Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Thamangani N’cholinga Choti Mukalandire Mphoto’

‘Thamangani N’cholinga Choti Mukalandire Mphoto’

‘Thamangani N’cholinga Choti Mukalandire Mphoto’

“Thamangani m’njira yoti mukalandire mphotoyo.”​—1 AKOR. 9:24.

1, 2. (a) Kodi Paulo anagwiritsira ntchito chiyani pofuna kulimbikitsa Akhristu achiheberi? (b) Kodi atumiki a Mulungu akulimbikitsidwa kuchita chiyani?

M’KALATA yake yopita kwa Aheberi, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo logwira mtima pofuna kulimbikitsa Akhristu anzake. Iye anawakumbutsa kuti sanali okha pa mpikisano wokalandira moyo. Iwo anali atazunguliridwa ndi ‘mtambo wa mboni waukulu,’ womwe unapambana mpikisanowo bwinobwino. Kukumbukira zinthu zosonyeza chikhulupiriro zimene anthu amenewa anachita ndiponso khama lawo kukanathandiza Akhristu achiheberi kuti alimbikire kuthamanga. Kukanawathandizanso kuti ayesetse kusabwerera m’mbuyo pa mpikisano wawo.

2 M’nkhani yapita tinakambirana za moyo wa anthu angapo amene ali m’gulu la “mtambo wa mboni.” Iwo ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo izi zinawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa iye mpaka mapeto a moyo wawo. Iwo anamaliza nawo mpikisanowo mpaka kulandira mphoto. Nanga kodi tingatani kuti nafenso tithamange nawo mpikisanowu mpaka kumapeto? Paulo ananena kuti: “Tiyeninso tivule cholemera chilichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta lija. Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.”​—Aheb. 12:1.

3. Kodi Akhristu angaphunzire chiyani pa malangizo amene Paulo ananena okhudza mpikisano wothamanga umene Agiriki ankachita?

3 Ponena za mipikisano ya nthawi imeneyo, buku lina limati: “Agiriki ankakonzekera ndiponso kuchita mpikisano wothamanga ali maliseche.” * (Backgrounds of Early Christianity) Pa mipikisano imeneyi, iwo ankavula chinthu chilichonse chomwe chingawalepheretse kuthamanga bwinobwino kapena chimene chingawachedwetse. Masiku ano kuthamanga chonchi kungakhale kochititsa manyazi. Koma iwo ankachita zimenezi n’cholinga choti alandire mphoto basi. Choncho pamene Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti ‘avule cholemera chilichonse,’ ankatanthauza kuti asiye chinthu chilichonse pa moyo wawo chimene chingawalepheretse kulandira mphoto ya moyo wosatha. Malangizo amenewa anali othandiza kwambiri kwa Akhristu pa nthawiyo ndipo ndi othandizanso masiku ano. Kodi ndi zinthu zolemera ziti zimene zingatilepheretse kulandira mphoto ya moyo wosatha?

“Tivule Cholemera Chilichonse”

4. Kodi anthu m’masiku a Nowa ankasokonezedwa ndi zinthu ziti?

4 Paulo ananena za ‘kuvula cholemera chilichonse.’ Zinthu zolemera zimenezi zikuphatikizapo chilichonse chomwe chingatilepheretse kuthamanga ndi mtima wonse mpaka kukamaliza mpikisanowu. Kodi zinthu zolemera zimenezi zingakhale chiyani? Zimene Yesu ananena zingatithandize kupeza yankho. Iye anafotokoza za Nowa amenenso Paulo anamutchula m’gulu la anthu a chikhulupiriro. Yesu anati: “Monga zinachitikira m’masiku a Nowa, zidzachitikanso chimodzimodzi m’masiku a Mwana wa munthu.” (Luka 17:26) Yesu kwenikweni sankatanthauza kuti chiwonongeko chomwe chikubwera chidzafanana ndi cha nthawi ya Nowa koma moyo wa anthu ndi umene udzakhale wofanana ndi wa anthu a m’nthawi ya Nowa. (Werengani Mateyu 24:37-39.) Anthu ambiri m’masiku a Nowa sankafuna kuphunzira za Mulungu kapena kuchita zinthu zomusangalatsa. Kodi n’chiyani chinkawasokoneza? Sikuti zinali zinthu zapadera ayi. Ankasokonezedwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku monga kudya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa. Yesu ananena kuti vuto lawo lenileni linali lakuti “ananyalanyaza zimene zinali kuchitika.”

5. N’chiyani chingatithandize kumaliza bwinobwino mpikisano?

5 Mofanana ndi Nowa ndi banja lake, ife tili ndi zinthu zambiri zoti tizichita tsiku ndi tsiku. Tiyenera kupeza zinthu zofunika pa moyo wa ifeyo patokha ndiponso wa banja lathu. Zimenezi zikhoza kutithera nthawi, mphamvu ndiponso katundu. Pa nthawi ya mavuto azachuma, zimakhala zosavuta kuti munthu azidera nkhawa zinthu zofunika pa moyo. Popeza ndife Akhristu odzipereka kwa Mulungu, tilinso ndi maudindo ena m’gulu la Mulungu. Timalalikira, kukonzekera misonkhano ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova pophunzira patokha komanso kuchita kulambira kwa pabanja. Ngakhale kuti panali zinthu zambiri zoti Nowa achite potumikira Mulungu, iye anakwanitsa kuchita zonse, ndipo “anachitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Ngati tikufuna kuchita zonse zimene Yehova akutipempha ndiponso kumaliza bwinobwino mpikisano, tiyenera kusiya chilichonse chimene chingatilepheretse kuthamanga mpaka kukalandira mphoto.

6, 7. Kodi tiyenera kukumbukira malangizo a Yesu ati?

6 Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene ananena kuti tivule “cholemera chilichonse”? N’zoona kuti pali maudindo ena amene tiyenera kuwasamalira. Koma pa nkhani imeneyi tiyenera kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” (Mat. 6:31, 32) Mawu a Yesu amenewa akusonyeza kuti zinthu zofunika monga chakudya ndi zovala zikhoza kutilepheretsa kutumikira Yehova ngati titapanda kusamala nazo.

7 Kumbukirani kuti Yesu anati: “Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” Izi zikutanthauza kuti Atate wathu wakumwamba Yehova adzatithandiza kuti tizipeza zinthu zofunika pa moyo wathu. N’zoona kuti mawu akuti “zinthu zonsezi” sakutanthauza chilichonse chimene timafuna kukhala nacho. Koma Yesu anatiuza kuti tisamadere nkhawa ‘zinthu zimene anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama.’ N’chifukwa chiyani sitiyenera kudera nkhawa zinthu zofunika pa moyo wathu? Yesu ananena kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.”​—Luka 21:34, 35.

8. N’chifukwa chiyani tikufunikira ‘kuvula cholemera chilichonse’ makamaka panopa?

8 Tatsala pang’ono kufika pamzere womaliza. Choncho tisalole chinthu china chilichonse kutilepheretsa kumaliza mpikisanowu. N’chifukwa chake tiyenera kuvula cholemera chilichonse. Mtumwi Paulo anapereka malangizo anzeru akuti: “Kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.” (1 Tim. 6:6) Ngati titsatira mawu a Paulo, tikhoza kuthamanga bwinobwino n’kulandira mphoto.

“Tchimo Limene Limatikola Mosavuta”

9, 10. (a) Kodi mawu akuti, “tchimo limene limatikola mosavuta,” akutanthauza chiyani? (b) Kodi tingakoledwe bwanji mosavuta?

9 Kuwonjezera pa kuvula “cholemera chilichonse,” Paulo ananenanso za kuvula “tchimo limene limatikola mosavuta.” Kodi tchimo limeneli ndi liti? Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kukola mosavuta’ amapezeka pa vesi lokhali m’Baibulo lonse. Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo dzina lake Albert Barnes, ananena kuti anthu othamanga pa nthawiyo ankapewa kuvala zinthu zimene zingawakole m’miyendo n’kuwalepheretsa kuthamanga. Ndiyeno ananenanso kuti Mkhristu aliyense sayenera kulola chilichonse kumulepheretsa kuthamanga pa mpikisano wathu. Sayenera kulola chilichonse kumukola kapena kuti kufooketsa chikhulupiriro chake ngakhalenso kusiya kukhulupirira Mulungu. Kodi Mkhristu angasiye bwanji kukhulupirira Mulungu?

10 Mkhristu sasiya kukhulupirira Mulungu kamodzi n’kamodzi. Izi zimachitika pang’onopang’ono ndipo zimakhala zovuta kuzindikira. M’kalata yomweyi, Paulo anali atanena za kuopsa ‘kotengeka pang’onopang’ono’ ndiponso ‘kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.’ (Aheb. 2:1; 3:12) Miyendo ya wothamanga ikakodwa ndi zovala, wothamangayo amagwa. Wothamanga amakhala pa ngozi yoti akhoza kukodwa ngati wavala zovala zolakwika n’kumaganiza kuti sizingamukole. Kodi n’chiyani chingachititse munthu kunyalanyaza zimenezi? Anganyalanyaze chifukwa cha kusasamala, kudzidalira kwambiri kapena kusokonezedwa ndi zinthu zina. Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo a Paulo amenewa?

11. Kodi n’chiyani chingatichititse kutaya chikhulupiriro?

11 Tiyenera kukumbukira kuti munthu amataya chikhulupiriro chake chifukwa cha zimene wakhala akuchita kwa nthawi yaitali. Ponena za “tchimo limene limatikola mosavuta,” katswiri wina ananena kuti tchimoli limatikola chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu, anthu amene timacheza nawo komanso zinthu zimene timalakalaka. Zinthu zimenezi zingachititse kuti chikhulupiriro chathu chifooke kapena kuti chitayike.​—Mat. 13:3-9.

12. Kodi ndi malangizo ati omwe tiyenera kumvera kuti tisataye chikhulupiriro chathu?

12 Kwa zaka zambiri, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lakhala likutikumbutsa kuti tizisamala ndi zinthu zimene timaonera kapena kumvetsera chifukwa zimalowa m’mitima ndi m’maganizo mwathu. Takhala tikuchenjezedwanso za kuopsa kofunafuna chuma. Tikamakonda kwambiri zosangalatsa za m’dzikoli ndiponso kulakalaka kukhala ndi zinthu zamakono tikhoza kusowa mpata wochitira zinthu zofunika kwambiri. Anthu ena amaganiza kuti malangizo amene timalandirawa ndi opondereza kwambiri. Amaganiza kuti malangizowa amafunikira anthu ena osati iwowo ndipo amaganiza kuti ndi olimba moti sangagwe m’mavuto. Kungakhale kulakwitsa kuganiza choncho. Satana amagwiritsa ntchito maganizo ndi zilakolako za m’dzikoli kuti tizinyalanyaza machenjezo a Mulungu. Iye safuna kuti timalize nawo mpikisano wathu. Anthu ena ataya chikhulupiriro chawo chifukwa cha kuchita zinthu mosasamala, kudzidalira kapena kusokonezedwa ndi zinthu za m’dzikoli. Ngati izi zitatichitikira tikhoza kulephera kulandira moyo wosatha.​—1 Yoh. 2:15-17.

13. Kodi tingatani kuti tisamatengere zochita za anthu a m’dzikoli?

13 Tsiku lililonse timakumana ndi anthu amene amafuna kuti tiziyendera maganizo a m’dzikoli. Amafuna kuti tizichita zimene iwo amachita komanso amafuna kuti zinthu zimene amaona kuti ndi zofunika, ifenso tiziziona chimodzimodzi. (Werengani Aefeso 2:1, 2.) Komabe tifunikira kusankha ngati tikufuna kuti tiziyendera maganizo amenewa kapena ayi. Paulo ananena kuti maganizo a anthu m’dzikoli ali ngati “mpweya” wa poizoni. Nthawi zonse tiyenera kusamala kwambiri kuti tisapume mpweya woipa umene uli m’dzikoli. Tisalole kuti tizingotengera maganizo a anthu m’dzikoli. Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kuti tipitirize kuthamanga mpikisanowu? Yesu anathamanga bwino mpikisanowu ndipo ndi chitsanzo chathu. (Aheb. 12:2) Paulo ndi chitsanzo chinanso chimene tingatengere chifukwa iye anadziikanso m’gulu la anthu amene akuchita mpikisano wachikhristu ndipo analimbikitsa okhulupirira anzake kutengera chitsanzo chake.​—1 Akor. 11:1; Afil. 3:14.

Kodi Mungatani Kuti Mukalandire Mphoto?

14. Kodi Paulo ankaiona bwanji nkhani yothamanga mpaka kumaliza mpikisano?

14 Kodi Paulo ankaiona bwanji nkhani yothamanga mpaka kumaliza mpikisano? M’mawu ake omaliza omwe analembera akulu a ku Efeso, Paulo analemba kuti: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu basi.” (Mac. 20:24) Iye anali wofunitsitsa kuchita chilichonse ngakhale kufa kumene, n’cholinga choti akamalize mpikisano. Paulo ankaona kuti zonse zimene anachita kuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino mwakhama zikanakhala zopanda pake ngati atalephera kukamaliza mpikisano. Komabe izi sizinamupangitse kudzidalira kwambiri n’kumaganiza kuti wamaliza kale mpikisanowo. (Werengani Afilipi 3:12, 13.) Chakumapeto kwa moyo wake m’pamene ananena motsimikiza kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.”​—2 Tim. 4:7.

15. Kodi Paulo anawalimbikitsa bwanji anzake omwe ankathamanga nawo pa mpikisano?

15 Paulo ankafunitsitsa kuti Akhristu anzake asasiye kuthamanga koma amalize nawo mpikisanowu. Mwachitsanzo anauza Akhristu a ku Filipi kuti ayesetse kuchita zinthu zimene zingawathandize kupulumuka. Iwo anafunika “kugwira mwamphamvu mawu amoyo.” Paulo ananenanso kufunika kochita zimenezi. Iye anati: “Kuti ndikakhale ndi chifukwa chosangalalira m’tsiku la Khristu, poona kuti sindinathamange pachabe, kapena kuchita khama pachabe.” (Afil. 2:16) Paulo analimbikitsanso Akhristu a ku Korinto kuti: “Thamangani m’njira yoti mukalandire mphotoyo.”​—1 Akor. 9:24.

16. N’chifukwa chiyani kulandira mphoto kuyenera kukhala chinthu chofunika kwa ife?

16 Pa mpikisano wothamanga, othamanga samaoneratu mzere womaliza. Ngakhale zili choncho, cholinga cha othamangawo chimakhala kufika pamzere womalizawo. Iwo amalimbikira kwambiri kuthamanga akaona kuti atsala pang’ono kufika kumapeto. Ndi mmenenso ziyenera kukhalira ndi ifeyo pamene tikuthamanga pa mpikisano wathu. Tiyenera kuganizira kwambiri za mphoto imene tilandire. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tilimbikire kuthamanga mpaka kumaliza mpikisanowu ndiponso kulandira mphoto yathu.

17. Kodi chikhulupiriro chimathandiza bwanji kuti munthu aziika maganizo ake onse pa kulandira mphoto?

17 Paulo analemba kuti: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Abulahamu ndi Sara analola kusiya moyo wabwino n’kukakhala ngati “alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.” Kodi chinawathandiza kuchita zimenezi n’chiyani? Iwo ‘anaona [kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu] ali patali.’ Mose anakana “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo” ndiponso “chuma cha Iguputo.” Kodi n’chiyani chinamuchititsa kuti akhale ndi chikhulupiriro komanso mphamvu zochitira zimenezi? Iye “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.” (Aheb. 11:8-13, 24-26) M’pake kuti Paulo ankayamba kufotokoza za anthu onsewa ndi mawu akuti “mwa chikhulupiriro.” Chikhulupiriro chinawathandiza kuti asamangoyang’ana za mavuto amene ankakumana nawo koma aziganizira za zimene Mulungu ankawachitira komanso zimene adzawachitire m’tsogolo.

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tivule “tchimo limene limatikola mosavuta”?

18 Kuganizira za chikhulupiriro cha amuna ndi akazi otchulidwa m’chaputala 11 cha Aheberi komanso kutsatira chitsanzo chawo, kungatithandize kuti nafenso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Kungatithandizenso kuvula “tchimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Komanso tikamasonkhana ndi anthu amene akufuna kukhala ndi chikhulupiriro choterechi, zitithandiza kuti ‘tiganizirane ndi kulimbikitsana pa chikondi ndi ntchito zabwino.’​—Aheb. 10:24.

19. N’chifukwa chiyani panopa tiyenera kupitiriza kuthamanga pa mpikisano kuti tikalandire mphoto?

19 Tatsala pang’ono kufika kumapeto kwa mpikisano wathu. Zili ngati tayandikira mzere womaliza. Kukhala ndi chikhulupiriro komanso kuthandizidwa ndi Yehova zingatithandize kuti nafenso “tivule cholemera chilichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta.” Tikhoza kuthamanga n’cholinga choti tikalandire mphoto yomwe ndi madalitso amene Atate wathu wakumwamba Yehova Mulungu watilonjeza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ayuda akale ankaona kuti zimenezi zinali zochititsa manyazi kwambiri. Buku lachiwiri la Amakabeo lomwe anawonjezera m’Mabaibulo ena, limanena kuti Ayuda ambiri anakwiya pamene mkulu wa ansembe dzina lake Jason ankafuna kuti ku Yerusalemu kukhale malo ochitira masewera ngati omwe anali ku Girisi.​—2 Amakabeo 4:7-17.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kuvula “cholemera chilichonse” kumatanthauza chiyani?

• Kodi n’chiyani chingachititse Mkhristu kutaya chikhulupiriro?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuika maganizo athu onse pa mphoto?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi “tchimo limene limatikola mosavuta” n’chiyani ndipo lingatikole bwanji?