Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali Uthenga Wabwino Wofunika Kuti Anthu Onse Amve

Pali Uthenga Wabwino Wofunika Kuti Anthu Onse Amve

Pali Uthenga Wabwino Wofunika Kuti Anthu Onse Amve

“Uthenga wabwino . . . ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka.”​—AROMA 1:16.

1, 2. N’chifukwa chiyani mumalalikira “uthenga wabwino wa ufumu,” ndipo ndi mbali ziti za uthengawu zimene mumatsindika?

KODI mumakonda kulalikira uthenga wabwino tsiku lililonse? Popeza ndinu Mboni yodzipereka ya Yehova, mukudziwa kufunika kolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu.” Mwina munaloweza mawu amene Yesu ananena pa ulosi wake wonena za kulalikira uthengawu.​—Mat. 24:14.

2 Pamene mukulalikira “uthenga wabwino wa ufumu” ndiye kuti mukupitiriza zimene Yesu anali kuchita. (Werengani Luka 4:43.) N’zosachita kufunsa kuti mfundo ina imene mumaitsindika polalikira ndi yakuti posachedwapa Mulungu adzalowerera pa zochitika za m’dzikoli. Pa “chisautso chachikulu” iye adzawononga chipembedzo chonyenga ndiponso anthu onse oipa. (Mat. 24:21) Muyenera kuti mumatsindikanso kuti Ufumu wa Mulungu udzabwezeretsa Paradaiso padzikoli n’cholinga choti pakhale mtendere ndi chimwemwe. Ndipotu “uthenga wabwino wa ufumu” ndi mbali ya “uthenga wabwino [womwe Mulungu analengezeratu] kwa Abulahamu, kuti: ‘Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.’”​—Agal. 3:8.

3. N’chiyani chikusonyeza kuti mtumwi Paulo anatsindika za uthenga wabwino m’buku la Aroma?

3 N’kutheka kuti sitiganizira kwambiri mbali ina ya uthenga wabwino yomwe ndi yofunika kwambiri kuti anthu amve. M’kalata yake yopita kwa Aroma imene anailemba m’Chigiriki, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti “Ufumu” kamodzi kokha, koma anagwiritsa ntchito mawu oti “uthenga wabwino” maulendo 12. (Werengani Aroma 14:17.) Kodi ndi mbali iti ya uthenga wabwino imene Paulo anaitchula mobwerezabwereza m’buku limeneli? N’chifukwa chiyani mbali imeneyi ya uthenga wabwino ili yofunika kwambiri? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira zimenezi polalikira “uthenga wabwino wa Mulungu” kwa anthu m’gawo lathu?​—Maliko 1:14; Aroma 15:16; 1 Ates. 2:2.

Zimene Anthu ku Roma Ankafunikira

4. Kodi Paulo analalikira za chiyani pa nthawi imene anamangidwa koyamba ku Roma?

4 Tikhoza kuphunzira zambiri pa nkhani zimene Paulo anatchula pa nthawi imene anamangidwa koyamba ku Roma. Timawerenga kuti Ayuda ambiri atabwera kumene iye ankakhala, ‘anawachitira umboni mokwanira za (1) ufumu wa Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza (2) Yesu.’ Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Ena anayamba kukhulupirira zimene ananenazo, koma ena sanakhulupirire.” Kenako Paulo ‘ankalandira ndi manja awiri anthu onse obwera kudzamuona ndipo anali kuwalalikira za (1) ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za (2) Ambuye Yesu Khristu.’ (Mac. 28:17, 23-31) Zikuonekeratu kuti Paulo ankalankhula kwambiri za Ufumu wa Mulungu. Koma iye anatsindikanso chinthu china chofunika kwambiri chokhudza Ufumu umenewu. Iye anatsindika udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.

5. Kodi m’buku la Aroma Paulo anasonyeza kuti anthu anafunika kudziwa chiyani?

5 Anthu onse afunika kudziwa Yesu ndiponso kumukhulupirira ndipo Paulo anasonyeza zimenezi m’buku la Aroma. Poyamba iye anatchula za mfundo imeneyi pamene analemba za Mulungu kuti “ndikumuchitira utumiki wopatulika ndi moyo wanga wonse polalikira uthenga wabwino wonena za Mwana wake.” Kenako anawonjezeranso kuti: “Pakuti sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro.” Pambuyo pake ananena kuti pali ‘tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze zinthu zobisika za anthu, mogwirizana ndi uthenga wabwino umene akulengeza.’ Ndiyeno ananena kuti: “Ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu kuyambira ku Yerusalemu, kuzungulira mpaka ku Iluriko.” * (Aroma 1:9, 16; 2:16; 15:19) N’chifukwa chiyani Paulo anatsindika za Yesu Khristu m’kalata yake yopita kwa Aroma?

6, 7. Kodi tikudziwa chiyani za kuyamba kwa mpingo wa Aroma ndiponso za anthu amene anali mu mpingowo?

6 Sitikudziwa mmene mpingo wa Aroma unayambira. Mwina Ayuda kapena anthu otembenukira ku Chiyuda amene analipo pa Pentekosite mu 33 C.E., anabwerera ku Roma ali Akhristu. (Mac. 2:10) Apo ayi, mwina Akhristu amene ankachita malonda ndiponso amene ankayendayenda ndi omwe anafalitsa choonadi ku Roma. Kaya zinthu zinali bwanji, pa nthawi imene Paulo ankalemba kalatayi mu 56 C.E., mpingowu unali utakhazikitsidwa kale. (Aroma 1:8) Kodi mu mpingo wa Aroma munali anthu otani?

7 Anthu ena anali achiyuda. Popereka moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, Paulo anawatchula kuti “achibale anga.” Choncho zikuoneka kuti iwo anali Ayuda anzake. Akula, yemwe ankakhala ku Roma limodzi ndi mkazi wake Purisikila, nayenso anali Myuda. (Aroma 4:1; 9:3, 4; 16:3, 7; Mac. 18:2) Koma abale ndi alongo ambiri amene Paulo anawapatsa moni m’kalata yake ayenera kuti anali a mitundu ina. N’kutheka kuti ena anali “a m’nyumba ya Kaisara,” kutanthauza kuti mwina anali akapolo kapena anthu ogwira ntchito kwa Kaisara.​—Afil. 4:22; Aroma 1:6; 11:13.

8. Kodi anthu a ku Roma anali ndi vuto lotani?

8 Mkhristu aliyense ku Roma anali ndi vuto. N’chimodzimodzi ndi ife masiku ano. Paulo anatchula vutolo ponena kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) N’zoonekeratu kuti anthu onse amene Paulo anali kuwalembera kalatayi anafunikira kuzindikira kuti iwo ndi ochimwa ndiponso kukhulupirira njira imene Mulungu adzawathandizira.

Anthu Ayenera Kuzindikira Kuti Ndi Ochimwa

9. Kodi Paulo anati uthenga wabwino uli ndi mphamvu yotani?

9 Kumayambiriro kwa kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo ananena mmene uthenga wabwino, umene ankautchula mobwerezabwereza, ungathandizire anthu. Iye anati: “Sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro, choyamba kwa Myuda kenako kwa Mgiriki.” Zinali zotheka kuti anthuwo apeze chipulumutso. Koma malinga ndi mfundo ya choonadi ya pa Habakuku 2:4, anthuwo anafunikira kukhala ndi chikhulupiriro. Pogwira mawu a Habakuku, Paulo anati: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Aroma 1:16, 17; Agal. 3:11; Aheb. 10:38) Ndiyeno kodi uthenga wabwino, umene ungapulumutse anthu, ukugwirizana bwanji ndi mfundo yakuti “onse ndi ochimwa”?

10, 11. N’chifukwa chiyani mfundo ya pa Aroma 3:23 si yachilendo kwa anthu ena koma ndi yachilendo kwa ena?

10 Munthu asanayambe kukhala ndi chikhulupiriro chimene chingamuthandize kupulumuka, ayenera kuvomereza kuti ndi wochimwa. Anthu amene anakula akukhulupirira Mulungu ndiponso akudziwa zina zokhudza Baibulo, sangaone zimenezi kukhala zachilendo. (Werengani Mlaliki 7:20.) Kaya iwo amavomereza kapena amakayikira mawu a Paulo, ayenera kuti amadziwa tanthauzo la mawu akewo akuti: “Onse ndi ochimwa.” (Aroma 3:23) Koma mu utumiki tikhoza kukumana ndi anthu ambiri amene samvetsa mawu amenewa.

11 Kumayiko ena, anthu ambiri amakula osadziwa kuti ndi ochimwa kapena kuti anabadwa ndi uchimo. Komabe ayenera kuti amadziwa zoti amalakwitsa zinthu zina, ali ndi makhalidwe ena amene si abwino ndiponso kuti achitapo zinthu zina zoipa. Iwo amaonanso kuti anthu ena ali ndi vuto lomweli. Koma chifukwa cha mmene anakulira, sazindikira chimene chimachititsa zonsezi. M’zinenero zina, mukanena kuti munthu ndi wochimwa, anthu ena angaganize zoti mukunena kuti munthuyo ndi wophwanya malamulo kapenanso chigawenga. N’zodziwikiratu kuti munthu amene wakula ali ndi maganizo amenewa, sangamvetse msanga kuti ndi wochimwa ngati mmene Paulo anafotokozera.

12. N’chifukwa chiyani anthu ambiri sakhulupirira zoti anthu onse ndi ochimwa?

12 Ngakhale m’mayiko amene amati ndi achikhristu, anthu ambiri sakhulupirira zoti ndi ochimwa. N’chifukwa chiyani sakhulupirira zimenezi? Ngakhale kuti nthawi zina amapita kutchalitchi, iwo amaona kuti nkhani ya m’Baibulo yonena za Adamu ndi Hava ndi yongopeka. Ena amakulira kumalo oti anthu ambiri sakhulupirira Mulungu. Iwo amakayikira zoti kuli Mulungu choncho sadziwa kuti kuli wina wapamwamba kwambiri amene anapereka malamulo kwa anthu. Sadziwanso kuti munthu amene satsatira malamulowo amakhala wochimwa. Anthu oterewa ali ngati anthu a m’nthawi ya atumwi amene Paulo anawanena kuti ‘alibe chiyembekezo’ ndiponso kuti ‘alibe Mulungu m’dzikoli.’​—Aef. 2:12.

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu alibe zifukwa zomveka zosakhulupirira mfundo yakuti kuli Mulungu ndiponso yakuti ndi ochimwa? (b) Kodi anthu ambiri amachita chiyani chifukwa chosakhulupirira zinthu zimenezi?

13 M’kalata yopita kwa Aroma, Paulo anapereka zifukwa ziwiri zosonyeza kuti anthu oterewa alibe zifukwa zomveka zosakhulupirira kuti kuli Mulungu ndiponso kuti ndi ochimwa. N’chimodzimodzinso masiku ano. Chifukwa choyamba n’chakuti chilengedwe chimapereka umboni wakuti kuli Mlengi. (Werengani Aroma 1:19, 20.) Izi zikugwirizana ndi mawu amene Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Aheberi pa nthawi imene anali ku Roma. Iye anati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti kuli Mlengi amene anamanga, kapena kuti kulenga, zinthu zonse.

14 Choncho m’pomveka kuti Paulo analembera Aroma kuti munthu aliyense, kuphatikizapo Aisiraeli akale, amene ankalambira mafano “alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.” N’chimodzimodzi ndi anthu amene ankachita zachiwerewere m’njira yosemphana ndi chibadwa pogonana ndi amuna anzawo kapena akazi anzawo. (Aroma 1:22-27) Pa chifukwa chimenechi, Paulo ananena kuti “onse, Ayuda ndi Agiriki, ndi ochimwa.”​—Aroma 3:8, 9.

Chikumbumtima “Chimachitira Umboni”

15. Kodi anthu onse ali ndi chiyani ndipo chimawathandiza bwanji?

15 Buku la Aroma limatchulanso chifukwa china chimene chingathandize anthu kuzindikira kuti ndi ochimwa ndipo akufunika kupulumutsidwa. Ponena za malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli akale, Paulo analemba kuti: “Onse amene anachimwa ali ndi chilamulo adzaweruzidwa ndi chilamulo.” (Aroma 2:12) Ndiyeno anapitiriza kuti anthu a mitundu ina amene sadziwa malamulo a Mulungu nthawi zambiri ‘amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo.’ Mwachitsanzo, anthu amenewa nthawi zambiri amaletsa kugonana ndi wachibale, kupha munthu ndiponso kuba. Paulo ananena kuti amatero chifukwa chakuti ali ndi chikumbumtima.​Werengani Aroma 2:14, 15.

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kukhala ndi chikumbumtima sikutanthauza kuti munthu sangachimwe?

16 Ngakhale kuti tili ndi chikumbumtima chimene chimachitira umboni za uchimo, si onse amene amachitsatira. Umboni wa zimenezi ndi zimene Aisiraeli akale ankachita. Mulungu anapatsa Aisiraeli chikumbumtima ndiponso malamulo oletsa kuba komanso chigololo. Koma nthawi zambiri iwo sankatsatira chikumbumtima chawo ndiponso malamulo a Yehova. (Aroma 2:21-23) Popeza anali ndi zinthu zonse ziwiri, tinganene kuti iwo analidi ochimwa chifukwa cholephera kutsatira mfundo ndiponso chifuniro cha Mulungu. Izi zinkasokoneza kwambiri ubwenzi wawo ndi Mlengi.​—Lev. 19:11; 20:10; Aroma 3:20.

17. Kodi buku la Aroma lili ndi mfundo yolimbikitsa iti?

17 Chifukwa cha zimene takambirana m’buku la Aroma, mwina tingaone ngati n’zosatheka kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Wamphamvuyonse. Koma Paulo sanaimire pomwepo. Pogwira mawu a Davide a pa Salimo 32:1, 2, mtumwiyu analemba kuti: “Odala ndi amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo aphimbidwa. Wodala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.” (Aroma 4:7, 8) Choncho tingati Mulungu wakonza njira yokhululukira machimo yogwirizana ndi malamulo ake.

Uthenga Wabwino Wokhudza Yesu

18, 19. (a) Kodi Paulo anatsindika mbali iti ya uthenga wabwino m’buku la Aroma? (b) Kodi tiyenera kuzindikira mfundo ziti kuti tipeze madalitso amene Ufumu udzabweretse?

18 Mwina munganene kuti, “Umenewutu ndi uthenga wabwino kwambiri.” Zimenezi ndi zoona ndipo zikutikumbutsa mbali ya uthenga wabwino imene Paulo anaitsindika m’buku la Aroma. Monga tanenera kale, Paulo analemba kuti: “Sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka.”​—Aroma 1:15, 16.

19 Mfundo yaikulu mu uthenga wabwino umenewu ndi yonena za udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Paulo ankayembekezera “tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze zinthu zobisika za anthu, mogwirizana ndi uthenga wabwino.” (Aroma 2:16) Ponena zimenezi, iye sanali kupeputsa “ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu” kapena zimene Mulungu adzachite kudzera mu Ufumu umenewu. (Aef. 5:5) M’malomwake anasonyeza kuti tingakhale ndi moyo ndiponso kupeza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse ngati tizindikira kuti (1) ndife ochimwa pa maso pa Mulungu ndiponso kuti (2) tifunikira kukhulupirira Yesu Khristu kuti machimo athu akhululukidwe. Munthu akazindikira ndiponso kuvomereza mfundo zimenezi zokhudza cholinga cha Mulungu, n’kuzindikiranso kuti akhoza kukhala ndi tsogolo labwino, anganenedi kuti, “Umenewu ndi uthenga wabwino kwambiri.”

20, 21. N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira uthenga wabwino umene wafotokozedwa m’buku la Aroma tikakhala mu utumiki, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?

20 Tiyenera kufotokozanso mbali imeneyi ya uthenga wabwino tikakhala mu utumiki wachikhristu. Ponena za Yesu, Paulo anagwira mawu a Yesaya kuti: “Palibe wokhulupirira iye, amene adzakhumudwe.” (Aroma 10:11; Yes. 28:16) Mfundo zikuluzikulu za uthenga wonena za Yesu si zachilendo kwa anthu amene akudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya uchimo. Koma kwa anthu ena, uthenga umenewu ndi wachilendo chifukwa chakuti ndi wokhudza zinthu zimene anthu a chikhalidwe chawo sazidziwa kapena kuzikhulupirira. Anthu oterewa akayamba kukhulupirira Mulungu ndiponso Malemba, tiyenera kuwafotokozera udindo wa Yesu. M’nkhani yotsatira tidzaona mmene chaputala 5 cha buku la Aroma chimafotokozera mbali imeneyi ya uthenga wabwino. Mosakayikira, zimene mudzaphunzira m’nkhani imeneyi zidzakuthandizani mu utumiki wanu.

21 N’zosangalatsa kuthandiza anthu amtima wabwino kuti amvetse uthenga wabwino womwe unatchulidwa mobwerezabwereza m’buku la Aroma. Uthenga umenewu “ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro.” (Aroma 1:16) Tidzasangalalanso kuona anthu akuvomereza mawu a Yesaya amene Paulo anawalemba pa Aroma 10:15 akuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwabasi!”​—Yes. 52:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mawu ngati amenewa amapezekanso m’mabuku ena ouziridwa.​—Maliko 1:1; Mac. 5:42; 1 Akor. 9:12; Afil. 1:27.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi buku la Aroma limatsindika mbali iti ya uthenga wabwino?

• Kodi tiyenera kuthandiza anthu ena kumvetsa mfundo iti?

• Kodi “uthenga wabwino wonena za Khristu” ungabweretse bwanji madalitso kwa ifeyo ndiponso kwa anthu ena?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Uthenga wabwino wa m’buku la Aroma umafotokoza udindo wa Yesu wofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 9]

Tonse tinabadwa ndi vuto lalikulu kwambiri, lomwe ndi uchimo