Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi?

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi?

▪ Popeza Baibulo limanena kuti Mulungu “analenga zinthu zonse,” anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene analenga Mdyerekezi. (Aefeso 3:9; Chivumbulutso 4:11) Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sanalenge Mdyerekezi.

Yehova analenga munthu amene pambuyo pake anadzakhala Mdyerekezi. Choncho kuti tidziwe zimene zinachitika kuti munthu ameneyu akhale wotsutsa wamkulu wa Mulungu kapena kuti Mdyerekezi, tiyenera kuganizira zimene Malemba amanena zokhudza Yehova monga Mlengi. Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” (Deuteronomo 32:3-5) Mawu amenewa, akusonyeza kuti poyamba Satana anali mmodzi mwa ana a Mulungu, mngelo wangwiro ndiponso wolungama. Palemba la Yohane 8:44 Yesu ananena kuti Mdyerekezi “sanakhazikike m’choonadi.” Zimenezi zikusonyeza kuti pa nthawi ina Satana anali m’choonadi ndipo sankachita zinthu zoipa.

Komabe monga mmene zilili ndi anthu komanso angelo onse amene Yehova analenga, mngelo amene anadzakhala Satana anali ndi ufulu wosankha kumvera kapena kusamvera Mulungu. Satana anasankha kutsutsana ndi Mulungu ndiponso anachititsa Adamu ndi Hava kugwirizana naye kupandukira Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, mngelo ameneyu anadzipangitsa kukhala Satana, kutanthauza “Wotsutsa.”​—Genesis 3:1-5.

Mngelo woipa ameneyu anadzipangitsanso kukhala Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza.” Satana anadzibisa pogwiritsa ntchito njoka ndipo mwachinyengo ananama pofuna kuti Hava aswe lamulo lomveka bwino limene Mlengi anawapatsa. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti Satana ndi “tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44.

Komano zinatheka bwanji kuti mngelo ameneyu ayambe kuganizira zoipa ngakhale kuti anali wangwiro, analibe uchimo komanso panalibe amene akanamuchitsa kuti achimwe? N’chifukwa chakuti anayamba kulakalaka kuti anthu azilambira iyeyo, m’malo molambira Mulungu yemwe ndiye woyenera kulambiridwa. Anaganizanso kuti akhoza kuchititsa anthu kuti azilamuliridwa ndi iyeyo m’malo molamuliridwa ndi Yehova. M’malo mosiya kuganiza zinthu zolakwikazi, iye anapitirizabe kuziganizira mpaka anazichitadi. Zimene iye anachitazi zafotokozedwa palemba la Yakobo 1:14, 15. Lembali limati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.”​—1 Timoteyo 3:6.

Kuti timvetse zimenezi tiyerekezere chonchi: Munthu wina amagwira ntchito yowerengera ndalama pakampani ndipo iye wayamba kuganiza zoti abe ndalama za kampaniyo mochenjera kwambiri posintha zina ndi zina pamalisiti. Iye nthawi yomweyo akhoza kusiya kuganizira zoipazo. Koma atapitiriza kuganizira zakubazo angayambe kusangalala ndi zimene akufuna kuchitazo ndipo pamapeto pake angabedi ndalamazo. Ngati angachitedi zimenezi, ndiye kuti wadzichititsa kukhala wakuba. Komanso ngati mabwana ake atamufunsa za mmene ndalamazo zayendera iye n’kunama, ndiye kuti wakhala wabodza. Mofanana ndi zimenezi, mmodzi mwa angelo amene Mulungu analenga anagwiritsa ntchito ufulu wosankha, n’kuchita zinthu mwachinyengo komanso kupandukira Atate wake. Iye anachita zimenezi chifukwa analakalaka zinthu zoipa zimene pamapeto pake anazichitadi. Choncho anakhala Satana Mdyerekezi.

Koma nkhani yosangalatsa ndi yakuti, Mulungu wakonza nthawi imene adzawononge Satana Mdyerekezi. (Aroma 16:20) Padakali pano anthu onse amene amalambira Yehova Mulungu akuchenjezedwa za misampha ya Satana ndipo akupatsidwa malangizo a mmene angadzitetezere ku misampha imeneyi. (2 Akorinto 2:11; Aefeso 6:11) Choncho, yesetsani kuchita china chilichonse chimene mungathe kuti ‘mutsutse Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.’​—Yakobo 4:7.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Mmodzi mwa angelo a Mulungu anasankha kuchita zinthu zotsutsana ndi Mulungu ndipo anadzichititsa kukhala Satana