Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

Yandikirani Mulungu

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

TAONANI chithunzi chimene chili patsamba lino. Kodi mukuganiza kuti kamwana ka nkhosako kakumva bwanji, ndi mmene m’busayo wakanyamulira pa chifuwa chake? Mu Salimo nambala 23, Baibulo limayerekezera mmene m’busa amasamalirira nkhosa zake ndi mmene Yehova amasamalirira atumiki ake mwachikondi. Yehova amafuna kuti ifenso tiziona kuti angatiteteze ngati mmene anachitira ndi Davide. Iye ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo ananena kuti: “Yehova ndi M’busa wanga.” *​—Vesi 1.

Amene analemba salimo limeneli ndi Davide ndipo iye ali mnyamata anali m’busa. Choncho iye ankadziwa zimene nkhosa zimafunikira komanso udindo umene m’busa amakhala nawo. Davide ankakhulupirira kuti Mulungu amamukonda ndipo ena amati salimo limeneli ndi “salimo la chikhulupiriro.” Dzina la Mulungu lakuti Yehova likupezeka koyambirira ndi kumapeto kwa salimo limeneli. (Vesi 1 ndi 6) Salimo limeneli likufotokoza njira zitatu zimene Yehova amasamalirira anthu ake monga mmene m’busa amasamalirira nkhosa zake.​—Salimo 100:3.

Yehova amatsogolera nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimasochera. N’chimodzimodzinso anthufe, pa moyo wathu timafunika wotitsogolera. (Yeremiya 10:23) Davide anafotokoza kuti Yehova amatsogolera anthu ake “m’mabusa a msipu wambiri,” ndi “m’malo opumira a madzi ambiri.” Amawatsogoleranso “m’tinjira tachilungamo.” (Vesi 2 ndi 3) Zimene Yehova amachitazi zikufanana ndi zimene m’busa amachita posamalira nkhosa zake ndipo zikutitsimikizira kuti tiyenera kumukhulupirira. Tikamatsatira malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo, tingakhale ndi moyo wokhutira, wosangalala ndiponso tingakhale ndi tsogolo labwino.

Yehova amateteza nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimachita mantha komanso zimasowa wozithandiza. Yehova amauza anthu ake kuti asachite mantha ngakhale ‘poyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani.’ Imeneyi ingakhale nthawi imene munthu amaona kuti ali pa mavuto adzaoneni. (Vesi 4) Pa nthawi imeneyi Yehova amaona zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo amakhala wokonzeka kuwathandiza. Iye amapatsa atumiki ake nzeru ndi mphamvu kuti athe kupirira mayesero awo.​—Afilipi 4:13; Yakobo 1:2-5.

Yehova amadyetsa nkhosa zake. Nkhosa zimadalira m’busa wawo kuti azipezere chakudya. Anthufe tili ndi zosowa zauzimu zimene Mulungu yekha ndi amene angatithandize kuti tizipeze. (Mateyu 5:3) Tikuyamikira kuti Yehova ndi Wowolowa manja ndipo amapatsa atumiki ake chakudya chauzimu chambiri. (Vesi 5) Tikamawerenga zinthu monga Baibulo komanso mabuku othandiza anthu kuphunzira Baibulo, ngati Nsanja ya Olonda imene mukuwerengayi, timapeza chakudya chauzimu chimene chimatithandiza kudziwa cholinga cha moyo komanso zimene Mulungu akufuna kudzatichitira.

Davide sankachita mantha chifukwa ankadziwa kuti ngati angakhalebe pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi M’busa wake, Yehovayo adzamusamalira mwachikondi “masiku onse a moyo [wake].” (Vesi 6) Kodi inunso mumafuna kuti muzikhala opanda mantha? Ngati ndi choncho, phunzirani zimene mungachite kuti muyandikire Yehova. Zimenezi zidzakuthandizani kuona kuti ndinu otetezeka m’manja mwa M’busa Wamkulu yemwe amatsogolera, kuteteza ndiponso kudyetsa anthu amene amakhalabe okhulupirika kwa iye.​—Yesaya 40:11.

Mavesi amene mungawerenge mu May:

Yobu chaputala 38-42 mpaka Salimo 1-25

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 M’Mabaibulo ena palembali pamati: “AMBUYE ndi M’busa wanga.” Kuti mudziwe chifukwa chake Mabaibulo ena anachotsa dzina la Mulungu lakuti Yehova, werengani tsamba 195 mpaka 197 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.