Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukonzekera Tsiku Lofunika Kwambiri Chaka Chino?

Kodi Mukukonzekera Tsiku Lofunika Kwambiri Chaka Chino?

Kodi Mukukonzekera Tsiku Lofunika Kwambiri Chaka Chino?

PATANGOTSALA maola ochepa kuti Yesu aphedwe, iye anayambitsa mwambo wapadera wokumbukira imfa yake. Mwambo umenewu umatchedwa kuti “chakudya chamadzulo cha Ambuye” kapena “mgonero wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:20; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Posonyeza kuti mwambo umenewu ndi wofunika kwambiri, Yesu ananena kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Kodi mukufunitsitsa kumvera Yesu? Ngati mukufunitsitsadi, chaka chilichonse muyenera kuona kuti tsiku lokumbukira imfa ya Yesu ndi lofunika kwambiri.

Koma kodi mwambo wokumbukira imfa ya Yesu uyenera kuchitika liti? Nanga kodi mungakonzekere bwanji kuti mudzapindule ndi mwambo wofunikawu? Mkhristu aliyense ayenera kuganizira bwino mafunso amenewa.

Kodi Mwambo Umenewu Uyenera Kuchitika Kangati pa Chaka?

Kawirikawiri mwambo wokumbukira chinthu chinachake chofunika kwambiri umachitika kamodzi pa chaka. Mwachitsanzo, pa September 11, 2001, nyumba ziwiri zazitali kwambiri ku America za World Trade Center, zinaphulitsidwa ndi zigawenga ndipo anthu ambiri anaphedwa. Ngakhale kuti anthu a mumzinda wa New York amene abale awo ndi mabwenzi awo anaphedwa saiwala zoopsa zimenezi, chaka chilichonse deti limeneli likafika, anthu okhudzidwawo amalikumbukira mwapadera.

Ndi mmenenso zinalili kale kwambiri. Anthu ankakumbukira zochitika zapadera kamodzi pa chaka (Esitere 9:21, 27) Yehova analamula Aisiraeli kuti chaka chilichonse azichita mwambo wokumbukira mmene iye anawamasulira mozizwitsa ku ukapolo ku Iguputo. M’Baibulo, mwambo umenewu umatchedwa Pasika ndipo Aisiraeli ankachita mwambowu kamodzi pa chaka, pa tsiku limene anamasulidwalo.​—Ekisodo 12:24-27; 13:10.

Pamene Yesu ankayambitsa mwambo wapadera wokumbukira imfa yake, n’kuti atangomaliza kumene kuchita mwambo wa Pasika ndi atumwi ake. (Luka 22:7-20) Ndipo Aisiraeli ankachita mwambo wa Pasika kamodzi pa chaka. Choncho tinganene kuti mwambo watsopanowu, umene unalowa m’malo mwa Pasika, uyeneranso kuchitika kamodzi pa chaka. Koma kodi uyenera kuchitika liti?

Kodi Mwambowu Uyenera Kuchitika Liti?

Kuti tiyankhe funsoli tifunika kumvetsa zinthu ziwiri. Choyamba, kalekale Aisiraeli ankaona kuti tsiku linkayamba madzulo dzuwa likangolowa ndipo linkatha madzulo a tsiku lotsatira dzuwa likalowa. Choncho tsiku linkayamba madzulo ndipo linkathanso madzulo tsiku lotsatira.​—Levitiko 23:32.

Chachiwiri, Baibulo siligwiritsa ntchito kalendala imene timagwiritsa ntchito masiku ano. M’malo mogwiritsa ntchito miyezi ya mayina ngati March ndi April, Baibulo limatchula miyezi ngati Adara ndi Nisani. (Esitere 3:7) Kwa Ayuda akale, kuchokera pamene mwezi watsopano waonekera kukafika pamene mwezi wina watsopano waonekeranso, ankaona kuti padutsa mwezi umodzi. Iwo ankachita Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani umene unali mwezi woyamba pa kalendala yachiyuda. (Levitiko 23:5; Numeri 28:16) Pa Nisani 14 ndi tsiku limenenso Aroma anapachika Ambuye wathu Yesu Khristu. Iye anamwalira patatha zaka 1,545 kuchokera pamene Aisiraeli anachita mwambo woyamba wa Pasika. Kunena zoona, Nisani 14 ndi tsiku lapaderadi kwambiri.

Koma kodi masiku ano pa kalendala yathu ndi tsiku liti limene limafanana ndi Nisani 14? Sizovuta kuwerengera kuti tidziwe tsiku lolondola. Timayamba kuwerengera madeti amenewa motsatira kayendedwe ka mwezi ku Yerusalemu. Nisani 1 imayamba madzulo dzuwa likamalowa, tsiku loyamba limene mwezi waonekera ku Yerusalemu. Nthawi imeneyi, tsiku la March 20 kapena 21 limakhala litatsala pang’ono kukwana kapena litangokwana kumene. Tikawerenga masiku 14 kuchokera pa deti limenelo, timafika pa Nisani 14 ndipo kawirikawiri, mwezi umakhala wathunthu. Potengera kawerengedwe ka m’Baibulo kameneka, chaka chino Nisani 14 idzayamba dzuwa litangolowa, Lamlungu pa April 17, 2011. *

N’chifukwa chake a Mboni za Yehova akukonzekera kuchita mwambowu chaka chino pamodzi ndi anthu enanso amene akufuna kudzakumbukira imfa ya Yesu. Iwo akukuitanani kuti mudzakhale nawo pa mwambo umenewu. Funsani a Mboni za Yehova akwanuko kuti mudziwe nthawi ndi malo kumene kudzachitikire mwambowu. Mwambo umenewu sudzachitika m’mawa kapena masana ayi, koma udzachitika madzulo dzuwa litalowa. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti malinga ndi zimene Baibulo limanena mwambo umenewu uyenera kukhala “chakudya chamadzulo.” (1 Akorinto 11:25) Madzulo a Lamlungu, pa April 17, 2011 ndi tsiku lochita mwambo wapadera umenewu, umene Yesu anayambitsa zaka 1,978 zapitazo. Pa tsiku limeneli dzuwa likadzangolowa, kudzakhala kuyambika kwa Nisani 14, tsiku limene Yesu anafa. Ndiyetu limeneli ndi tsiku loyenereradi kudzakumbukira imfa ya Yesu.

Kodi Tikonzekere Bwanji?

Kodi panopa mungatani pokonzekera mwambo umenewu womwe umachitika kamodzi pa chaka? Njira imodzi ndi kuganizira mofatsa zimene Yesu anatichitira. Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * lathandiza anthu kuyamikira kwambiri mmene imfa ya Yesu imatithandizira.​—Mateyu 20:28.

Pokonzekera mwambo wapadera umenewu tingawerengenso zimene zinachitika pa nyengo imene Yesu anafa. Pamasamba otsatirawa mupezapo tchati. Danga limene lili kumanja lili ndi ndandanda ya nkhani zofanana za m’Baibulo zonena zimene zinachitika Yesu atatsala pang’ono kufa. Tchatichi chilinso ndi ndandanda ya mitu ya m’buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako * imene ikufotokoza zochitika zimenezi.

Danga limene lili kumanzere lili ndi masiku a chaka chino amene akugwirizana ndi masiku amene zinthu zimenezi zinachitika. Tikukupemphani kuti, kutatsala masiku angapo kuti tsiku la Chakudya cha Madzulo cha Ambuye lifike, tsiku lililonse muzidzawerenga mavesi a m’Baibulo amene asonyezedwa patchatichi. Zimenezi zidzakuthandizani kukonzekera tsiku lofunika kwambiri pa chaka limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Koma mwina tsiku limeneli silingafanane ndi limene Ayuda amachita Pasika masiku ano. N’chifukwa chiyani zili choncho? Ayuda ambiri masiku ano amachita Pasika pa Nisani 15 chifukwa amakhulupirira kuti lamulo la pa Ekisodo 12:6 linkanena kuti azichita Pasika pa Nisani 15. (Werengani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1990, tsamba 14.) Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene mungawerengere masiku kuti mupeze tsiku limeneli, werengani Nsanja ya Olonda yachingerezi ya June 15, 1977, tsamba 383 mpaka 384.

^ ndime 14 Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Onani tsamba 47 mpaka 56 ndiponso tsamba 206 mpaka 208. Mukhozanso kuwerenga buku limeneli lachingelezi pa Intaneti pa adiresi iyi: www.pr418.com.

^ ndime 15 Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Mudzakumbukire nawo imfa ya Yesu Lamlungu, April 17, 2011

[Tchati/​Zithunzi pamasamba 23, 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MLUNGU WOMALIZA

2011 Lachiwiri, April 12

Tsiku la Sabata

Yohane 11:55–12:1

gt 101, ndime 2-4 *

NISANI 9 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

Kale Aisiraeli ankaona kuti tsiku linkayamba madzulo dzuwa litangolowa ndipo linkatha tsiku lotsatira dzuwa likulowa

Kudya ndi Simoni wakhate

Mariya adzoza Yesu mafuta onunkhiraa nado

Ayuda abwera kudzaona Yesu ndi Lazaro

Mateyu 26:6-13

Maliko 14:3-9

Yohane 12:2-11

gt 101, pars. 5-9

2011 Lachitatu, April 13

▪ Alowa Yerusalemu mwaulemerero

Aphunzitsa m’kachisi

Mateyu 21:1-11, 14-17

Maliko 11:1-11

Luka 19:29-44

Yohane 12:12-19

gt 102

NISANI 10 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

Agona ku Betaniya

2011 Lachinayi, April 14

▪ Ulendo wam’mawa wolowa mu Yerusalemu

▪ Achotsa ochita malonda m’kachisi

▪ Mawu a Yehova amveka kuchokera kumwamba

Mateyu 21:12, 13,18, 19

Maliko 11:12-19

Luka 19:45-48

Yohane 12:20-50

gt 103, 104

NISANI 11 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

2011 Lachisanu, April 15

▪ Aphunzitsa m’kachisi pogwiritsa ntchito mafanizo

▪ Adzudzula Afarisi

▪ Aona mayi akupereka ndalama m’kachisi

▪ Aneneratu za kuwonongedwa kwa Yerusalemu

▪ Anena chizindikiro cha m’tsogolo cha kukhalapo kwake

Mateyu 21:19–25:46

Maliko 11:20–13:37

Luka 20:1–21:38

gt 105 to 112, ndime 1

NISANI 12 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

2011 Loweruka, April 16

▪ Apuma ndi ophunzira ake ku Betaniya

▪ Yudasi akonza zomupereka

Mateyu 26:1-5, 14-16

Maliko 14:1, 2, 10, 11

Luka 22:1-6

gt 112, ndime 2-4

NISANI 13 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

2011 Lamlungu, April 17

▪ Petulo ndi Yohane apita kukakonza a Pasika

▪ Yesu ndi atumwi ake ena 10 akufika madzulo

Mateyu 26:17-19

Maliko 14:12-16

Luka 22:7-13

gt 112, ndime 5​ 113, ndime 1

NISANI 14 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

▪ Achita Pasika

▪ Asambitsa mapazi a atumwi ake

▪ Auza Yudasi kuti achoke

▪ Ayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake

Mateyu 26:20-35

Maliko 14:17-31

Luka 22:14-38

Yohane 13:1–17:26

gt 113, ndime. 2​–mutu 116

pakati pa usiku

2011 Lolemba, April 1

▪ Aperekedwa ndi kumangidwa m’munda wa Getsemani

▪ Atumwi athawa

▪ Azengedwa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda

▪ Petulo akana Yesu

Mateyu 26:36-75

Maliko 14:32-72

Luka 22:39-62

Yohane 18:1-27

gt 117​–mutu 120

▪ Amuitanitsanso ku Khoti Lalikulu la Ayuda

▪ Apita naye kwa Pilato, kenako kwa Herode ndipo abwereranso naye kwa Pilato

▪ Aweruzidwa kuti kenako apachikidwa

▪ Afa cha m’ma 3 koloko madzulo

▪ Achotsa mtembo wake n’kuuika m’manda

Mateyu 27:1-6

Maliko 15:1-47

Luka 22:63–23:56

Yohane 18:28-19:42

gt 121​127, ndime 7

NISANI 15 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

Tsiku la Sabata

2011 Lachiwiri, April 19

▪ Pilato alamula kuti aike alonda pamanda a Yesu

Mateyu 27:62-66

gt 127, ndime 8-9

NISANI 16 (ikuyamba madzulo dzuwa litangolowa)

Maliko 16:1

2011 Lachitatu, April 20

▪ Aukitsidwa

▪ Aonekera kwa ophunzira ake

Mateyu 28:1-15

Maliko 16:2-8

Luka 24:1-49

Yohane 20:1-25

gt 127, ndime 10​–mutu 129, ndime 10

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 29 Manambalawa akusonyeza mitu ya m’buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (gt). Mungaone tchati chosonyeza tsatanetsatane wa zimene Yesu anachita masiku ake omaliza kuchita utumiki, mu buku lachingelezi la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” tsamba 290. Mabuku amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.