Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

“Uthenga wabwino uwu . . . ”​—MATEYU 24:14.

AKHRISTU ayenera kumalalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Ayeneranso kufotokozera ena kuti Ufumuwo ndi boma la m’tsogolo limene lidzalamulira dziko lonse lapansi mwachilungamo. Komabe m’Baibulo mawu akuti “uthenga wabwino” amagwiritsidwanso ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli mawu ngati, “uthenga wabwino wa chipulumutso” (Salimo 96:2); “uthenga wabwino wa Mulungu” (Aroma 15:16); ndi “uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu.”​—Maliko 1:1.

Mwachidule, uthenga wabwino ndi mfundo zonse za choonadi zimene Yesu ananena ndiponso zimene ophunzira ake analemba. Yesu asanapite kumwamba anauza otsatira ake kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20) Choncho ntchito ya Akhristu oona sikungouza anthu za Ufumu, koma ayeneranso kuyesetsa kuphunzitsa anthuwo kuti akhale ophunzira a Yesu.

Koma kodi matchalitchi akuchitadi zimenezi? Anthu ambiri sadziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi chiyani ndipo anthu oterewa sangaphunzitse ena zolondola ponena za Ufumuwo. M’malomwake, iwo amalalikira zinthu zongofuna kusangalatsa anthu, zokhudza kukhululukidwa machimo ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu. Komanso iwo amamanga zipatala, masukulu ndiponso nyumba za anthu osauka ndi cholinga chakuti anthu alowe tchalitchi chawo. N’zoonadi kuti zimenezi zingachititse anthu ambiri kulowa m’zipempedzozo, komabe sizingathandize anthuwo kukhala Akhristu oona, otsatira ndi mtima wonse zimene Yesu anaphunzitsa.

Katswiri wina wa maphunziro achipembedzo analemba kuti: “Akatswiri a maphunziro achipembedzo ndiponso azibusa ambiri amavomereza mfundo yakuti Akhristu ayenera kuphunzitsa ena kuti akhale ophunzira a Yesu. Amavomerezanso kuti Akhristu ayenera kuphunzitsa anthu zonse zimene Yesu ananena. . . . Zimene Yesu analamula pa nkhani imeneyi ndi zomveka bwino. Kungoti ifeyo sitichita zimene iye ananena. Tilibe nazo chidwi kwenikweni ndipo zikuoneka kuti sitidziwa mmene tingachitire zimenezi.”

Mofanana ndi zimene katswiriyu ananena, kafukufuku amene magazini ina yachikatolika ku United States inachita anasonyeza kuti Akatolika okwana 95 pa 100 alionse amavomereza kuti kulalikira uthenga wabwino ndi kofunika kwambiri pa chikhulupiriro chawo. Komabe pafupifupi onse mwa anthuwa ananena kuti njira yabwino yofalitsira uthenga wabwino sikulankhula ndi anthu za uthengawo koma kukhala munthu wachitsanzo chabwino kwa ena. Mmodzi mwa anthu amene anafunsidwawo ananena kuti: “Tikati kulalikira uthenga wabwino sizitanthauza kuti tizilankhulalankhula za uthengawo ayi. Koma ifeyo ndi amene tiyenera kukhala Uthenga Wabwino.” Magazini imene inachita kafukufuku uja inanenanso kuti anthu ambiri safuna kuuza ena zimene amakhulupirira chifukwa “chaposachedwa tchalitchi cha Katolika chatchuka ndi mbiri zoipa zokhudza ansembe ochita zachiwerewere ndi ana komanso chifukwa cha ziphunzitso zolakwika zimene tchalitchichi chimaphunzitsa.”​—U.S. Catholic.

Ndiponso bishopu wina wa tchalitchi cha Methodist anadandaula kuti tchalitchi chawo chagawikana komanso anthu ake asokonezeka kwambiri moti sangathe kugwira ntchito yolalikira. Iye ananenanso kuti khalidwe la anthu atchalitchichi silisiyana ndi la wina aliyense amene sapemphera. Kenako mothedwa nzeru bishopuyu anafunsa kuti: “Kodi ndani kwenikweni amene akuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu?”

Bishopuyu sanayankhe funso lakeli. Koma yankho la funso limeneli lilipo ndipo mulipeza m’nkhani yotsatira.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Uthenga wabwino umanena za Ufumu wa Mulungu komanso chipulumutso chimene anthu angapeze chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu