Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulosi Wachiwiri: Njala

Ulosi Wachiwiri: Njala

Ulosi Wachiwiri: Njala

“Kudzakhala njala.”​—MALIKO 13:8.

● Munthu wina anathawira m’mudzi wina wotchedwa Quaratadji m’dziko la Niger. Abale ake enanso a munthuyu anafika m’mudzi womwewu kudzafuna chakudya kuchokera m’madera ena a dzikoli. Koma munthuyu anapezeka atagona yekhayekha pamphasa. Kodi n’chifukwa chiyani anali yekha? Amfumu a m’mudzimo dzina lawo a Sidi, ananena kuti: “Munthuyu sakufuna kukhala ndi [banja lake] chifukwa akulephera kulidyetsa choncho zimukumumvetsa chisoni kuti azingowayang’ana anthu a m’banja lakewo akufa ndi njala.”

KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Padziko lonse, pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 7 aliwonse, tsiku lililonse sadya chakudya chokwanira. Vutoli ndi lalikulu kwambiri ku Africa kuno makamaka m’mayiko a kum’mwera kwa chipululu cha Sahara kumene munthu mmodzi pa atatu alionse amagona ndi njala tsiku lililonse. Kuti timvetse zimenezi, tiyerekeze kuti pali banja limene muli bambo, mayi ndi mwana. Ndiye ngati chakudya chomwe chilipo n’chongokwana anthu awiri basi, kodi amene akuyenera kukhala ndi njala ndani? Kodi ndi bambo, mayi kapena mwana? Mabanja ambiri tsiku ndi tsiku amafunika kusankha zochita pa nkhani ngati imeneyi.

KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? M’dzikoli anthu amakolola chakudya chambiri choti chingakwanire wina aliyense chinanso n’kutsala. Chongofunika n’kuonetsetsa kuti sitikuwononga zinthu zachilengedwe.

KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Zoti alimi masiku ano akukolola chakudya chambiri komanso akutumiza chakudya m’madera osiyanasiyana padziko lapansi kuposa mmene zinalili kale ndi zoona. Ndipo zimenezi zinayenera kuchititsa kuti mayiko athetse vuto la njala padzikoli. Komabe ngakhale kuti patha zaka zambiri mayiko akuyesetsa kuti njala ithe, njala sikutha.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi pamenepa sitinganene kuti lemba la Maliko 13:8 likukwaniritsidwa? Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo, kodi sizoona kuti anthu akuvutikabe ndi njala padziko lonse?

Nthawi zambiri zivomezi ndiponso njala zimayambitsanso mavuto ena, ndipo mavuto amenewa ndi mbali inanso ya chizindikiro cha masiku otsiriza.

[Chithunzi patsamba 5]

“Pa ana amene amamwalira ndi matenda a chibayo, kutsegula m’mimba ndiponso matenda ena, pafupifupi hafu ya anawa akhoza kuchira atakhala kuti amadya chakudya chokwanira ndiponso chopatsa thanzi.”​—ANN M. VENEMAN, YEMWE ANALI MKULU WA BUNGWE LOONA ZA ANA PADZIKO LONSE.

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

© Paul Lowe/​Panos Pictures