Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha

Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha

Anthu Ovomerezeka ndi Mulungu Adzapeza Moyo Wosatha

“Inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama. Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.”​—SAL. 5:12.

1, 2. Kodi Eliya anapempha chiyani kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati, nanga anamutsimikizira chiyani?

MKAZI wamasiye wa ku Zarefati pamodzi ndi mwana wake anali ndi njala. Atatsala pang’ono kusonkha moto kuti aphike chakudya kunafika Eliya mneneri wa Mulungu, amenenso anali ndi njala, ndipo anapempha madzi akumwa ndi mkate. Mayiyu ankafuna kupatsa Eliya madzi akumwa koma anali ndi “ufa pang’ono mumtsuko waukulu ndi mafutanso pang’ono mumtsuko waung’ono” zoti aphikire chakudya. Mayiyu anaona kuti analibe chakudya chokwanira choti n’kugawirako mneneriyo ndipo anamuuza zimenezi.​—1 Maf. 17:8-12.

2 Koma Eliya anakakamiza mayiyu kuti: “Pa zimene uli nazozo, ukayambe wandikonzera mtanda waung’ono wa mkate, n’kubwera nawo kwa ine. Kenako, ukakonze chakudya chako ndi cha mwana wako. Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu siutha, ndipo mafuta amene ali mumtsuko waung’ono saatha.’”​—1 Maf. 17:13, 14.

3. Kodi tiyenera kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri iti?

3 Nkhani imene mkazi wamasiyeyu anakumana nayo inali yaikulu kwambiri. Sikuti iye anangofunika kusankha kugawirako chakudya chochepa chimene anali nacho kwa mneneriyu. Nkhani yake inali yakuti, kodi akanakhulupirira Yehova kuti adzamupulumutsa pamodzi ndi mwana wake? Kapena kodi akanaika patsogolo zofuna zake zakuthupi m’malo mokhala wovomerezeka ndi Mulungu ndiponso kukhala naye pa ubwenzi? Ifenso tiyenera kusankha pa nkhani ngati imeneyi. Kodi tidzasonyeza kuti kukhala ovomerezeka ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi zinthu zakuthupi? Tilitu ndi zifukwa zabwino zokhulupirira ndiponso kutumikira Mulungu. Ndipotu pali zinthu zimene tingachite kuti tikhale ovomerezeka ndi Mulungu.

‘Ndinu Woyenera Kulambiridwa’

4. N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kuti tizimulambira?

4 Yehova amayembekezera kuti anthu azimutumikira mmene iye akufunira ndipo salakwitsa kuyembekezera zimenezi. Nthawi ina gulu la atumiki ake akumwamba linatsimikizira mfundo imeneyi ponena kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chiv. 4:11) Yehova ndi woyenera kulambiridwa chifukwa chakuti ndi Mlengi wa zinthu zonse.

5. N’chifukwa chiyani chikondi cha Mulungu chiyenera kutilimbikitsa kumutumikira?

5 Chifukwa china chimene timatumikirira Yehova n’chakuti palibe wina amene amatikonda kuposa iyeyo. Baibulo limati: “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.” (Gen. 1:27) Anthu ali ndi ufulu wosankha zochita ndipo Mulungu anawalenga ndi luso loti azitha kusankha bwino. Yehova ndi Atate wa anthufe chifukwa ndiye anatipatsa moyo. (Luka 3:38) Mofanana ndi bambo aliyense wabwino, iye amapatsa ana ake chilichonse chofunikira kuti azisangalala ndi moyo. “Iye amawalitsira dzuwa lake” ndiponso “kuvumbitsira mvula” padziko kuti pakhale chakudya chambiri komanso kuti dzikolo likhale lokongola.​—Mat. 5:45.

6, 7. (a) Kodi Adamu anabweretsera ana ake onse mavuto ati? (b) Kodi nsembe ya Khristu idzathandiza bwanji anthu amene amafuna kukhala ovomerezeka ndi Mulungu?

6 Yehova anatipulumutsanso ku zotsatira zoipa za uchimo. Pamene Adamu anachimwa anakhala ngati munthu wotchova juga amene anaba ndalama zofunika kugwiritsa ntchito panyumba n’kukatchovera juga. Popandukira Mulungu, Adamu anabera ana ake tsogolo lawo labwino lokhala ndi moyo wosangalala kwamuyaya. Popeza kuti anachita zinthu modzikonda, anachititsa anthu kukhala akapolo a kupanda ungwiro. Choncho anthu onse amadwala, amakumana ndi zinthu zokhumudwitsa ndipo pamapeto pake amafa. Koma kuti kapolo amasulidwe pamafunika malipiro ndipo Yehova wapereka malipirowo kuti atipulumutse ku zotsatira zoipa za ukapolowo. (Werengani Aroma 5:21.) Yesu Khristu anachita mogwirizana ndi chifuniro cha Atate wake mwa kupereka “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Posachedwapa anthu onse amene Mulungu akuwavomereza adzapindula kwambiri ndi dipo limene Mulunguyo analipira.

7 Mlengi wathu Yehova watipatsa zinthu zambiri kuposa wina aliyense kuti tikhale ndi moyo wabwino ndi wosangalala. Ngati tipitiriza kukhala ovomerezeka ndi Mulungu tidzaona mmene iye adzathetsere mavuto onse a anthu. Yehova adzapitiriza kusonyeza aliyense wa ife payekha kuti iye “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”​—Aheb. 11:6.

“Anthu Ako Adzadzipereka Mofunitsitsa”

8. Kodi zimene zinachitikira Yesaya zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yotumikira Mulungu?

8 Kuti tikhale ovomerezeka ndi Mulungu tiyenera kugwiritsa ntchito bwino ufulu wathu wosankha zinthu. Izi zili choncho chifukwa Yehova sakakamiza munthu kuti azimutumikira. Mu nthawi ya Yesaya, Mulungu anafunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” Yehova ankalemekeza mneneri wake Yesaya ndiponso ufulu wake wosankha zinthu. Taganizirani mmene Yesayayo anamvera mumtima mwake pamene anasankha yekha ndi kuyankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”​—Yes. 6:8.

9, 10. (a) Kodi tizitumikira Mulungu ndi mtima wotani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutumikira Yehova ndi mtima wathu wonse?

9 Anthu ali ndi ufulu wosankha kutumikira Mulungu kapena ayi. Yehova amafuna kuti tizimutumikira mwa kufuna kwathu. (Werengani Yoswa 24:15.) Munthu aliyense amene amatumikira Mulungu monyinyirika kapena amene amamutumikira pongofuna kusangalatsa anthu ena sakondweretsa Mulungu. (Akol. 3:22) Sitingakhale ovomerezeka ndi Mulungu tikamachita utumiki wathu wopatulika “monyinyirika” mwa kulola zinthu za m’dzikoli kudodometsa kulambira kwathu. (Eks. 22:29) Yehova amadziwa kuti tikamamutumikira ndi mtima wathu wonse tidzapindula. N’chifukwa chake Mose analimbikitsa Aisiraeli kuti asankhe kukhala ndi moyo ‘mwa kukonda Yehova Mulungu wawo, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira.’​—Deut. 30:19, 20.

10 Poimba nyimbo yotamanda Yehova, Mfumu Davide ya ku Isiraeli inati: “Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo. Wadzikongoletsa ndi ulemerero, ndipo gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.” (Sal. 110:3) Masiku ano anthu ambiri amangokhalira kufunafuna chuma ndiponso kusangalala. Koma anthu amene amakonda Yehova, nthawi zonse amaika patsogolo utumiki wopatulika. Iwo akamachita khama polalikira uthenga wabwino, amasonyeza kuti utumiki wopatulika ndi wofunika kwambiri pa moyo wawo. Amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akhoza kuwasamalira tsiku ndi tsiku.​—Mat. 6:33, 34.

Nsembe Zimene Mulungu Amavomereza

11. Kodi Aisiraeli ankayembekezera kupindula chiyani chifukwa chopereka nsembe kwa Yehova?

11 Pa nthawi ya pangano la Chilamulo, anthu ankapereka nsembe zovomerezeka kuti Mulungu awayanje. Lemba la Levitiko 19:5 limati: “Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni.” M’buku lomweli la m’Baibulo timawerenganso kuti: “Mukafuna kupereka nsembe yoyamikira kwa Yehova muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni.” (Lev. 22:29) Pamene Aisiraeli ankapereka nsembe za nyama zovomerezeka paguwa la nsembe la Yehova, utsi umene unkakwera kumwamba unali ngati ‘fungo lokhazika mtima pansi’ kwa Mulungu woona. (Lev. 1:9, 13) Mulungu ankasangalala ndi kutsitsimulidwa ndi nsembe zimene anthu ankapereka chifukwa chomukonda. Tikhoza kupeza mfundo zotithandiza masiku ano pa zimene zinkachitika m’nthawi ya Chilamuloyi. Masiku anonso, Yehova amayanja anthu amene amapereka nsembe zovomerezeka kwa iye. Koma kodi Mulungu amavomereza nsembe zotani? Tiyeni tikambirane njira ziwiri zoperekera nsembe zovomerezeka. Njirazi ndi zochita ndiponso zolankhula zathu.

12. Kodi ndi makhalidwe ati amene angachititse ‘kupereka matupi athu ngati nsembe’ kukhala konyansa kwa Mulungu?

12 M’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aroma anati: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Kuti munthu ayanjidwe ndi Mulungu, nthawi zonse thupi lake liyenera kukhala lovomerezeka. Ngati munthu angadzidetse ndi fodya, chamba, mankhwala osokoneza bongo kapena kuledzera, nsembe yake ingakhale yopanda phindu. (2 Akor. 7:1) Komanso popeza munthu amene “amachita dama amachimwira thupi lake,” ndiye kuti khalidwe loipa la mtundu uliwonse limachititsa kuti nsembe yake ikhale yonyansa kwa Yehova. (1 Akor. 6:18) Kuti munthu akondweretse Mulungu ayenera ‘kukhala woyera m’makhalidwe ake onse.’​—1 Pet. 1:14-16.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kutamanda Yehova?

13 Nsembe ina imene Yehova amasangalala nayo ndi yokhudza zolankhula zathu. Nthawi zonse anthu amene amakonda Yehova amalankhula zinthu zabwino za iye akakhala pa gulu kapena pamene ali paokha kunyumba kwawo. (Werengani Salimo 34:1-3.) Werengani Masalimo 148 mpaka 150 kuti muone mmene masalimo atatu amenewa akutilimbikitsira mobwerezabwereza kutamanda Yehova. Ndithudi, “m’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.” (Sal. 33:1) Ndipotu Yesu Khristu, amene ndi chitsanzo chathu, anagogomezera kufunika kotamanda Mulungu mwa kulalikira uthenga wabwino.​—Luka 4:18, 43, 44.

14, 15. Kodi Hoseya analimbikitsa Aisiraeli kupereka nsembe zotani, ndipo Yehova anachita chiyani?

14 Tikamalalikira mwakhama timasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso timafuna kukhala ovomerezeka ndi iye. Mwachitsanzo, taganizirani mmene mneneri Hoseya analimbikitsira Aisiraeli atayamba kulambira konyenga n’kusiya kukhala ovomerezeka ndi Mulungu. (Hos. 13:1-3) Hoseya anawalimbikitsa kuchonderera Yehova kuti: “Tikhululukireni zolakwa zathu. Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.”​—Hos. 14:1, 2.

15 Mwana wamphongo wa ng’ombe anali nsembe ya mtengo wapatali kwambiri imene Mwisiraeli akanapereka kwa Yehova. Choncho mawu ochokera pansi pa mtima amene munthu analankhula atawaganizira bwino potamanda Mulungu woona, ankaimira “ana amphongo a ng’ombe.” Kodi Yehova ankawachitira chiyani anthu amene ankapereka nsembe zoterozo? Iye anati: “Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hos. 14:4) Yehova ankakhululukira, kuyanja ndiponso kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene anapereka nsembe zotamandazi.

16, 17. Kodi Yehova amaona bwanji munthu akamalalikira uthenga wabwino chifukwa chomukhulupirira?

16 Kuyambira kalekale, kutamanda Yehova poyera kwakhala kofunika kwambiri pa kulambira koona. Wamasalimo ankaona kulemekeza Mulungu woona kukhala kofunika kwambiri moti anachonderera Mulungu kuti: “Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga.” (Sal. 119:108) Nanga bwanji masiku ano? Ponena za khamu la anthu masiku ano, mneneri Yesaya analosera kuti: ‘Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse. Mulungu adzalandira mphatso zawo paguwa lake lansembe.’ (Yes. 60:6, 7) Pokwaniritsa ulosi umenewu, anthu mamiliyoni ambiri ‘akupereka kwa Mulungu nsembe yomwe ndi chipatso cha milomo yawo. Amagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.’​—Aheb. 13:15.

17 Kodi inuyo mumapereka kwa Mulungu nsembe zovomerezeka? Ngati panopa simukuchita zimenezi, kodi mungasinthe zinthu zina pa moyo wanu kuti muyambe kutamanda Yehova poyera? Nsembe zanu “zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ng’ombe yamphongo” ngati mutayamba kulalikira uthenga wabwino chifukwa cha chikhulupiriro chanu. (Werengani Salimo 69:30, 31.) Dziwani kuti ‘fungo lokhazika mtima pansi’ la nsembe zanu zotamanda lidzafika kwa Yehova ndipo adzakuvomerezani. (Ezek. 20:41) Pamenepo mudzasangalala koposa.

‘Yehova Adzadalitsa Aliyense Wolungama’

18, 19. (a) Kodi anthu ambiri amaona bwanji kutumikira Mulungu masiku ano? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu amene asiya kuvomerezedwa ndi Mulungu?

18 Masiku ano, anthu ambiri amanena mawu ofanana ndi amene anthu a mu nthawi ya Malaki ankanena, kuti: “Kutumikira Mulungu n’kopanda phindu. Tapindulanji chifukwa chomutumikira?” (Mal. 3:14) Anthuwa amasokonezeka chifukwa chongofunafuna zinthu za kuthupi moti amaona kuti n’zosatheka kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Amaonanso kuti malamulo a Mulungu ndi osathandiza masiku ano. Chifukwa cha zimenezi amaona kuti kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi kungotaya nthawi komanso kuti ndi chinthu chongowavutitsa.

19 Maganizo amenewa anayambira m’munda wa Edeni pamene Satana anakopa Hava. Iye anachititsa Hava kuganiza kuti moyo wabwino umene Yehova anali atamupatsa si wofunika komanso kuti kuvomerezedwa ndi Mulungu n’kopanda phindu lililonse. Masiku ano Satana amachititsanso anthu kukhulupirira kuti palibe chimene angapindule chifukwa chochita zimene Mulungu amafuna. Komatu Hava ndi mwamuna wake anadzazindikira kuti zotsatira za kusiya kuvomerezedwa ndi Mulungu ndi imfa basi. Masiku anonso, anthu amene amatsatira chitsanzo chawo choipa, posachedwapa adzazindikiranso zomwezo.​—Gen. 3:1-7, 17-19.

20, 21. (a) Kodi mkazi wamasiye wa ku Zarefati anachita chiyani ndipo zinthu zinamuyendera bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira mkazi wamasiye wa ku Zarefati ndipo tingachite bwanji zimenezi?

20 Tsopano taganizirani kusiyana kwa zinthu zomvetsa chisoni zimene Adamu ndi Hava anakumana nazozi ndi zimene tatchula koyambirira kuja zokhudza Eliya ndi mkazi wamasiye wa ku Zarefati. Atamva mawu olimbikitsa a Eliya, mayiyo anakonza mkate ndipo anayamba ndi kupatsa mneneriyo chakudya. Kenako Yehova anakwaniritsa lonjezo limene ananena kudzera mwa Eliya. Nkhaniyi imati: “[Mayiyo], banja lake, ndi Eliya anadya kwa masiku ambiri. Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe, ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya.”​—1 Maf. 17:15, 16.

21 Mkazi wamasiye wa ku Zarefati anachita zinthu zimene anthu ochepa kwambiri padzikoli angachite. Iye anakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu adzamupulumutsa ndipo Mulungu sanamutaye. Nkhaniyi ndiponso nkhani zina za m’Baibulo zimatitsimikizira kuti Yehova ndi woyeneradi kuti tizimukhulupirira. (Werengani Yoswa 21:43-45; 23:14.) Zinthu zimene zachitikira Mboni za Yehova masiku ano zimaperekanso umboni wakuti Mulungu sadzataya anthu amene iye amawavomereza.​—Sal. 34:6, 7, 17-19. *

22. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri panopa kuti tiziyesetsa kukhala ovomerezeka ndi Mulungu?

22 Tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo kwa anthu “onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi” layandikira kwambiri. (Luka 21:34, 35) Palibe munthu amene angathawe chiweruzo chimenechi. Palibe chuma kapena zinthu zakuthupi zimene mtengo wake ungafanane ndi kumva mawu a Woweruza wosankhidwa ndi Mulungu akuti: “Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu.” (Mat. 25:34) Ndithudi, ‘Yehova adzadalitsa aliyense wolungama. Adzamutchinga ndi chivomerezo chake ngati kuti akum’teteza ndi chishango chachikulu.’ (Sal. 5:12) Tiyenitu tiziyesetsa kukhala ovomerezeka ndi Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 2005, tsamba 13, ndime 15; ndiponso ya August 1, 1997, tsamba 20 mpaka 25.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kuti tizimulambira ndi mtima wathu wonse?

• Kodi Yehova amalandira nsembe zotani masiku ano?

• Kodi “ana amphongo a ng’ombe” amaimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kupereka nsembe zoterezi kwa Yehova?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ovomerezeka ndi Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi mneneri wa Mulungu anauza mayi wosauka kuti asankhe pa nkhani iti?

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi timapindula bwanji tikamapereka nsembe zotamanda kwa Yehova?

[Chithunzi patsamba 17]

Simudzagwiritsidwa mwala mukamakhulupirira Yehova ndi mtima wonse