Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukulola Yehova Kukhala Cholowa Chanu?

Kodi Mukulola Yehova Kukhala Cholowa Chanu?

Kodi Mukulola Yehova Kukhala Cholowa Chanu?

“Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”​—MAT. 6:33.

1, 2. (a) Kodi “Isiraeli wa Mulungu” wotchulidwa pa Agalatiya 6:16 akuimira ndani? (b) Nanga kodi “mafuko 12 a Isiraeli” otchulidwa pa Mateyu 19:28 akuimira ndani?

KODI mukawerenga dzina loti Isiraeli m’Baibulo mumaganizira za ndani? Kodi mumaganizira za Yakobo amene anadzatchedwa Isiraeli? Kapena mumaganizira za mtundu wa Isiraeli womwe unali mbadwa za Yakobo? Koma Baibulo limanenanso za Isiraeli wauzimu kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu.” Mawu amenewa amanena za anthu 144,000 odzozedwa ndi mzimu woyera. Anthu amenewa adzakhala mafumu ndiponso ansembe kumwamba. (Agal. 6:16; Chiv. 7:4; 21:12) Komabe, pa Mateyu 19:28 Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti Isiraeli m’njira inanso yapadera.

2 Yesu ananena kuti: “Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.” Mawu akuti “mafuko 12 a Isiraeli” pa lembali akuimira anthu amene adzalandire moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Anthu amenewa adzaweruzidwa ndi ophunzira a Yesu odzozedwa 144,000 amene azidzatumikira monga ansembe.

3, 4. Kodi odzozedwa okhulupirika amapereka chitsanzo chabwino chiti?

3 Mofanana ndi ansembe komanso Alevi akale, odzozedwa amaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira Yehova. (Num. 18:20) Odzozedwa sayembekezera kuti apatsidwe malo enieni padzikoli ngati cholowa chawo. M’malomwake, lemba la Chivumbulutso 4:10, 11 limasonyeza kuti iwo adzapitiriza kutumikira Yehova kumwamba ndipo kumeneko akakhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Yesu Khristu.​—Ezek. 44:28.

4 Pa nthawi imene ali padziko lapansi, moyo wa odzozedwawa umasonyeza kuti Yehova ndi cholowa chawo. Iwo amaona kuti kutumikira Mulungu ndi mwayi wa mtengo wapatali. Amakhulupiriranso nsembe ya dipo ya Khristu ndi kumutsatira nthawi zonse. Chifukwa chochita zimenezi, ‘amapitiriza kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha.’ (2 Pet. 1:10) Zimene odzozedwa ena amakwanitsa kuchita ndi zosiyana ndi zimene ena amakwanitsa. Komabe iwo salola kuti zimene amalephera kuchita ziwasiyitse kutumikira Mulungu mwakhama. M’malomwake iwo amaonetsetsa kuti kutumikira Mulungu kuzikhala patsogolo pa moyo wawo. Iwo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu amene adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi.

5. Kodi Akhristu onse angasonyeze bwanji kuti Yehova ndi cholowa chawo, ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungakhale kovuta?

5 Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tiyenera ‘kudzikana tokha ndi kunyamula mtengo wathu wozunzikirapo ndipo timutsatire Khristu mosalekeza.’ (Mat. 16:24) Anthu ambirimbiri amene akuyembekezera moyo padziko lapansi la Paradaiso, akulambira Mulungu ndiponso kutsatira Khristu m’njira imeneyi. Iwo sakhutira ndi kungochita zinthu zochepa ngati akuona kuti akhoza kuchita zambiri kuposa zimenezo. Ambiri asintha zinthu pa moyo wawo kuti achite upainiya. Ena amakwanitsa kuchita upainiya miyezi ina pachaka. Komabe anthu ena amene sangakwanitse kuchita upainiya amayesetsa kuchita zambiri mu utumiki. Anthu oterewa ndi odzipereka ngati Mariya, yemwe anathira m’mutu mwa Yesu mafuta onunkhira kwambiri. Yesu anamuyamikira ponena mawu akuti: “Iyetu wandichitira zinthu zabwino. . . . Mayiyu wachita zimene angathe.” (Maliko 14:6-8) Komabe kuchita zimene tingathe kungakhale kovuta chifukwa chakuti tikukhala m’dziko lolamuliridwa ndi Satana. Ngakhale zili choncho, timachita khama kwambiri ndipo timadalira Yehova. Tiyeni tikambirane njira zinayi za mmene tingachitire zimenezi.

Kufunafuna Ufumu Choyamba

6. (a) Kodi anthu m’dzikoli asonyeza motani kuti cholowa chawo chili m’moyo uno basi? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutengera chitsanzo cha Davide?

6 Yesu anauza otsatira ake kuti azifunafuna choyamba Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu. Masiku ano anthu amangokhalira kufunafuna zosowa zawo zakuthupi. Ponena za anthu amenewa, Baibulo limati iwo ndi “anthu a m’nthawi ino, amene gawo lawo lili m’moyo uno.” (Werengani Salimo 17:1, 13-15.) Anthu ambiri saganizira n’komwe za Mlengi wawo. Iwo amatanganidwa ndi kufunafuna chuma kuti azikhala moyo wa wofuwofu. Amatanganidwanso ndi kusamalira banja lawo ndiponso kuti apeze zinthu zodzasiyira ana awo. Cholowa cha anthu amenewa chili m’moyo uno basi. Koma Davide ankafuna kukhala ndi “mbiri yabwino” kwa Yehova ndipo mwana wake Solomo anati tonsefe tiyenera kutengera chitsanzo chimenechi. (Mlal. 7:1) Mofanana ndi Asafu, Davide sankaika zofuna zake patsogolo. Koma ankaona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kofunika kwambiri. Iye ankasangalala kuyenda ndi Mulungu. Masiku ano, Akhristu ambiri amaika patsogolo zinthu zauzimu osati ntchito yawo.

7. Kodi m’bale wina anadalitsidwa bwanji chifukwa choika Ufumu patsogolo?

7 Taganizirani za Jean-Claude wa ku Central African Republic. Iye ndi wokwatira, ali ndi ana atatu ndipo ndi mkulu. M’dziko limeneli ntchito n’zosowa kwambiri ndipo anthu ambiri amachita chilichonse chimene angathe kuti ntchito isawathere. Tsiku lina Jean-Claude anauzidwa ndi abwana ake kuti ayambe kugwiranso ntchito usiku kuyambira 6:30 tsiku lililonse. Jean-Claude anafotokozera abwana akewo kuti amafunika kusamalira banja lake mwakuthupi komanso mwauzimu. Iye anawauzanso kuti ali ndi udindo wosamalira mpingo. Kodi mukudziwa zimene abwana akewo ananena? Anati: “Ngati munthu wapeza ntchito ayenera kuiwala zonse kuyambira mkazi wake, ana ake ndiponso mavuto ake. Ayenera kudzipereka pa ntchito. Sayenera kuganiziranso china chilichonse koma ntchito basi. Ndiye usankhe chimodzi, chipembedzo kapena ntchito.” Kodi mukanakhala inuyo mukanatani? Jean-Claude anadziwa kuti akachotsedwa ntchito, Mulungu adzamusamalira. Iye akanakhalabe ndi zochita zambiri potumikira Mulungu ndipo Yehova akanamuthandiza kusamalira banja lake. Choncho anapita ku misonkhano ya mkati mwa mlungu umenewo. Kenako anakonzeka kuti azipita kuntchito koma akukayikira zoti akapitiriza ntchito. Ndiyeno nthawi yomweyo analandira foni yonena kuti bwana wakeyo wachotsedwa ntchito koma m’baleyu akupitiriza ntchito yake.

8, 9. Kodi tingatsanzire bwanji ansembe ndi Alevi polola Yehova kukhala cholowa chathu?

8 Anthu ena akaona kuti ntchito iwathera amada nkhawa n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndizidzasamalira bwanji banja langa?’ (1 Tim. 5:8) Kaya mwakumanapo ndi vuto ngati limeneli kapena ayi, muyenera kuti mumadziwa kuti ngati munthu alola Mulungu kukhala cholowa chake ndiponso ngati amaona kutumikira Mulungu kukhala chinthu chamtengo wapatali, sadzagwiritsidwa mwala. Pamene Yesu anauza otsatira ake kuti pitirizani kufunafuna ufumu choyamba, anawatsimikizira kuti ‘zina zonse’ monga chakudya ndi zovala ‘zidzawonjezedwa kwa iwo.’​—Mat. 6:33.

9 Taganizirani za Alevi amene sankalandira cholowa cha malo. Popeza kuti kulambira koyera kunali chinthu chofunika kwambiri kwa iwo, ankafunika kudalira Yehova kuti apeze zofunika pa moyo wawo. Yehova anawauza kuti: ‘Ine ndine cholowa chanu.’ (Num. 18:20) Ngakhale kuti ifeyo sitikutumikira m’kachisi weniweni ngati mmene ansembe ndi Alevi ankachitira, tikhoza kuwatsanzira pokhulupirira kuti Yehova adzatisamalira. Pamene tili mkatikati mwa masiku otsiriza m’pamenenso tikufunika kudalira kwambiri Mulungu kuti atipatsa zofunika pa moyo wathu.​—Chiv. 13:17.

Kufunafuna Choyamba Chilungamo cha Mulungu

10, 11. Kodi anthu ena asonyeza bwanji kuti amadalira Yehova posankha ntchito? Perekani chitsanzo.

10 Yesu analimbikitsanso ophunzira ake ‘kupitiriza kufunafuna choyamba chilungamo chake.’ (Mat. 6:33) Izi zikutanthauza kuti m’malo motsatira maganizo a anthu, timatsatira maganizo a Yehova pa nkhani ya zabwino kapena zoipa. (Werengani Yesaya 55:8, 9.) Mwina mungakumbukire kuti anthu ena m’mbuyomu ankalima ndiponso kugulitsa fodya. Ena ankaphunzitsa anthu kumenya nkhondo kapena kukonza ndi kugulitsa zida zankhondo. Koma ataphunzira choonadi, ambiri anasintha ntchito zawo kuti ayenerere ubatizo.​—Yes. 2:4; 2 Akor. 7:1; Agal. 5:14.

11 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Andrew. Pamene iye ndi mkazi wake anaphunzira za Yehova anatsimikiza mtima kumutumikira. Andrew ankakonda kwambiri ntchito yake koma anaisiya. Kodi n’chifukwa chiyani anaisiya? N’chifukwa choti ankagwira ntchito m’bungwe limene linkakonza zida zankhondo. Koma ankafunitsitsa kuika chilungamo cha Mulungu patsogolo. Pamene ankasiya ntchitoyi anali ndi ana awiri koma anali ndi tindalama tochepa kwambiri tongokwanira kudya miyezi yowerengeka. Malinga ndi kuona kwa anthu iye analibe ‘cholowa.’ Iye anayamba kufufuza ntchito ndipo ankadalira kwambiri Mulungu. Akaganizira zimene zawachitikira m’mbuyomu, iye ndi banja lake amakhulupirira kuti dzanja la Yehova si lalifupi. (Yes. 59:1) Chifukwa cha moyo wawo wosalira zambiri, Andrew ndi mkazi wake akhala ndi mwayi wochita utumiki wa nthawi zonse. Iye anati: “Nthawi zina timada nkhawa chifukwa cha kusowa ndalama, kusowa pokhala, kudwala ndiponso ukalamba. Koma Yehova wakhala akutisamalira ndipo sanatisiye. . . . Tinganene mosakayika kuti kutumikira Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri ndiponso chopindulitsa.” *​—Mlal. 12:13.

12. Kodi munthu amafunikira kukhala ndi khalidwe liti kuti afunefune chilungamo cha Mulungu? Perekani chitsanzo cha komwe mukukhala.

12 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.” (Mat. 17:20) Kodi ndinu okonzeka kutsatira mfundo za Mulungu ngakhale pamene mukuona kuti mukumana ndi mavuto? Ngati mukukayikira kuti mukhoza kuchita zimenezi, mungalankhule ndi anthu ena mu mpingo wanu. Mudzalimbikitsidwa kwambiri kumva zimene akumana nazo pa moyo wawo.

Kuyamikira Zinthu Zauzimu Zimene Yehova Amatigawira

13. Tikamachita khama potumikira Yehova, kodi tidzapeza madalitso auzimu otani?

13 Ngati mumaona kuti kutumikira Yehova ndi mwayi waukulu, muyenera kukhulupirira kuti adzakusamalirani mwakuthupi ndi mwauzimu ngati mmene anachitira ndi Alevi. Taganizirani chitsanzo cha Davide. Ngakhale kuti anali m’phanga, iye ankadalira Mulungu kuti amusamalira. Ifenso tingadalire Yehova ngakhale pamene tikuona kuti tikusowa mtengo wogwira. Kumbukirani kuti Asafu atalowa “m’malo opatulika aulemerero a Mulungu,” anamvetsa zimene zinkamusowetsa mtendere. (Sal. 73:17) Nafenso tiyenera kudalira Mulungu amene amatipatsa chakudya chathu chauzimu. Choncho kaya tikumane ndi zotani tiyenera kuyamikira mwayi wathu wotumikira Mulungu. Tikamatero ndiye kuti tikulola Yehova kukhala cholowa chathu.

14, 15. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati zimene zinafotokozedwa m’mbuyomu pa malemba ena zasintha, ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Kodi mumatani ngati Yehova yemwe ndi Gwero la chakudya chathu chauzimu watiululira “zinthu zozama za Mulungu” zopezeka m’Baibulo? (1 Akor. 2:10-13) Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi zimene mtumwi Petulo anachita pamene Yesu anauza anthu kuti: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, mulibe moyo mwa inu.” Ophunzira a Yesu ambiri amene anaganiza kuti mawu amenewa ankatanthauza kudya mnofu weniweni ndi kumwa magazi a Yesu enieni anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?” Choncho iwo “anamusiya ndi kubwerera ku zinthu zakumbuyo.” Koma Petulo anati: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”​—Yoh. 6:53, 60, 66, 68.

15 Petulo sanamvetse tanthauzo la mawu a Yesu onena za kudya mnofu wake ndi kumwa magazi ake. Komabe mtumwiyu anadalira kwambiri Mulungu kuti amuululire zinthu zauzimu. Ngati zimene zinafotokozedwa pa lemba lina m’mbuyomu zasintha, kodi mumayesetsa kuti mumvetse chifukwa chake pali kusintha? (Miy. 4:18) M’nthawi ya atumwi anthu a ku Bereya “analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku anali kufufuza Malemba mosamala.” (Mac. 17:11) Mukamatsanzira anthu amenewa mudzayamba kuyamikira kwambiri mwayi wanu wotumikira Yehova ndipo iye adzakhala cholowa chanu.

Muzikwatira Kapena Kukwatiwa mwa Ambuye

16. Kodi Mulungu angakhale bwanji cholowa chathu tikamatsatira lamulo lopezeka pa 1 Akorinto 7:39?

16 Mbali ina imene Akhristu angasonyezere kuti amaganizira zolinga za Mulungu ndiyo kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Ambiri asankha kusakwatira kapena kusakwatiwa m’malo monyalanyaza malangizo a Mulungu amenewa. Mulungu amasamalira anthu oterewa mwachifundo. Kodi Davide anatani pa nthawi imene anali yekhayekha n’kumadzimva kuti alibe womuthandiza? Iye anati: “Ndinapitirizabe kumukhuthulira [Mulungu] nkhawa zanga. Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga. Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga unalefuka.” (Sal. 142:1-3) N’kutheka kuti mneneri Yeremiya, amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri asanakwatire, analinso ndi maganizo amenewo. Mungachite bwino kuphunzira nkhani yake m’mutu 8 wa buku lakuti, God’s Word for Us Through Jeremiah.

17. Kodi mlongo wina amene ndi wosakwatiwa amachita chiyani akayamba kusungulumwa?

17 Mlongo wina wosakwatiwa wa ku United States anati: “Si cholinga changa kukhala wosakwatiwa. Ndine wokonzeka kukwatiwa ndikapeza m’bale woyenerera. Mayi anga si mboni ndipo ankandiuza kuti ndingokwatiwa ndi mwamuna wina aliyense. Ndinawafunsa kuti ‘ngati banja langa lingadzavute kodi mungadzandithandize?’ Patapita nthawi ataona kuti ndapeza ntchito yabwino, ndikutha kudzisamalira ndiponso ndikukhala wosangalala, anasiya kundivutitsa.” Nthawi zina mlongo ameneyu amasungulumwa ndithu. Koma ananena kuti, “Ndikayamba kusungulumwa ndimakhulupirira Yehova ndipo iye sandisiya.” Kodi n’chiyani chomwe chamuthandiza kuti azikhulupirira Yehova? Iye anati: “Pemphero limandithandiza kuona kuti Mulungu ndi weniweni ndiponso kuti sindili ndekha. Ngati Wam’mwambamwamba amandimvetsera, kodi pali chifukwa choti ndizimva kuti ndine wonyozeka kapena ndizikhala wosasangalala?” Iye amakhulupirira kuti, “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” Iye anati: “Ndimadzipereka kuti ndithandize anthu ena ndipo sindiyembekezera kuti nawonso andichitire zomwezo. Ndimasangalala kwambiri ndikamafufuza njira zoti ndithandizire munthu wina.” (Mac. 20:35) Mlongoyu walola Yehova kukhala cholowa chake ndipo akusangalala ndi mwayi womutumikira.

18. Kodi mungakhale bwanji cholowa cha Yehova?

18 Kaya mukukumana ndi zotani pa moyo wanu, mukhoza kulola Mulungu kukhala cholowa chanu. Izi zidzachititsa kuti mukhale m’gulu la anthu ake osangalala. (2 Akor. 6:16, 17) Mukatero inunso mungakhale cholowa cha Yehova ngati mmene zinalili ndi anthu ena m’mbuyomu. (Werengani Deuteronomo 32:9, 10.) Mulungu anasankha mtundu wa Isiraeli kukhala cholowa chake, choncho akhozanso kusankha inuyo kukhala cholowa chake ndi kukusamalirani bwino kwambiri.​—Sal. 17:8.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi mungatani kuti Yehova akhale cholowa chanu m’mbali zotsatirazi,

• pofunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake?

• poyamikira chakudya chauzimu chimene amatigawira?

• pomvera lamulo la Mulungu la kukwatira kapena kukwatiwa mwa Ambuye?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Yehova amakhala cholowa chathu ngati timaona kumutumikira kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu

[Chithunzi patsamba 15]

Chitsanzo cha Yeremiya n’cholimbikitsa kwambiri