Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mulungu Ndi Wosamvetsetseka—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

1 Mulungu Ndi Wosamvetsetseka—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

1 Mulungu Ndi Wosamvetsetseka​—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

Mwina munamvapo izi: “Zochita za Mulungu n’zosamvetsetseka.”

Pofotokoza chiphunzitso cha Utatu chimene matchalitchi ambiri achikhristu amaphunzitsa, chikalata china chakale kwambiri chimati: “Atate ndi Wosamvetsetseka, Mwana ndi Wosamvetsetseka, nawonso Mzimu Woyera ndi Wosamvetsetseka.”​—The Athanasian Creed.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: Yesu ananena kuti anthu amene ‘amaphunzira ndi kudziwa za Mulungu yekhayo amene ali woona,’ adzalandira madalitso. (Yohane 17:3) Ndiye kodi tingaphunzire bwanji ndi kudziwa za Mulungu ngati Mulunguyo ali wosamvetsetseka? Mulungu sadzibisa ndipo amafuna kuti aliyense amudziwe.​—Yeremiya 31:34.

N’zoona kuti sitingathe kudziwa zonse zokhudza Mulungu. Zimenezi zili choncho chifukwa maganizo ndiponso njira za Mulungu ndi zosiyana kwambiri ndi zathu.​—Mlaliki 3:11; Yesaya 55:8, 9.

Kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji? Ngati Mulungu ali wosamvetsetseka, ndiye kuti kuyesetsa kuti timudziwe kungakhale kopanda phindu. Komatu iye amatithandiza kuti timudziwe komanso kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Ponena za Abulahamu, yemwe anali munthu wokhulupirika, Mulungu ananena kuti iye anali ‘bwenzi lake.’ Komanso Davide, yemwe anali mfumu ya Isiraeli analemba kuti: “Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.”​—Yesaya 41:8; Salimo 25:14.

Kodi mukuona kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? Mwinadi poyamba zingaoneke ngati zosatheka, koma taganizirani zimene lemba la Machitidwe 17:27 limanena. Limati: “[Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.” Kodi iye sali kutali motani? Kudzera m’Baibulo, Mulungu watipatsa zonse zofunikira kuti timudziwe bwino. *

Mulungu amatiuza kuti dzina lake ndi Yehova. (Yesaya 42:8) Iye analemba nkhani zosiyanasiyana zofotokoza zimene wakhala akuchita ndi anthu m’mbuyomu n’cholinga choti timudziwe. Kuwonjezera pamenepo, kudzera m’Mawu ake, Mulungu amatithandiza kudziwa mmene amamvera anthufe tikamachita zinthu zosiyanasiyana. Iye ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Ekisodo 34:6) Zochita zathu zingachititse kuti iye asangalale kapena akhumudwe. Mwachitsanzo, pamene mtundu wakale wa Isiraeli unamupandukira, iye ‘anakhumudwa.’ Koma anthu amene anamumvera, anasangalatsa mtima wake.​—Salimo 78:40; Miyambo 27:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mudziwe zambiri pa zimene Baibulo limanena zokhudza Mulungu, werengani mutu 1 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Kodi Mulungu akanakhala kuti ndi Utatu wosamvetsetseka, zikanakhala zotheka kumudziwa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

The Trinity c.1500, Flemish School, (16th century)/​H. Shickman Gallery, New York, USA/​The Bridgeman Art Library International