Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Posachedwapa Zinthu Padzikoli Zikhala Bwino

Posachedwapa Zinthu Padzikoli Zikhala Bwino

Posachedwapa Zinthu Padzikoli Zikhala Bwino

“Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—SALIMO 37:10, 11.

N’ZOSAKAYIKITSA kuti mungafune kudzaona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa ndipo pali zifukwa zabwino zotipangitsa kukhulupirira kuti zimenezi zichitikadi posachedwapa.

Mu nkhani zapitazi, takambirana ena mwa maulosi a m’Baibulo amene akusonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Mulungu anauzira anthu ena amene analemba Baibulo kuneneratu kuti zinthu zimenezi zidzachitika. Iye anachita zimenezi n’cholinga chakuti ifeyo tiziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Aroma 15:4) Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kukutanthauza kuti mavuto amene tikukumana nawowa atha posachedwa.

Kodi n’chiyani chidzachitika pambuyo pa masiku otsiriza ano? Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira anthu onse. (Mateyu 6:9) Taonani zimene Baibulo limanena za mmene zinthu zidzakhalire pa dziko lapansi pa nthawi imeneyo.

Sikudzakhalanso njala. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

Sikudzakhala matenda. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”​—Yesaya 33:24.

Dziko lapansili lidzakonzedwanso. “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”​—Yesaya 35:1.

Amenewa ndi ochepa mwa maulosi a m’Baibulo amene atsala pang’ono kukwaniritsidwa. Mungachite bwino kufunsa a Mboni za Yehova kuti akuuzeni chifukwa chake iwo amakhulupirira kuti posachedwapa zinthu padzikoli zikhala bwino.