Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa” Amalemekeza Mulungu

“Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa” Amalemekeza Mulungu

“Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa” Amalemekeza Mulungu

“Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri.”​—YOH. 15:8.

1, 2. (a) Kodi tili ndi mipata iti yolimbikitsa anthu ena? (b) Kodi ndi mphatso iti yochokera kwa Yehova imene imatithandiza pomutumikira?

TAGANIZIRANI zochitika ziwiri izi. Tiyerekeze kuti mlongo wina akuona mlongo wachitsikana amene akuoneka kuti ali ndi nkhawa. Ndiyeno akukonza zoti ayendere limodzi mu utumiki wa kumunda. Pochoka panyumba ina kupita ina alongowo akucheza ndipo mlongo wachitsikanayo akufotokoza zimene zikumudetsa nkhawa. Madzulo ake, mlongo wachitsikanayo akupemphera kwa Yehova ndi kumuthokoza chifukwa chakuti mlongo wachikulireyo wamusonyeza chikondi ndipo chilimbikitso chimenecho n’chimene ankafuna kwambiri. Tiyerekezenso kuti kudera lina, banja lomwe linapita kukagwira ntchito yolalikira kudziko lina langofika kumene. Pamene likucheza ndi anthu ena, likufotokoza mosangalala zimene linakumana nazo ndipo pali m’bale wachinyamata amene akumvetsera ali phe. Patapita zaka zingapo, m’baleyo akukonzekera kukatumikira kudziko lina ndipo akuganizira zimene banjalo linanena, zomwe zinamulimbikitsa kuti akhale mmishonale.

2 Mwina zochitika ziwirizi zakukumbutsani za munthu wina amene anakuthandizani kwambiri kapena amene munamuthandiza. N’zoona kuti nthawi zambiri munthu sangasinthe moyo wake chifukwa chongocheza ndi munthu wina kamodzi kokha. Koma tsiku lililonse timakhala ndi mipata yolimbikitsa anthu ena. Kodi simungayamikire patakhala chinthu chimene chingakuthandizeni kukhala ndi maluso ndiponso makhalidwe abwino kuti muthandize kwambiri abale anu komanso kuti mutumikire bwino Mulungu? Yehova watipatsa mphatso yotere. Mphatso imeneyi ndi mzimu woyera. (Luka 11:13) Mzimu wa Mulunguwu ukamagwira ntchito pa moyo wathu, umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino amene ndi ofunika kwambiri potumikira Mulungu. Mzimu woyera ndi mphatso yamtengo wapatali ndithu.​—Werengani Agalatiya 5:22, 23.

3. (a) Kodi timalemekeza bwanji Mulungu tikamayesetsa kukhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa”? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndi amene Yehova Mulungu, yemwe amapereka mzimuwo, ali nawo. (Akol. 3:9, 10) Yesu anatchula chifukwa chachikulu chimene chingalimbikitse Akhristu kuchita khama potsanzira Mulungu. Iye anauza atumwi ake kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri.” * (Yoh. 15:8) Tikamayesetsa kukhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa,” zimaonekera pa zolankhula ndiponso zochita zathu. Zotsatira zake ndi zakuti Mulungu amalemekezeka. (Mat. 5:16) Kodi makhalidwe amene mzimu umatulutsa amasiyana bwanji ndi makhalidwe a m’dziko la Satanali? Kodi tingatani kuti tikhale ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa? N’chifukwa chiyani kukhala ndi makhalidwe amenewa kumavuta? Tikambirana mafunso amenewa pamene tikuona makhalidwe atatu oyambirira amene mzimu woyera umatulutsa. Makhalidwe ake ndi chikondi, chimwemwe ndiponso mtendere.

Chikondi Choyendera Mfundo Zapamwamba

4. Kodi Yesu anaphunzitsa otsatira ake kusonyeza chikondi chotani?

4 Chikondi chimene mzimu woyera umatulutsa n’chosiyana kwambiri ndi chikondi chimene chafala m’dzikoli. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti chimayendera mfundo zapamwamba. Yesu anafotokoza kusiyana kwake pa ulaliki wa paphiri. (Werengani Mateyu 5:43-48.) Iye anasonyeza kuti ngakhale anthu ochimwa amachitira anthu ena zimene anthuwo amawachitira. Anthu amene amasonyeza “chikondi” chimenechi salolera kuvutikira ena koma amangobwezera zabwino zimene enawo awachitira. Tiyenera kukhala osiyana ndi anthu amenewa ngati tikufuna ‘kusonyeza kuti ndifedi ana a Atate wathu wakumwamba.’ M’malo mongochitira anthu zimene iwowo atichitira, tiyenera kuwaona ndiponso kuwachitira zinthu mmene Yehova amachitira. Koma kodi tingatsatire bwanji lamulo la Yesu lakuti tizikonda adani athu?

5. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu amene amatizunza?

5 Tiyeni tione chitsanzo chimodzi cha m’Baibulo. Pamene Paulo ndi Sila ankalalikira ku Filipi anamangidwa, kukwapulidwa, kutsekeredwa m’chipinda chamkati cha ndende ndiponso mapazi awo anamangidwa m’matangadza. N’kutheka kuti woyang’anira ndende anawazunzanso. Koma kodi iwo atamasulidwa mwadzidzidzi chifukwa cha chivomezi, anaganiza zobwezera woyang’anira ndendeyo? Ayi. Chifukwa cha chikondi chawo chololera kuvutikira ena, anamuthandiza mwamsanga ndipo izi zinachititsa kuti iye ndi anthu onse a m’nyumba yake akhale okhulupirira. (Mac. 16:19-34) Masiku anonso, abale athu ambiri ‘amadalitsa anthu amene amawazunza.’​—Aroma 12:14.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale athu moti tikhoza kulolera kuwavutikira? (Onani bokosi patsamba 21.)

6 Akhristu anzathu ndi ofunika kuti tiziwakonda kwambiri. “Tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.” (Werengani 1 Yohane 3:16-18.) Koma nthawi zambiri tingasonyeze chikondi m’njira zing’onozing’ono. Mwachitsanzo, ngati talankhula kapena kuchita zinthu zimene zakhumudwitsa m’bale wathu, tingasonyeze chikondi mwa kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tikhazikitse mtendere. (Mat. 5:23, 24) Nanga bwanji ngati wina watikhumudwitsa? Kodi ndife ‘okonzeka kukhululuka’ kapena nthawi zina timakonda kusunga chakukhosi? (Sal. 86:5) Chikondi champhamvu chimene mzimu woyera umatulutsa chingatithandize kukwirira zinthu zing’onozing’ono zimene ena atilakwira. Chingatithandizenso kuti tiziwakhululukira ndi mtima wonse ‘monga Yehova anatikhululukira ndi mtima wonse.’​—Akol. 3:13, 14; 1 Pet. 4:8.

7, 8. (a) Kodi kukonda Mulungu kumagwirizana bwanji ndi kukonda anthu? (b) Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri Yehova? (Onani chithunzi m’munsimu.)

7 Kodi tingatani kuti tizikonda abale athu mpaka kulolera kuwavutikira? Kukonda kwambiri Mulungu n’kumene kungatithandize kuchita zimenezi. (Aef. 5:1, 2; 1 Yoh. 4:9-11, 20, 21) Tikamawerenga Baibulo, kusinkhasinkha ndiponso kupemphera timakhala ngati tikufatsa patokha ndi Yehova ndipo izi zimatithandiza kuti tizikonda Atate wathu wakumwamba ndi mtima wathu wonse. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kupatula nthawi yoti tiyandikire Mulungu.

8 Tiyerekeze kuti tsiku lililonse, mumakhala ndi mpata wa ola limodzi lokha pa nthawi inayake kuti muwerenge Mawu a Mulungu, kusinkhasinkha ndiponso kupemphera. Kodi simungayesetse kuti chilichonse chisasokoneze nthawi imene mumalankhulana ndi Yehovayi? Zoona zake n’zakuti palibe amene angatilepheretse kulankhula ndi Mulungu m’pemphero ndipo ambirife tingathe kuwerenga Baibulo pa nthawi iliyonse imene tafuna. Koma tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti zochita zathu za tsiku ndi tsiku zisatiwonongere nthawi yathu yolimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Kodi mumayesetsa mmene mungathere kupatula nthawi tsiku lililonse yoti muyandikire Yehova?

“Chimwemwe cha Mzimu Woyera”

9. Kodi chimwemwe chimene mzimu woyera umatulutsa n’chotani?

9 Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa sasinthasintha ngakhale pamene takumana ndi mavuto. Chimwemwe, chomwe ndi khalidwe lachiwiri limene tikambirane, sichisinthasinthanso. Chimwemwe chili ngati chomera champhamvu chimene chimasangalalabe ngakhale pamene nyengo ndi nthaka sizili bwino. Atumiki a Mulungu padziko lonse ‘amalandira mawuwo ndi chimwemwe cha mzimu woyera ngakhale kuti ali m’masautso ambiri.’ (1 Ates. 1:6) Ena amakumana ndi mavuto ambiri komanso amasowa zinthu zofunika pa moyo. Ngakhale zili choncho, Yehova amawalimbikitsa ndi mzimu wake kuti ‘athe kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’ (Akol. 1:11) Koma kodi chimwemwe chimenechi chimachokera kuti?

10. Kodi chimwemwe chimene timakhala nacho chimachokera kuti?

10 Mosiyana ndi “chuma chosadalirika” cha m’dziko la Satanali, chuma chauzimu chimene Yehova watipatsa chingatithandize kwamuyaya. (1 Tim. 6:17; Mat. 6:19, 20) Iye akufuna kuti tidzakhale ndi moyo wosangalala komanso wosatha. Ndife osangalala kukhala pa ubale wa padziko lonse ndi Akhristu anzathu. Koma koposa zonse ndife osangalala chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Timamva ngati mmene ankamvera Davide. Ngakhale pa nthawi imene moyo wake unali wothawathawa, iye anatamanda Yehova poimba kuti: “Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo, milomo yanga idzakuyamikirani. Choncho ndidzakutamandani pa nthawi yonse ya moyo wanga.” (Sal. 63:3, 4) Ngakhale pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto, mumtima mwathu timatamanda Mulungu mosangalala.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kutumikira Yehova mosangalala?

11 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani.” (Afil. 4:4) N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kutumikira Yehova mosangalala? Chifukwa cha nkhani imene Satana anayambitsa yokhudza ulamuliro wa Yehova. Satana amanena kuti palibe amene amatumikira Mulungu mwa kufuna kwake. (Yobu 1:9-11) Ngati timatumikira Yehova mongotsatira malamulo ake koma mosasangalala, nsembe zathu zotamanda zingakhale zoperewera. Choncho ndi bwino kuyesetsa kutsatira malangizo a wamasalmo akuti: “Tumikirani Yehova mokondwera. Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.” (Sal. 100:2) Mulungu amalemekezeka tikamamutumikira mosangalala kuchokera mumtima.

12, 13. Kodi tingatani ngati takhumudwa ndi zinazake?

12 Kunena zoona, ngakhale atumiki okhulupirika a Yehova nthawi zina amakhumudwa ndipo zimakhala zovuta kuti akhalebe osangalala. (Afil. 2:25-30) Kodi n’chiyani chingatithandize ngati zimenezi zatichitikira? Lemba la Aefeso 5:18, 19 limati: “Khalanibe odzaza ndi mzimu. Mukakhala pakati panu muziimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba nyimbo zotamanda Yehova m’mitima mwanu.” Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa?

13 Ngati takhumudwa ndi zinthu zinazake, tiyenera kuchonderera Yehova kuti atithandize n’kumayesetsa kuganizira zinthu zotamandika. (Werengani Afilipi 4:6-9.) Anthu ena apeza kuti kuimba chamumtima nyimbo za Ufumu kumawathandiza kuti mtima wawo ukhale m’malo komanso kuti ayambe kuganizira zinthu zolimbikitsa. M’bale wina amene anali ndi vuto limene linkamukhumudwitsa ndiponso kumutayitsa mtima anati: “Ndinkapemphera pafupipafupi kuchokera pansi pa mtima komanso ndinaloweza nyimbo za Ufumu zingapo. Ndinkatsitsimulidwa kwambiri ndikamaimba mokweza kapena chamumtima nyimbo zosangalatsa zotamanda Yehova zimenezi. Komanso buku lakuti Yandikirani kwa Yehova linatulutsidwa pa nthawi imeneyi. Ndinaliwerenga kawiri chaka chotsatira. Bukuli linangokhala ngati mankhwala othandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo. Ndikudziwa kuti Yehova anadalitsa khama langa.”

‘Mtendere Ndi Chomangira Chotigwirizanitsa’

14. Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mtendere umene mzimu woyera umatulutsa?

14 Pa misonkhano ya mayiko, anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana amasangalala kwambiri kucheza ndi Akhristu anzawo. Zimenezi zimangosonyezeratu kuti mtendere umene anthu a Mulungu ali nawo masiku ano umawachititsa kuti azikhala ogwirizana kwambiri padziko lonse. Anthu ena amagoma kwambiri akaona anthu amene iwo amaganiza kuti sangagwirizane ‘akuyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wawo mwa mzimuwo, ndi mwamtendere monga chomangira chowagwirizanitsa.’ (Aef. 4:3) Mgwirizano umenewu ndi wodabwitsa kwambiri tikaganizira mmene aliyense wasinthira kuti izi zitheke.

15, 16. (a) Kodi Petulo ayenera kuti anali ndi maganizo ati kuyambira ali mwana ndipo maganizowo akanamulepheretsa kuchita chiyani? (b) Kodi Yehova anathandiza bwanji Petulo kusintha maganizo ake?

15 Kugwirizanitsa anthu ochokera m’zikhalidwe zosiyana si chinthu chapafupi. Kuti timvetse zimene munthu ayenera kusintha n’cholinga choti agwirizane ndi anzake, tiyeni tikambirane chitsanzo cha mtumwi Petulo. Mawu ena amene iye ananena amasonyeza mmene ankaonera anthu a mitundu ina omwe sanali odulidwa. Iye anati: “Inunso mukudziwa bwino kuti n’kosaloleka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa fuko lina kapena kumuyandikira. Koma tsopano Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti woipitsidwa kapena wonyansa.” (Mac. 10:24-29; 11:1-3) Malinga ndi maganizo amene Ayuda anali nawo pa nthawi imeneyo, Petulo ayenera kuti kuyambira ali mwana ankakhulupirira kuti Chilamulo chimawauza kuti azikonda Ayuda anzawo basi. Mwina Petulo sankaganiza kuti ndi kulakwa kuona anthu a mitundu ina ngati adani awo. *

16 Kodi mukuganiza kuti Petulo anamva bwanji pamene ankalowa m’nyumba ya Koneliyo? Kodi zikanathekadi kuti munthu amene poyamba ankadana ndi anthu amitundu ina ‘alumikizane nawo bwino’ ndiponso akhale nawo pa ‘mtendere, umene ndi chomangira chogwirizanitsa’? (Aef. 4:3, 16) Inde, chifukwa chakuti masiku ochepa izi zisanachitike, mzimu wa Mulungu unathandiza Petulo kusintha mtima ndi maganizo ake atsankho. M’masomphenya, Yehova anamuthandiza kuzindikira kuti Mulungu saona anthu amtundu wina kapena a dziko lina kukhala ofunika kuposa ena. (Mac. 10:10-15) Choncho, Petulo anatha kuuza Koneliyo kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Petulo anasintha n’kuyamba kugwirizana ndi “gulu lonse la abale.”​—1 Pet. 2:17.

17. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti mgwirizano wa anthu a Mulungu ndi wodabwitsa?

17 Zimene zinachitika ndi Petulo zimatithandiza kumvetsa mmene anthu a Mulungu akusinthira kwambiri masiku ano. (Werengani Yesaya 2:3, 4.) Anthu mamiliyoni ambiri ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” asintha maganizo awo kuti agwirizane ndi “chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Chiv. 7:9; Aroma 12:2) Ambiri mwa anthu amenewa m’mbuyomu ankafanana ndi anthu a m’dziko la Satanali. Iwo ankadana kwambiri ndi anthu ena ndiponso anali atsankho. Koma chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu ndiponso kuthandizidwa ndi mzimu woyera, iwo aphunzira kutsatira “zinthu zobweretsa mtendere.” (Aroma 14:19) Zimenezi zimachititsa kuti akhale ogwirizana ndipo mgwirizanowo umalemekeza Mulungu.

18, 19. (a) Kodi aliyense wa ife angalimbikitse bwanji mtendere ndi mgwirizano mu mpingo? (b) Kodi mu nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

18 Kodi aliyense wa ife angalimbikitse bwanji mtendere ndi mgwirizano wa anthu a Mulungu? M’mipingo yambiri muli anthu ochokera kumayiko ena. Ena mwa iwo ali ndi zikhalidwe zosiyana ndi chathu kapena salankhula bwino chinenero chathu. Kodi timayesetsa kucheza nawo? Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuchita zimenezi. Akhristu a mu mpingo wa ku Roma anali Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina. Ndiyeno m’kalata imene Paulo analembera mpingowo, anati: “Landiranani, monga mmene Khristu anatilandirira, kuti ulemerero upite kwa Mulungu.” (Aroma 15:7) Kodi mu mpingo wanu muli munthu amene muyenera kuyesetsa kuti muyambe kucheza naye?

19 Kodi n’chiyaninso chimene tiyenera kuchita kuti mzimu woyera uzititsogolera? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli ndipo tidzakambirana makhalidwe ena amene mzimu woyera umatulutsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zipatso zimene Yesu anatchulazi ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa” ndiponso “chipatso cha milomo yathu” chimene Akhristu amapereka kwa Mulungu akamalalikira za Ufumu.​—Aheb. 13:15.

^ ndime 15 Lemba la Levitiko 19:18 limanena kuti: “Usabwezere choipa kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Atsogoleri a chipembedzo chachiyuda ankanena kuti mawu akuti “anthu amtundu wako” ndiponso “mnzako” amanena za Ayuda okha. Chilamulo chinkauza Aisiraeli kuti azikhala osiyana ndi anthu a mitundu ina. Komabe, sichinkalimbikitsa maganizo amene atsogoleri achipembedzo ankalimbikitsa m’nthawi ya atumwi. Atsogoleriwo ankati munthu aliyense wa mtundu wina anali mdani wawo ndipo sanali woyenera kumukonda.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale athu moti tikhoza kulolera kuwavutikira?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kutumikira Mulungu mosangalala?

• Kodi tingalimbikitse bwanji mtendere ndi mgwirizano mu mpingo?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 21]

“Anthu Awa Ndi Akhristu Oona”

M’buku lina lofotokoza zimene zinachitikira Mboni za Yehova m’nthawi ya chipani cha Nazi, muli mawu a mnyamata wina wachiyuda yemwe anali mkaidi. Mnyamatayu ananena za nthawi yoyamba imene anakumana ndi Mboni za Yehova atangofika kumene kundende ya Neuengamme.

Iye anati: “Titangofika kundendeyo kuchokera ku Dachau, Ayuda anzathu anayamba kubisa zinthu zawo n’cholinga choti asatigawire. . . . Tisanamangidwe, Ayudafe tinkathandizana. Koma m’ndendemu, pamene moyo unali pa ngozi, aliyense ankangoganiza zopulumutsa moyo wake osati wa anzake. Koma zimene Ophunzira Baibulo ankachita zinali zosiyana kwambiri. Pa nthawi imeneyo, iwo ankagwira ntchito yovuta kwambiri yokonza mapaipi a madzi. Kunja kunkazizira kwambiri ndipo iwo ankaima tsiku lonse m’madzi oziziranso kwambiri. Aliyense ankadabwa kwambiri ndi kupirira kwawo. Iwo ankanena kuti Yehova ndi amene amawapatsa mphamvu. Mofanana ndi ife, iwo ankafunika kudya buledi wawo chifukwa nawonso anali ndi njala. Koma kodi iwo anachita chiyani? Anasonkhanitsa buledi wawo n’kutenga hafu kuti adye iwowo ndipo hafu inayo anapatsa Akhristu anzawo amene anali atangofika kumene kuchokera ku Dachau. Iwo anawalandira bwino n’kuwapsompsona. Asanadye bulediyo, anapemphera. Atadya, onse anali kusangalala. Ananena kuti njala yonse inatha. Izi n’zimene zinandichititsa kuganiza kuti, ‘Anthu awa ndi Akhristu oona.’”​—Between Resistance and Martyrdom​—Jehovah’s Witnesses in the Third Reich.

[Zithunzi patsamba 19]

Kodi mumapatula nthawi tsiku lililonse kuti muyandikire Yehova?