Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

M’munsi mwa Phiri la Moto

M’munsi mwa Phiri la Moto

Kalata Yochokera ku Congo (Kinshasa)

M’munsi mwa Phiri la Moto

UKAKHALA mumzinda wa Goma, dzuwa likamatuluka, kumwamba kumaoneka mitundu yosiyanasiyana yofiirira yokongola kwambiri. Tsiku lililonse timasangalala kuona phiri lochititsa chidwi la Nyiragongo, lomwe lili m’gulu la mapiri apadziko lonse amene amaphulika kawirikawiri. Paphirili pali phanga limene limatulutsa utsi nthawi zonse. Usiku utsiwu umaoneka wofiira chifukwa cha ziphalaphala zotentha zimene zili m’phangalo.

Mu Chiswahili, phirili amalitchula kuti Mulima ya Moto, kutanthauza kuti Phiri la Moto. Kuphulika kwakukulu komaliza kwa phiri la Nyiragongo kunachitika mu 2002. Pa nthawi imeneyo, anzathu ambiri komanso anthu ena amene timakhala nawo pafupi mumzinda wa Goma zinthu zawo zonse zinawonongeka. M’dera lina limene ineyo ndi mwamuna wanga timalalikira, timayenda paziphalaphala zouma zimene zinaphulika m’phiri limeneli ndipo n’zovuta kufotokoza mmene kuyenda paziphalaphala zoumazi kumamvekera. Koma mitima ya anthu a m’derali si youma ngati ziphalaphalazi. Anthuwa ndi amitima yabwino komanso ochezeka ndipo amamvetsera uthenga wabwino umene timalalikira. Zimenezi zimachititsa kuti kutumikira m’munsi mwa Phiri la Moto limeneli, kukhale kosangalatsa kwambiri.

M’mawa wa Loweruka ndinadzuka ndili wosangalala kwambiri chifukwa cha zimene tinkayembekezera kuchita pa tsikulo. Pa tsikuli, ine ndi mwamuna wanga komanso anzathu amene anabwera kudzatichezera ndiponso amishonale ena tinali ndi ulendo wopita kukalalikira kumsasa wina wa anthu othawa kwawo wotchedwa Mugunga. Msasa umenewu uli kumadzulo kwa mzinda wa Goma. Anthu ambiri amene ali pamsasawu anathawa kwawo chifukwa cha ziwawa.

Tinakweza m’galimoto lathu mabuku ophunzitsa Baibulo a m’zinenero za Chifulenchi, Chiswahili, ndi Chinyarwanda ndipo kenako tinanyamuka. Pomwe tinkadutsa msewu wina wamabampu wotchedwa Route Sake, tinaona anthu mumzindawu ali pikitipikiti. Anyamata ambiri ankakankha ngolo zamatabwa zodzaza ndi katundu zomwe amazitchula kuti chukudu. Tinaonanso azimayi ovala masiketi owala atasenza katundu wambirimbiri koma akuyenda bwinobwino. Nawonso a njinga zamoto zahayala anali kalikiliki kunyamula anthu opita kuntchito ndiponso kumsika. M’derali muli nyumba zambiri zamatabwa zopakidwa penti wakuda koma zopaka penti wa buluu m’mbali mwa zitseko ndi mawindo.

Kenako tinafika pa Nyumba ya Ufumu ya Ndosho pomwe tinapeza anzathu ena a Mboni za Yehova amene ankatidikira kuti tipitire limodzi kukalalikira kumsasawo. Ena mwa anthu amenewa anali ana, azimayi komanso ana amasiye ndiponso anthu ena amene anali ndi mavuto osiyanasiyana okhudza thanzi lawo. Zimenezi zinandikhudza mtima kwambiri. Ochuluka mwa anthu amenewa akumana ndi mavuto ambiri pa moyo wawo komabe ali ndi moyo wabwino chifukwa chosankha kutsatira mfundo za m’Baibulo. Iwo amakhulupirira kwambiri malonjezo a m’Baibulo ndipo ndi ofunitsitsa kuuza ena za malonjezowo. Pambuyo pa msonkhano wachidule wokambirana ena mwa malemba amene angakhale olimbikitsa kwa anthu amene tingakumane nawo, anthu tonse okwana 130 tinanyamuka ndipo tinakwera maminibasi 5 komanso galimoto ina ya bokosibode.

Titayenda kwa mphindi pafupifupi 30, tinafika kumsasawo. Pamalowa panali matenti ang’onoang’ono ambirimbiri amene anamangidwa paziphalaphala zoti zinauma. Pakati pa msasawo panali zimbudzi zomangidwa m’mizere yooneka bwino ndiponso malo amene anthu onse amachapirapo. Pamsasawu panali anthu ambirimbiri. Ena anali akuchapa, kuphika, kusenda nyemba ndiponso kusesa panja.

Tinakumana ndi abambo enaake achikulire omwe anthu amawatchula kuti Bambo Jacques ndipo amayang’anira mbali ina ya msasawu. Iwo anali ndi nkhawa ya mmene angalerere ana awo pa nthawi yovuta ngati imeneyi. Anasangalala titawapatsa buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa ndipo ananena kuti awerenga bukuli kenako asonkhanitsa anthu m’timagulu n’kuwauza zomwe awerengazo.

Titayenda pang’ono, tinakumananso ndi mayi ena achikulire omwe anthu amawatchula kuti Mayi Beatrice. Mayiwa anatifunsa chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Iwo ankaona kuti akulangidwa ndi Mulungu. Ankaganiza zimenezi chifukwa chakuti amuna awo anaphedwa pa nkhondo, mwana wawo wamkazi, amene amakhalanso pamsasa womwewu, sali pa banja koma ali ndi mwana wakhanda amene amavutika kumusamalira. Mayiwa alinso ndi mwana wamwamuna amene anabedwa miyezi ingapo yapitayo ndipo sadziwa kuti mwana wawoyo ali kuti.

Nkhani zomvetsa chisoni zimene Mayi Beatrice anatifotokozera zinandipangitsa kuganiza mmene Yobu anamvera atalandira mauthenga onena za zinthu zoipa zimene zinam’chitikira. Tinawafotokozera chifukwa chake timavutika komanso tinawatsimikizira kuti mavuto awowo si umboni woti Mulungu akuwalanga. (Yobu 34:10-12; Yakobo 1:14, 15) Tinawafotokozeranso mmene Ufumu wa Mulungu udzasinthire zinthu padzikoli posachedwapa. Atamva zimenezi, anayamba kumwetulira ndipo anatiuza kuti apitiriza kuphunzira Baibulo ndi kupemphera kwa Mulungu kuti aziwathandiza.

Aliyense amene tinapita naye kumsasa umenewu anasangalala kwambiri. Tinaonanso kuti Yehova watithandiza kwambiri kuti tilimbikitse komanso kupatsa chiyembekezo anthu amene tinawalalikira. Mmene timachoka, anthu ambiri a pamsasawu ananyamula m’mwamba timapepala, magazini komanso mabuku amene tinawagawira kwinaku akutiimikira manja potsanzikana nafe.

Tikubwerera, tinayamba kuganizira zimene zinachitika patsikuli. Tsiku limeneli linali lapadera kwambiri kwa ine. Ndinakumbukira za Bambo Jacques amene anayamikira uthenga umene tinawauza. Ndinakumbukiranso mmene uthenga wathu unathandizira Mayi Beatrice, komanso ndinakumbukira za mayi wina amene anandigwira chanza mwamphamvu n’kumangomwetulira. Ndinakumbukiranso achinyamata amene ankatifunsa mafunso anzeru ngati anthu akuluakulu. Komanso ndinachita chidwi kwambiri kuona anthuwa akumwetulira ndiponso kuseka ngakhale kuti akumana ndi zinthu zoopsa m’moyo wawo.

M’dziko lino muli anthu osiyanasiyana amene amayesetsa ndi mtima wonse kuthandiza anthu omwe akuvutika. Ndipo lero tinali ndi mwayi wogwiritsa ntchito Baibulo posonyeza anthu njira imene Mulungu adzagwiritse ntchito pothetsa mavuto awo onse. Ndikusangalala kwambiri kuti ndikuchita nawo ntchito yofunika kwambiri imeneyi yothandiza anthu mwauzimu, imene siidzabwerezedwanso.