Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Ufumu umenewu udzalowa m’malo mwa maboma onse ndipo udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba ndi padziko lapansi. Choncho Ufumu wa Mulungu ndi boma labwino kwambiri limene anthufe tikufunikira.​—Werengani Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu yake. Choncho, Yehova anasankha Mwana wake Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu umenewu Mulungu.​—Werengani Luka 1:30-33.

2. N’chifukwa chiyani Yesu ali woyenera kukhala Mfumu?

Mwana wa Mulungu ndi woyenera kukhala Mfumu chifukwa ndi wokoma mtima, amachita zinthu zonse mwachilungamo komanso ali ndi mphamvu zoti angathe kuthandiza anthu. (Mateyu 11:28-30) Yesu ataukitsidwa, anakwera kumwamba ndipo kumeneko anakhala kudzanja lamanja la Yehova kudikira kuti apatsidwe Ufumu. (Aheberi 10:12, 13) Nthawi itakwana, Mulungu anamupatsa mphamvu zoti ayambe kulamulira ali kumwambako.​—Werengani Danieli 7:13, 14.

3. Kodi ndani adzalamulire ndi Yesu?

Anthu amene adzalamulire ndi Yesu kumwamba, amasankhidwa ndi Mulungu ndipo amene Baibulo limawatcha kuti “oyera.” (Danieli 7:27) Anthu oyambirira kusankhidwa kuti akhale m’gulu la oyera, anali atumwi okhulupirika a Yesu. Kuyambira kale, Yehova wakhala akusankha amuna ndi akazi okhulupirika kuti akhale m’gulu la anthu oyera. Anthu amenewa akafa, amaukitsidwa ali ndi thupi lauzimu monga mmene zinachitikira ndi Yesu.​—Werengani Yohane 14:1-3; 1 Akorinto 15:42-45.

Kodi ndi anthu angati amene amapita kumwamba? Yesu ananena kuti anthu amene amapita kumwamba ndi “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Anthu amenewa adzakhalapo okwana 144,000, ndipo iwo limodzi ndi Yesu adzalamulira dziko lapansi.​—Werengani Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1.

4. Kodi Ufumu wa Mulungu unayamba liti kulamulira?

Yesu anakhala Mfumu mu 1914. * Atangokhala Mfumu, anachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba n’kuwaponyera padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-10, 12) Kuyambira nthawi imeneyo, mavuto a anthu padziko lapansi akhala akuwonjezeka kwambiri. Zina mwa zinthu zimene zikusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndi nkhondo, zivomezi, njala, miliri komanso kuphwanya malamulo. (2 Timoteyo 3:1-5) Anthu amene akufuna kudzapeza madalitso a Ufumu wa Mulungu ayenera kuphunzira zimene angachite kuti akhale otsatira a Yesu, yemwe ndi Mfumu.​—Werengani Luka 21:7, 10, 11, 31, 34, 35.

5. Kodi Ufumu wa Mulungu wakwanitsa kuchita chiyani?

Kudzera mu ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse, Ufumu wa Mulungu wayamba kale kuthandiza anthu amitundu yonse kuphunzira zimene Mulungu amafuna. (Mateyu 24:14) Ufumu umenewu udzawononga dongosolo loipa lilipoli ndipo udzapulumutsa “khamu lalikulu la anthu” omwe ndi nzika zokhulupirika za Ufumu wa Mulungu.​—Werengani Chivumbulutso 7:9, 10, 13-17.

Kwa zaka 1,000 Ufumu wa Mulungu udzasintha dziko lapansili pang’onopang’ono mpaka lonse lidzakhala paradaiso. Kenako, Yesu adzabwezera Ufumuwo kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24-26) Kodi pali aliyense amene mungamuuzeko za Ufumu wa Mulungu?​—Werengani Salimo 37:10, 11, 29.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 8 ndi 9 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri zokhudza ulosi wa m’Baibulo umene umasonyeza kuti chaka cha 1914 ndi chimene Yesu anakhala Mfumu, werengani tsamba 215 mpaka 218 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.