Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yabwino kwa Osauka

Nkhani Yabwino kwa Osauka

Nkhani Yabwino kwa Osauka

MAWU A MULUNGU amalimbikitsa anthu osauka kuti: “Waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse.” (Salimo 9:18) Komanso amanena za Mlengi wathu, kuti: “Mumatambasula dzanja lanu ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.” (Salimo 145:16) Mawu olimbikitsa amenewa si nkhambakamwa chabe. Mulungu Wamphamvuyonse adzachita zonse zimene zingathandize kuti umphawi uthe. Koma kodi chikufunika n’chiyani kuti umphawi uthe?

Katswiri wina wazachuma ku Africa kuno ananena kuti kwenikweni chimene mayiko osauka akufunikira ndi “mtsogoleri wamphamvu komanso wachifundo.” Apa mfundo ndi yakuti, umphawi ungathe ngati titamalamulidwa ndi munthu yemwe ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu komanso amene angachitire chifundo anthu osauka. Tinganenenso kuti, munthu amene angathetsedi umphawi wa wina aliyense ayenera kukhala mtsogoleri wa dziko lonse lapansi. Tikutero chifukwa kusiyana kumene kulipo pakati pa mayiko olemera ndi osauka ndi kumene kumapangitsa kuti anthu ena azivutika kwambiri ndi umphawi. Komanso, wolamulira amene angathetse umphawi ayenera kukhala yemwe angachotse chimene chimayambitsa umphawiwo, chomwe ndi mtima wodzikonda. Kodi wolamulira wotereyu tingam’peze kuti?

Mulungu anatumiza Yesu kuti adzauze anthu osauka uthenga wabwino. Pa nthawi ina Yesu anawerengera anthu malemba okhudza ntchito imene Mulungu anamupatsa. Iye ananena kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka.”​—Luka 4:16-18.

Kodi Uthenga Wabwino Umanena za Chiyani?

Mulungu anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ndipo imeneyi ndi nkhani yabwino. Yesu ndi Wolamulira amene angathetsedi umphawi chifukwa (1) adzalamulira anthu onse ndipo ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu; (2) amachitira chifundo anthu osauka ndipo anaphunzitsanso otsatira ake kuti azichita chimodzimodzi; komanso (3) angathe kuchotsa chimene chimayambitsa umphawi chomwe ndi mtima wodzikonda umene anthufe timabadwa nawo. Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zitatu zimenezi.

1. Yesu ali ndi mphamvu zolamulira padziko lonse Ponena za Yesu Mawu a Mulungu amati: “Anamupatsa ulamuliro . . . kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.” (Danieli 7:14) Tangoganizani mmene zinthu zingakhalire bwino ngati padziko lonseli patakhala wolamulira mmodzi. Sipangapezekenso anthu okanganirana zinthu zachilengedwe zimene zili padzikoli ndipo zinthu zimene zili padzikoli zingamapindulitse anthu mofanana. Yesu anatsimikizira otsatira ake kuti iye adzakhala Wolamulira wa dziko lonse ndipo ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu. Iye anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”​—Mateyu 28:18.

2. Yesu amachitira chifundo anthu osauka Pa nthawi yonse imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi, anachitira chifundo anthu osauka. Mwachitsanzo, mayi wina amene chuma chake chonse chinatha chifukwa cholipirira matenda ake, anagwira malaya a Yesu ndi chikhulupiriro chakuti achira. Mayiyu anali atatha zaka 12 akudwala nthenda yotaya magazi ndipo zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi vuto losowa magazi. Malinga ndi Chilamulo, aliyense amene akanakhudza mayiyu nayenso akanakhala wodetsedwa. Koma Yesu anamukomera mtima mayiyu ndipo anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”​—Maliko 5:25-34.

Zimene Yesu anaphunzitsa zingathandize kuti anthu asinthe n’kuyamba kuchitira anthu anzawo chifundo. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu anayankha munthu wina atamufunsa zimene angachite kuti azikondweretsa Mulungu. Munthu ameneyu ankadziwa kuti Mulungu amafuna kuti tizikonda anthu anzathu, koma anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?”

Poyankha, Yesu ananena fanizo lomwe ndi lotchuka kwambiri lonena za munthu amene anali paulendo wochokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anakumana ndi achifwamba amene anamumenya koopsa “n’kumusiya ali pafupi kufa.” Ndiyeno wansembe wina ankayenda mumsewu womwewo koma atamuona anangomulambalala. Mlevi winanso atamuona, anachita chimodzimodzi. “Koma panafika Msamariya wina amene anali kudutsanso msewu umenewo. Ndipo atamuona, anagwidwa chifundo.” Iye anatsuka mabala a munthuyo n’kupita naye kunyumba ya alendo ndipo analipira mwini nyumba ya alendoyo kuti asamalire munthu wovulalayo. Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Ndani . . . amene iweyo ukuona kuti anakonda munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” Munthu uja anayankha kuti: “Ndi amene anam’chitira chifundoyo.” Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”​—Luka 10:25-37.

Anthu amene aphunzira Baibulo n’kukhala a Mboni za Yehova amaphunzira zinthu ngati zimenezi, zimene Yesu anaphunzitsa. Iwo akaphunzira amasintha n’kuyamba kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza anthu osowa. Mwachitsanzo, mayi wina wolemba mabuku wa ku Latvia analemba m’buku lake lina (Women in Soviet Prisons) zimene zinamuchitikira akudwala pamene anali kundende ya ku Potma, m’zaka za m’ma 1960. Iye anati: “Pa nthawi yonse imene ndinkadwala [a Mboni] anandisamalira bwino kwambiri. Palibe chithandizo chimene ndikanalandira choposa chimenechi.” Iye ananenanso kuti: “A Mboni za Yehova amaona kuti ndi udindo wawo kuthandiza aliyense mosaganizira chipembedzo kapena dziko limene munthuyo amachokera.”

Pa nthawi imene dziko la Ecuador linali pa mavuto azachuma, a Mboni za Yehova ambiri a mumzinda wa Ancón ankavutika kupeza ndalama ndipo ena ntchito inawathera. Zimenezi zitachitika, a Mboni za Yehova anzawo anaganiza zomaphika chakudya n’kumagulitsa n’cholinga chakuti apeze ndalama kuti awathandize. Iwo ankagulitsa chakudyacho kwa asodzi akamachokera kopha nsomba (onani chithunzi chili kumanja). Anthu onse mumpingo, ndi ana omwe, anathandiza nawo pa ntchitoyi. Anthuwa ankadzuka 1 koloko usiku n’cholinga chakuti maboti akamabwera cha m’ma 4 koloko m’mawa akhale atamaliza kuphika chakudya. Ndalama zimene a Mboni amenewa anapeza anazigawa kwa anthu ovutikawo mogwirizana ndi zosowa za aliyense.

Zimene a Mboni za Yehova anachitazi zikusonyeza kuti kutsatira zimene Yesu ankachita komanso zimene ankaphunzitsa kungathandize anthu kusintha n’kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza osowa.

3. Yesu ali ndi mphamvu zotha kusintha khalidwe la anthu Palibe aliyense amene angakane kuti anthufe tili ndi mtima wodzikonda ndipo mtima umenewu timachita kubadwa nawo. Baibulo limati mtima wodzikonda ndi tchimo. Ngakhalenso mtumwi Paulo anachita kunena kuti: “Ndimapeza lamulo ili lakuti: Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi? Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu.” (Aroma 7:21-25) Pamenepa Paulo anatchula zimene Mulungu adzachite kudzera mwa Yesu n’cholinga chofuna kupulumutsa olambira oona ku uchimo umene amabadwa nawo. Umodzi mwa uchimo umenewu ndi kudzikonda ndipo kudzikonda ndi kumene kumayambitsa umphawi. Kodi Mulungu adzapulumutsa bwanji anthu ku uchimo?

Patapita nthawi Yesu atabatizidwa, Yohane M’batizi anauza anthu za Yesu kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!” (Yohane 1:29) Posachedwapa padziko lapansili padzakhala anthu amene adzamasulidwe ku uchimo wobadwa nawo, kuphatikizapo kudzikonda. (Yesaya 11:9) Pamenepo Yesu adzakhala atathetsa umphawi.

Timasangalala kwambiri tikamaganiza za nthawi imene aliyense sadzasowa chilichonse pa moyo wake. Mawu a Mulungu amati: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:4) Mawu amenewa akufotokoza mmene anthu adzasangalalire umphawi ukadzatha pamene anthu onse adzakhale ndi ntchito yabwino ndiponso sazidzaopa chilichonse. Zimenezi zidzachititsa kuti Yehova atamandidwe.