Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha Ndiponso Umachita Mantha?

Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha Ndiponso Umachita Mantha?

ANTHU ambiri masiku ano amaona kuti ali wokha ndiponso kuti palibe amene amawakonda. Anthu akuluakulu nthawi zambiri ndi amene amamva choncho. Koma masiku ano ana, ngakhale amene amatumikira Mulungu, nawonso amaona kuti ali wokha ndipo amachita mantha. Kodi ukudziwa chifukwa chake?​ *

Pangakhale zifukwa zambiri. Mwachitsanzo, tiye tikambirane za munthu wina amene anakhalako kalekale, zaka pafupifupi 1,000 Yesu asanabadwe. Dzina lake linali Eliya. Iye anakhalapo pa nthawi imene Aisiraeli ambiri anali atasiya kutumikira Mulungu woona Yehova. Ambiri anali atayamba kulambira mulungu wonyenga dzina lake Baala. Eliya ananena kuti: “Ine ndatsala ndekhandekha.” Koma kodi ukuganiza kuti pa nthawi imeneyo amene anatsala akutumikira Yehova analidi Eliya yekha basi?

Eliya sankadziwa kuti ku Isiraeli kunali anthu enanso amene ankatumikirabe Mulungu woona. Kungoti anali atapita kukabisala chifukwa ankachita mantha kwambiri. Kodi ukudziwa chifukwa chake?​

Ahabu mfumu ya Aisiraeli anali atasiya kutumikira Yehova ndipo ankalambira Baala, mulungu wonyenga wa Yezebeli, mkazi wake. Choncho Yezebeli ndi Ahabu ankasakasaka anthu amene ankalambira Yehova n’cholinga chakuti awaphe ndipo makamaka ankafunitsitsa kupha Eliya. N’chifukwa chake Eliya anathawa. Iye anayenda ulendo wamakilomita 483 mpaka anakafika kuchipululu cha Horebe, malo amene m’Baibulo amatchedwanso Sinai. Pamalo amenewa, ndi pamene zaka zambiri m’mbuyomu Yehova anapatsa anthu ake Malamulo Khumi komanso malamulo ake ena. Eliya anabisala m’phanga ku Horebi ndipo anali yekhayekha. Kodi ukuganiza kuti Eliya ankafunikadi kuchita mantha chonchi?​

Baibulo limasonyeza kuti zimenezi zisanachitike, Yehova anathandiza Eliya kuchita zozizwitsa. Pa nthawi ina Yehova anayankha pemphero la Eliya ndipo anagwetsa moto womwe unanyeketsa nsembe. Mwa kuchita zimenezi, Yehova anasonyeza kuti iye ndiye Mulungu woona, osati Baala. Ndiyeno Eliya ali kuphanga kuja, Yehova analankhula naye.

Yehova anafunsa Eliya kuti: “Ukufuna chiyani kuno?” Apa m’pamene Eliya ananena kuti, ‘Ine ndatsala ndekhandekha amene ndikulambira inu.’ Ndiyeno Yehova mokoma mtima anauza Eliya kuti zimenezo sizinali zoona. Yehova anena kuti, ‘panalinso anthu ena okwana 7,000 amene ankamulambira.’ Yehova anauza Eliya kuti abwerere ndipo anamufotokozera kuti pali ntchito yambiri yoti akagwire.

Kodi ukuganiza kuti tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Eliya?​— Tikuphunzira kuti, ngakhale anthu amene amatumikira Yehova, nthawi zina angachite mantha. Choncho tonsefe, ana ndi aakulu omwe, tiyenera kupempha Yehova kuti azitithandiza. Baibulo limanena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”

Tikuphunziraponso kuti, padziko lonse pali abale ndi alongo amene amakonda Yehova komanso amatikonda ifeyo. Baibulo limati: “[Anzathunso] m’gulu lonse la abale [athu] m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.” Popeza wadziwa kuti si uli wekha, kodi sukusangalala ndi zimenezi?​

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.