Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi “Mapeto” N’chiyani?

Kodi “Mapeto” N’chiyani?

Kodi “Mapeto” N’chiyani?

“ . . . kenako mapeto adzafika.”​—MATEYU 24:14.

MASIKU ano pali nkhani zambirimbiri zokhudza kutha kwa dziko. Mwachitsanzo pali mabuku, mafilimu, magazini a nkhani zoseketsa komanso a zasayansi onena nkhani zoopsa zokhudza kutha kwa dziko. Zoopsa zimenezi ndi monga nkhondo ya zida zoopsa, kuombana kwa dziko lapansi ndi chimwala m’mlengalenga, matenda oopsa kwambiri, kusintha kwa nyengo kumene anthu sangakuthetse ndiponso nkhani zokhudza anthu achilendo ochokera m’mlengalenga.

Zipembedzo zosiyanasiyana zilinso ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti padzikoli, zinthu zonse zamoyo zidzawonongedwa ndipo amenewa ndi amene adzakhale “mapeto.” Ponena za lemba la Mateyu 24:14, katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Vesi limeneli ndi limodzi mwa mavesi ofunika kwambiri m’Mawu a Mulungu . . . M’badwo wathu wonsewu udzawonongedwa. Komabe ndi anthu ochepa chabe amene timaganizira zinthu zoopsa zimene zidzachitike pa nthawiyo.”

Maganizo ngati amenewa amachititsa anthu kuiwala mfundo yofunika yakuti: Yehova Mulungu ‘anakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi ndipo sanalilenge popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.’ (Yesaya 45:18) Choncho, pamene Yesu ananena za “mapeto” sankatanthauza kuti dziko lapansili lidzawonongedwa kapenanso kuti anthu onse adzawonongedwa. Koma iye ankatanthauza kuti anthu oipa ndi amene adzawonongedwe. Anthu amenewa ndi amene amakanitsitsa kutsatira malangizo amene Yehova amapereka chifukwa chotikonda.

Kuti mumvetse mfundo imeneyi, ganizirani chitsanzo ichi. Tiyerekeze kuti inuyo muli ndi nyumba yokongola kwambiri ndipo mwalola kuti anthu ena azikhala m’nyumba mwanumo kwaulere. Ena mwa anthu amene akukhala m’nyumba yanuyo akukhala mwamtendere ndipo akuisamalira bwino kwambiri. Koma enawo ndi ovutitsa kwambiri. Amangomenyana ndipo amazunza anthu abwino aja. Anthu oipawo akuwononga nyumbayo ndipo ndi amwano moti safuna kumvera malangizo anu.

Kodi mungatani pamenepa? Kodi mungangogwetsa nyumbayo? N’zodziwikiratu kuti simungachite zimenezo. Mwina zimene mungachite ndi kungothamangitsa anthu oipawo, n’kukozanso zinthu zimene awonongazo.

Zimenezi n’zimenenso Yehova adzachite. Iye anauzira munthu wina amene analemba nawo Masalimo kulemba kuti: “Ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:9-11.

Nayenso mtumwi Petulo ananenapo za nkhani imeneyi. Iye anauziridwa kulemba kuti: “Panali kumwamba kuchokera kalekale, ndipo mwa mawu a Mulungu, dziko lapansi linali loumbika motsendereka pamwamba pa madzi ndi pakati pa madzi, ndipo mwa zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.” (2 Petulo 3:5, 6) Pamenepa mtumwiyu ankanena za Chigumula cha m’nthawi ya Nowa. Nthawi imeneyo anthu osaopa Mulungu ndi amene anawonongedwa, osati dziko lapansi. Chigumula cha dziko lonse chimenecho chinali “chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.”​—2 Petulo 2:6.

Kenako Petulo ananenanso kuti: “Kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto.” Koma powerenga vesili mutangosiyira pamenepa, mungamve molakwika chifukwa vesili limapitiriza kunena kuti: “Ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” Choncho chimene chidzawonongedwe si dziko lapansili ayi koma anthu osaopa Mulungu. Ndiye kodi kenako chidzachitike n’chiyani? Petulo anapitiriza kunena kuti: “Pali kumwamba kwatsopano [Ufumu wa Mulungu womwe mfumu yake ndi Mesiya] ndi dziko lapansi latsopano [anthu olungama] zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”​—2 Petulo 3:7, 13.

Ulosi wina wa m’Baibulo umasonyezanso kuti “mapeto” ali pafupi kwambiri. Kuti muone umboni wa zimenezi, werengani Mateyu 24:3-14 ndi 2 Timoteyo 3:1-5. *

Kodi inuyo zikukudabwitsani kuona kuti anthu ambiri samvetsa bwino Mateyu 24:14, vesi limene ngakhale mwana angalimvetse mosavuta? Pali zimene zimachititsa kuti anthuwa asalimvetse. Satana wachititsa khungu anthu kuti asadziwe choonadi cha mtengo wapatali chimene chili m’Mawu a Mulungu. (2 Akorinto 4:4) Komanso Mulungu wabisira cholinga chake anthu odzikuza ndipo wachiulula kwa anthu odzichepetsa. Pa nkhani imeneyi Yesu anati: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana.” (Mateyu 11:25) Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala m’gulu la anthu odzichepetsa amene amadziwadi tanthauzo la Ufumu wa Mulungu, ndiponso amene akuyembekezera madalitso omwe Ufumuwo udzabweretse kwa anthu onse amene amaukhulupirira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 9 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 9]

Ufumu udzawononga anthu onse ochita zoipa padzikoli ndipo amenewo adzakhala “mapeto”