Onani zimene zilipo

Baibo Imasintha Anthu

Baibo Imasintha Anthu

Baibo Imasintha Anthu

KODI mukudziŵa zimene zinacititsa mzimayi wina wa zaka zoposa 60 kusiya kulambila mafano? Nanga n’ciani cinacititsa kuti wansembe wina wacishinto asiye nchito yake ya pakacisi wolambila makolo n’kukhala Mkhristu? Komanso kodi n’ciani cinacititsa kuti mayi wina amene analeledwa na anthu omwe si makolo ake, asiye kudela nkhawa kwambili zoti makolo ake omubeleka anamutaya? Ŵelengani nkhani zotsatilazi kuti mumve zimene anthu amenewa akunena.

“N’nasiya kulambila mafano.”ABA DAN SOU

CAKA COBADWA: 1938

DZIKO: BENIN

POYAMBA: N’NALI KULAMBILA MAFANO

KALE LANGA: N’nakulila m’mudzi winawake wa m’mbali mwa nyanja wochedwa So-Tchahoué. Anthu a m’mudzi umenewu ni asodzi komanso amaweta ng’ombe, mbuzi, nkhosa, nkhumba, nkhuku ni nkhunda. Kudelali kulibe misewu conco anthu akafuna kuyenda amagwilitsa nchito maboti na mabwato. Nyumba zambili n’zomangidwa na matabwa komanso udzu ndipo ni anthu ocepa okha amene amamanga nyumba zawo na ncelwa. Anthu ambili m’delali ni osauka komabe sikucitika zaumbava kapena ciwawa kaŵili-kaŵili ngati mmene zilili m’mizinda.

Nili mwana, bambo anga ananitumiza ineyo ni mkulu wanga kumalo olambililako milungu ya makolo komwe tinaphunzilako kulambila milungu imeneyi. Nitakula ninayamba kulambila mulungu waciyoruba wochedwa Dudua, kapena kuti Oduduwa. Ninamangila nyumba mulungu ameneyu ndipo nthawi zambili n’nali kupeleka kwa iye nsembe za zilazi, mafuta akanjedza, nkhono, nkhuku, nkhunda ni nyama zosiyana-siyana. N’nali kuwononga ndalama zambili kuti nipeze zinthu zimenezi, moti nthawi zambili n’nali kutsala opanda ndalama iliyonse.

MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA: N’tayamba kuphunzila Baibo, ninazindikila kuti Yehova yekha ndiye Mulungu woona. N’naphunzilanso kuti Yehova amadana na kulambila mafano. (Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14) N’nazindikila kuti n’nafunika kusintha, conco n’nataya mafano anga onse ndiponso n’nacotsa m’nyumba mwanga ciliconse cogwilizana na kupembedza mafano. Komanso n’nasiya kupita kwa owombeza, kucita nawo miyambo yacipembedzo komanso miyambo yosiyana-siyana ya pa malilo.

Koma kucita zimenezi sikunali kopepuka kwa mayi wazaka zoposa 60 ngati ine. Anzanga, abale anga komanso anthu okhala nawo pafupi sanasangalale na zimenezi ndipo anali kuninyoza. Koma n’napemphela kwa Yehova kuti anithandize kuti nipitilize kucita zabwino. Komanso lemba la Miyambo 18:10 linanilimbikitsa cifukwa limanena kuti: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawila mmenemo ndipo amatetezedwa.”

Cinanso comwe cinanithandiza ni kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Kumeneko ananisonyeza cikondi cimene Akhristu oona amayenela kukhala naco ndipo n’nacita cidwi kwambili kuona kuti anthu amenewa amayesetsa kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino. Zimene ninaona kumeneko zinanipangitsa kukhulupilila kuti cipembedzo ca Mboni za Yehova cimaphunzitsadi zoona.

PHINDU LIMENE NAPEZA: Kutsatila mfundo za m’Baibo kwanithandiza kuti nizigwilizana kwambili na ana anga. Komanso nikuona kuti cimtolo colemetsa cimene ninasenza nacitula pansi. Poyamba n’nali kuwononga ndalama zanga kupeleka nsembe ku mafano opanda moyo amene anali osathandiza ngakhale pang’ono. Koma panopa nikulambila Yehova, Mulungu amene wakonza zodzathetsa mavuto athu onse. (Chivumbulutso 21:3, 4) Komanso ndine wosangalala kwambili cifukwa panopa sindinenso kapolo wa mafano koma nikutumikila Yehova. Kucita zimenezi kwacititsa kuti nikhale ni tsogolo labwino.

Kuyambila nili mwana n’nali kufunitsitsa kudziŵa Mulungu.”—SHINJI SATO

CAKA COBADWA: 1951

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: N’NALI WANSEMBE WA CIPEMBEDZO CACISHINTO

KALE LANGA: N’nakulila m’tawuni yaing’ono m’cigawo ca Fukuoka ndipo makolo anga anali kukonda kwambili kupemphela. Kuyambila nili mwana, ananiphunzitsa kuti nizilemekeza milungu yacipembedzo cacishinto. Nili mnyamata, nthawi zambili n’nali kuganizila kwambili zimene ningacite kuti nidzapulumuke komanso n’nali kufunitsitsa kuthandiza anthu ovutika. Nikukumbukila tili ku pulayimale, aphunzitsi athu anatifunsa zimene tikufuna kudzacita tikadzakula. Anzanga onse ananena kuti akufuna kuti adzagwile nchito zapamwamba monga kukhala asayansi. Koma ine n’nayankha kuti nimafuna kudzatumikila Mulungu ndipo anzanga onse ananiseka.

N’tamaliza maphunzilo a ku sekondale, n’nayamba kuphunzila nchito yoti nizidzaphunzitsa anthu kukhala atsogoleli acipembedzo. Pa nthawi imeneyi, n’nakumana na wansembe wina wacishinto amene amayesetsa kupeza nthawi n’kumaŵelenga buku inayake yacikuto cakuda. Tsiku lina wansembeyu ananifunsa kuti “Kodi Sato, buku ili ukulidziŵa?” N’taona cikuto ca bukulo, n’nayankha kuti: “Inde nikuidziŵa, ni Baibo.” Ndiyeno iye ananiuza kuti: “Aliyense amene akufuna kudzakhala wansembe wacishinto ayenela kuŵelenga buku imeneyi.”

Nthawi yomweyo n’napita kokagula Baibo. N’nali kuisunga pamalo abwino ndipo n’nali kuyesetsa kuisamalila. Komabe sin’nali kupeza nthawi yoliŵelenga cifukwa n’nali kutanganidwa kwambili na sukulu. N’tamaliza sukulu ninayamba kugwila nchito pakacisi ngati wansembe wacishinto ndipo n’nali kuona kuti nakwanilitsa maloto anga.

Koma pasanapite nthawi n’nadabwa kuona kuti zinthu zimene ansembe acishinto anali kucita sizimene n’nali kuyembekezela. Ansembe ambili analibe cikondi komanso sanali kukhudzidwa na mavuto a anthu. Komanso iwo sanali kukhulupilila kwambili Baibo. Wansembe wina amene anali kutiyang’anila anafika poniuza kuti: “Ngati ukufuna zinthu zikuyendele bwino, uzilankhula zimene akatswili a nzelu za anthu amaphunzitsa basi. Pano sitifuna anthu olankhula zinthu zauzimu ayi.”

Mawu amenewa ananikhumudwitsa kwambili ndipo ananipangitsa kuti niyambe kukayikila cipembedzo cacishinto. Ngakhale kuti n’napitiliza kugwila nchito pamalopa, n’nayamba kufufuza ziphunzitso za zipembedzo zina. Koma sin’napeze cipembedzo cimene cinali kuphunzitsa zogwila mtima. Pa zipembedzo zonse zimene n’nafufuza, palibe cimene n’nakhutila naco. Conco n’nayamba kuganiza kuti palibe cipembedzo cimene cimaphunzitsa zoona.

MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA: M’caka ca 1988, n’nakumana ni munthu wina wacipembedzo cacibuda, amene ananilimbikitsa kuti n’ziŵelenga Baibo. N’nakumbukila kuti izi n’zimenenso wansembe wacishinto uja ananiuza zaka zingapo m’mbuyomo, conco ninaganiza zotsatiladi malangizo amenewa. N’tayamba kuŵelenga Baibo, sin’nali kufunanso kuisiya moti nthawi zina n’nali kuliŵelenga usiku wonse mpaka m’mawa.

Zimene n’nali kuŵelenga zinanicititsa kuyamba kupemphela kwa Mulungu amene amachulidwa m’Baibo. Ninayamba ni pemphelo la Ambuye lomwe limapezeka pa Mateyu 6:9-13 ndipo n’nali kuibweleza pakadutsa maola aŵili alionse. N’nali kucita zimenezi ngakhale pogwila nchito yanga ya unsembe pakacisi wacishinto.

N’nali na mafunso ambili-mbili okhudza zinthu zomwe n’nali kuŵelenga m’Baibo. Pa nthawi imeneyi n’kuti n’takwatila ndipo n’nali kudziŵa kuti a Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibo cifukwa anali atabwelapo kunyumba kwathu kudzaceza na mkazi wanga. Conco n’nayamba kufufuza a Mboni ndipo n’napeza mayi wina yemwe n’namufunsa mafunso ambili-mbili. N’nagoma nitaona kuti anagwilitsa nchito Baibo kuyankha funso iliyonse. Iye anakonza zoti a Mboni aziphunzila nane Baibo.

Pasanapite nthawi n’nayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Poyamba sin’nazindikile kuti a Mboni ena amene n’nakumana nawo kumeneku anali oti n’nawacitapo cipongwe m’mbuyomu. Koma iwo ananipatsa moni mwansangala ndipo anasonyeza kuti anilandila na manja aŵili.

Ku misonkhanoko n’naphunzila kuti Mulungu amafuna kuti amuna azikonda akazi awo komanso azisamalila mabanja awo. Nisanaphunzile zimenezi, n’nali kuthela nthawi yambili nikugwila nchito yanga ya unsembe moti sinali kuceza kwenikweni na mkazi wanga komanso ana athu. N’nazindikila kuti n’nali kumvetsela mwacidwi anthu akabwela kukacisi kudzaniuza mavuto awo koma sin’nali kumvetsela mkazi wanga akamanilankhula.

Kuphunzila Baibo kunanithandiza kudziŵa zambili za Yehova ndipo izi zinan’thandiza kuti nikhale naye pa ubwenzi. N’nakhudzidwa mtima kwambili na malemba ena ngati ya Aroma 10:13 imene imati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Kuyambila nili mwana, n’nali kufunitsitsa nitadziŵa Mulungu woona ndipo pa nthawiyi ninaona kuti namupeza.

N’nayamba kuona kuti siinenso woyenela kumagwila nchito pakacisi wacishinto. Koma poyamba n’nali kudela nkhawa kuti anthu ena aganiza ciani nikasiya cipembedzoci. Nthawi zonse n’nali kudziuza kuti n’kadzangopeza Mulungu woona nidzasiya cipembedzo cacishinto. Conco mu 1989, n’nasiya cipembedzoci n’kuyamba kutumikila Yehova.

Komabe kusiya cipembedzo canga kunali kovuta kwambili. Ansembe amene anali kutiyang’anila anakwiya nane kwambili ndipo anali kunikakamiza kuti nisacoke. Koma n’nali kudanso nkhawa kwambili kuti nikawafotokozela bwanji makolo anga za nkhaniyi. Tsiku lomwe n’nali kupita kunyumba kwa makolo anga kuti nikawauze za nkhaniyi, n’nali na nkhawa kwambili moti pamtima panga panali kupweteka komanso miyendo yanga inali kungonjenjemela. Nili m’njila ninaima kangapo konse kupemphela kwa Yehova kuti anipatse mphamvu.

N’tafika kunyumba kwa makolo anga, n’nali ni mantha kwambili kuti niyambitse nkhaniyi moti panadutsa nthawi nisanainene. Kenako, n’tapemphela kwambili, n’nawafotokozela bambo zimene n’nabwelela. N’nawauza kuti napeza Mulungu woona ndipo nikufuna kusiya cipembedzo cacishinto kuti niyambe kumutumikila. Bambo anga sanakhulupilile zimenezi ndipo anakhumudwa kwambili. Kunabwelanso acibale ena ndipo anayesetsa kunikakamiza kuti nisinthe maganizo. Sin’nali kufuna kukhumudwitsa abale anga komabe n’nali kudziwanso kuti niyenela kutumikila Yehova basi. Koma patapita nthawi, iwo anayamba kunilemekeza cifukwa ca zimene ninasankha.

Ngakhale kuti n’nali n’tasiya cipembedzo cacishinto, n’nafunikanso kusintha maganizo anga komanso mmene n’nali kuonela zinthu. Moyo waunsembe unali utanilowelela kwambili. N’nali kuyesetsa kuti niiwale, koma ciliconse cimene n’nali kucita cinkangondikumbutsa zimene n’nali kucita nili wansembe.

Koma pali zinthu ziŵili zomwe zinanithandiza kuti niiwale moyo wanga wakale. Coyamba, n’nafufuza bwino-bwino m’nyumba mwanga kuti nipeze ciliconse cogwilizana na cipembedzo canga cakale. N’napeza mabuku, zithunzi komanso zinthu zina ndipo zonsezo n’naziwocha ngakhale kuti zina mwa zinthu zimenezi zinali zodula. Caciŵili, n’nali kuyesetsa kupeza nthawi yoceza na a Mboni ndipo kuceza na anthu amenewa kunan’thandiza kwambili. Pang’ono-pang’ono n’nayamba kuiwala za cipembedzo canga cakale.

PHINDU IMENE NAPEZA: Poyamba sin’nali kupeza nthawi yoceza na mkazi wanga na ana ndipo izi zinali kupangitsa kuti azikhala osasangalala. Koma n’tayamba kutsatila malangizo a m’Baibo akuti amuna azipeza nthawi yoceza na akazi awo ndiponso ana awo, tinayamba kugwilizana kwambili. Patapita nthawi mkazi wanga nayenso anayamba kutumikila Yehova. Panopa ineyo na mkazi wanga, mwana wathu wamwamuna komanso mwana wathu wamkazi na mwamuna wake, tonse tikutumikila Mulungu.

Nili mwana, n’nali kufunitsitsa kuti nikadzakula nizidzatumikila Mulungu ndiponso kuthandiza anthu. Panopa nimaona kuti nakwanilitsadi colinga cangaci komanso nakwanitsa kucita zinthu zina zimene n’nali nisanaziganizepo. Nikuyamikila kwambili Yehova cifukwa ca zimene wanicitila.

“N’nali kudziŵa kuti cinacake cikusoweka pa moyo wanga.”

LYNETTE HOUGHTING

CAKA COBADWA: 1958

DZIKO: SOUTH AFRICA

POYAMBA: N’NALI KUONA KUTI MAKOLO ANGA ANANITAYA

KALE LANGA: N’nabadwila m’tawuni ya Germiston. Anthu ambili m’tawuniyi si osauka kwenikweni ndipo amagwila nchito m’migodi. Komanso m’tawuniyi simucitika zaumbava kapena zaciwawa zambili. N’tangobadwa, makolo anga anaona kuti sangakwanitse kunilela conco anaganiza zonipeleka kwa amene angafune kunitenga n’kumanilela ngati mwana wawo. Conco nili na milungu iŵili yokha, banja lina linanitenga. Anthu amenewa anali acikondi kwambili moti n’nali kuwaona kuti ni makolo anga enieni. Komabe, n’tadziŵa kuti anthuwa sanali makolo anga enieni, n’nayamba kumadzimvela cisoni poganiza kuti makolo anga ananitaya. Makolo onilela aja n’nasiya kuwaona ngati makolo anga enieni komanso n’nali kuona kuti sakunimvetsa.

Nili na zaka 16 n’nayamba kupita kumabala ni anzanga komwe tinali kukavina komanso kuonelela anthu akuimba. Caka cotsatila, n’nayamba kusuta fodya n’colinga cakuti nicepe thupi mpaka nifanane na anthu ochuka amene amawaonetsa akamanenelela fodya. Kenako n’nayamba kugwila nchito mumzinda wa Johannesburg ndipo n’nayamba kuceza na anthu a makhalidwe oipa. Apa n’kuti nili na zaka 19. Pasanapite nthawi n’nayamba kutukwana, kusuta kwambili, komanso kumwa mowa mwaucidakwa.

Ngakhale zinali conco, n’nali kuona kuti n’nali munthu wathanzi. N’nali kukonda kucita masewela olimbitsa thupi, mpila wamiyendo wa azimayi komanso masewela ena. N’nali kulimbikilanso kwambili nchito yanga ya zamakompyuta ndipo n’nachuka kwambili cifukwa ca nchitoyi. Zimenezi zinacititsa kuti nizipeza ndalama zambili ndipo anthu anali kuona kuti zinthu zikuniyendela. Koma zoona zinali zakuti n’nali munthu wosasangalala ndipo n’nali kuona kuti cinacake cikusoweka pa moyo wanga.

MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA: N’tayamba kuphunzila Baibo, n’nazindikila kuti Yehova ni Mulungu wacikondi. N’naphunzilanso kuti anasonyeza cikondi cimeneci potipatsa Mawu ake Baibo. Baibo ili ngati kalata ya malangizo imene iye watilembela n’colinga coti azititsogolela pa moyo wathu. (Yesaya 48:17, 18) Conco n’nazindikila kuti ngati nikufuna kuti Yehova azinitsogolela, n’nayenela kusiya makhalidwe onse oipa.

Cinthu cina comwe n’nafunikila kusintha, ni anthu omwe n’nali kuceza nawo. N’nakhudzidwa mtima kwambili na mawu a pa Miyambo 13:20 amene amati: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mfundo imeneyi inanicititsa kuti nisiye kuceza na anthu omwe n’nali kuceza nawo poyamba, n’kuyamba kuceza na anthu a Mboni za Yehova.

Koma vuto lalikulu linali kusiya kusuta, cifukwa khalidwe limeneli linali litanilowelela kwambili. Koma ninayesetsa mpaka n’nasiyadi komano n’nakumananso na vuto lina. Vuto lake linali lakuti n’tasiya kusuta n’nanenepa kwambili. Zimenezi zinali kunicititsa manyazi kwambili moti zinanitengela zaka 10 kuti nicepe thupi kufika pamene n’nali kufuna. Komabe n’nali kuona kuti niyenela kusiya kusuta fodya basi. N’napemphela kwa Yehova kambili-mbili kuti anithandize.

PHINDU LIMENE NAPEZA: Panopa nili na thanzi labwino kuposa kale. Komanso nine wosangalala cifukwa sinikuvutikanso kucita zinthu zambili kuti nipeze cimwemwe cimene anthu amaganiza kuti cimapezeka ukakhala pa nchito yabwino, ukakhala na udindo kapenanso ukakhala na cuma. M’malomwake nikusangalala cifukwa couza ena coonadi copezeka m’Baibo. Zimenezi zacititsa kuti anthu atatu amene n’nali kugwila nawo nchito ndiponso mwamuna wanga ayambe kutumikila Yehova. Komanso makolo anga amene ananilela aja asanamwalile, n’nawauza lonjezo la m’Baibo lonena kuti anthu akufa adzaukitsidwa n’kukhala m’paradaiso padziko lapansi.

Kukhala pa ubwenzi na Yehova kwanithandiza kuti nisiye kudela nkhawa kwambili zoti makolo anga onibeleka ananitaya. Yehova wanithandiza kuona kuti nili m’banja lalikulu la padziko lonse la anthu omwe amamulambila. M’gulu la anthu amenewa napezamo amayi, atate, abale anga, azilongosi, komanso abale anga.—Maliko 10:29, 30.

[Cithunzi]

A Mboni za Yehova anzanga amanisonyeza cikondi cimene Akhristu oona amayenela kukhala naco

[Cithunzi]

Kacisi wacishinto komwe n’nali kupemphela