Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake

ELIYA anali pa ulendo wake wopita ku Yezereeli ndipo pa nthawiyi n’kuti kunja kukuda komanso kukugwa mvula. Panali padakali ulendo wautali kuti akafike ku Yezereeli komanso anali munthu wachikulire. Ngakhale zinali choncho, iye ankathamanga osatopa chifukwa “dzanja la Yehova” linali naye. Pa nthawiyi, Yehova anali atamupatsa mphamvu zoti sanakhalepo nazo chiyambire moti anathamanga mpaka kupitirira gulu la mahatchi amene ananyamula Mfumu Ahabu pa galeta lake lachifumu.​—1 Mafumu 18:46.

Eliya anapitirira galeta la Mfumu Ahabu lija moti linali m’mbuyo kwambiri. Komabe panali padakali mtunda wautali kuti Eliya akafike ku Yezereeli. Pa nthawi yonse imene Eliya ankathamangayi ayenera kuti ankangoganizira zinthu zosaiwalika zimene zinachitika tsiku limenelo, kwinaku madzi amvula akuyenderera nkhope yake yonse. Tsopano Eliya sakanathanso kuona phiri la Karimeli chifukwa pa nthawiyi n’kuti lili kutali kwambiri ndiponso kunja kunali mitambo ya mvula. N’zosachita kufunsa kuti zimene zinachitika paphiri la Karimeli tsiku limenelo zinachititsa kuti Mulungu wa Eliya atamandidwe komanso zinakweza kulambira koona. Paphiri limeneli ndi pamene Yehova anagwiritsa ntchito Eliya kugonjetsa mwamphamvu komanso mozizwitsa anthu olambira Baala. Aneneri a Baala mazanamazana anadziwika kuti anali achinyengo komanso oipa ndipo anaphedwa. Kenako Eliya anapemphera kwa Yehova kuti chilala chimene chinachitika kwa zaka zitatu ndi hafu chithe. Mulungu anayankhadi pempheroli moti mvula inayamba kugwa. *​—1 Mafumu 18:18-45.

Pamene Eliya ankathamanga pa ulendowu, womwe unali wamakilomita 30, kupita ku Yezereeli ayenera kuti ankaganiza kuti mmene zateremu ndiye kuti zinthu zikhala bwino chifukwa Ahabu asintha. Iye ankaganiza kuti zimene Ahabu anaona pa tsikuli zimuchititsa kuti asiye kulambira Baala, aletse mkazi wake kuchita zinthu zoipa komanso kuti asiye kuzunza atumiki a Yehova.

Zinthu zikatiyendera bwino, mwachibadwa timayamba kuganiza kuti ndiye kuti zipitirizabe kuyenda bwino. Mwinanso timaganiza kuti ngakhale mavuto aakulu amene tinali nawo atha. N’kutheka kuti Eliya anaganizanso choncho chifukwa iye “anali munthu monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Koma chimene Eliya sanadziwe n’choti mavuto ake anali akungoyambika kumene ndipo sanadziwe kuti sipapita nthawi yaitali kuti achite mantha kwambiri komanso akhale ndi nkhawa mpaka kulakalaka kufa. Kodi chinachitika n’chiyani? Kodi Yehova anathandiza bwanji mneneri wakeyu kuti akhalenso ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti ayambirenso kuchita zinthu molimba mtima? Tiyeni tione.

Zinthu Zinasintha Mwadzidzidzi

Kodi Ahabu atafika kunyumba yake yachifumu ku Yezereeli anachita zilizonse zosonyeza kuti wasintha n’kukhala munthu wokonda Mulungu? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Ahabu anauza Yezebeli zonse zimene Eliya anachita, ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.” (1 Mafumu 19:1) Onani kuti pofotokozera mkazi wake zimene zinachitika tsiku limenelo, Ahabu sanatchule Yehova, Mulungu wa Eliya. Iye sankaona zinthu mwauzimu ndipo ankaganiza kuti zodabwitsa zimene zinachitikazo, zinachitika chifukwa cha mphamvu ya Eliya basi. N’chifukwa chake ananena kuti, ‘zimene Eliya wachita.’ Apa n’zoonekeratu kuti Ahabu sanaphunzire kulemekeza Yehova Mulungu. Kodi Yezebeli, yemwe anali ndi mtima wofuna kubwezera, anachita chiyani?

Yezebeli anakwiya kwambiri. Kenako anatumiza uthenga kwa Eliya wonena kuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati pofika nthawi ino mawa sindidzachititsa moyo wako kukhala ngati moyo wa aliyense wa aneneriwo.” (1 Mafumu 19:2) Apatu Yezebeli anaopseza Eliya kuti amupha imfa yowawa kwambiri. Pamenepa Yezebeli analumbira kuti ngati tsiku lingathe asanaphe Eliya, pobwezera imfa ya aneneri a Baala, iyeyo ayenera kufa. Taganizirani mmene Eliya anamvera atadzutsidwa m’kanyumba kamene anagona ku Yezereeli usiku umenewu mphepo ikuwomba, n’kumva uthenga wochititsa mantha umenewu, wochokera kwa Yezebeli mkazi wa mfumu. Kodi Eliya anatani atamva zimenezi?

Anakhumudwa Kwambiri Ndiponso Anachita Mantha

Ngati Eliya ankanyadira kuti nkhondo yolimbana ndi olambira Baala yatha, ndiye kuti anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti si mmene zinthu zinalili. Zimene zinachitikazo sizinapangitse Yezebeli kusintha n’kukhala munthu wabwino. Anthu ambiri okhulupirika ngati Eliya anali ataphedwa kale potsatira zimene Yezebeli analamula ndipo tsopano Eliya anaona kuti nayenso aphedwa basi. Baibulo limanena kuti: “Eliya anachita mantha.” Kodi Eliya ankaona m’maganizo mwake imfa yowawa imene Yezebeli anamukonzera? Ngati iye ankangoganiza kwambiri za imfa imeneyo, n’zosadabwitsa kuti anachita mantha kwambiri. Choncho Eliya ‘anayamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake.’​—1 Mafumu 18:4; 19:3.

Palinso anthu ena amene anali ndi chikhulupiriro ngati Eliya amene pa nthawi ina anachita mantha. Mwachitsanzo, patapita zaka zambiri kuchokera nthawi ya Eliya, mtumwi Petulo nayenso anasonyeza kuti anali ndi mantha. Pamene Yesu anamuuza Petulo kuti ayende naye pamadzi, mtumwiyu anayamba kuyang’ana “mphepo yamkuntho.” Kenako anachita mantha ndipo anayamba kumira. (Mateyu 14:30) Chitsanzo cha Petulo ndi cha Eliya chikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Ngati tikufuna kupitirizabe kuchita zinthu molimba mtima, tiyenera kupewa kumangoganizira zinthu zimene zikutichititsa mantha. Tiyenera kudalira kwambiri Yehova yemwe ndi amene amatipatsa mphamvu komanso chiyembekezo.

“Basi Ndatopa Nazo”

Chifukwa cha mantha, Eliya anayenda ulendo wa makilomita 150 kukafika ku Beere-seba, tauni yomwe inali kufupi ndi kum’mwera kwenikweni kwa dziko la Yuda. Atafika kumeneko, anasiya mtumiki wake ndipo anapita yekha kuchipululu. Nkhaniyi imati iye anayenda “ulendo wa tsiku limodzi.” Choncho, tinganene kuti iye ananyamuka m’mawa dzuwa litangotuluka kumene ndipo ayenera kuti sanatenge chakudya, madzi akumwa kapena chilichonse. Chifukwa cha nkhawa komanso mantha, iye anayenda movutika zedi m’dera lamapiri komanso m’chipululu ndipo pa nthawiyi n’kuti kuli dzuwa loswa mtengo. Pomwe dzuwa linkalowa, n’kuti Eliya atatopa kwambiri. Choncho anakhala pansi pa kamtengo kenakake kopanda mthunzi wambiri komwe anakapeza m’chipululumo.​—1 Mafumu 19:4.

Ndiyeno ali pamenepo, Eliya anapemphera mosonyeza kuti wathedwa nzeru ndipo anapempha Yehova kuti angofa. Iye anati: “Sindine woposa makolo anga.” Iye ankadziwa kuti makolo ake amene anamwalira sangathe kuchita chabwino chilichonse chifukwa anasanduka dothi. (Mlaliki 9:10) Choncho Eliya ankadziona kuti ndi wosafunika ndipo panalibe chifukwa choti azikhalabe ndi moyo. N’chifukwa chake ananena kuti: “Basi ndatopa nazo.”

Kodi n’zodabwitsa kuti munthu wa Mulungu anada nkhawa ndiponso kukhumudwa kwambiri chonchi? Ayi, chifukwa Baibulo limanena za atumiki a Yehova ena amene nthawi ina anavutika maganizo kwambiri moti analakalaka atangofa. Ena mwa anthu amenewa ndi Rabeka, Yakobo, Mose ndi Yobu.​—Genesis 25:22; 37:35; Numeri 11:13-15; Yobu 14:13.

Tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” Choncho n’zosadabwitsa kuona kuti anthu ambiri, ngakhale atumiki a Mulungu, nthawi zina amavutika maganizo kwambiri chifukwa cha zimene amakumana nazo pa moyo wawo. (2 Timoteyo 3:1) Zoterezi zikakuchitikirani, tsanzirani zimene Eliya anachita. Pempherani kwa Mulungu ndi kumuuza nkhawa zanu zonse. Musaiwale kuti Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akorinto 1:3) Kodi Yehova anatonthoza, kapena kuti kulimbikitsa Eliya?

Yehova Anathandiza Mneneri Wake

Kodi mukuganiza kuti Yehova anamva bwanji pamene anayang’ana ali kumwambako n’kuona mneneri wake wokondedwa atagona m’chipululu pansi pa kamtengo akupempha kuti angofa? Kuti tidziwe mmene Yehova anamvera, tiyeni tione zimene zinachitika. Eliya atagona, Yehova anatumiza mngelo. Mngeloyo anadzutsa Eliya mwa kumugwedeza mwachifundo ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye.” Eliya anadzukadi ndipo anadya mkate wotentha ndiponso anamwa madzi amene mngeloyo anamubweretsera. Sitikudziwa ngati Eliya anathokoza mngeloyo chifukwa nkhaniyi imangofotokoza kuti mneneriyu anadya ndi kumwa ndipo atatero anagonanso. N’kutheka kuti Eliya sanathokoze chifukwa chakuti anali atakhumudwa kwambiri moti sankafunanso kulankhula. Komabe patapita nthawi mngeloyo anadzutsanso Eliya kachiwiri ndipo mwina tsopano unali m’bandakucha. Apanso mngeloyo anauza Eliya kuti: “Dzuka udye,” ndipo anawonjezeranso kuti: “Popeza ulendowu wakukulira.”​—1 Mafumu 19:5-7.

Yehova anathandiza mngeloyo kudziwa kumene Eliya ankapita. Mngeloyu anadziwanso kuti, kwa Eliya, ulendo umenewu unali wautali moti sakanatha kuuyenda mwa mphamvu zake zokha. Ndiyetu n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amene timamutumikira amadziwa bwino zolinga zathu komanso zimene sitingakwanitse. (Salimo 103:13, 14) Kodi chakudya chimene Eliya anadya chinamuthandiza bwanji?

Baibulo limati: “ Anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anatha kuyenda masiku 40, usana ndi usiku, mpaka kukafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.” (1 Mafumu 19:8) Eliya anasala kudya kwa masiku 40 usana ndi usiku. Zimenezi ndi zofanana ndi zimenenso Mose anachita zaka pafupifupi 600 m’mbuyomo komanso zimene Yesu anachita patatha zaka pafupifupi 1,000 kuchokera pamene Eliya anamwalira. (Ekisodo 34:28; Luka 4:1, 2) Sikuti chakudya chimene Eliya anadya tsiku limeneli chinathetsa mavuto ake onse, komabe chinamuthandiza mozizwitsa. Tangoganizani, munthu wachikulire ameneyu anayenda movutikira m’chipululu chopanda misewucho tsiku ndi tsiku ndipo anayenda ulendowu kwa pafupifupi mwezi ndi hafu.

Masiku anonso Yehova amathandiza atumiki ake, osati powapatsa chakudya mozizwitsa, koma mwa njira ina yofunika kwambiri kuposa imeneyi. Iye amathandiza atumiki ake mwauzimu. (Mateyu 4:4) Kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, kumatithandiza kuti tipeze zosowa zathu zauzimu. Zinthu zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu ndiponso m’mabuku ofotokoza Baibulo amenewa sizingachititse kuti mavuto athu onse athe, komabe zingatithandize kupirira mavuto amene patokha sitikanatha kuwapirira. Zingatithandizenso kuti tidzapeze “moyo wosatha.”​—Yohane 17:3.

Eliya anayenda makilomita pafupifupi 320 mpaka anakafika kuphiri la Horebe. Kuphiri limeneli ndi kumene, kudzera mwa mngelo, Yehova Mulungu anaonekera kwa Mose m’chitsamba choyaka moto zaka zambiri m’mbuyomo komanso ndi kumene Yehova anachita pangano la Chilamulo ndi Aisiraeli. Atafika paphiri limeneli, Eliya analowa kuphanga.

Mmene Yehova Analimbikitsira Mneneri Wake

Ndiyeno Eliya anamva “mawu” a Yehova kudzera mwa mngelo akumufunsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?” N’zachidziwikire kuti funsoli linafunsidwa mokoma mtima chifukwa linachititsa kuti Eliya afotokoze maganizo ake. Iye anati: “Ndachitira nsanje kwambiri inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu. Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.” (1 Mafumu 19:9, 10) Mawu a Eliya amenewa akusonyeza zinthu zitatu zomwe zinamuchititsa kuti ade nkhawa kwambiri.

Choyamba, Eliya ankaona kuti ntchito yonse imene anagwira inangopita pachabe. Iye ‘anachita nsanje kwambiri’ potumikira Yehova kutanthauza kuti anayesetsa kukweza dzina lopatulika la Mulungu ndiponso anayesetsa kuti anthu adziwe kuti Yehova ndiye Mulungu woyenera kumulambira. Koma ngakhale kuti anachita zonsezi, ankaona kuti zinthu zikungoipiraipira. Anthu anapitirizabe kukhala osakhulupirika komanso opanduka ndipo kulambira konyenga kunali ponseponse. Chachiwiri, Eliya ankaona kuti watsala yekhayekha. Iye ananena kuti: “Ine ndatsala ndekhandekha” ngati kuti pa Aisiraeli onse ndi iye yekha amene anatsala akulambirabe Yehova. Chachitatu, Eliya anali ndi mantha kwambiri chifukwa aneneri anzake anali ataphedwa ndipo iye ankakhulupirira kuti nayenso aphedwa basi. Eliya sanalole kuti kunyada kapena manyazi zimulepheretse kuvomereza kuti umu ndi mmene ankamvera. Iye anapemphera kwa Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo pamenepa anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki onse okhulupirika a Yehova.​—Salimo 62:8.

Eliya atafotokoza zinthu zimene zinkamuchititsa mantha ndiponso kumudetsa nkhawa, kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Mngelo uja anauza Eliya kuti aimirire pakhomo la phanga limene anabisalako. Eliya anachitadi zimenezi ngakhale kuti sankadziwa kuti chichitike n’chiyani. Mwadzidzidzi pamalopa panawomba chimphepo champhamvu. Payenera kuti panamveka chiphokoso chifukwa chimphepocho chinali champhamvu kwambiri moti chinang’amba mapiri ndi matanthwe. Yerekezerani kuti mukuona Eliya akuyesetsa kuphimba nkhope yake kwinaku atagwira mwamphamvu chovala chake chokhuthala chaubweya chomwe chinkauluzika ndi chimphepocho. Komanso akuyesetsa kuti aime bwinobwino n’cholinga chakuti asagwe chifukwa pamalo amene waimawo nthaka ikugwedezeka chifukwa cha chivomezi. Koma pamene chimphepo ndiponso chivomezi chija changotha, nthawi yomweyo pakubuka moto ndipo izi zikuchititsa Eliya kubwerera kuphanga pothawa kutentha kwa motowo.​—1 Mafumu 19:11, 12.

Nkhaniyi imafotokoza kuti Yehova sanali mu zinthu zachilengedwe monga mphepo, chivomezi ndiponso moto zimene Eliya anaonazi. Eliya ankadziwa kuti Yehova si mulungu wongoganiziridwa kuti alipo ngati mmene zinalili ndi Baala amene anthu omwe ankamulambira ankamutamanda kuti ndi “Woyendetsa Mitambo,” kapena wobweretsa mvula. Mphamvu zochititsa mantha zimene zili m’zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, kwenikweni zinachokera kwa Yehova. Koma iye ndi wamkulu kwambiri kuposa chilichonse chimene analenga. Ndipo ngakhale kumwamba kumene timaonaku Yehova sangakwaneko. (1 Mafumu 8:27) Ndiyeno kodi zimene Eliya anaonazi zinamuthandiza bwanji? Kumbukirani kuti Eliya anapezeka pamalo amenewa chifukwa chochita mantha. Popeza kuti Yehova Mulungu anali kumbali ya Eliya, ndipo Eliyayo anaona mphamvu zochititsa mantha za Yehova, panalibe chifukwa chakuti iye aziopa Ahabu ndi Yezebeli.​—Salimo 118:6.

Moto uja utapita, pamalopo panakhala bata ndipo Eliya anamva “mawu achifatse apansipansi.” Mawuwo anali omupempha kuti anenenso maganizo ake ndipo zimenezi zinachititsa kuti kachiwirinso Eliya afotokoze zinthu zomwe zinkamudetsa nkhawa. * Zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsa kwambiri. Komanso mosakayikira, Eliya analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene “mawu achifatse apansipansi” aja anamuuza. Yehova anatsimikizira Eliya kuti ndi munthu wofunika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Mulungu anamuuza kuti nkhondo yothetsa kulambira Baala mu Isiraeli ipitirizabe. Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti ntchito imene Eliya anagwira sinapite m’madzi chifukwa Mulungu anali akuyendetsabe zinthu kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Komanso, Yehova anali akugwiritsabe ntchito Eliya popeza anamupatsa malangizo omveka bwino n’kumutumizanso kuti akagwire ntchito yomweyi.​—1 Mafumu 19:12-17.

Nanga kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya pa vuto lake loona kuti watsala yekhayekha? Iye anachita zinthu ziwiri. Choyamba, anauza Eliya kuti akadzoze Elisa kukhala mneneri amene adzalowe m’malo mwa Eliyayo. Elisa, yemwe pa nthawiyo anali wachinyamata, anali kudzakhala mnzake wa Eliya komanso womuthandiza kwa zaka zambiri. Pamenepatu Yehova anamulimbikitsa kwambiri. Chachiwiri, Yehova anauza Eliya nkhani yabwino kwambiri. Iye anati: “Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli, amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.” (1 Mafumu 19:18) Choncho, Eliya sanatsale yekha. Zimene Yehova ananena zoti panalinso anthu ena okhulupirika masauzande ambiri amene anakana kulambira Baala, ziyenera kuti zinamulimbitsa mtima kwambiri Eliya. Iye anafunika kupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika kuti apereke chitsanzo kwa anthuwo makamaka pa nthawi imeneyi pamene zinthu sizinali bwino. Eliya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kumva “mawu achifatse apansipansi” a Mulungu wake kudzera mwa mngelo.

Mofanana ndi Eliya, ifenso nthawi zina tingachite mantha chifukwa cha mphamvu zoopsa zimene zili m’chilengedwechi. Mphamvu zimene chilengedwechi chimasonyeza ndi umboni wakuti Mlengi ndi wamphamvu kwambiri. (Aroma 1:20) Choncho masiku ano Yehova amagwiritsirabe ntchito mphamvu zake zopanda malirezo pothandiza atumiki ake okhulupirika. (2 Mbiri 16:9) Komabe njira yaikulu imene Mulungu amathandizira anthu ake ndi mwa kulankhula nawo kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (Yesaya 30:21) Choncho, tingati Baibulo lili ngati “mawu achifatse apansipansi” amene Yehova amagwiritsa ntchito masiku ano pofuna kutilangiza, kutilimbikitsa komanso kutitsimikizira kuti amatikonda kwambiri.

Kodi Eliya anaonadi kuti Yehova wamulimbikitsa ndi zimene anamuuza ndiponso zimene anamusonyeza paphiri la Horebe? Inde, chifukwa pasanapite nthawi yaitali, mneneri Eliya anayambiranso kugwira ntchito yake yolimbana ndi kulambira konyenga ndipo anachita zimenezi molimba mtima ndiponso mokhulupirika ngati mmene ankachitira poyamba. Ifenso tikamatsatira mawu ouziridwa a Mulungu, kapena kuti ‘malemba amene amatilimbikitsa,’ tidzatsanzira chikhulupiriro cha Eliya.​—Aroma 15:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani nkhani yakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—Sanasunthike Pakulambira Koona,” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008, ndi yakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—Anali Watcheru Ndiponso Anadikira,” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2008.

^ ndime 29 “Mawu achifatse apansipansi” amenewa ayenera kuti anali a mngelo amene anagwiritsidwanso ntchito kunena “mawu a Yehova” amene ali palemba la 1 Mafumu 19:9. Pa vesi 15 anangomutchula kuti “Yehova.” Zimenezi zingatikumbutse mngelo yemwe Yehova anamugwiritsira ntchito kutsogolera Aisiraeli m’chipululu. Ponena za mngelo ameneyu, Mulungu anati: “Dzina langa lili mwa iye.” (Ekisodo 23:21) Ngakhale kuti Baibulo silinena mwatchutchutchu kuti mngelo amene analankhula ndi Eliya anali Yesu, mfundo yofunika kuidziwa ndi yakuti Yesu asanakhale munthu Yehova ankamugwiritsa ntchito monga “Mawu,” kapena kuti Womulankhulira.​—Yohane 1:1.

[Chithunzi patsamba 19]

Yehova anadalitsa kwambiri Eliya pa nthawi imene zinthu zinali bwino komanso pa nthawi ya mavuto

[Chithunzi patsamba 20]

Pa nthawi imene Eliya anathedwa nzeru, anafotokozera Yehova nkhawa zake mochokera pansi pa mtima

[Chithunzi patsamba 21]

Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake zazikulu kulimbikitsira Eliya