwitsa kuti Mulungu anapanga zinthu mwaluso kwambili kuposa mmene anthufe tingapangile?

Ndipo tikanena zolenga mkazi pogwilitsa nchito nthiti ya mwamuna, kwa Mulungu imeneyo sinkhani.  e Mulungu akanatha kugwilitsa nchito njila ina, koma kulenga mkazi pogwilitsa nchito nthiti ya mwamuna kunali na tanthauzo lalikulu. Iye anafuna kuti mwamuna na mkaziyo akwatilane na kumakondana kwambili monga “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mwamuna na mkazi angathe kuthandizana pa zinthu zambili, kupanga ubwenzi wolimba ndiponso wosatha. Kodi umenewu si umboni wakuti kuli Mlengi wanzelu komanso wacikondi?

Komanso akatswili ena ofufuza za maselo a m’thupi amavomeleza kuti anthu onse anacokela kwa mwamuna na mkazi mmodzi. Ndiyeno kodi zimenezi sizikugwilizana na zimene buku la Genesis limanena?

3. Nkhani ya mtengo wodziwitsa cabwino na coipa imamveka ngati yopeka.

Nkhani ya m’buku la Genesis siinena kuti mitengo imeneyi inali na mphamvu zapadela. Koma inali mitengo ngati mmene mtengo uliwonse umakhalila kungoti inaali kuimila zinazake.

Anthunso amacita zofanana na zimenezi nthawi zina. Mwacitsanzo poweluza mlandu, woweluza angacenjeze anthu kuti azilemekeza khothi cifukwa kupanda kutelo ndiye kuti akuphwanya lamulo. Pamenepo sikuti akutanthauza kuti munthu ayenela kulemekeza mipando, matebulo na zipupa za khotilo ayi. Koma akutanthauza anthu amene ali na ulamulilo m’khotimo. Mafumu enanso amakhala na lichowa, ndodo, kapena cisoti cacifumu monga cizindikilo ca ulamulilo wawo.

Ndiye kodi mitengo iŵili ija inali kuimila ciani? Anthu ali na maganizo osiyana-siyana ovuta kumva pa nkhani imeneyi. Koma yankho la funso limeneli ni losavuta kumva ndipo lili na tanthauzo lalikulu kwambili. Mtengo wodziwitsa zabwino na zoipa unali kuimila udindo umene Mulungu yekha ni amene ali nawo, wotha kudziŵa cabwino na coipa. (Yeremiya 10:23) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti kuba zipatso za mtengo umenewu kunali kuswa lamulo. Mtengo wa moyo unali kuimila mphatso ya moyo wosatha yomwe Mulungu yekha ni amene angaipeleke.—Aroma 6:23.

4. Ena amaona kuti nkhaniyi ni yopeka cifukwa njoka singalankhule.

Kunena zoona nkhani ya m’buku la Genesis imeneyi ingakhale yovuta kuimvetsa maka-maka ngati munthu sakuganizila mfundo zinanso za m’Baibo. Komabe Malemba amatithandiza kumvetsa nkhani yovuta koma yocititsa cidwi imeneyi.

Kodi ndani anacititsa kuti njoka ija izioneka ngati ikulankhula? Anthu a ku Isiraeli wakale anali kudziŵa mfundo zina zimene zinawathandiza kumvetsa cimene cinacitika kuti njokayo ilankhule. Mwacitsanzo, iwo anali kudziŵa kuti ngakhale kuti nyama sizilankhula, mngelo angathe kucititsa kuti nyama izioneka ngati ikulankhula. Mose analembanso nkhani ya Balamu yonena kuti Mulungu anatumiza mngelo kuti acititse bulu wa Balamu kulankhula ngati munthu.—Numeri 22:26-31; 2 Petulo 2:15, 16.

Kodi angelo ena omwe ni adani a Mulungu angacite zozizwitsa? Inde cifukwa Mose anaonapo ansembe amatsenga a ku Iguputo akutengela zina mwa zozizwitsa za Mulungu monga kusandutsa ndodo kuti izioneka ngati njoka. N’zoonekelatu kuti angelo opanduka, amene ni adani a Mulungu, ni amene anacititsa kuti amatsengawo acite zimenezi.—Ekisodo 7:8-12.

Zikuoneka kuti Mose ni amenenso anauzilidwa kulemba buku la m’Baibo la Yobu. Buku limeneli limanenanso zambili za Satana yemwe ni mdani wamkulu wa Mulungu. Iye anatsutsa zoti atumiki onse a Yehova angakhaledi okhulupilika kwa iye zivute zitani. (Yobu 1:6-11; 2:4, 5) N’kutheka kuti cifukwa ca zimenezi, Aisiraeli anadziŵa kuti Satana ni amene anacititsa kuti njoka ya m’munda wa Edeni izioneka ngati ikulankhula, n’kunyenga Hava kuti asakhale wokhulupilika kwa Mulungu.

Koma kodi Satana ni amenedi analankhula kudzela mwa njoka ija? Inde, cifukwa patapita nthawi, Yesu ananena kuti Satana ni “wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Mwina mungavomeleze kuti amene anayambilila kunena bodza ndiye akuyenela kukhala “tate wake wa bodza.” Bodza loyamba limapezeka m’mawu amene njoka inauza Hava. Njoka inatsutsa zimene Mulungu anacenjeza anthu kuti akadzadya zipatso za mtengo woletsedwa adzafa. Njokayo inati: “Kufa simudzafa ayi.” (Genesis 3:4) N’zodziŵikilatu kuti Yesu anali kudziŵa kuti Satana ni amene analankhulitsa njokayo. M’masomphenya amene Yesu anaonetsa mtumwi Yohane, Satana akuchulidwa kuti “njoka yakale ija” ndipo zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino nkhani ya m’munda wa Edeni.—Chivumbulutso 1:1; 12:9.

Kodi ni zovuta kukhulupilila kuti mzimu wamphamvu ungacititse njoka kulankhula ngati munthu? Ngakhale kuti anthu ni ocepa mphamvu poyelekezela na mizimu, amatha kucita zinthu zina zodabwitsa kwambili monga kucititsa zidole kuoneka ngati zikulankhula komanso kupanga zithunzi zooneka ngati zikuyenda.

Umboni Wosatsutsika

Tsopano kodi simukuvomeleza kuti anthu amene amatsutsa nkhani za m’buku la Genesis alibe zifukwa zenizeni zotsutsila? Ndipotu pali umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhani imeneyi inacitikadi.

Mwacitsanzo Yesu Khristu amachedwa “mboni yokhulupilika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Popeza iye ni wangwilo sananamepo kapena kupotoza nkhani inayake. Kuwonjezela pamenepo, iye anauza anthu kuti anali kumwamba kwa zaka zambili-mbili asanabwele padziko lapansi. Ndipotu iye anali kukhala kumwambako na Atate wake, Yehova, “dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:5) Conco analipo pamene zinthu zamoyo padziko lapansi zinayamba kulengedwa. Kodi Yesu ameneyu, yemwe ni mboni yodalilika kuposa onse, anapeleka umboni wotani wokhudza nkhani ya m’munda wa Edeni?

Yesu ananena za Adamu na Hava mosonyeza kuti anali anthu enieni. Iye anachula za ukwati wawo pamene anali kufotokoza zimene Yehova amafuna zoti mwamuna ayenela kukhala na mkazi mmodzi. (Mateyu 19:3-6) Zikanakhala kuti Adamu na Hava sanakhaleko ndipo nkhani yonena za munda wa Edeni, umene iwo anali kukhalamo, ni nthano cabe, ndiye kuti Yesu ananamizidwa kapena ananama. Koma Yesu sanganamizidwe ndiponso sanganame. Pamene nkhani imeneyi inali kucitika m’munda wa Edeni, Yesu anali kumwamba ndipo anali kuona zimene zinali kucitikazo. Conco palibe umboni wina wolondola kwambili kuposa wa Yesu.

Kunena zoona kukayikila nkhani za m’buku la Genesis kumacititsanso kuti anthu asamakhulupilile Yesu. Komanso zimacititsa kuti anthu azilephela kukhulupilila malonjezo odalilika ndiponso nkhani zina zikulu-zikulu za m’Baibo. Tiyeni tione cifukwa cake tikutelo.

[Mau apansi]

a M’Baibo dzina la Mulungu ni Yehova.

b Mfundo imeneyi ni yosiyana na zimene Baibo imaphunzitsa cifukwa Baibo imaphunzitsa kuti zonse zimene Mulungu analenga zinali zabwino. Imafotokozanso kuti pali wina amene anayambitsa zoipa. (Deuteronomo 32:4, 5) Yehova atamaliza kulenga zinthu padziko lapansi ananena kuti zonse zimene analengazo “zinali zabwino kwambili.”—Genesis 1:31.

c Mulungu ni amene anabweletsa Cigumula cimeneci ndipo zikuoneka kuti cinafafanizilatu munda wa Edeni. Lemba la Ezekieli 31:18 limasonyeza kuti pofika zaka za m’ma 1600 B.C.E. “mitengo ya mu Edeni” inali itatha kale. Conco onse amene anayesetsa kufuna-funa malo amene panali munda wa Edeni anangotaya nthawi cifukwa sakanaupeza.

d Onani kabuku kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, kofalitsidwa na Mboni za Yehova.

e N’zocititsa cidwi kuti madokotala masiku ano apeza kuti nthiti imatha kudzicilitsa mwa njila yodabwitsa. Mosiyana na mafupa ena, ngati minofu yake siinaduke nthiti imatha kumelanso.