Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulosi Wachitatu: Matenda

Ulosi Wachitatu: Matenda

Ulosi Wachitatu: Matenda

“Kudzakhala miliri.”​—LUKA 21:11.

● Munthu wina dzina lake Bonzali, anali dokotala pachipatala china m’dziko lina la ku Africa kuno limene munkachitika nkhondo yapachiweniweni. Iye anayesetsa kuti apulumutse anthu ogwira ntchito mu mgodi wina amene ankadwala matenda otchedwa Marburg. * Bonzali anayesetsa kupempha thandizo kwa akuluakulu a m’zipatala za mumzinda wina waukulu koma sanamuthandize. Kenako patatha miyezi inayi, akuluakulu aja anapereka thandizo limene Bonzali anapempha koma pa nthawiyi iye anali atamwalira. Bonzali anamwalira ndi matenda a Marburg amene anawatenga pomwe ankayesetsa kuthandiza anthu ogwira ntchito mu mgodi aja.

KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Matenda a chibayo, kutsegula m’mimba, Edzi, TB ndi malungo ndi ena mwa matenda amene akupha anthu ambiri. Posachedwapa, matenda amenewa anapha pafupifupi anthu 10.7 miliyoni chaka chimodzi. M’mawu ena tingati pa masekondi atatu alionse, munthu mmodzi ankamwalira ndi matendawa, m’chaka chimenecho.

KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Chiwerengero cha anthu chikuchuluka tsiku lililonse. Zimenezi zingapangitse kuti anthu ambiri azipatsirana matenda. Choncho n’zosadabwitsa kuti padzikoli pali matenda osiyanasiyana.

KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Zoti chiwerengero cha anthu padzikoli chikuwonjezeka n’zoona. Koma tisaiwale kuti anthu masiku ano apeza njira zambiri zodziwira, zopewera ndiponso kuchizira matenda. Ndiyeno kodi zimenezi sizikanapangitsa kuti matenda achepe? Koma m’malo moti matenda achepe, akungowonjezereka.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi si zoona kuti anthu akuvutika ndi matenda oopsa mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera?

Zivomezi, njala ndiponso matenda, ndi mavuto oopsa amene akuvutitsa kwambiri anthu masiku ano. Koma palinso anthu ena ambiri amene akuchitiridwa nkhanza ndi anthu anzawo ndipo ambiri mwa anthu amenewa amachitiridwa nkhanza ndi anthu amene anayenera kuwateteza. Taonani zimene ulosi wina wa m’Baibulo unanena kuti zidzachitika.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Matenda a Marburg Hemorrhagic Fever amayamba ndi kachilombo kofanana ndi kamene kamayambitsa matenda a Ebola.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“N’zoopsa kwambiri kudyedwa ndi mkango kapena chilombo china cholusa, koma n’zoopsanso kwambiri kudyedwa ndi kachilombo koyambitsa matenda, n’kumaona matendawo akufalikira thupi lako lonse.”​—MICHAEL OSTERHOLM, KATSWIRI WOFUFUZA ZA MILIRI.

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

© William Daniels/​Panos Pictures