Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Misonkhano Yachigawo ku Russia Imabweretsa Madalitso

Misonkhano Yachigawo ku Russia Imabweretsa Madalitso

Misonkhano Yachigawo ku Russia Imabweretsa Madalitso

ANTHU a ku Russia amakonda zachilengedwe ndipo chaka chilichonse ambiri amachoka m’tauni kupita kumidzi kukakhala m’nyumba zimene amazitchula kuti dachas. Iwo amaona kuti akapita kumidziko amapumako pang’ono moyo wotopetsa wam’tauni. Kwa zaka zingapo zapitazi, a Mboni za Yehova ku Russia akhala akupita m’madera akumidzi koma cholinga chawo sichikhala kukapuma moyo wa m’tawuni.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova akuletsedwa kuti asamalalikire m’mizinda ina ku Russia, iwo akupitirizabe kuchita misonkhano yawo kuti alambire Mulungu. Amachita zimenezi chifukwa malamulo adzikolo amanena kuti aliyense ali ndi ufulu wolambira. Komabe, nthawi zina iwo amatsutsidwa ndiponso kuvutitsidwa ndi atsogoleri atchalitchi cha Russian Orthodox komanso akuluakulu ena a boma amene anauzidwa zolakwika zokhudza Mboni za Yehova. Zimenezi zimachititsa kuti azivutika kupeza malo abwino ochitira misonkhano yawo yachigawo imene imachitika chaka chilichonse m’chilimwe. N’chifukwa chake a Mboni anakonza zomachitira misonkhano yawo “m’nkhalango.” Kuchokera mu 2007 kufika mu 2009, misonkhano yotereyi, yokwana 40 yakhala ikuchitika m’dziko la Russia, m’madera okwana 25.

Munthu wina wa Mboni, amene kwa zaka zambiri wakhala akuchita nawo misonkhano ku Russia, ananena kuti: “Zaka za m’mbuyomu tinkachita lendi masitediyamu komanso nyumba zina m’mizinda ikuluikulu ndipo anthu amtima wabwino ankatha kuona okha kuti gulu lathu ndife anthu abwino chifukwa ankaona kuti ndife aukhondo ndiponso timachita zinthu mwadongosolo. Koma panopa chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawo, tikuchitira misonkhano yathu m’nkhalango komwe anthu sangathe kutiona. N’zomvetsa chisoni kuti anthu sakuthanso kuona misonkhano yathuyi komwe kumakhala anthu amitundu, zikhalidwe ndi zipembedzo zosiyanasiyana.”

Ngakhale kuti misonkhano imeneyi imakhala yosangalatsa, wa Mboni wina ananena kuti: “Timasangalala kuona kudzipereka ndi kukhulupirika kwa a Mboni anzathu amene akupitirizabe kulambira Yehova ngakhale zinthu zitavuta. Koma kunena zoona, akuluakulu a boma akatilepheretsa kuchita misonkhano yathu yachigawo, zimakhala zovuta kwambiri chifukwa zimakhala zokhumudwitsa ndiponso zotopetsa kwambiri. Komanso zimasokoneza ufulu wathu wolambira Mulungu wathu wamphamvuyonse m’njira yolemekezeka.” Kodi a Mboni za Yehova a ku Russia achita chiyani kuti azichitabe misonkhano yawo?

Amachita Misonkhano M’nkhalango

Nthawi zambiri akauzidwa kuti sachita msonkhano pamalo amene anachita lendi, anthu amene akuyendetsa ntchito yokonzekera msonkhanowo amakhala ndi nthawi yochepa yoti apezenso malo ena. Zimakhalanso zovuta kuti apeze njira zina zodzasamalirira anthu obwera kumsonkhanowo. Mwachitsanzo, mu 2008 a Mboni m’chigawo cha Cheboksary, ku Chuvash Republic anachita msonkhano wachigawo pamalo ena pomwe panali mitengo. Malo amenewa ali pafupi ndi mtsinje wa Volga. Kuti msonkhanowu utheke panafunika khama kwambiri. Pa anthu 1,930 amene ankayembekezereka kufika pamsonkhanowu, anthu okwanira 1,700 anali oti adzagona pamalo a msonkhano pomwepo. Pankafunika malo osambira okhala ndi mashawa, masinki okhala ndi madzi otentha ndi ozizira, zimbuzi ndiponso magetsi. Pankafunikanso kukonza chakudya chokwanira anthu onsewa.

Abale anayesetsa kupeza zinthu zimenezi. Anapeza anthu amene amadziwa ntchito za ukalipentala, zokonza mapaipi a madzi komanso zamagetsi. A Mboni okwana 350 anadzipereka kugwira nawo ntchitoyi ndipo 14 mwa anthu amenewa anagona pamalo antchitowo kwa masiku 10. Abale amenewa anadula matabwa ndipo anamanga matenti, mabafa ndiponso zimbudzi. Panali gulu la abale ena amene ankapita kutawuni kukagula zinthu zofunika pa ntchitoyi. Popeza kuti panalibe mafiliji osungira zakudya kuti zisawonongeke, tsiku lililonse abalewa ankaphika chakudya m’mawa, masana ndi madzulo ndi cholinga choti anthu pamsonkhanowo azidya chakudya chotentha. Mkulu woyang’anira malowo anathandizanso chifukwa anatumiza anthu odzathandiza kuphika chakudya cha anthu obwera pamsonkhanopo. Pamsonkhanowu, anthu okwana 500 anagona m’matenti awo amene anabweretsa, 150 anachita lendi m’nyumba zapafupi ndi malowa, 15 ankagona paudzu odyetsera ziweto pamalo ena osungira ziweto ndipo anthu otsalawo ankagona m’matenti amene abale anawakonzera.

Pamene anthu ankafika pamsonkhanowu, anapeza mipando yapulasitiki yokongola itaikidwa mwadongosolo. Kutsogolo kwa mipandoyi kunali mapulatifomu awiri okongoletsedwa ndi maluwa. Pulatifomu ina ya anthu achinenero cha Chirasha ndipo ina ya chinenero cha Chichuvashi. Aliyense anasangalala ndi msonkhanowu ndipo anayamikira kwambiri anthu amene anadzipereka kugwira mwakhama ntchito yokonzekera msonkhanowo. Mmodzi wa anthu amene anaphika nawo zakudya pamsonkhanopo ananena kuti: “Ndaona ndekha ndi maso angawa kuti gulu lanuli ndi ladongosolo komanso logwirizana kwambiri. Ndikanakhala kuti sindinafike pano, sindikanakhulupirira kuti pangakhale gulu ngati limeneli.” Ena ananena kuti msonkhano umenewo unali ngati Zikondwerero za Misasa zimene Aisiraeli akale ankachita.

M’mizinda ina, nthawi zambiri a Mboni amauzidwa kutangotsala tsiku limodzi kuti sachitira msonkhano pamalo amene anachita lendi. Zikatero amafunika kupeza malo ena. Mwachitsanzo, ku Nizhniy Novgorod anthu odzipereka anagwira ntchito usana ndi usiku mosinthanasinthana kukonza malo ena kuti achitirepo msonkhano. Iwo anafunika kudula mitengo, kutchetcha udzu komanso kupha nthata ndi nyerere pamalopo. Pomwe anthu ankafika m’mawa Lachisanu kudzachita msonkhano, anthu odziperekawa anali atabweretsa mipando yapulasitiki yokwana 2,000 ndi matoileti ochita kunyamula okwana 10. Anakonza malo osambira m’manja, pulatifomu komanso analumikiza jenereta ndi zokuzira mawu. M’bale wina ananena kuti: “Zinali zochititsa chidwi kuona kuti abale amene anagwira ntchito usana ndi usikuwo, sanadzitamandire chifukwa cha ntchito imene anagwira. Iwo modzichepetsa anapitirizabe kutumikira anthu pamsonkhanowo. Anadzipereka kwambiri n’cholinga chakuti abale ndi alongo akhale ndi zinthu zokwanira zogwiritsa ntchito pamsonkhanowu komanso kuti apindule.”

M’bale wina analemba kuti: “Abale anagwira ntchito mogwirizana kwambiri. Ngakhale kuti aka kanali koyamba kuti akonze msonkhano wachigawo wochitikira m’nkhalango, komanso nthawi yokonzekera inali yochepa, iwo anakonzekera bwino kwambiri n’cholinga chakuti pasadzakhale zododometsa zambiri. Msonkhanowo utatha sitinali wotopa kwambiri ndipo tinaona kuti Yehova watipatsa mphamvu.”

Mzimu wa Mulungu Ukugwira Ntchito

A Mboni za Yehova amalimbana ndi mavuto ambiri akamakonzekera msonkhano. Komabe zimenezi zimathandiza kuti adziwane bwino komanso zimasonyeza kuti mzimu wa Mulungu ukuwatsogolera. Chitsanzo cha zimenezi ndi zimene zinachitika ku Smolensk. Eni malo ena amene abale analipira kuti anthu obwera pamsonkhanowu adzagone anasintha maganizo n’kunena kuti abalewo sagwiritsa ntchito malowo. M’bale wina yemwe ndi mkulu ananena kuti: “Mabasi onyamula anthu odzachita msonkhano atafika 1 koloko usiku, tinasowa malo owapatsa kuti agone. Ndinalira kwambiri chifukwa ndinasowa chochita. Kenako ndinapemphera kwa Yehova kuti atithandize. Koma ndinasangalala kwambiri chifukwa mmene pankatha ola limodzi n’kuti titapeza malo ogona anthu onsewa. Zinali zodabwitsa kwambiri ndipo umenewu unali umboni wosonyeza kuti Yehova amasamalira anthu olungama amene avutika.” Pamsonkhano wina umene unachitikira m’nkhalango, a Mboni za Yehova anapita kumudzi wa m’deralo kukafuna malo oti anthu agone. Chifukwa cha mbiri yabwino imene a Mboni za Yehova ali nayo m’derali, anthu a m’mudzimo analola kuti anthu okwana 2,000 agone m’nyumba zawo pa nthawi yonse ya msonkhanowo.

Munthu wina wa Mboni ananena kuti: “Popeza zinatheka kuchita msonkhano, umenewu ndi umboni wakuti tifunika kudalira kwambiri Yehova, zivute zitani.” Mwachitsanzo, tangoganizirani zimene zinachitika ku Novoshakhtinsk pamene wansembe wina wa tchalitchi cha Russian Orthodox anafika pamsonkhano wina ndi cholinga chodzasokoneza. Wansembeyu anabwera ndi anthu ena ochita zionetsero ndipo anayamba kuimba nyimbo zawo pogwiritsa ntchito zokuzira mawu. Iwo ankachita zimenezi ndi cholinga chofuna kusokoneza m’bale amene pa nthawiyo ankakamba nkhani. Komabe apolisi anafika pamalowo n’kuwaletsa. Mayi wina wa tchalitchi cha Orthodox, yemwenso ankachita nawo zionetserozo, anakomoka chifukwa cha kutentha. Nthawi yomweyo a Mboni anamutengera ku Dipatimenti ya Zachipatala ya pamsonkhanopo ndipo anamupatsa chithandizo. Mayiyu anadabwa kwambiri ndi zimenezi.

Anagoma ndi Zimene Anaona

Chifukwa cha kuchuluka kwa zauchigawenga, nthawi zambiri apolisi ku Russia amakhala tcheru anthu ambiri akasonkhana. Anthu wamba nawonso amafika pamene pasonkhana anthu ambiri kuti adzaone zimene zikuchitika. Mwachitsanzo, pamsonkhano wina umene unachitikira m’nkhalango ku Volzhskiy kunafika apolisi apadera olimbana ndi zauchigawenga. Mmodzi wa apolisiwo anataya foni yake ndipo a Mboniwo anamuuza kuti akafufuze ku Dipatimenti ya Zotayika ya pamsonkhanopo. Patangotha nthawi yochepa, abwana ake anamuimbira foni kumufunsa ngati pamsonkhanopo pankachitika zachiwawa kapena ngati pankanenedwa zinthu zoyambitsa chiwawa. Wapolisiyo anayankha kuti: “Zonse zili bwino, pasonkhana anthu okwana 5,000 koma palibe amene akuchita zachiwawa. A Mboni sachita zachiwawa. Taganizirani zimene zachitika kunoko, foni yanga inatayika koma a Mboniwo anaitola ndipo andibwezera.”

Pamalo ena pamene a Mboni anachitira msonkhano, mlonda wina anagoma ataona kuti a Mboniwo ndi anthu aukhondo. Anadabwa kuona kuti ngakhale kuti panali ana ambiri, panalibe mapepala a masiwiti ngakhale limodzi. Apolisi anafika pamalo ena pamene a Mboni ankachitira msonkhano wawo ndipo anakumana ndi mwiniwake wa malowo. Anthu ena ndi amene anauza apolisiwo za msonkhanowo. Mwini malowo anapita ndi mkulu wa apolisiyo pachipinda chachitatu chapamwamba cha nyumba yosanjikizana ndipo anakaima pamalo ena poyang’anizana ndi bwalo limene a Mboniwo ankachitira msonkhano wawo. Ndiyeno mwinimalowo anauza wapolisiyo kuti: “Ndikufuna kuti muone nokha zimene anthu amenewa akuchita. Akuchita zinthu mwamtendere komanso mwadongosolo.” Mwini malowo anagoma kwambiri kuti a Mboniwo sankamwa mowa kapena kusuta fodya ndipo msonkhanowo utatha, panalibe chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti anachitirapo msonkhano. Pochoka pamalowa, a Mboniwo anachotsa zinyalala zonse. Wapolisiyo ananena kuti: “Koma ndiyetu malo amenewa anasanduka paradaiso.”

Umboni Wosonyeza Kuti Anthu a Mulungu Ndi Ogwirizana

Msonkhano wina umene unachitikira kunkhalango utatha, a mfumu a mudzi woyandikana ndi malowo ananena kuti: “Ndimadziwa kuti ndinu anthu odzichepetsa. Koma ndaonanso kuti ndinu anthu amphamvu. Pamene aliyense masiku ano angochita zofuna zake, inuyo mukuthandiza anthu kuti azikhala mogwirizana.” M’dziko lonse la Russia, kuyambira ku Kaliningrad mpaka ku Kamchatka, anthu akugoma ndi kugwirizana kumene anthu a Mulungu amasonyeza akamachita misonkhano yawo ikuluikulu. Ngakhale patachitika zamwadzidzidzi moti akufunika kusintha pulogalamu yawo, iwo nthawi zonse amalemekeza akuluakulu aboma komanso anthu anzawo.

Kaya akumana ndi zotani m’tsogolo muno, koma panopa a Mboni za Yehova ku Russia akupitirizabe kusonkhana kuti aphunzire zinthu zauzimu. Iwo amapemphera ‘m’malo mwa mafumu ndi anthu onse apamwamba, kuti [a Mboniwo] akhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso akhale oganiza bwino.’​—1 Timoteyo 2:2.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Munthu wina wa Mboni za Yehova amene anadzipereka kugwira nawo ntchito yokonzekera msonkhano

[Mawu Otsindika patsamba 29]

A Mboni za Yehova ku Russia akupitirizabe kukhala ‘moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kukhala odzipereka kwa Mulungu mokwanira’

[Zithunzi patsamba 28]

Anthu akugwira ntchito modzipereka kuyeretsa malo amsonkhano komanso kuphika chakudya cha anthu amene afika pamsonkhanopo

[Zithunzi patsamba 29]

Aliyense anasangalala ndi msonkhanowu ndipo anayamikira kwambiri anthu amene anadzipereka kugwira ntchito mwakhama