Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Okalamba Adzakhalanso Achinyamata

Okalamba Adzakhalanso Achinyamata

Yandikirani Mulungu

Okalamba Adzakhalanso Achinyamata

NDANI wa ife amene amafuna atakalamba, thupi lake lonse n’kuchita makwinya, maso ake kumaona movutikira, kumalephera kumva komanso kumayenda miyendo ili njenjenje? Mukaganizira zinthu ngati zimenezi, mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga anthufe kuti tizisangalala ndi unyamata kenako n’kukalamba?’ Koma n’zosangalatsa kudziwa kuti, Mulungu sanafune kuti tizikalamba. Iye amatikonda moti wakonza zoti posachedwapa athetse ukalamba. Taonani mawu amene Yobu ananena, opezeka pa Yobu 33:24, 25.

Taganizirani zimene zinachitikira Yobu, munthu wokhulupirika amene ankakondedwa ndi Yehova. Iye sankadziwa kuti Satana anamunenera zoipa, kuti amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera, osati chifukwa chomukonda. Koma Yehova anali ndi chikhulupiriro choti Yobu akhoza kukhalabe wokhulupirika ngakhale atayesedwa. Ankadziwanso kuti iyeyo ali ndi mphamvu zochotsa choipa chilichonse chimene chingamuchitikire Yobu. Choncho analola kuti Satana ayese Yobu. Satana ‘anagwetsera Yobu zilonda zopweteka, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.’ (Yobu 2:7) Thupi la Yobu linkatuluka mphutsi ndipo khungu lake linkang’ambika n’kumatuluka mafinya, linada komanso linkangoyoyoka. (Yobu 7:5; 30:17, 30) N’zosakayikitsa kuti Yobu ankamva ululu woopsa. Koma iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ndipo anati: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”​—Yobu 27:5.

Komabe nthawi ina Yobu analakwitsa kwambiri. Pomwe zinkaoneka ngati watsala pang’ono kufa, anayamba kudziona kuti ndi wolungama ndipo “ankanena kuti anali wolungama, osati Mulungu.” (Yobu 32:2) Elihu, yemwe ankalankhula m’malo mwa Mulungu, anadzudzula Yobu. Komabe Elihu anauzanso Yobu uthenga wosangalatsa wochokera kwa Mulungu. Iye anati: “M’pulumutseni [Yobu] kuti asapite m’dzenje, [kutanthauza manda a anthu onse] chifukwa ndapeza dipo. Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.” (Yobu 33:24, 25) Yobu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu amenewa. Mawu amenewa anasonyeza kuti iye savutika mpaka kumwalira. Yobu akanalapa, Mulungu anali wokonzeka kulandira dipo loperekedwa chifukwa cha iyeyo n’kumuchotsera mavuto onsewo. *

Modzichepetsa, Yobu anavomereza kulakwa kwake ndipo analapadi. (Yobu 42:6) Zikuoneka kuti Yehova analandira dipo m’malo mwa Yobu, limene linaphimba machimo ake, zimene zinachititsa kuti Mulungu athetse mavuto a Yobu ndi kumudalitsa. Baibulo limati, Yehova “anadalitsa kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12-17) Taganizirani mmene Yobu anamvera pamene Mulungu anamudalitsa m’njira zambiri kuphatikizapo kuti matenda ake osautsa aja anatha, mnofu wake n’kukhala wosalala “kuposa mmene unalili ali mnyamata.”

Komabe dipo limene linaperekedwa kwa Mulungu chifukwa cha Yobu, linagwira ntchito kwa nthawi yochepa chifukwa Yobuyo anakhalabe wopanda ungwiro ndipo patapita nthawi anamwalira. Koma ifeyo tili ndi dipo loposa limeneli. Chifukwa chotikonda, Yehova anapereka Mwana wake Yesu monga dipo lathu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Anthu onse amene amakhulupirira dipo limeneli, ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Pa nthawi imeneyo, Mulungu adzathetsa ukalamba moti palibe amene adzakalambenso. Mungachite bwino kuphunzira zambiri za zimene mufunika kuchita kuti mudzakhalepo pamene mnofu wa okalamba ‘udzasalale kuposa mmene unalili ali mnyamata.’

Mavesi amene mungawerenge mu April:

Yobu Chaputala 16 mpaka 37

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Palembali, mawu amene anawamasulira kuti “dipo” akutanthauza “kuphimba.” (Yobu 33:24; mawu am’munsi) Pa nkhani ya Yobu, dipo liyenera kuti inali nsembe ya nyama imene Mulungu anailandira kuti iphimbe kapena kuti kulipira machimo a Yobu.​—Yobu 1:5.