Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulosi Woyamba: Zivomezi

Ulosi Woyamba: Zivomezi

Ulosi Woyamba: Zivomezi

“Kudzachitika zivomezi zamphamvu.”​—LUKA 21:11.

● Mwana wina wa chaka chimodzi ndi miyezi inayi dzina lake Winnie, anapulumuka nyumba itamugwera chifukwa cha chivomezi chimene chinachitika ku Haiti. Ngoziyo itachitika, atolankhani a wailesi ina ya TV anapita kumalo angoziwo ndipo anamva Winnie akulira chapansipansi. Ngakhale kuti mwanayu anapulumuka, makolo ake anafa pa ngoziyi.

KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Chivomezi champhamvu zokwana 7.0 chitachitika ku Haiti m’mwezi wa January 2010, anthu oposa 300,000 anaphedwa. Mu kanthawi kochepa kameneka, nyumba za anthu ena okwana 1.3 miliyoni zinagwa ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthuwa asowe pokhala. Komatu ngakhale kuti chivomezi cha ku Haiti chinali champhamvu kwambiri, m’mayiko enanso munachitika zivomezi zina zambiri. Mwachitsanzo, kuyambira mu April 2009 mpaka mu April 2010 panachitika zivomezi zikuluzikulu zosachepera 18 m’malo osiyanasiyana padziko lapansi.

KODI AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Sikuti padzikoli pakuchitika zivomezi zambiri kuposa kale, kungoti masiku ano kuli zipangizo zamakono zimene zikuchititsa kuti tizidziwa zambiri zokhudza zivomezi kusiyana ndi kale.

KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Taganizirani mfundo iyi: Baibulo silinena kuti m’masiku otsiriza ano padzikoli pachitika zivomezi zingati. Koma limanena kuti “zivomezi zamphamvu” zidzachitika “m’malo osiyanasiyana.” Zimenezi zachititsa kuti zivomezi zikhale chimodzi mwa zinthu zodziwika bwino zimene zikuchitika padzikoli.​—Maliko 13:8; Luka 21:11.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi masiku ano padzikoli sipakuchitika zivomezi zamphamvu ngati mmene Baibulo linaloserera?

Ena angaone kuti zivomezi pazokha sizingakhale umboni wokwanira wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Komabe zivomezi ndi umodzi wa maulosi amene akukwaniritsidwa. Taonaninso ulosi wachiwiri.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Ifeyo [asayansi] timazitchula kuti zivomezi zamphamvu koma anthu ena onse amati ndi masoka oopsa achilengedwe.”​—KEN HUDNUT, WA M’BUNGWE LA KU AMERICA LOONA ZA NTHAKA NDI MIYALA.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

© William Daniels/​Panos Pictures