Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi n’chifukwa chiyani Satana anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava?

Kodi n’chifukwa chiyani Satana anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi n’chifukwa chiyani Satana anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava?

▪ Monga taonera patsamba 8, Satana ndi amene anachititsa kuti njoka ija ilankhule ndi Hava. Ndipo zimenezi ndi zimene Baibulo limanena. Komabe mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani cholengedwa chauzimu chimenechi chinalankhula ndi Hava kudzera mwa njoka?’

Baibulo limanena kuti Satana amachita zinthu ‘mwachinyengo,’ ndipo nkhani ya njokayi ndi umboni wa zimenezi. (Aefeso 6:11) Zimene zinachitika ku Edeni si nthano chabe yonena za nyama inayake imene inalankhula, koma ndi chitsanzo champhamvu chosonyeza kuti Satana amachita zinthu mochenjera ndiponso mwachinyengo pofuna kukopa anthu kuti asamvere Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero?

Satana anayamba waganiza kaye asanasankhe woti alankhule naye. Hava anali womalizira kulengedwa pa zolengedwa zonse zanzeru zimene Mulungu analenga. Choncho Satana anapezerapo mwayi womunamiza ndiponso kum’pusitsa chifukwa choti Hava sankadziwa zambiri. Pogwiritsa ntchito njoka, imene ndi nyama yochenjera kwambiri, Satana anadzibisa kuti zolinga zake zoipa komanso zadyera zisaonekere. (Genesis 3:1) Ndiponso taganizirani zimene zinachitika chifukwa chakuti Satana anachititsa kuti njoka izioneka ngati ikulankhula.

Choyamba, Hava anachita chidwi kwambiri kumva njoka ikulankhula ndipo anafuna kumva zambiri. Iye ankadziwa kuti njoka sizilankhula. Mwamuna wake ndi amene anatchula mayina nyama zonse kuphatikizapo njoka ndipo ayenera kuti anachita zimenezi pambuyo poti wazidziwa bwino nyama zonse. (Genesis 2:19) N’kutheka kuti Hava nayenso anali ataidziwa bwino nyama yochenjera imeneyi. Choncho chinyengo cha Satana chinachititsa Hava kufuna kuchita zinthu zimene anamvazo. Maganizo ake onse anangokhala pamtengo umodzi womwe unali woletsedwa m’munda wonse wa Edeni. Mfundo yachiwiri ndi yakuti, ngati njokayo inalankhula naye ili mumtengo woletsedwawo, kodi Hava ayenera kuti anaganiza chiyani? Mwina anaganiza kuti nyama yosalankhula imeneyo yayamba kulankhula chifukwa choti yadya chipatso choletsedwacho. Mwina anaganiza kuti ngati njoka yayamba kulankhula itadya chipatso cha mumtengowo, ndiye kuti nayenso atadya angachite zoposera pamenepo. Sitingathe kudziwa bwinobwino zimene Hava ankaganiza pa nthawiyi komanso sitikudziwa ngati njokayo inadyadi zipatso za mtengowo. Koma chimene tikudziwa n’chakuti, njokayo itamuuza kuti akadya zipatsozo ‘afanana ndi Mulungu,’ Hava anayamba kukhulupirira zimenezi.

Mawu amene Satana anagwiritsa ntchito polankhula ndi Hava akutiuzanso zambiri. Iye anachititsa Hava kuyamba kuganiza kuti pali zinthu zina zabwino zimene Mulungu sakumupatsa ndiponso kuti akumuphera ufulu. Kuti chiwembu cha Satana chitheke zikanadalira kuti Hava akopeke ndiponso aiwaleko za ubwenzi wake ndi Mulungu, ngakhale kuti Mulungu ndi amene anamupatsa zonse zimene anali nazo. (Genesis 3:4, 5) Chomvetsa chisoni n’chakuti chinyengo cha Satanacho chinagwiradi ntchito. Hava ngakhalenso Adamu sankakonda Yehova mmene anayenera kumukondera. Masiku anonso Satana samalimbikitsa anthu kusonyeza khalidwe lodzikonda komanso lonyalanyaza malangizo a Mulungu?

Nanga kodi cholinga cha Satana pochita zimenezi chinali chiyani kwenikweni? M’munda wa Edeni Satana sanazidziwikitse komanso anabisa zolinga zake. Koma patapita nthawi Satana anadzidziwikitsa. Pamene ankayesa Yesu, anadziwa kuti palibe chifukwa chobisira zolinga zake. Choncho anauza Yesu mosapita m’mbali kuti: ‘Mungogwada pansi n’kundiweramira.’ (Mateyu 4:9) N’zoonekeratu kuti kwa nthawi yaitali Satana wakhala akuchita nsanje poona kuti Yehova Mulungu amalambiridwa. Iye akuchita chilichonse chimene angathe n’cholinga chofuna kulepheretsa anthu kulambira Mulungu kapena kuchititsa kuti kulambira kwawo kukhale kosayenera pamaso pake. Satana amafuna kuti anthu asakhale okhulupirika kwa Mulunguyo.

Baibulo limanena momveka bwino kuti Satana amachita zinthu mwachinyengo kwambiri kuti akwaniritse zofuna zake. Koma ndi zolimbikitsa kudziwa kuti mosiyana ndi Hava, tikhoza kupewa kupusitsidwa ndi Satana “pakuti tikudziwa bwino ziwembu zake.”​—2 Akorinto 2:11.