Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuwerenga Baibulo Kwandilimbikitsa pa Moyo Wanga Wonse

Kuwerenga Baibulo Kwandilimbikitsa pa Moyo Wanga Wonse

Kuwerenga Baibulo Kwandilimbikitsa pa Moyo Wanga Wonse

Yosimbidwa ndi Marceau Leroy

TSIKU lina ndinalowa kuchipinda kwanga n’kudzitsekera. Kenako ndinayamba kuwerenga mawu a m’Baibulo akuti: “Pa chiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndinadzitsekera kuchipinda chifukwa chakuti bambo anga sankakhulupirira zoti kuli Mulungu, choncho sakanasangalala kuona ndikuwerenga Baibulo.

Ndinali ndisanawerengepo Baibulo moyo wanga wonse moti mawu amenewo anachititsa thupi langa tsemwe. Ndinaganiza kuti, ‘Apa ndiye ndapeza mayankho a mafunso okhudza chilengedwe chimene ndakhala ndikudabwa nacho.’ Chifukwa chosangalala ndi zimene ndinali kuwerenga, ndinayamba kuliwerenga kuyambira m’ma 8 koloko usiku mpaka 4 koloko m’mawa. Apa m’pamene panayambira chizolowezi changa chowerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Dikirani ndikufotokozereni mmene kuwerenga Baibulo kwandilimbikitsira pa moyo wanga.

“Uzingokhalira Kuliwerenga Tsiku Lililonse”

Ndinabadwa m’chaka cha 1926 m’mudzi wina wotchedwa Vermelles, wokhala ndi mgodi wa malasha kumpoto kwa dziko la France. Pa nthawi imene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inkachitika, malasha anali chinthu chofunika kwambiri m’dziko la France. Ndiye chifukwa choti ndinkagwira ntchito kumgodi wa malasha, sanandikakamize kupita kunkhondo. Ndinayambanso kuphunzira ntchito yokonza mawailesi ndi ya zamagetsi n’cholinga choti ndizipeza ndalama zokwanira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndimvetse mmene mphamvu za m’chilengedwe zimayendera. Ndili ndi zaka 21, mnzanga amene ndimaphunzira naye kalasi imodzi anandipatsa Baibulo n’kunena kuti, “Ndi buku lofunika kuliwerenga.” Aka kanali koyamba kukhala ndi Baibulo. Nditamaliza kuliwerenga kwa nthawi yoyamba, ndinakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu ochokeradi kwa Mulungu.

Poganizira kuti anzanga ena oyandikana nawo nyumba akhozanso kusangalala ndi kuwerenga Baibulo, ndinapeza Mabaibulo ena 8. Koma ndinadabwa kuona kuti anthuwo ankandiseka ndiponso kunditsutsa. Anthu okhulupirira malodza ankanena kuti, “Ukangoyamba kuwerenga buku limeneli uzingokhalira kuliwerenga tsiku lililonse.” Ine ndiye ndinaliwerengadi ndipo sindidandaula chifukwa chochita zimenezi. Chinakhala chizolowezi cha moyo wanga wonse.

Anthu ena ataona kuti ndimakonda kuwerenga Baibulo ankandipatsa mabuku a Mboni za Yehova amene ankalandira. Kabuku monga One World, One Government * (komwe takasonyeza m’Chifalansa) kanafotokoza chifukwa chake Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu ndi wokhawo umene tingaudalire kuti udzathetsa mavuto a anthu. (Mat. 6:10) Kuposa kale ndinatsimikiza mtima kuuza anthu ena za chiyembekezo chimenechi.

Munthu woyamba amene analandira Baibulo nditamupatsa anali mnzanga yemwe ndinkasewera naye tili ana, dzina lake Noël. Popeza iye anali wakatolika, anakonza zoti tikakumane ndi munthu amene ankaphunzira kuti akhale wansembe. Poyamba ndinachita mantha kukakumana naye, koma ndinakumbukira lemba la Salimo 115:4-8 ndi la Mateyu 23:9, 10. Malembawa amanena kuti Mulungu sakondwera ndi kulambira mafano komanso kulemekeza atsogoleri achipembedzo powapatsa mayina aulemu. Kukumbukira malemba amenewa kunandithandiza kuti ndilimbe mtima n’kufotokoza zimene ndinayamba kukhulupirira. Zotsatira zake zinali zakuti Noël anayamba kuphunzira choonadi ndipo ndi Mboni yokhulupirika mpaka pano.

Pa nthawi ina ndinapita kunyumba kwa mchemwali wanga. Mwamuna wake anali ndi mabuku a zamizimu ndipo ziwanda zinkamusowetsa mtendere kwambiri. Ngakhale kuti poyamba ndinkachita mantha, malemba monga Aheberi 1:14, anandithandiza kudziwa kuti angelo a Yehova anali nane. Pamene mlamu wanga anatsatira mfundo za m’Baibulo n’kutaya zinthu zonse zokhudza zamizimu, ziwanda zinasiya kumuvutitsa. Iye ndi mchemwali wanga anakhala Mboni zakhama.

Mu 1947, m’bale wina wochokera ku America dzina lake Arthur Emiot, anafika kunyumba kwanga. Ndinamufunsa kumene a Mboni ankasonkhana. Iye anandiuza kuti kunali kagulu kamene kankasonkhana ku Liévin, ndipo kuti ndikafike kumeneko panali mtunda wa makilomita 10 kuchokera kunyumba kwanga. Nthawi imeneyo kunalibe njinga zofika kumeneko moti kwa miyezi ingapo ndinkayenda wapansi popita ndi pobwera ku misonkhano. Ntchito ya Mboni za Yehova inali italetsedwa kwa zaka 8 ku France. Pa nthawiyi kunali a Mboni 2,380 okha m’dzikoli ndipo ambiri anali ochokera ku Poland. Koma pa September 1, 1947, ntchito yathu inavomerezedwa mwalamulo. Ofesi ya Nthambi inatsegulidwanso ku Villa Guibert mumzinda wa Paris. Chifukwa chakuti ku France kunalibe mpainiya ndi mmodzi yemwe, mu December 1947 Utumiki Wathu wa Ufumu (pa nthawiyo unkatchedwa Informant) unali ndi nkhani yopempha anthu kuti ngati angakwanitse achite upainiya wokhazikika ndipo azilalikira maola 150 pa mwezi. (Mu 1949 chiwerengero cha maola chinachepetsedwa kufika pa 100.) Nditamvetsa mawu a Yesu a pa Yohane 17:17 akuti “Mawu [a Mulungu] ndiwo choonadi,” ndinabatizidwa mu 1948, ndipo mu December 1949, ndinayamba upainiya.

Kuchoka Kundende N’kubwereranso ku Dunkerque

Malo omwe ndinatumikira koyamba anali mumzinda wa Agen, kum’mwera kwa France, koma sindinakhalitseko. Kusiya ntchito ya kumgodi kunapangitsa kuti akuluakulu a boma andikakamize kupita kunkhondo. Ndinakana kulowa ntchito ya usilikali choncho ananditsekera kundende. Ngakhale kuti sindinkaloledwa kukhala ndi Baibulo, ndinapeza masamba angapo a buku la Masalimo. Kuwerenga masamba amenewa kunkandilimbikitsa kwambiri. Nditatuluka m’ndende ndinkadzifunsa kuti: Kodi ndisiye utumiki wa nthawi zonse kuti ndikhazikike bwinobwino? Pamenepanso zimene ndinawerenga m’Baibulo zinandithandiza. Ndinaganizira mawu a Paulo omwe ali pa Afilipi 4:11-13, akuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” Ndinaona kuti ndi bwino kupitiriza upainiya. Mu 1950, ndinatumizidwanso ku tauni ya Dunkerque komwe ndinkalalikira poyamba paja.

Pamene ndinkafika ku Dunkerque n’kuti ndilibe chilichonse. Tauniyo inali itasakazidwa kwadzaoneni pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndipo nyumba zinkasowa. Ndinaganiza zopita kukaona banja lina limene ndinkaphunzira nalo Baibulo. Mayi wa kumeneko atandiona anasangalala kwambiri. Iye ananena kuti: “Bambo Leroy, ndasangalala kwambiri kuti mwabwerako kundende. Mwamuna wanga amanena kuti kukanakhala kuti dziko lonse lili ndi anthu ngati inuyo, sibwenzi kutachitika nkhondo.” Banjali linali ndi nyumba yogona alendo choncho anandiuza kuti ndizikhalamo mpaka nyengo imene alendo amabwera kudzaona malo. Tsiku lomwelo, mchimwene wake wa Arthur Emiot, dzina lake Evans, anandipezera ntchito. * Evans ankagwira ntchito yomasulira padoko ndipo ankafuna munthu woti azilondera sitima usiku. Iye anandipititsa kwa bwana wina wa pamalopo. Pa nthawi yomwe ndinkatuluka kundende ndinali nditaonda kwambiri moti ndinali mafupa okhaokha. Evans atafotokoza chifukwa chake ndinali woonda choncho, bwanayo anandiuza kuti njala ikandiwawa ndizitenga zakudya m’firiji n’kumadya. Tangoganizani, tsiku limodzi lokha ndinapeza malo ogona, ntchito ndi chakudya. Izi zinachititsa kuti ndikhulupirire kwambiri mawu a Yesu a pa Mateyu 6:25-33.

Nthawi imene alendo ambiri amabwera kudzaona malo itafika, ine ndi mnzanga yemwe tinkachitira limodzi upainiya, dzina lake Simon Apolinarski, tinafunika kuchoka pamalowa. Komabe tinatsimikiza kuti ngakhale zili choncho tizikhalabe m’tauni yomweyo. Tinapatsidwa malo ogona m’kanyumba kena komwe kanali khola la mahatchi ndipo tinkagona pa udzu wodyetsera mahatchi. Tinkathera nthawi yaitali mu utumiki. Tinalalikira kwa mwini wake wa kakholako ndipo anali mmodzi mwa anthu ambiri amene anaphunzira choonadi. Pasanapite nthawi yaitali, m’nyuzipepala munatuluka nkhani yochenjeza anthu ku Dunkerque kuti asamale ndi Mboni za Yehova chifukwa zinkayenda paliponse. Komatu Mboni tinangokhala ine, Simon ndi ofalitsa ena ochepa kwambiri. Tikakumana ndi mavuto, tinkalimbikitsidwa tikaganizira za chiyembekezo chathu ndiponso mmene Yehova watisamalirira. Pa nthawi imene ndinkachoka ku Dunkerque mu 1952 kunali apainiya okhazikika pafupifupi 30.

Baibulo Linandilimbikitsa Kuti Ndisamalire Maudindo Ena

Nditakhala kwa nthawi yochepa mumzinda wa Amiens, ndinapemphedwa kuti ndikatumikire monga mpainiya wapadera ku Boulogne-Billancourt, kadera komwe kali chapafupi ndi mzinda wa Paris. Ndinali ndi maphunziro a Baibulo ambiri ndipo ena anayamba utumiki wa nthawi zonse ndi umishonale. Mnyamata wina dzina lake Guy Mabilat, anaphunzira choonadi ndipo anadzakhala woyang’anira dera ndipo kenako anadzakhala woyang’anira chigawo. Kenako anadzakhala woyang’anira ntchito yomanga nyumba yosindikizira mabuku. Panopa nyumbayi anaisandutsa Beteli ndipo ili ku Louviers pafupi ndi mzinda wa Paris. Kukambirana Baibulo ndi anthu mu utumiki kwakhomereza Mawu a Mulungu m’maganizo mwanga ndipo kwandipangitsa kuti ndikhale wosangalala komanso kuti ndiziphunzitsa mwaluso.

Ndiyeno mosayembekezereka, mu 1953 ndinapemphedwa kukhala woyang’anira dera ku Alsace-Lorraine. Dera limeneli linalandidwa kawiri ndi dziko la Germany m’zaka za pakati pa 1871 ndi 1945. Choncho ndinafunika kuphunzira Chijeremani. Pamene ndinkayamba ntchito yoyang’anira dera, n’kuti zinthu monga magalimoto, ma TV, makina olembera, mawailesi ndiponso makompyuta zili zochepa m’derali. Komabe moyo wanga sunali wosasangalatsa kapena wotopetsa. Ndipo imeneyi inali nthawi yosangalatsa kwambiri pa moyo wanga. Pa nthawiyo, zinali zosavuta kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizikhala ndi ‘diso lolunjika pa chinthu chimodzi’ chifukwa zinthu zosokoneza munthu kutumikira Yehova zinali zochepa tikayerekezera ndi masiku ano.​—Mat. 6:19-22.

Sindiiwala zimene zinachitika pa msonkhano wakuti “Ufumu Wolakika,” womwe unachitikira mumzinda wa Paris mu 1955. Kumeneko ndi kumene ndinakumana ndi Irène Kolanski yemwe anadzakhala mkazi wanga. Iye anali atayamba utumiki wa nthawi zonse chaka chimodzi ineyo ndisanayambe. Makolo ake anali ochokera ku Poland ndipo anali Mboni zokhulupirika kwa nthawi yaitali. Ali ku France anayenderedwapo ndi m’bale Adolf Weber. M’bale ameneyu ankasamalira maluwa kunyumba ya m’bale Russell ndipo anabwera ku Ulaya kudzalalikira uthenga wabwino. Ine ndi Irène tinakwatirana mu 1956 ndipo tinayamba kuyendera limodzi m’dera. Iye wakhala akundithandiza kwambiri pa zaka zonsezi.

Patadutsa zaka ziwiri ndinapatsidwa mwayi wotumikira monga woyang’anira chigawo. Koma popeza kunalibe abale oyenerera okwanira, ndinkayenderabe mipingo ina monga woyang’anira dera. Ndinkakhala wotanganidwa kwambiri. Kuwonjezera pa kulalikira maola 100 pa mwezi, mlungu uliwonse ndinkafunika kukamba nkhani, kuyendera magulu atatu a maphunziro a buku a mpingo, kuona mafaelo a mpingo ndiponso kulemba lipoti. Ndiye pamenepa nthawi yowerenga Baibulo ndinkaipeza kuti? Ndinapeza njira imodzi yondithandiza. Ndinkathothola masamba angapo a Baibulo lakale n’kumayenda nawo. Ndikamadikira munthu wina amene ndapangana naye, ndinkawerenga masambawo. Zimenezi zinkandilimbikitsa kwambiri kuti ndisasiye utumiki wanga.

Mu 1967 ine ndi Irène tinaitanidwa kukakhala ku Beteli ku Boulogne-Billancourt. Ndinayamba kutumikira m’Dipatimenti ya Utumiki ndipo ndakhala ndikutumikira m’dipatimenti imeneyi kwa zaka 40. Chimene chimandisangalatsa pa utumiki wangawu ndi kuyankha makalata ofunsa mafunso okhudza Baibulo. Ndimasangalala kwambiri kufufuza m’Mawu a Mulungu ndi “kuteteza uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Ndimasangalalanso kutsogolera pulogalamu yauzimu yam’mawa tisanayambe kudya. Mu 1976 ndinasankhidwa kukhala m’Komiti ya Nthambi ya ku France.

Imeneyi Ndi Njira Yokhalira ndi Moyo Wabwino

N’zoona kuti ndakumana ndi mavuto ambiri, koma panopa ukalamba ndiponso matenda zimandisowetsa mtendere chifukwa chakuti ine ndi Irène sitithanso kuchita zambiri. Komabe kuwerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu limodzi kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo. Timasangalala kukwera basi n’kupita kugawo la ku mpingo wathu kukauza ena za chiyembekezo chathuchi. Tikaphatikiza zaka zimene tonse takhala tili mu utumiki wa nthawi zonse zikukwana zaka zoposa 120. Zimene takumana nazo pa zaka zimenezi zimatichititsa kulimbikitsa ndi mtima wonse anthu amene akufuna kuyamba moyo wosangalatsa ndiponso waphindu umenewu. Pamene Mfumu Davide ankalemba mawu a pa Salimo 37:25 anali ‘atakula’ ndipo sanaonepo “munthu aliyense wolungama atasiyidwa.” Inenso ndakula ndipo sindinaonepo zimenezi.

Pa moyo wanga wonse, Yehova wakhala akundilimbikitsa ndi Mawu ake. Zaka 60 zapitazo, achibale anga ananena kuti ndizidzangokhalira kuwerenga Baibulo moyo wanga wonse. Ankanenadi zoona. Ndakhala ndikuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo sindinadandaulepo chifukwa cha zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kofalitsidwa mu 1944, koma panopa sikakusindikizidwanso.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya Evans Emiot, werengani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1999, tsamba 22 ndi 23.

[Chithunzi patsamba 5]

Ine ndi Simon

[Chithunzi patsamba 5]

Ndikutumikira monga woyang’anira chigawo

[Chithunzi patsamba 5]

Baibulo lofanana ndi limene ndinalandira koyamba

[Chithunzi patsamba 6]

Pa tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 6]

Ine ndi Irène timakonda kuwerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu