Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinkangomva Ngati Akuimba Kanyimbo Kosangalatsa

Ndinkangomva Ngati Akuimba Kanyimbo Kosangalatsa

Kalata Yochokera ku Madagascar

Ndinkangomva Ngati Akuimba Kanyimbo Kosangalatsa

INE ndi mwamuna wanga tinatumizidwa kuchilumba cha Madagascar kuti tikatumikire monga amishonale. Tinatsazikana ndi achibale athu ndi anzathu ndipo tinalimba mtima komanso tinkakhulupirira kuti Yehova akatisamalira kulikonse kumene iye angafune kuti tikatumikire.

Sitidzaiwala tsiku lathu loyamba kusonkhana ndi mpingo watsopano kudera limene anatitumizali. M’bale amene ankachititsa phunziro la Nsanja ya Olonda ankangokhala ngati akutsogolera gulu la anthu kuimba nyimbo. Chifukwa chakuti Chimalagase chinkativuta kumva, munthu akamalankhula tinkangomva ngati akuimba kanyimbo kosangalatsa. Zinatitengera nthawi kuti tiyambe kumvetsa zimene akulankhula.

Tsiku limene ndinasonyeza kuti ndayamba kumvetsa chinenero chawo ndi pa phunziro la Nsanja ya Olonda. Pamene wochititsa anafunsa funso lowonjezera, ndinangopezeka kuti ndayankha mokweza mawu. Anthu amene anakhala nafe pafupi anamva zimene ndinayankhazo moti ndinachita kudzigwira pakamwa kuti ndisamveke kuseka. Ndinachita manyazi, komabe ndinasangalala kuti ndinamva zimene zinanenedwazo.

M’malo moti ndikhale chitsanzo chabwino kwa ena muutumiki, ndinkaona kuti ineyo ndi amene ndikuthandizidwa. Mwachikondi, abale ndi alongo ankandithandiza kukonzekera mmene ndingakalankhulire zomveka mu utumiki komanso malemba amene ndingakawerenge.

Ndikukumbukira kuti tsiku lina ndili muutumiki mwana wina anakuwa kuti: “Vazaha! Vazaha!” Mawu amenewa ndi odziwika bwino m’Chimalagase ndipo amatanthauza munthu wochokera kudziko lina. Titamva zimenezi tinayamba kuyenda mofulumira poopa kuti mwina ana enanso angayambe kukuwa chimodzimodzi. Koma mnyamata wina anakalipira mwanayo ndipo anamuuza kuti: “Amenewatu ndi a konkuno ndipo amatha kulankhula chinenero chathu.” Mlongo amene ndinayenda naye ndi amene anachita kundimasulira zimene anawa ankanena chifukwa ankalankhula mofulumira moti sindinkamva chilichonse. Komabe ndinkaona kuti pang’onopang’ono, ndayamba kudziwa Chimalagase. M’kupita kwa nthawi, ku Madagascar tinayamba kukuzolowera.

Nthawi zambiri ndinkati ndikayamba kusungulumwa, ndinkangoona kamwana kabwera n’kundigwira dzanja, kwinaku kakumwetulira. Zikatere ndinkamvako bwino mumtima poona kuti ana akufuna kuti ndizicheza nawo ngakhale kuti sindinkatha kulankhula nawo bwinobwino chinenerochi. Kukhala ndi ana oterewa mu mpingo ndi dalitso lalikulu lochokera kwa Yehova. Kamtsikana kena dzina lake Hasina ndi kamene kamandithandiza kwambiri pomasulira zimene anthu akunena komanso zimene ineyo ndikutanthauza. Nthawi zina anthu onse amalephera kumvetsa zimene ndikutanthauza koma Hasina amaoneka kuti akumva. Komanso tikamacheza, alongo ena samvetsa zimene ndikunena. Zikatere, Hasina amawafotokozera zimene ndikutanthauza.

Mpingo umene ine ndi mwamuna wanga tinafikira, unkafunika kugawidwa. Zimenezi zinatanthauza kuti anthu amene ankaphunzira Baibulo, anafunika apatsidwe kwa anthu a m’gawo limene ophunzirawo anali. Mlongo wina anandipempha kuti ndiziphunzira ndi munthu amene ankaphunzira naye. Ndinachita mantha ndipo ndinamuuza kuti sindinafike poti n’kumachititsa phunziro koma iye analimbikirabe kundiuza kuti ndizichititsa phunzirolo. Ananditsimikizira kuti Yehova andithandiza ndipo zonse ziyenda bwino. Mlongoyu anandiuza kuti posachedwa ndizidzatha kuphunzitsa anthu mmene ndimafunira. Iye anandiuza zimenezi akundiyang’ana mwachifundo ndipo ankayesetsa kulankhula nane m’njira yosavuta kumva. Mawu akewo anandilimbikitsa kwambiri.

Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzira Baibulo ameneyu wapita patsogolo mwauzimu. Tsiku lina ndili panja ndinamumva akundiitana. Pa nthawiyi iye ndi mwamuna wake n’kuti akupita kukalembetsa ukwati wawo ku boma. Mwamuna wake wayambanso kuphunzira ndipo onse ali ndi zolinga zauzimu zimene akufuna kuzikwaniritsa. Chimodzi mwa zolinga zimenezi ndi kubatizidwa. Ndinanyadira kwambiri ngakhale ndikudziwa kuti Yehova ndi amene amakoka anthu kuti abwere m’gulu lake.

Pali zinthu zambiri zimene taphunzira ku Madagascar kuno. Ngakhale kuti timasowa achibale ndi mabwenzi athu, timamvabe ngati tili nawo konkuno. Nthawi zambiri timakonda kuuza abale ndi alongo athu a kuno nkhani zokhudza anzathu ndiponso achibale athu moti panopa iwo amatifunsa mmene anthu amenewa alili komanso zambiri za iwo. Tikuyembekezera nthawi imene achibale athu adzakumane ndi abale athu auzimu amene tawapeza kuno.

Anthu akamalankhula ndimamvabe ngati akuimba kanyimbo kosangalatsa kungoti masiku ano ndimamva zimene akulankhulazo. Ndikudziwa kuti m’tsogolomu ndizidzatha kulankhula bwinobwino ndi anthu achinenero chimenechi osati kumangolankhula mwa apa ndi apo chifukwa chosadziwa bwino chinenero chawo. Yesu anati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.” (Mateyu 6:34) Choncho tipitirizabe kuphunzira pang’onopang’ono, mawu amodzi pa nthawi imodzi mpaka tidzachidziwe bwino chinenerochi. Panopa, ndikuyesetsa kumamvetsera kwambiri anthu akamalankhula komanso ndikuyesetsa kuti ndiziganiza ngati mmene iwo amaganizira. Ndikuchita zimenezi n’cholinga chakuti ndizitha kutumikira bwino ndi abale ndi alongo athu oleza mtima ndiponso achikondi a ku Madagascar amenewa.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndikulalikira ndi Hasina