Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Moyo Umaoneka Ngati Wopanda Phindu?

Kodi N’chifukwa Chiyani Moyo Umaoneka Ngati Wopanda Phindu?

Kodi N’chifukwa Chiyani Moyo Umaoneka Ngati Wopanda Phindu?

MALINGA ndi zimene ananena Mfumu Solomo, moyo wathu ndi “waufupi ndiponso wachabechabe” komanso umazimiririka “ngati mthunzi.” (Mlaliki 6:12, The New English Bible) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti m’tsogolo moyo sudzakhala wotere? Baibulo, lomwe ndi buku lodalirika komanso ndi louziridwa ndi Mulungu, limalonjeza kuti m’tsogolo muno moyo udzakhala wosangalatsa kwambiri komanso waphindu.​—2 Timoteyo 3:16, 17.

Baibulo limatiuza chifukwa chake Mulungu analenga dzikoli. Limafotokozanso chifukwa chake padzikoli pamachitika zinthu zopanda chilungamo, kuponderezana ndiponso mavuto ena. Kodi ndi chifukwa chiyani tiyenera kudziwa zoona pa nkhani zimenezi? N’chifukwa chakuti mfundo yaikulu imene imapangitsa anthu kuganiza kuti moyo ulibe phindu, ndi yoti iwo sadziwa chifukwa chake Mulungu analenga dziko lapansili kapena amanyalanyaza dala cholinga cha Mulungucho.

Kodi Mulungu Analengeranji Dziko Lapansili?

Yehova Mulungu * analenga dziko lapansi kuti likhale paradaiso n’cholinga choti anthu angwiro azikhalamo mosangalala mpaka kalekale. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ena amaphunzitsa. Iwo amati Mulungu analenga dzikoli kuti angoyeseramo anthu n’cholinga chakuti aone ngati ndi oyenera kukakhala kumwamba kapena ayi. Onani bokosi lakuti,  “Kodi Anthu Afunika Kupita Kumwamba Kuti Akhale Ndi Moyo Wosangalala”? patsamba 6.

Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi m’chifaniziro Chake komanso m’njira yoti azitha kusonyeza makhalidwe Ake abwino kwambiri. (Genesis 1:26, 27) Mulungu anawalenga anthu amenewa angwiro. Anthuwa anali ndi zonse zofunika moti akanatha kuchita zinthu zambiri zaphindu komanso akanakhala ndi moyo wosangalala mpaka muyaya. Iwo akanadzaza dziko lapansi ndi kuliyang’anira komanso kugwira ntchito yokonza dziko lonse kuti likhale paradaiso ngati mmene munda wa Edeni unalili.​—Genesis 1:28-31; 2:8, 9.

Kodi Chinalakwika N’chiyani?

N’zoonekeratu kuti chinachake chinalakwika kwambiri. Tikutero chifukwa anthu samasonyeza makhalidwe abwino a Mulungu komanso dzikoli silili paradaiso. Kodi ndi chifukwa chiyani zili chonchi? N’chifukwa chakuti makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, sanagwiritse ntchito bwino ufulu wosankha umene Mulungu anawapatsa. Iwo ankafuna kuti “afanane ndi Mulungu,” kuti azisankha okha “zabwino ndi zoipa.” Pamenepa iwo anagwirizana ndi Satana Mdyerekezi yemwe anali atapandukira kale Mulungu.​—Genesis 3:1-6.

Choncho si zoona kuti Mulungu anakonzeratu kuti padzikoli pazichitika zoipa zimene zikuchitikazi. Zoipa zinayamba pamene Satana, ndipo kenako Adamu ndi Hava, anapandukira ulamuliro wa Mulungu. Chifukwa choti anapandukira Mulungu, makolo athu oyambawa anathamangitsidwa m’Paradaiso ndipo sanalinso angwiro. Zimenezi zinabweretsa uchimo ndiponso imfa, osati kwa iwo okha, komanso kwa anthu onse padziko lapansi. (Genesis 3:17-19; Aroma 5:12) Izi ndi zimene zapangitsa kuti moyo wathu uzioneka ngati wopanda phindu.

Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanawononge Opandukawo Nthawi Yomweyo?

Anthu ena angadabwe kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu sanawononge Satana ndi opanduka enawo nthawi yomweyo, n’kulenganso anthu ena n’cholinga choti padzikoli pasakhale mavuto?’ Koma kodi ikanakhala nzeru kuchita zimenezi? Kodi inuyo mungaganize chiyani mutamva kuti pali boma linalake limene limati likangomva kuti winawake akutsutsana nalo limamupha nthawi yomweyo? Zimenezi zingachititse kuti anthu okonda chilungamo azidana ndi bomalo ndipo boma lotereli silingakhale chitsanzo chabwino pa nkhani ya kayendetsedwe koyenera ka boma.

N’chifukwa chake Mulungu anasankha kusawononga anthu opandukawo nthawi yomweyo. Mwanzeru, iye analola kuti papite nthawi n’cholinga chakuti nkhani zokhudza ulamuliro wake zimene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni, zithetsedwe ndipo ulamuliro wake usadzatsutsidwenso.

Posachedwapa Mulungu Athetsa Zoipa Padzikoli

Mfundo yofunika kwambiri kuikumbukira ndi yakuti: Mulungu walola kuti zoipa zizichitika padzikoli, koma sadzalola kuti zichitike mpaka kalekale. Iye wachita zimenezi chifukwa akudziwa kuti adzathetsa mavuto onse, nkhani yokhudza ulamuliro wake ikadzathetsedwa.

Mulungu sanaiwale cholinga chake chokhudza anthu komanso dziko la pansili ndipo akufuna kuti chidzakwaniritsidwe. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova akutitsimikizira kuti iye ndi Mlengi wa dziko lapansi ndipo ‘sanalilenge popanda cholinga, koma analiumba kuti anthu akhalemo.’ (Yesaya 45:18) Posachedwapa, Mulungu ayamba kukonza zinthu padzikoli kuti zikhale mmene iye anafunira poyamba. Mulungu akadzasonyeza kuti iye ndiye woyenera kulamulira dziko lonse, anthu onse adzaona kuti iye wagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake zopanda malire kuwononga anthu oipa onse ndiponso kukwaniritsa cholinga chake. (Yesaya 55:10, 11) M’pemphero la chitsanzo, Yesu Khristu anapempha Mulungu kuti akwaniritse chifuno chake. Iye anatiphunzitsa kuti tizipemphera kuti: “Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi zina zimene Mulungu akufuna kudzachita ndi ziti?

Chifuno Cha Mulungu Chokhudza Dziko Lapansi

Zina mwa zimene Mulungu akufuna ndi zoti, ‘anthu ofatsa adzalandire dziko lapansi.’ (Salimo 37:9-11, 29; Miyambo 2:21, 22) Yesu Khristu “adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika.” Iye “adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.” (Salimo 72:12-14) Sikudzakhalanso nkhondo, imfa, kulira, kubuula kapena zopweteka. (Salimo 46:9; Chivumbulutso 21:1-4) Anthu ambirimbiri amene amwalira pa nthawi yonse imene Mulungu walola kuti zoipa zizichitika padzikoli, adzaukitsidwa ndipo adzasangalala ndi madalitso amenewa komanso ena ambiri.​—Yohane 5:28, 29.

Choncho, Yehova adzathetsa zoipa zonse zimene zakhala zikuchitika chifukwa cha kupanduka kwa Satana. Iye adzachotseratu chilichonse choipa moti “masautso akale [mavuto onse amene timakumana nawo masiku ano] adzaiwalika.” (Yesaya 65:16-19) Malonjezo amenewa adzakwaniritsidwadi chifukwa Mulungu sanama ndipo zonse zimene walonjeza zimachitika. Pa nthawi imeneyo, moyo sudzakhalanso ‘wachabechabe ngati kuthamangitsa mphepo.’ (Mlaliki 2:17) M’malomwake moyo udzakhala wosangalatsa kwambiri komanso waphindu.

Nanga bwanji masiku ano? Kodi kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kumvetsa cholinga cha Mulungu chokhudza dzikoli kungakuthandizeni kukhala ndi moyo wasangalala panopa? Nkhani yotsatira ili ndi yankho la funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.

[Bokosi patsamba 6]

 Kodi Anthu Afunika Kupita Kumwamba Kuti Akhale Ndi Moyo Wosangalala?

Kwa zaka zambiri anthu amene sadziwa cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili akhala akuphunzitsa kuti, anthufe tingakhale ndi moyo wosangalala pokhapokha titapita kumwamba.

Ena amaphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu womwe “poyamba unkakhala ndi moyo wosangalala kwinakwake usanadzalowe m’thupi la munthu.” (New Dictionary of Theology) Enanso amaphunzitsa kuti “mzimu umaikidwa m’thupi la munthu ngati chilango cha machimo amene mzimuwo unachita uli kumwamba”​—Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature.

Akatswiri achigiriki, Socrates komanso Plato, ankaphunzitsa mfundo yakuti: Mzimu ukachoka m’thupi la munthu ndi “pamene umasiya zoyendayenda, kuchita zinthu zopanda nzeru, mantha, zilakolako zoipa komanso umasiyana ndi mavuto onse amene anthu amakumana nawo.” Zikatero umakakhala “ndi milungu kwamuyaya.”​—Plato’s Phaedo, 81, A.

Kenako anthu amene ankati ndi atsogoleri achikhristu anatengera mfundo za akatswiri achigiriki “zonena kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa” ndipo anaziphatikiza ndi ziphunzitso zawo.​—Christianity​—A Global History.

Tayerekezerani mfundo zimenezi ndi mfundo zitatuzi zopezeka m’Baibulo:

1. Cholinga cha Mulungu n’chakuti dziko lapansili likhale kwawo kwa anthu mpaka kalekale, osati angokhala malo oyeserako anthu kuti adziwe ngati akuyenerera kukakhala naye kumwamba. Adamu ndi Hava akanakhala kuti anamvera malamulo a Mulungu, sikuti akanapita kumwamba koma akanakhalabe padziko lapansi m’paradaiso mpaka lero.​—Genesis 1:27, 28; Salimo 115:16.

2. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa. Koma Baibulo limaphunzitsa mfundo yosavuta kumva yakuti: Mulungu analenga munthu kuchokera “kufumbi lapansi” ndipo kenako anauzira mpweya wa moyo kapena kuti mzimu m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala “wamoyo.” (Genesis 2:7) Baibulo silinena kuti mzimu wa munthu umakhalabe ndi moyo munthuyo akamwalira. Koma limanena kuti munthu akafa, mzimu kapena kuti mphamvu ya moyo, siipezekanso kulikonse. (Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4, 20) Munthu woyamba Adamu, anafa ndipo anabwerera kufumbi kumene anatengedwa. Zimenezi zikutanthauza kuti iye atafa, anathera pomwepo ndipo sanali kulikonse, ngati mmene zinalili asanalengedwe.​—Genesis 2:17; 3:19.

3. Kuti munthu adzakhale ndi moyo wosatha m’tsogolo, sizidalira kuti iye akafa mzimu wake upite kumwamba. Koma zikudalira kuti Mulungu adzamuukitse kuti adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso monga mmene analonjezera.​—Danieli 12:13; Yohane 11:24-26; Machitidwe 24:15.