Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukulola Mzimu wa Mulungu Kukutsogolerani?

Kodi Mukulola Mzimu wa Mulungu Kukutsogolerani?

Kodi Mukulola Mzimu wa Mulungu Kukutsogolerani?

“Mzimu wanu ndi wabwino. Unditsogolere m’dziko la olungama.”​—SAL. 143:10.

1, 2. (a) Tchulani zochitika zina zimene zikusonyeza kuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuthandiza atumiki ake. (b) Kodi mzimu woyera umagwira ntchito pa zochitika zapadera zokha? Fotokozani.

N’CHIYANI chimabwera m’maganizo mwanu mukaganizira mmene mzimu woyera umagwirira ntchito? Kodi mumaganizira za zinthu zikuluzikulu zimene Gidiyoni ndi Samisoni anachita? (Ower. 6:33, 34; 15:14, 15) Mwina mumaganizira za kulimba mtima kwa Akhristu oyambirira kapena kupanda mantha kwa Sitefano pamene anali m’bwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mac. 4:31; 6:15) Masiku anonso pali zitsanzo zina zimene zimasonyeza mmene mzimu woyera umagwirira ntchito. Mwachitsanzo, taganizirani za chimwemwe chimene chimakhalapo pa misonkhano yathu yamayiko, kukhulupirika kwa abale athu amene aikidwa m’ndende chifukwa chosalowerera ndale ndiponso mmene ntchito yolalikira ikupitira patsogolo. Zitsanzo zonsezi zimapereka umboni wakuti mzimu woyera ukugwira ntchito.

2 Kodi mzimu woyera umagwira ntchito pa zochitika zapadera kapena pa zinthu zikuluzikulu zokha basi? Ayi. Mawu a Mulungu amanena kuti Akhristu ‘amayenda mwa mzimu,’ ‘kutsogoleredwa ndi mzimu’ ndiponso ‘kukhala mwa mzimu.’ (Agal. 5:16, 18, 25) Mawu amenewa akusonyeza kuti mzimu woyera ukhoza kugwira ntchito pa moyo wathu nthawi zonse. Tsiku lililonse tiyenera kupempha Yehova ndi mtima wonse kuti mzimu wake woyera uzititsogolera tikamaganiza, kulankhula kapena kuchita zinthu. (Werengani Salimo 143:10.) Tikamalola kuti mzimu woyera uzigwira ntchito kwambiri pa moyo wathu, ungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe amene amatsitsimula ena ndiponso kulemekeza Mulungu.

3. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsogoleredwa ndi mzimu woyera? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 N’chifukwa chiyani kutsogoleredwa ndi mzimu woyera kuli kofunika kwambiri? N’chifukwa chakuti pali mphamvu ina yotsutsana ndi mzimu woyera imene imafuna kutilamulira. Malemba amatiuza kuti mphamvu imeneyi ndi “thupi,” kutanthauza zilakolako za thupi lathu lochimwa, kapena kuti zotsatira za kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa kholo lathu Adamu. (Werengani Agalatiya 5:17.) Ndiyeno, kodi tingalole bwanji kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu? Kodi pali zilizonse zimene tingachite kuti tisamalamulidwe ndi thupi lathu lochimwali? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa pamene tikuona makhalidwe ena 6 amene “mzimu woyera umatulutsa.” Makhalidwe ake ndi “kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”​—Agal. 5:22, 23.

Kufatsa Ndiponso Kuleza Mtima Zimalimbikitsa Mtendere mu Mpingo

4. Kodi kufatsa ndi kuleza mtima zimathandiza bwanji kuti mu mpingo mukhale mtendere?

4 Werengani Akolose 3:12, 13. Kufatsa ndiponso kuleza mtima zimayendera limodzi polimbikitsa mtendere mu mpingo. Makhalidwe amenewa, omwe mzimu woyera umatulutsa, amatithandiza kuchitira ena ulemu, kusapsa mtima ena akatiputa ndiponso kupewa kubwezera zinthu zopweteka zimene ena atichitira kapena kutilankhula. Tikasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu, kuleza mtima kungatithandize kuti tisasiye kuchita zonse zimene tingathe pofuna kukhazikitsa mtendere ndi munthuyo. Koma kodi kufatsa ndi kuleza mtima n’zofunikadi mu mpingo? Inde, chifukwa chakuti tonse ndife opanda ungwiro.

5. Kodi n’chiyani chinachitika pakati pa Paulo ndi Baranaba ndipo zimenezi zikusonyeza chiyani?

5 Taganizirani zimene zinachitikira Paulo ndi Baranaba. Kwa zaka zambiri, iwo anagwira limodzi ntchito yolalikira uthenga wabwino. Aliyense anali ndi makhalidwe abwino kwambiri. Koma pa nthawi ina panabuka “mkangano woopsa” pakati pawo. (Mac. 15:36-39) Izi zikusonyeza kuti nthawi zina ngakhale atumiki a Mulungu okhulupirika akhoza kusemphana maganizo. Ngati Akhristu awiri asemphana maganizo, kodi iwo angatani kuti asapsetsane mtima kwambiri n’kuwononga ubwenzi wawo kwa nthawi yaitali?

6, 7. (a) Ngati tayamba kupsa mtima pokambirana ndi Mkhristu mnzathu, kodi tiyenera kutsatira malangizo ati a m’Malemba? (b) Kodi kukhala ‘wofulumira kumva, wodekha polankhula ndiponso wosafulumira kukwiya’ kungathandize bwanji?

6 Mawu akuti “panabuka mkangano woopsa” akusonyeza kuti kusemphana maganizo kwa Paulo ndi Baranaba kunachitika mosayembekezereka ndipo zinthu zinafika poipa. Mkhristu akaona kuti wayamba kupsa mtima pamene akukambirana ndi Mkhristu mnzake, angachite bwino kutsatira malangizo opezeka pa Yakobo 1:19, 20 akuti: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya, chifukwa mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” Malinga ndi mmene zinthu zilili, munthu akaona kuti wayamba kupsa mtima angasankhe kuyambitsa nkhani ina, kupempha kuti nkhaniyo adzaipitirize nthawi ina, kapena kungochokapo mwaulemu.​—Miy. 12:16; 17:14; 29:11.

7 Kodi kutsatira malangizo amenewa kuli ndi ubwino wotani? Mkhristu akapeza nthawi yoti mtima wake ukhale m’malo, kupempherera nkhaniyo ndiponso kuganizira mmene angayankhire bwino, ndiye kuti akulola kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. (Miy. 15:1, 28) Mothandizidwa ndi mzimu, iye angasonyeze kufatsa ndi kuleza mtima. Izi zingamuthandize kutsatira malangizo opezeka pa Aefeso 4:26, 29 akuti: “Kwiyani, koma musachimwe. . . . Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” N’zoona kuti tikakhala ofatsa ndiponso oleza mtima timathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendere ndi mgwirizano.

Muzitsitsimula Banja Lanu ndi Khalidwe la Kukoma Mtima Ndiponso Ubwino

8, 9. Kodi munthu wokoma mtima ndiponso wabwino amakhala wotani, ndipo kodi makhalidwe amenewa amathandiza bwanji m’banja?

8 Werengani Aefeso 4:31, 32; 5:8, 9Mofanana ndi kamphepo kayeziyezi ndiponso kumwa madzi ozizira kunja kukatentha kwambiri, anthu okoma mtima ndiponso abwino amatitsitsimula. Kukoma mtima ndiponso ubwino zimathandiza kuti anthu m’banja azikhala mosangalala. Munthu amakhala wokoma mtima chifukwa chokonda anthu ena ndipo amasonyeza kukoma mtimako mwa kuthandiza anthu kapena kulankhula mowaganizira. Izi zimachititsa kuti anthu azimukondanso. Mofanana ndi kukoma mtima, munthu amasonyeza kuti ndi wabwino mwa kuthandiza ena. Munthu wabwino amakhala wowolowa manja. (Mac. 9:36, 39; 16:14, 15) Koma pali zinthu zinanso zimene zimafunika kuti munthu akhale wabwino.

9 Ubwino sumangokhudza zochita za munthu koma khalidwe lake lonse, kapena kuti mmene alili mumtima mwake. Tingayerekezere zimenezi ndi chipatso chimene mayi akuchikonza kuti banja lake lidye. Mayiyo amayang’anitsitsa mbali iliyonse ya chipatsocho pofuna kutsimikizira kuti ndi chakupsa, chotsekemera ndiponso chosawola kunja ndi mkati momwe. Nawonso ubwino umene mzimu woyera umatulutsa umakhudza mbali iliyonse ya moyo wa Mkhristu.

10. Kodi n’chiyani chingathandize anthu m’banja kuti azikhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa?

10 Kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kuti akhale wokoma mtima ndi wabwino pochita zinthu ndi ena m’banja? Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kungathandize kwambiri pa nkhani imeneyi. (Akol. 3:9, 10) Mitu ya mabanja ena imakonza zoti pa Kulambira kwa Pabanja aziphunziranso makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Kuchita zimenezi n’kosavuta. Mukhoza kufufuza nkhani zokhudza khalidwe lililonse palokha m’mabuku ndi m’magazini. Ndiyeno mukhoza kuphunzira khalidwe limodzi kwa milungu ingapo mwa kukambirana ndime zochepa mlungu uliwonse. Pophunzira muziwerenga ndiponso kukambirana malemba amene ali mu nkhaniyo. Onani mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwaphunzira ndipo muzipempha Yehova kuti adalitse khama lanu. (1 Tim. 4:15; 1 Yoh. 5:14, 15) Kodi kuphunzira kotereku kungathandizedi pochita zinthu ndi ena m’banja?

11, 12. Kodi kuphunzira za kukoma mtima kunathandiza bwanji mabanja awiri achikhristu?

11 Banja lina lachinyamata linaganiza zophunzira mozama makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa n’cholinga choti banja lawo liziyenda bwino. Kodi zimenezi zawathandiza bwanji? Mkaziyo anati: “Kudziwa kuti munthu wokoma mtima amakhala wokhulupirika ndipo sachita chiwerewere kwathandiza kuti aliyense asinthe mmene amachitira zinthu ndi mnzake m’banja lathu. Taphunzira kukhala ololera ndiponso kukhululuka. Taphunziranso kunena kuti ‘zikomo kwambiri’ ndiponso ‘pepani’ pakafunika kutero.”

12 Banja linanso lachikhristu limene linali ndi mavuto a m’banja linazindikira kuti vuto lawo linali kuchita zinthu mosakomerana mtima. Iwo anaganiza zophunzira limodzi nkhani ya kukoma mtima. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mwamuna wa m’banjalo anati: “Titaphunzira za kukoma mtima, tinaona kuti si bwino kuthamangira kuimbana mlandu poganiza kuti mnzathu ali ndi zolinga zoipa koma tiyenera kuyesetsa kuona zabwino mwa mnzathuyo. Tinayambanso kuganizira kwambiri zofuna za wina. Ndinaona kuti ndingasonyeze kukoma mtima mwa kulola mkazi wanga kufotokoza maganizo ake momasuka. Koma kuti ndimulole kuchita zimenezi popanda kukhumudwa ndi zimene akunena, ndinayenera kusiya kudzikuza. Pamene tinayamba kukomerana mtima m’banja, tinasiya mtima wofuna kudziikira kumbuyo nthawi zonse. Zimenezi zinathandiza kuti tizikambirana momasuka.” Kuphunzira makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa kukhoza kuthandizanso banja lanu.

Khalani ndi Chikhulupiriro Mukakhala Kwanokha

13. Kodi tiyenera kusamala ndi zinthu ziti zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova?

13 Akhristu ayenera kulola mzimu wa Mulungu kuwatsogolera akakhala pa gulu ndiponso kwaokha. Masiku ano m’dziko la Satanali, zithunzi ndiponso zosangalatsa zonyansa zili ponseponse. Zimenezi zikhoza kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi Mkhristu ayenera kutani? Mawu a Mulungu amatilangiza kuti: “Siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe lochita zoipa, lomwe ndi losafunika, ndipo vomerezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu, kuti abzalidwe mwa inu.” (Yak. 1:21) Chikhulupiriro ndi khalidwe lina limene mzimu woyera umatulutsa. Tiyeni tikambirane mmene chingatithandizire kukhalabe oyera kwa Yehova.

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zingakhale zosavuta kuti munthu amene alibe chikhulupiriro achite zoipa?

14 Chikhulupiriro kwenikweni chimatanthauza kuona kuti Yehova Mulungu ndi weniweni kwa ife. Ngati Mulungu si weniweni kwa ife zingakhale zosavuta kuti tichite zoipa. Taganizirani zimene anthu a Mulungu ankachita kalelo. Yehova anaululira Ezekieli zinthu zonyansa zimene zinali kuchitika m’malo obisika. Mulungu anati: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mu mdima? Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita m’chipinda chamkati mmene muli fano lake losema? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona. Yehova wachokamo m’dziko muno.’” (Ezek. 8:12) Kodi mwaona chimene chinayambitsa vutoli? Iwo sankakhulupirira kuti Yehova akuona zimene akuchita. Yehova sanali weniweni kwa iwo.

15. Kodi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova kungatiteteze bwanji?

15 Koma tsopano tiyeni tione chitsanzo chabwino cha Yosefe. Ngakhale kuti Yosefe anali kutali ndi achibale ake ndiponso anthu a mtundu wake, iye anakana kuchita chigololo ndi mkazi wa Potifara. N’chifukwa chiyani anakana? Iye ananena kuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” (Gen. 39:7-9) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova anali weniweni kwa iye. Ngati Mulungu ndi weniweni kwa ife, sitingaonere zinthu zoipa kapena kuchita mwamseri zinthu zimene tikudziwa kuti Mulungu amadana nazo. Maganizo athu adzafanana ndi a wamasalimo amene anaimba kuti: “Ndidzayendayenda m’nyumba yanga ndi mtima wanga wosagawanika. Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.”​—Sal. 101:2, 3.

Tetezani Mtima Wanu mwa Kudziletsa

16, 17. (a) Mogwirizana ndi nkhani ya m’buku la Miyambo, kodi “mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake” anayamba bwanji kuchita zoipa? (b) Malinga ndi chithunzi chimene chili patsamba 26, kodi munthu, kaya akhale wa msinkhu wotani, angachite bwanji zimene mnyamatayu anachita?

16 Kudziletsa, lomwe ndi khalidwe lomaliza limene mzimu woyera umatulutsa, kumatithandiza kukana zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Kudziletsa kungatithandize kuteteza mtima wathu. (Miy. 4:23) Taganizirani nkhani yopezeka pa Miyambo 7:6-23 yofotokoza mmene “mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake” anakopekera ndi hule. Iye anakopeka pamene “anali kuyenda mumsewu pafupi ndi mphambano yopita kunyumba” kwa mkaziyo. Mwina chidwi chongofuna kumuona n’chimene chinamuchititsa kuyenda pafupi ndi nyumba yake. Koma mosayembekezereka, iye anatengeka osazindikiranso kuti akuyamba kuchita zinthu zopanda nzeru zimene “zikukhudza moyo wake.”

17 Kodi mnyamatayu akanapewa bwanji kuchita zimenezi? Iye akanapewa mwa kutsatira chenjezo lakuti: “Usayendeyende m’njira zake.” (Miy. 7:25) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Ngati tikufuna kuti mzimu wa Mulungu uzititsogolera tiyenera kupewa zinthu zimene zingatiyese. Munthu amene amangokhalira kufufuza matchanelo pa TV kapena amene amangoona zilizonse pa Intaneti, akhoza kukumana ndi mavuto ofanana ndi amene “mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake” anakumana nawo. Munthu wotereyu akhoza kuona mwadala kapena mwangozi zinthu zomuchititsa kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana. Pang’onopang’ono angayambe chizolowezi choonera zolaula, ndipo izi zingawononge chikumbumtima chake ndiponso ubwenzi wake ndi Mulungu. Izi zikhoza kuwononganso moyo wake.​—Werengani Aroma 8:5-8.

18. Kodi Mkhristu angachite chiyani kuti ateteze mtima wake, ndipo kudziletsa kungathandize bwanji pa nkhani imeneyi?

18 N’zoona kuti tiyenera kudziletsa mwa kuchitapo kanthu mwamsanga tikangoona zinthu zimene zingatichititse kufuna kugonana. Koma tingachite bwino kwambiri kupeweratu kuona zinthu zoterezi. (Miy. 22:3) Tingakhalenso odziletsa tikamadziikira malire n’kumayesetsa kusapitirira malirewo. Mwachitsanzo, kuika kompyuta pamalo oonekera kungatiteteze. Ena amaona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito kompyuta kapena kuonera TV pokhapokha ngati anthu ena alipo. Koma ena anasankha zoti asakhale ndi Intaneti. (Werengani Mateyu 5:27-30.) Tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe pofuna kudziteteza ndiponso kuteteza banja lathu n’cholinga choti tizilambira Yehova kuchokera “mumtima woyera, m’chikumbumtima chabwino, ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.”​—1 Tim. 1:5.

19. Kodi kulola kuti mzimu woyera uzititsogolera kuli ndi phindu lotani?

19 Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndi othandiza kwambiri. Kufatsa ndi kuleza mtima zimathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendere. Kukoma mtima ndi ubwino zimathandiza kuti banja likhale losangalala. Chikhulupiriro ndi kudziletsa zimatithandiza kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso kuti tikhale oyera kwa iye. Ndipotu lemba la Agalatiya 6:8 limatitsimikizira kuti: “Amene akutsatira mzimu wa Mulungu adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.” Chifukwa cha dipo la Khristu, Yehova adzagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti apereke moyo wosatha kwa anthu amene amalola kutsogoleredwa ndi mzimuwo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kufatsa ndi kudziletsa zimalimbikitsa bwanji mtendere mu mpingo?

• N’chiyani chingathandize Akhristu kukhala okoma mtima ndiponso abwino m’banja?

• Kodi chikhulupiriro ndi kudziletsa zingathandize bwanji Mkhristu kuteteza mtima wake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi mungachite chiyani kuti musapse mtima pokambirana ndi munthu wina?

[Chithunzi patsamba 25]

Kuphunzira makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa kungathandize kwambiri banja lanu

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi chikhulupiriro ndi kudziletsa zingatiteteze ku zinthu ziti?