Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu Ulemu

Phunzitsani Ana Anu Ulemu

Phunzitsani Ana Anu Ulemu

MWAMBI wina wa ku Germany umati: “Munthu amene amavula chipewa amatha kuyenda bwinobwino kulikonse.” Anthu azikhalidwe zosiyanasiyana amaona kuti munthu ndi waulemu akavula chipewa polowa m’nyumba ya munthu wina kapena akamapatsana moni. Choncho mwambi umene tatchulawu umatanthauza kuti anthu amalandira bwino ndiponso kukomera mtima munthu waulemu.

Zimakhala zosangalatsa kwambiri ana akakhala aulemu. M’bale wina woyang’anira dera ku Honduras amayenda ndi ofalitsa a misinkhu yosiyanasiyana mu ulaliki wa khomo ndi khomo. Iye anati, “Ndaona kuti ana amene amaphunzitsidwa kukhala ndi ulemu, anthu amawamvetsera bwino kwambiri kuposa ineyo.”

Masiku ano, pamene anthu ambiri sakusonyezanso ulemu, kukhala waulemu n’kothandiza kwambiri. Koma chifukwa chachikulu chokhalira aulemu n’chakuti Malemba amatilangiza kuti “makhalidwe anu akhale oyenera uthenga wabwino wa Khristu.” (Afil. 1:27; 2 Tim. 3:1-5) Choncho, tiyenera kuphunzitsa ana athu kuti azilemekeza ena. Kodi tingawaphunzitse bwanji kusonyeza ulemu mochokera pansi pa mtima osati mwachiphamaso? *

Apatseni Chitsanzo pa Nkhani ya Ulemu

Ana amaphunzira zinthu mwa kutengera zitsanzo zimene aona. Choncho njira yabwino imene makolo angaphunzitsire ana awo ndi kukhala chitsanzo chabwino iwowo pa nkhani yopereka ulemu. (Deut. 6:6, 7) Kukambirana ndi ana anu za ubwino wa ulemu n’kofunika ndithu koma pakokha si kokwanira. Kuwonjezera pa zimenezi, kuwapatsa chitsanzo pa nkhaniyi n’kofunika kwambiri.

Taganizirani za Paula * amene analeredwa ndi mayi ake okha m’banja lachikhristu. Iye amalemekeza munthu aliyense. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Iye anati, “Mayi athu ankapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi, choncho anafe tinatengera.” Mkhristu wina, dzina lake Walter, anaphunzitsa ana ake kuti azilemekeza mayi awo omwe si Mkhristu. Iye anati: “Ndinkaphunzitsa ana anga kulemekeza mayi awo mwa kuwapatsa chitsanzo. Sindinkalankhula zinthu zonyoza mkazi wanga.” Walter anapitiriza kuphunzitsa ana ake aamuna Mawu a Mulungu ndipo ankapempha Yehova kuti amuthandize pa nkhaniyi. Panopa mwana mmodzi akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ndipo wina akuchita upainiya. Anyamatawa amakonda ndiponso kulemekeza makolo awo onse awiri.

Baibulo limanena kuti: “Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.” (1 Akor. 14:33) Zinthu zonse zimene Yehova amachita amazichita mwadongosolo. Akhristu ayenera kutengera khalidwe la Mulungu limeneli n’kumakhala aukhondo kunyumba kwawo. Makolo ena amaphunzitsa ana awo kuti aziyala pabedi m’mawa uliwonse asanapite kusukulu, aziika zovala zawo pamalo oyenera ndiponso azigwira nawo ntchito zina zapakhomo. Ana akamaona kuti pakhomo m’paukhondo, nawonso amakhala aukhondo ndipo chipinda ndi zinthu zawo zimakhalanso zaukhondo.

Kodi ana anu amaona bwanji zimene amaphunzira kusukulu? Kodi amayamikira zimene aphunzitsi awo amawachitira? Nanga kodi makolonu mumasonyeza kuyamikira aphunzitsi a ana anu? Ana anu adzatengera chitsanzo chanu pa mmene mumaonera maphunziro ndiponso aphunzitsi awo. Alimbikitseni kuti azithokoza aphunzitsi awo. Munthu akathokoza munthu wina chifukwa chakuti wamuthandiza pa zinazake, amasonyeza kuti ndi waulemu. Tingathokoze anthu monga aphunzitsi, adokotala, ndiponso ogulitsa m’sitolo. (Luka 17:15, 16) Tikuyamikira kwambiri ana achikhristu amene amasiyana ndi anzawo pa nkhani ya ulemu ndiponso makhalidwe abwino.

Abale ndi alongo mu mpingo wachikhristu ayenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya ulemu. Zimakhala zosangalatsa kuona ana mu mpingo akusonyeza khalidwe labwino mwa kupempha zinthu mwaulemu komanso kunena kuti “zikomo.” Akuluakulu akamalemekeza Yehova mwa kumvetsera mwatcheru pa misonkhano, ana amatengera chitsanzo chawo. Ana akhoza kuphunzira kulemekeza anthu ena akamaona chitsanzo chabwino pa Nyumba ya Ufumu. Mwachitsanzo, mwana wina wa zaka zinayi dzina lake Andrew waphunzira kale kunena mawu aulemu monga akuti “wawa” kapena “tikudutsa” akamadutsana ndi anthu akuluakulu.

Kodi pali njira inanso imene makolo angaphunzitsire ana awo khalidwe labwino? Makolo ayenera kupatula nthawi yokambirana ndi ana awo zitsanzo za m’Mawu a Mulungu za anthu amene anasonyeza ulemu.​—Aroma 15:4.

Aphunzitseni Zitsanzo za M’Baibulo

Mayi a Samueli ayenera kuti anamuphunzitsa kugwadira Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe. Pa nthawi imene anapita naye kuchihema chopatulika, Samueli ayenera kuti anali ndi zaka zitatu kapena zinayi zokha. (1 Sam. 1:28) Mwina mungachite bwino kuphunzitsa mwana wanu kuti azipereka bwinobwino moni wa kudera lanu, monga “Muli bwanji?,” “Mwadzuka bwanji?” kapena “Mwaswera bwanji?” Mofanana ndi Samueli, ana anu akhoza “kukondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.”​—1 Sam. 2:26.

Mungachite bwinonso kugwiritsa ntchito zitsanzo za m’Baibulo powathandiza kusiyanitsa ulemu ndi mwano. Mwachitsanzo, mfumu ya Isiraeli, Ahaziya, yemwe anali wosakhulupirika, atafuna kuonana ndi mneneri Eliya, anatuma “mtsogoleri wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50” kuti akamutenge. Mtsogoleriyo atafika analankhula molamula kuti mneneriyo atsagane naye. Apatu anachitira mwano munthu woimira Mulungu. Kodi Eliya anayankha bwanji? Iye anati: “Ngati ndili munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Izi n’zimene zinachitikadi. “Moto unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50.”​—2 Maf. 1:9, 10.

Kenako mtsogoleri winanso wa asilikali 50 anatumizidwa kukatenga Eliya. Nayenso analamula Eliya kuti atsagane naye. Apanso, moto unatsika kumwamba n’kuwanyeketsa. Koma mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 atafika kwa Eliya, anasonyeza ulemu. M’malo molamula Eliya, iye anagwada n’kupempha mochonderera kuti: “Inu munthu wa Mulungu woona, chonde moyo wanga ndi moyo wa atumiki anu 50 awa ukhale wamtengo wapatali m’maso mwanu. Pajatu moto unatsika kumwamba n’kunyeketsa atsogoleri awiri aja ndi magulu awo a asilikali 50, koma tsopano moyo wanga ukhale wamtengo wapatali m’maso mwanu.” Kodi mneneri wa Mulunguyu akanapempha kuti moto utsike n’kunyeketsa munthu amene mwina anachita mantha koma analankhula mwaulemu? Ayi ndithu. M’malomwake mngelo wa Yehova anauza Eliya kuti atsagane ndi mtsogoleriyo. (2 Maf. 1:11-15) Izitu zikusonyeza kuti ulemu ndi wofunika kwambiri.

Mtumwi Paulo atagwidwa pakachisi ndi asilikali achiroma sanangoganiza kuti ali ndi ufulu wolankhula. Iye anapempha mwaulemu kwa mkulu wa asilikaliwo kuti: “Mungandilole kodi kulankhula nanu pang’ono?” Izi zinachititsa kuti Paulo apatsidwe mwayi woyankhapo pa mlandu wake.​—Mac. 21:37-40.

Pa nthawi imene ankaweruzidwa, Yesu anamenyedwa mbama. Koma iye anafunsa mwanzeru kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?” Pa mawu amenewa palibe amene akananena kuti Yesu walankhula mwamwano.​—Yoh. 18:22, 23.

Mawu a Mulungu amatipatsanso zitsanzo za mmene tingayankhire ngati wina akutidzudzula mwamphamvu kapena mmene tingavomerezere mwaulemu zinthu zimene tinalakwitsa kapena zimene tinalephera kuchita. (Gen. 41:9-13; Mac. 8:20-24) Mwachitsanzo, Abigayeli anapepesa chifukwa cha chipongwe chimene mwamuna wake Nabala anachitira Davide. Kuwonjezera pamenepo, anapereka mphatso zambirimbiri. Davide anachita chidwi kwambiri ndi zimene Abigayeli anachita moti Nabala atamwalira Davide anamukwatira.​—1 Sam. 25:23-41.

Muziphunzitsa ana anu kuti akhale aulemu nthawi zonse ngakhale pamene apanikizika kwambiri. ‘Tikamaonetsa kuwala kwathu pamaso pa anthu’ mwanjira imeneyi, zimathandiza kuti ‘Atate wathu wakumwamba alemekezeke.’​—Mat. 5:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Komabe pamene makolo akuthandiza ana awo kuti azilemekeza akuluakulu, ayeneranso kuwathandiza kuti asamangololera zofuna za anthu amene angafune kuwachita zachipongwe. Onani Galamukani! ya October 2007, tsamba 3 mpaka 11.

^ ndime 7 Tasintha mayina ena.