Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Muzilemekeza Anthu Amene Akugwira Ntchito Mwakhama Pakati Panu”

“Muzilemekeza Anthu Amene Akugwira Ntchito Mwakhama Pakati Panu”

“Muzilemekeza Anthu Amene Akugwira Ntchito Mwakhama Pakati Panu”

“Muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye ndi kukulangizani.”​—1 ATES. 5:12.

1, 2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji mu mpingo wa Tesalonika pa nthawi imene Paulo ankawalembera kalata yake yoyamba? (b) Kodi Paulo analimbikitsa Atesalonika kuchita chiyani?

MPINGO wa Tesalonika unali umodzi mwa mipingo yoyambirira kukhazikitsidwa ku Ulaya. Mtumwi Paulo anakhala nthawi yaitali akulimbikitsa abale kumeneku. N’kutheka kuti iye anaikanso akulu mu mpingowu kuti azitsogolera ngati mmene anachitira ndi mipingo ina. (Mac. 14:23) Koma mpingowu utakhazikitsidwa, Ayuda anasonkhanitsa gulu lachiwawa kuti lithamangitse Paulo ndi Sila mumzindawo. Akhristu amene anatsala ayenera kuti ankamva kuti ali okhaokha ndipo mwina ankachita mantha. Kodi inuyo mukanakhalako mukanamva bwanji?

2 M’pomveka kuti atachoka ku Tesalonika, Paulo ankadera nkhawa mpingo watsopanowu. Iye anayesetsa kuti abwerereko koma “Satana anatchinga njira” yake. Choncho anatumiza Timoteyo kuti akalimbikitse mpingowu. (1 Ates. 2:18; 3:2) Timoteyo atabwera kuchokera ku mpingo wa Tesalonika n’kufotokoza zinthu zabwino zokhudza mpingowu, Paulo anaona kuti ndi bwino kuulembera kalata. Chinthu china chimene Paulo anawalimbikitsa kuchita chinali ‘kulemekeza anthu amene ankawatsogolera.’​—Werengani 1 Atesalonika 5:12, 13.

3. Kodi Akhristu a ku Tesalonika anafunika kupereka ulemu waukulu kwa akulu pa zifukwa ziti?

3 Abale amene ankatsogolera Akhristu a ku Tesalonika sankadziwa zinthu ngati Paulo ndi anzake amene ankayenda nawo. Komanso iwo anali asanakhale m’choonadi nthawi yaitali ngati akulu a ku Yerusalemu. Ndipotu mpingowu unali usanathe chaka chiukhazikitsireni. Ngakhale zinali choncho, anthu mu mpingowu anali ndi zifukwa zomveka zoyamikirira akulu amene anali ‘kugwira ntchito mwakhama,’ ‘kutsogolera’ mpingo komanso ‘kulangiza’ abale. Iwo analidi ndi zifukwa zabwino zopatsira akulu “ulemu waukulu mwachikondi.” Atawapempha kuti azilemekeza akulu, mtumwi Paulo anawalangiza kuti ‘azikhala mwamtendere pakati pawo.’ Kodi inuyo mukanakhala ku Tesalonika mukanayamikira kwambiri ntchito imene akulu ankagwira? Nanga mumayamikira “mphatso za amuna” zimene Mulungu wapereka mu mpingo wanu kudzera mwa Khristu?​—Aef. 4:8.

“Akugwira Ntchito Mwakhama”

4, 5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti akulu a m’nthawi ya Paulo ankagwira ntchito mwakhama kuti aphunzitse mpingo, nanga n’chifukwa chiyani zilinso chimodzimodzi masiku ano?

4 Pambuyo potumiza Paulo ndi Sila ku Bereya, kodi akulu a ku Tesalonika ankagwira bwanji ntchito “mwakhama”? Mosakayikira, iwo ankaphunzitsa mpingo pogwiritsa ntchito Malemba ngati mmene Paulo ankachitira. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Akhristu a ku Tesalonika ankakondadi Mawu a Mulungu?’ Pajatu Baibulo limanena kuti anthu a ku Bereya anali “a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. . . . Tsiku ndi tsiku anali kufufuza Malemba mosamala.” (Mac. 17:11) Apa Baibulo likuyerekezera anthu a ku Bereya ndi Ayuda a ku Tesalonika, osati ndi Akhristu. Anthu amene anakhala okhulupirira ‘sanalandire mawu a Mulungu monga mawu a anthu ayi, koma monga mawu a Mulungu.’ (1 Ates. 2:13) Akulu ayenera kuti ankagwira ntchito mwakhama kuti adyetse anthu amenewa mwauzimu.

5 Masiku ano, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limadyetsa nkhosa za Mulungu “chakudya pa nthawi yoyenera.” (Mat. 24:45) Motsogoleredwa ndi kapoloyu, akulu m’mipingo amagwira ntchito mwakhama kuti adyetse abale mwauzimu. M’mipingo yambiri anthu ali ndi mabuku ofotokoza Baibulo ambirimbiri ndipo m’zilankhulo zina pali zinthu monga Watch Tower Publications Index ndiponso Watchtower Library ya pakompyuta. Kuti mpingo upindule mwauzimu, akulu amakonzekera nkhani zawo kwa maola ambiri n’cholinga choti akakambe mogwira mtima. Kodi munaganizirapo nthawi imene akulu amakhala akukonzekera nkhani za pa misonkhano ya mpingo, yadera ndiponso yachigawo?

6, 7. (a) Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani kwa akulu a ku Tesalonika? (b) N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti akulu atengere chitsanzo cha Paulo?

6 Akulu a ku Tesalonika ankakumbukira chitsanzo chabwino cha Paulo pa nkhani yoweta nkhosa. Sikuti Paulo ankangoyendera nkhosa mwamwambo kapena pongofuna kukwaniritsa udindo wake monga mkulu. Monga taonera m’nkhani yapitayi, Paulo ‘anakhala wodekha . . . monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira ana ake.’ (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Iye anali wokonzeka ‘kuwapatsa moyo wake weniweniwo.’ Poweta nkhosa, akuluwo anafunika kukhala ngati iye.

7 Masiku ano, abusa achikhristu amatsanzira Paulo akamasamalira nkhosa mwachikondi. Mwachibadwa, anthu ena mu mpingo si ochezeka ndipo ndi ovuta kumasuka nawo. Ngakhale zili choncho, akulu amayesetsa kuchita zinthu mozindikira ‘ndi kupeza zabwino’ mwa anthu oterowo. (Miy. 16:20) N’zoona kuti chifukwa cha kupanda ungwiro zingakhale zovuta kuti akulu aziona zabwino mwa aliyense. Komabe akulu amayesetsa mmene angathere kukhala odekha kwa anthu onse. Tiyenera kuwayamikira kwambiri chifukwa amachita khama kuti akhale abusa abwino motsogoleredwa ndi Khristu.

8, 9. Kodi akulu masiku ano ‘amayang’anira miyoyo yathu’ m’njira ziti?

8 Tonsefe tili ndi zifukwa zotichititsa ‘kugonjera’ akulu. Paulo analemba kuti ‘iwo amayang’anira miyoyo yathu.’ (Aheb. 13:17) Mawu amenewa amatikumbutsa za m’busa weniweni amene sagona pofuna kuteteza nkhosa zake. Nawonso akulu, nthawi zina sagona mokwanira chifukwa chothandiza anthu amene akudwala, kuvutika maganizo kapena amene ali ndi vuto lauzimu. Mwachitsanzo, abale amene ali m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala amadzutsidwa usiku pakakhala wodwala amene akufunika thandizo. Timayamikira kwambiri ntchito imene abale amenewa amagwira tikakumana ndi vuto lokhudza matenda.

9 Akulu amene amagwira nawo ntchito zomanga Nyumba za Ufumu ndiponso amene ali m’makomiti oyang’anira ntchito yopereka chithandizo pakagwa tsoka, amachita khama kwambiri pothandiza abale. Tiyenera kuwalimbikitsa ndiponso kuwayamikira ndi mtima wonse. Taganizirani za chithandizo chimene chinaperekedwa ku Myanmar mu 2008 kutachitika mphepo ya mkuntho yotchedwa Nargis. Kuti gulu lopereka chithandizo likafike ku mpingo wa Bothingone, linadutsa m’chigawo cha Irrawaddy komwe kunali kutawonongeka ndi mphepo ya mkunthoyo ndipo mitembo inali mbwee. Abale a kumeneko ataona kuti m’gululo muli m’bale wina amene kale anali woyang’anira dera wawo anafuula kuti: “Anthuni! Woyang’anira dera wathu uja uyo! Mwamuona? Yehova watipulumutsa basi!” Kodi mumayamikira ntchito imene akulu amagwira mwakhama usana ndi usiku? Akulu ena amapemphedwa kuti akhale m’makomiti apadera n’cholinga choti asamalire milandu ina yovuta kwambiri. Akulu amenewa sadzitamanda chifukwa cha zimene akuchita koma anthu amene amawathandizawo amayamikira kwambiri.​—Mat. 6:2-4.

10. Kodi akulu amagwiranso ntchito zosaonekera kwambiri ziti?

10 Akulu ambiri masiku ano amakhalanso ndi ntchito zolembalemba. Mwachitsanzo, wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu amakonza ndandanda za misonkhano ya mlungu ndi mlungu. Mlembi wa mpingo amasonkhanitsa ndi kulemba malipoti a utumiki wakumunda a mwezi uliwonse ndiponso a chaka chonse. Woyang’anira sukulu nayenso amalemba mosamala kwambiri ndandanda ya sukulu. Pa miyezi itatu iliyonse akulu amawerengera maakaunti a mpingo. Iwo amawerenganso makalata ochokera ku ofesi ya nthambi ndipo amagwiritsa ntchito malangizo amene awerengawo pofuna kuti pakhale “umodzi m’chikhulupiriro.” (Aef. 4:3, 13) Chifukwa chakuti akulu amagwira ntchito mwakhama, ‘zinthu zonse zimachitika moyenera ndi mwadongosolo.’​—1 Akor. 14:40.

“Amakutsogolerani”

11, 12. Kodi ndani amatsogolera mu mpingo, nanga ‘kutsogolera’ kumatanthauza chiyani?

11 Paulo ananena kuti akulu a ku Tesalonika, amene ankagwira ntchito mwakhama, ‘ankatsogolera’ mpingo. (1 Ates. 5:12) Mawu amene anawamasulira kuti ‘kutsogolera’ kwenikweni amatanthauza “kuima patsogolo.” Paulo anali kunena za akulu onse mu mpingo osati “woyang’anira wotsogolera” mmodzi. Akulu onse anali ‘kugwira ntchito mwakhama’ ndiponso ‘kutsogolera’ mu mpingo. Masiku ano, akulu ambiri amaima patsogolo mu mpingo kuti achititse misonkhano. Mawu akuti “wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu,” amene tayamba kuwagwiritsa ntchito posachedwapa, amatithandiza kuona kuti akulu onse ndi bungwe limodzi logwirizana.

12 Koma ‘kutsogolera’ mpingo sikumangotanthauza kuphunzitsa. Mawu amene anawamasulira kuti ‘kutsogolera’ ndi ofanana ndi amene anawamasulira kuti ‘kuyang’anira’ pa lemba la 1 Timoteyo 3:4. Paulo ananena kuti woyang’anira mu mpingo ayenera kukhala “mwamuna woyang’anira bwino banja lake. Wa ana omumvera ndi mtima wonse.” Mawu amene anawamasulira kuti ‘kuyang’anira’ pa lembali samangotanthauza kuphunzitsa ana ake koma amatanthauzanso kuwatsogolera m’njira zina ndiponso kuti anawo ‘azimumvera.’ Nawonso akulu amatsogolera mpingo akamathandiza anthu mu mpingomo kuti azimvera Yehova.​—1 Tim. 3:5.

13. N’chifukwa chiyani zingatenge nthawi kuti akulu asankhe zochita pa msonkhano wawo?

13 Pofuna kutsogolera bwino nkhosa, akulu amakhala pansi ndi kukambirana zosowa za mpingo n’kuona zimene angachite kuti akonze zinthu mu mpingowo. N’zoona kuti zingaoneke zosavuta kuti mkulu mmodzi asankhe yekha zochita zonse mu mpingo. Koma potengera chitsanzo cha bungwe lolamulira la nthawi ya atumwi, mabungwe a akulu masiku ano amakambirana zinthu momasuka n’kumafufuza malangizo a m’Malemba. Cholinga chawo chimakhala kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba pothandiza mpingo. Zokambirana zawozi zimakhala zothandiza kwambiri ngati mkulu aliyense amakonzekera msonkhano wa akulu poona Malemba othandiza komanso malangizo ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Koma kuti zimenezi zitheke pamatenga nthawi. Nthawi zina akulu angakhale ndi maganizo osiyana pa nkhani inayake monga mmene zinachitikira ndi bungwe lolamulira m’nthawi ya atumwi. Zimenezi zikachitika, akulu angafunikire kupeza nthawi yoti afufuze bwinobwino nkhaniyo kuti asankhe zinthu zogwirizana ndi Malemba.​—Mac. 15:2, 6, 7, 12-14, 28.

14. Kodi n’chifukwa chiyani mumayamikira kuti akulu amagwira ntchito limodzi monga bungwe logwirizana?

14 Kodi chingachitike n’chiyani ngati mkulu wina amaumirira maganizo ake n’kumafuna kuti anthu atsatire zofuna zake? Nanga chingachitike n’chiyani ngati mkulu wina amasokoneza mgwirizano ngati mmene ankachitira Diotirefe m’nthawi ya atumwi? (3 Yoh. 9, 10) Zimenezi zikhoza kusokoneza mpingo wonse. Satana ankafuna kusokoneza mpingo m’nthawi ya atumwi ndiye n’zosachita kufunsa kuti masiku anonso amafuna kusokoneza mtendere mu mpingo. Iye angachite zimenezi pochititsa munthu kuyamba mtima wofuna malo apamwamba. Choncho akulu ayenera kukhala odzichepetsa n’kumagwira ntchito monga bungwe logwirizana. Tiyenera kuyamikira kwambiri akulu amene amachita zimenezi.

‘Amakulangizani’

15. Kodi akulu ayenera kukhala ndi maganizo otani akamalangiza m’bale kapena mlongo?

15 Kenako Paulo ananena kuti akulu amalangiza nkhosa. Imeneyi ndi ntchito yovuta koma yofunika kwambiri. M’Malemba Achigiriki, Paulo yekha ndi amene anagwiritsa ntchito mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kulangiza.” Mawuwa angatanthauze kupereka uphungu mwamphamvu koma osati mokalipa. (2 Ates. 3:15) Mwachitsanzo, Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Sikuti ndikulemba zinthu zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni monga ana anga okondedwa.” (1 Akor. 4:14) Iye ankapereka malangizo chifukwa chokonda kwambiri anthu ena.

16. Kodi akulu angachite bwino kukumbukira chiyani akamalangiza ena?

16 Akulu amakumbukiranso kuti kupereka malangizo m’njira yoyenera n’kofunika kwambiri. Iwo amayesetsa kupereka malangizo mokoma mtima, mwachikondi komanso mothandiza ngati mmene ankachitira Paulo. (Werengani 1 Atesalonika 2:11, 12.) Akulu ‘amagwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso, kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola.’​—Tito 1:5-9.

17, 18. Kodi muyenera kukumbukira chiyani mkulu akakupatsani malangizo?

17 Komabe, akulu ndi opanda ungwiro ndipo nthawi zina angalankhule zinthu zimene pambuyo pake akhoza kumva nazo chisoni. (1 Maf. 8:46; Yak. 3:8) Akulu amadziwanso kuti nthawi zambiri uphungu umene abale ndi alongo amalandira ‘sumveka wosangalatsa koma wowawa.’ (Aheb. 12:11) Choncho mkulu akamapita kukapereka malangizo kwa munthu wina amakhala atapempherera nkhaniyo ndiponso kuiganizira bwino. Kodi mumayamikira chikondi chimene mkulu wasonyeza pokupatsani malangizo?

18 Tayerekezani kuti mukudwala koma zikuoneka kuti madokotala akulephera kudziwa matenda anu. Ndiyeno dokotala wina wazindikira vuto lanu koma ndi loti simungakonde kulimva. Kodi mungadane ndi dokotalayo chifukwa chopeza vutolo? Ayi. Mungalole chithandizo chilichonse, ngakhale atanena kuti muchitidwe opaleshoni. Mungatero chifukwa chokhulupirira kuti akakuthandizani muchira. N’zoona kuti zingakupwetekeni ngati dokotalayo sanakuuzeni za vuto lanulo m’njira yabwino. Koma kodi zimenezi zingakuchititseni kukana chithandizocho? Ayi. N’chimodzimodzi ndi kupatsidwa malangizo. Musalephere kulandira malangizo chifukwa cha mmene munthu wawaperekera. Yehova ndi Yesu angagwiritse ntchito anthu otero pofuna kukuthandizani kudziwa zimene mungachite kuti mukhale otetezeka komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mwauzimu.

Tiziyamikira Akulu Chifukwa Ndi Mphatso Yochokera kwa Yehova

19, 20. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira “mphatso za amuna”?

19 Kodi mungachite chiyani ngati munthu wina wakukonzerani mphatso inayake n’kukupatsani? Kodi mungasonyeze kuti mukuiyamikira poigwiritsa ntchito? Yehova wakupatsani “mphatso za amuna” kudzera mwa Yesu Khristu. Njira imodzi imene mungasonyezere kuyamikira mphatso zimenezi ndiyo kumvetsera mwatcheru nkhani zimene akulu amakamba ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo zimene mwamva m’nkhanizo. Kupereka ndemanga zogwira mtima pa misonkhano ndi njira inanso imene mungasonyezere kuti mumayamikira mphatsozi. Muzithandizanso pa ntchito imene akulu akutsogolera monga utumiki wakumunda. Ngati mwapindula kwambiri ndi malangizo amene mkulu wina anakupatsani, mungachite bwino kumudziwitsa. Ndi bwinonso kumayamikira anthu a m’banja la akulu. Kumbukirani kuti nthawi imene akulu akugwira ntchito mwakhama mu mpingo ndi nthawi imene akanakhala ndi banja lawo ndipo banjalo limalolera zimenezi.

20 Anthufe tilidi ndi zifukwa zambiri zosonyezera kuti timayamikira akulu amene akugwira ntchito mwakhama pakati pathu, kutitsogolera ndiponso kutilangiza. “Mphatso za amuna” zimenezi ndi umboni wamphamvu wakuti Yehova amatikonda kwambiri.

Kodi Mukukumbukira

• Kodi Akhristu a ku Tesalonika anali ndi zifukwa ziti zoyamikirira anthu amene ankatsogolera pakati pawo?

• Kodi akulu mu mpingo wanu amagwira ntchito mwakhama pochita zinthu ziti?

• Kodi akulu amene amatsogolera pakati panu amakuthandizani bwanji?

• Kodi muyenera kukumbukira chiyani ngati mkulu wakupatsani malangizo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 27]

Kodi mumayamikira zinthu zosiyanasiyana zimene akulu amachita poweta mpingo?