Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu

Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu

Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu

“Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”​—MIY. 14:15.

1, 2. (a) Kodi cholinga chathu chachikulu posankha zochita chiyenera kukhala chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

 TSIKU lililonse timasankha zochita. Zosankha zambiri zimakhala zing’onozing’ono koma zina zimakhudza kwambiri moyo wathu. Pa zinthu zonse zimene timasankha, kaya zikhale zazing’ono kapena zazikulu, cholinga chathu chachikulu chiyenera kukhala kulemekeza Mulungu.​—Werengani 1 Akorinto 10:31.

2 Kodi mumavutika kusankha zochita? Kuti tikhale okhwima mwauzimu, tiyenera kuphunzira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera kenako n’kusankha zochita mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu osati cha ena. (Aroma 12:1, 2; Aheb. 5:14) Kodi kuphunzira kusankha zochita mwanzeru n’kofunika pa zifukwa zinanso ziti? N’chifukwa chiyani nthawi zina timavutika kwambiri kusankha zochita? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kusankha zochita zimene zimalemekeza Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusankha Zochita?

3. Tikamasankha zochita, kodi sitiyenera kulola zinthu ziti kutisokoneza?

3 Kukayikakayika posankha zochita pa nkhani zokhudza mfundo za m’Baibulo kungachititse anzathu a kusukulu kapena kuntchito kuganiza kuti tilibe chikhulupiriro cholimba ndiponso kuti tikhoza kumangotsatira maganizo alionse. Anzathuwo akhoza kunama, kuchita chinyengo kapena kuba, kenako n’kumatinyengerera kuti ‘tizingotsatira khamu la anthu’ mwa kuchita nawo zinthuzo kapena kusaulula zimene iwowo akuchita. (Eks. 23:2) Koma munthu amene amadziwa kusankha zochita zimene zimalemekeza Mulungu sangalole kuchita zinthu zotsutsana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo chifukwa cha mantha kapena kufuna kusangalatsa anthu.​—Aroma 13:5.

4. N’chifukwa chiyani anthu ena angafune kutisankhira zochita?

4 Sikuti anthu onse amene amafuna kutisankhira zochita amakhala ndi zolinga zolakwika. Anzathu ena otifunira zabwino angakonde kuti titsatire malangizo awo. Ngakhale ngati sitikukhalabe kunyumba, achibale athu angakhalebe ndi mtima wofuna kutisankhira zochita pa nkhani zikuluzikulu. Iwo angachite zimenezi chifukwa chotidera nkhawa. Mwachitsanzo, angafune kutisankhira zinthu pa nkhani ya mankhwala. Baibulo limatsutsa mwachindunji kugwiritsa ntchito magazi molakwika. (Mac. 15:28, 29) Koma pali nkhani zina zokhudza thandizo la kuchipatala zimene sizitchulidwa mwachindunji m’Baibulo ndipo aliyense amayenera kusankha yekha zochita. a Achibale athu angafune kuti titsatire maganizo awo pa nkhani zimenezi. Koma posankha zochita pa nkhani zoterezi, Mkhristu aliyense wobatizidwa ayenera kunyamula yekha “katundu wake.” (Agal. 6:4, 5) Cholinga chathu chachikulu posankha zochita ndicho kukhala ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu osati kwa anthu.​—1 Tim. 1:5.

5. Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chisasweke ngati ngalawa?

5 Kukayikakayika posankha zochita kungatibweretsere mavuto aakulu. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, analemba kuti munthu wokayikakayika amakhala “wosakhazikika m’njira zake zonse.” (Yak. 1:8) Iye amakhala ngati munthu amene ali m’boti lopanda chiwongolero limene likuyenda panyanja kuli mphepo yamkuntho. Iye amatengekatengeka ndi maganizo a anthu omwe amasinthasintha. Zimakhala zosavuta kuti chikhulupiriro cha munthu wotereyu chisweke ngati ngalawa kenako n’kumaimba ena mlandu. (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji zimenezi? Tiyenera “kukhazikika m’chikhulupiriro.” (Werengani Akolose 2:6, 7.) Kuti tikhale okhazikika m’chikhulupiriro, tiyenera kusankha zochita zimene zimasonyeza kuti timakhulupirira Mawu ouziridwa ndi Mulungu. (2 Tim. 3:14-17) Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kusankha zinthu mwanzeru?

Zimene Zimachititsa Kuti Kusankha Zochita Kukhale Kovuta

6. Kodi mantha angatilepheretse bwanji kusankha zochita?

6 Tingalephere kusankha zochita chifukwa cha mantha. Mwina tingamaope kusankha zolakwika, kulephera kuchita zimene tasankhazo kapena tingaope kuoneka opepera kwa anthu ena. N’zomveka kuchita mantha ndi zinthu ngati zimenezi. Palibe amene amafuna kusankha zolakwika zimene pambuyo pake zingatichititse manyazi kapena kubweretsa mavuto. Komabe, kukonda Mulungu ndiponso Mawu ake kungatithandize kuchepetsa mantha. Kodi kungatithandize bwanji? Kukonda Mulungu kungatilimbikitse kuti nthawi zonse tizifufuza m’Mawu ake ndiponso m’mabuku ofotokoza Baibulo tisanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tisamalakwitselakwitse posankha zochita. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Baibulo limathandiza kuti “munthu wosadziwa akhale wochenjera, kuti wachinyamata akhale wodziwa zinthu ndiponso kuti azitha kuganiza bwino.”​—Miy. 1:4.

7. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Mfumu Davide?

7 Kodi zingatheke kuti nthawi zonse tizisankha zochita mwanzeru? Ayi, sizingatheke. Tonsefe timalakwitsa. (Aroma 3:23) Mwachitsanzo, Mfumu Davide inali yanzeru ndiponso yokhulupirika. Koma nthawi zina Davide sankasankha zochita mwanzeru ndipo zinkabweretsa mavuto kwa iyeyo ndiponso kwa anthu ena. (2 Sam. 12:9-12) Ngakhale zinali choncho, Davide sanalole zimenezi kumulepheretsa kusankha zochita zimene Mulungu anasangalala nazo. (1 Maf. 15:4, 5) Mofanana ndi Davide, tikamakumbukira kuti Yehova amakhululuka machimo athu ndi kuiwala zolakwa zathu, tikhoza kumasankha zochita mwanzeru ngakhale kuti m’mbuyomu tinasankhapo zolakwika. Yehova adzapitirizabe kuthandiza anthu amene amamukonda ndi kumumvera.​—Sal. 51:1-4, 7-10.

8. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene mtumwi Paulo ananena zokhudza ukwati?

8 N’zotheka kuchepetsa nkhawa imene timakhala nayo tikamafuna kusankha zochita. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuzindikira kuti nthawi zina pamakhala njira zingapo zimene n’zolondola. Taganizirani zimene mtumwi Paulo ananena pa nkhani ya ukwati. Iye anauziridwa kulemba kuti: “Koma ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha, ngati wapitirira pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenera kutero, achite mmene akufunira, sachimwa. Akwatire. Koma ngati wina ndi wokhazikika mumtima mwake ndipo alibe chomuvutitsa, koma amatha kulamulira mtima wake, ndipo wasankha mumtima mwake kukhalabe wosakwatira, wachita bwino.” (1 Akor. 7:36-38) Paulo analimbikitsa anthu kuti angachite bwino kwambiri kukhala osakwatira kapena osakwatiwa. Koma sananene kuti njira yabwino ndi yokhayi.

9. Kodi tiyenera kuganizira mmene anthu ena angaonere zosankha zathu? Fotokozani.

9 Nthawi zina ndi bwino kuganizira mmene anthu ena angaonere zosankha zathu. Taganizirani zimene Paulo ananena pa nkhani yokhudza kudya nyama imene inkaoneka kuti inali yopereka nsembe ku mafano. Iye anasonyeza kuti zimene munthu angasankhe pa nkhani imeneyi mwina si zolakwika koma zikhoza kuvutitsa chikumbumtima cha munthu amene si wokhwima mwauzimu. Kodi Paulo anasankha kuchita chiyani? Iye analemba kuti: “Ngati chakudya chikukhumudwitsa m’bale wanga, sindidzadyanso nyama m’pang’ono pomwe, kuti ndisakhumudwitse m’bale wanga.” (1 Akor. 8:4-13) Ifenso tiyenera kuganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire chikumbumtima cha anthu ena. Komabe cholinga chathu chachikulu n’chakuti zosankha zathu zisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. (Werengani Aroma 14:1-4.) Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingatithandize kusankha zinthu zimene zingalemekeze Mulungu?

Zinthu 6 Zotithandiza Kusankha Mwanzeru

10, 11. (a) Kodi tingapewe bwanji kudzikweza m’banja? (b) Kodi akulu azikumbukira chiyani akamasankha zinthu zokhudza mpingo?

10 Pewani kudzikweza. Tisanasankhe zochita ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndi udindo wangadi kusankha zimenezi?’ Mfumu Solomo inalemba kuti: “Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika. Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”​—Miy. 11:2.

11 Makolo angalole ana awo kusankha zochita pa nkhani zina, koma anawo sayenera kungoganiza okha kuti ali ndi udindo wochita zimenezi. (Akol. 3:20) Akazi ndiponso amayi amakhala ndi mphamvu m’banja koma ayenera kuzindikira kuti mwamuna ndi mutu wa banja. (Miy. 1:8; 31:10-18; Aef. 5:23) Nawonso amuna ayenera kuzindikira kuti udindo wawo uli ndi malire ndiponso kuti ayenera kugonjera Khristu. (1 Akor. 11:3) Zinthu zimene akulu amasankha zimakhudza mpingo. Koma amaonetsetsa kuti ‘asapitirire zinthu zolembedwa’ m’Mawu a Mulungu. (1 Akor. 4:6) Iwo amatsatiranso kwambiri malangizo ochokera kwa kapolo wokhulupirika. (Mat. 24:45-47) Ngati tikhala odzichepetsa n’kumapewa kusankha zochita pa zinthu zimene si udindo wathu, tidzapewa kudzibweretsera mavuto ndiponso kuvutitsa anthu ena.

12. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kufufuza? (b) Fotokozani mmene munthu angafufuzire zinthu.

12 Muzifufuza. Solomo analemba kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miy. 21:5) Mwachitsanzo, kodi mukuganiza zochita bizinezi ndi munthu wina? Pewani kuchita zinthu mongotengeka. Fufuzani mfundo zonse zofunika, pemphani malangizo kwa anthu amene akudziwa bwino bizineziyo ndipo pezani mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize pa nkhaniyi. (Miy. 20:18) Pofufuza mungachite bwino kulemba mndandanda wa zinthu zabwino zimene mungapeze ndiponso mavuto amene mungadzakumane nawo. Musanasankhe zochita, muyenera ‘kuwerengera ndalama zimene mudzawononge.’ (Luka 14:28) Sitiyenera kungoganiza za ndalama zimene tingawononge koma tiyenera kuganiziranso mmene zosankhazo zingakhudzire moyo wathu wauzimu. Kufufuza kumafuna nthawi komanso khama. Koma kuchita zimenezi kungakuthandizeni kupewa kusankha zochita mopupuluma n’kudzanong’oneza bondo.

13. (a) Kodi lemba la Yakobo 1:5 limatitsimikizira za chiyani? (b) Kodi kupempha nzeru kwa Mulungu kungatithandize bwanji?

13 Pemphani Mulungu kuti akupatseni nzeru. Zosankha zathu zingalemekeze Mulungu ngati timamupempha kuti atithandize kusankha mwanzeru. Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yak. 1:5) Kupempha Mulungu kuti atipatse nzeru zotithandiza kusankha zochita si nkhani yochititsa manyazi. (Miy. 3:5, 6) Tiyenera kukumbukira kuti kungodalira luso lathu lomvetsa zinthu kukhoza kutisocheretsa. Tikamapempha Mulungu kuti atipatse nzeru ndiponso tikamafufuza mfundo za m’Mawu a Mulungu, timalola mzimu woyera kutithandiza kuzindikira zolinga zenizeni zimene tikufunira kuchita zinazake.​—Aheb. 4:12; werengani Yakobo 1:22-25.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuzengereza?

14 Sankhani zochita. Musafulumire kusankha zochita musanafufuze ndiponso kupempha Mulungu kuti akupatseni nzeru. Munthu wanzeru “amaganizira” kaye asanasankhe zochita. (Miy. 14:15) Koma musazengereze kusankha zochita. Munthu amene amazengereza angapereke zifukwa zosamveka zomulepheretsa kuchita zinthu zina. (Miy. 22:13) Munthu wozengereza kwenikweni amakhala akusankha kuti anthu ena aziyendetsa moyo wake.

15, 16. Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu atsatire zimene wasankha?

15 Tsatirani zomwe mwasankha. Khama limene tinachita posankha zinthu likhoza kukhala lopanda ntchito tikalephera kuchitanso khama kutsatira zimene tasankhazo. Solomo analemba kuti: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Mlal. 9:10) Kuti mukwanitse kuchita zimene mwasankhazo muyenera kuonetsetsa kuti muli ndi zonse zofunika. Mwachitsanzo, wofalitsa mu mpingo angaganize zochita upainiya. Kodi angatani kuti akwanitse? Iye akhoza kukwanitsa ngati sangalole ntchito kapena zosangalatsa kumuthera mphamvu ndi nthawi zimene angafunikire pochita upainiyawo.

16 Nthawi zambiri zosankha zabwino kwambiri zimakhala zovuta kuzitsatira. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Tiyenera kulimbana ndi “olamulira dziko a mdimawu ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aef. 6:12) Mtumwi Paulo ndiponso Yuda anasonyeza kuti anthu amene asankha kulemekeza Mulungu adzakhala pa nkhondo.​—1 Tim. 6:12; Yuda 3.

17. Tikasankha zochita, kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?

17 Onaninso zimene mwasankha n’kusintha zina ngati m’pofunika kutero. Sikuti zonse zimene tasankha kuchita zimachitika ndendende mmene tinakonzera. “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka” zimagwera tonsefe. (Mlal. 9:11) Ngakhale zili choncho, Yehova amafuna kuti tizitsatirabe zinthu zina zimene tasankha zivute zitani. Mwachitsanzo, munthu amene wadzipereka kwa Yehova kapena amene wachita malumbiro a ukwati sangathe kudzasintha pambuyo pake. Mulungu amafuna kuti tizitsatira zimene tasankha pa nkhani ngati zimenezi. (Werengani Salimo 15:1, 2, 4.) Koma zosankha zambiri sizikhala zikuluzikulu ngati zimenezi. Choncho munthu wanzeru amaonanso mobwerezabwereza zimene wasankha. Munthu wotere sakhala wonyada kapena woumirira pa zimene wasankha. Iye amalolera kusintha zosankha zake. (Miy. 16:18) Cholinga chake chachikulu n’choti apitirize kulemekeza Mulungu.

Thandizani Ena Kuti Zosankha Zawo Zizilemekeza Mulungu

18. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kusankha zochita mwanzeru?

18 Makolo angathandize kwambiri ana awo kuti aphunzire kusankha zimene zimalemekeza Mulungu. Ana angaphunzire zambiri pa chitsanzo cha makolo. (Luka 6:40) Nthawi zina, makolo angafotokozere ana awo zimene zinawathandiza kusankha zinazake. Mwinanso angalole ana awo kusankha zochita pa nkhani zina ndiyeno n’kuwayamikira zosankha zawo zikayenda bwino. Koma nanga bwanji ngati mwanayo sanasankhe bwino? Nthawi zambiri makolo angafune kuteteza kapena kuikira kumbuyo ana awo koma zimenezi sizikhala zothandiza nthawi zonse. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwana wabwereka njinga kwa mnzake. Kenako mwanayo wawononga njingayo chifukwa chosasamala. Mwina makolo angakakonzetse njingayo. Koma ngati makolowo angauze mwanayo kuti akakonzetse yekha, zikhoza kumuthandiza kuti aphunzire kukhala wosamala.​—Aroma 13:4.

19. Kodi anthu amene timaphunzira nawo Baibulo tiyenera kuwaphunzitsa chiyani, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

19 Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu ena. (Mat. 28:20) Chinthu china chofunika kwambiri chimene tingaphunzitse anthu amene timaphunzira nawo Baibulo ndicho kusankha zochita mwanzeru. Kuti tiwaphunzitse bwino, tiyenera kupewa kuwauza zochita. Zingakhale bwino kuwaphunzitsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kuti azitha kusankha okha zochita. Pajatu, “aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Choncho aliyense ayenera kusankha zinthu zimene zimalemekeza Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, tsamba 3 mpaka 6.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kusankha zochita?

• Kodi mantha angatilepheretse bwanji kusankha zochita ndipo tingapewe bwanji zimenezi?

• Kodi ndi zinthu 6 ziti zimene zingatithandize kusankha zinthu zimene zimalemekeza Mulungu?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 16]

Zinthu Zimene Zingatithandize Kusankha Mwanzeru

1 Pewani Kudzikweza

2 Muzifufuza

3 Pemphani Mulungu Kuti Akupatseni Nzeru

4 Sankhani Zochita

5 Tsatirani Zomwe Mwasankha

6 Onaninso Zimene Mwasankha ndi kusintha Zina

[Chithunzi patsamba 15]

Munthu wokayikakayika amakhala ngati munthu amene ali m’boti lopanda chiwongolero limene likuyenda panyanja kuli mphepo yamkuntho