Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• N’chifukwa chiyani timakhulupirira zoti munda wa Edeni unalikodi?

Baibulo limasonyeza kuti mundawu unalikodi ndipo limatchula malo enieni pamene mundawu unali. Mitsinje iwiri imene imatchulidwa pofotokoza za mundawu idakalipobe. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi nthano zimene anthu amakamba chifukwa sizitchula malo enieni. Yesu, yemwe ndi Mboni yokhulupirika, ananena za Adamu ndi Hava mosonyeza kuti anali anthu enieni.​—1/1, tsamba 5-6, 9.

• Kodi Mulungu anadziwiratu kuti Adamu ndi Hava adzachimwa?

Ayi. Yehova anapatsa Adamu ndi Hava nzeru komanso ufulu wosankha zochita. Iwo akanatha kumumvera kapena ayi. Ngakhale kuti ali ndi mphamvu yodziwiratu za m’tsogolo, si nthawi zonse pamene Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu imeneyi.​—1/1, tsamba 13-15.

• Kodi Akhristu amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu ngati chithumwa?

Anthu ena amaganiza kuti zinthu ndiponso zizindikiro zina zili ndi mphamvu yamatsenga ndipo zitha kuwateteza. Koma si mmene anthu a Mulungu amaonera dzina lake. Iwo amapeza chitetezo m’dzina la Yehova mwa kumukhulupirira ndi kuchita chifuniro chake. (Zef. 3:12, 13)​—1/15, tsamba 5-6.

• Kodi ku Isiraeli ndani ankapindula ndi lamulo lokhudza khunkha?

Anthu onse ankapindula. Kwa anthu osauka amene ankakunkhawo, lamuloli linkawaphunzitsa kugwira ntchito mwakhama. Kwa ena, lamulo limeneli linkawalimbikitsa kukhala owolowa manja ndiponso kukhulupirira kuti Mulungu awadalitsa.​—2/1, tsamba 15.

• N’chifukwa chiyani Yehova anakana Mfumu Sauli?

Sauli anafunika kuyembekezera mneneri wa Mulungu kuti adzapereke nsembe, koma mfumuyi sinamvere. M’malomwake, Sauli anapereka yekha nsembeyo. Pa nthawi inanso, iye sanamvere lamulo loti aononge Aamaleki onse omwe anali adani awo.​—2/15, tsamba 22-23.

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadana ndi kusamvera malamulo?

Tingasonyeze zimenezi mwa kupewa kukhala akapolo a mowa, kupewa zamizimu ndiponso kumvera chenjezo la Yesu pa nkhani ya chiwerewere. Mwachitsanzo, tiyenera kupewa kuonera zinthu zolaula ndiponso kuganizira zinthu zimenezi. (Mat. 5:27, 28) Komanso tiyenera kupewa kucheza ndi anthu amene achotsedwa mu mpingo.​—2/15, tsamba 29-32.

• Kodi n’chifukwa chiyani zili zochititsa chidwi kuti posachedwapa akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza ming’oma ku Israel?

Ofukula zinthu zakale anapeza ming’oma yoposa 30 ku Israel, ndipo akatswiri ena akuganiza kuti mwina pa chaka ankafula uchi wokwana makilogalamu pafupifupi 500 m’ming’oma imeneyi. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ankachita ulimi wa njuchi m’dziko limene Mulungu ananena kuti lidzakhala “loyenda mkaka ndi uchi.” (Eks. 3:8)​—3/1, tsamba 15.

• Kodi Yeremiya anali ngati mtengo “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi” m’njira ziti? (Yer. 17:7, 8)

Yeremiya sanasiye kubala zipatso ndipo sanalole kufooketsedwa ndi anthu amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa madzi opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Mulungu anamuuza.​—3/15, tsamba 14.

• Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza Malita kuti zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi? (Luka 10:41, 42)

Iye sankatanthauza kuti Malita ankakondetsa zinthu zakuthupi pamene anaphika chakudya chamitundumitundu. Yesu sanalinso kunyoza khama lake pa ntchito. Iye ankangomuthandiza kuti adziwe zinthu zofunika kwambiri. Malita sanali kugwiritsa ntchito mwayi wapadera wolimbitsa chikhulupiriro chake.​—4/1, tsamba 12-13.

• Kodi ndi zinthu ziti zotsutsana ndi malamulo zimene zinachitika pozenga mlandu wa Yesu?

Bwalo la milandu silinalole kumvetsera zifukwa zomumasulira. Anagwiritsa ntchito mboni zabodza. Mlanduwo unazengedwa usiku. Anayamba kuzenga mlandu n’kuumaliza tsiku lomwelo.​—4/1, tsamba 20.