Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

4 Mulungu Amachita Zinthu Mopanda Chilungamo—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

4 Mulungu Amachita Zinthu Mopanda Chilungamo—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

4 Mulungu Amachita Zinthu Mopanda Chilungamo​—Kodi Zimenezi ndi Zoona?

Mwina munamvapo izi: “Mulungu ndi amene amayendetsa zinthu zonse padzikoli ndipo zonse zimachitika mogwirizana ndi chifuniro chake. Choncho, popeza m’dzikoli mwadzaza kusalana, kupanda chilungamo ndiponso kuponderezana, ndiye kuti Mulungu ndi amene akuchititsa zimenezi.”

Zimene Baibulo limaphunzitsa: Mulungu si amene amachititsa zinthu zopanda chilungamo zomwe zimachitika padzikoli. Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama.”​—Deuteronomo 32:4.

Mulungu ndi wowolowa manja kwa anthu onse, ngakhale kwa anthu amene amaoneka ngati sayenera kulandira zabwino kuchokera kwa iye. Mwachitsanzo, “iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyu 5:45) Lemba la Machitidwe 10:34, 35 limasonyeza kuti iye sakondera anthu amtundu kapena chikhalidwe chilichonse. Lembali limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”

Nangano, kodi ndani amachititsa zinthu zopanda chilungamozi? Anthu ambiri amasankha kuchita zinthu mokondera, m’malo motsatira chitsanzo cha Mulungu yemwe amachita zinthu mwachilungamo. (Deuteronomo 32:5) Komanso Baibulo limasonyeza kuti Mulungu walola kuti mdani wake Mdyerekezi azilamulira dzikoli. * (1 Yohane 5:19) Komabe Mulungu salola kuti Mdyerekezi alamulire dzikoli mpaka kalekale. Iye athetsa ulamuliro wa Satana posachedwapa ndipo wakonza kale njira ‘yowonongera ntchito za Mdyerekezi.’​—1 Yohane 3:8.

Kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji? N’kutheka kuti mumathedwa nzeru mukamva malipoti ambirimbiri onena za katangale, kuponderezana komanso kupanda chilungamo. Komabe kudziwa chimene chimachititsa mavuto amenewa kungakuthandizeni kumvetsa chifukwa chake zinthu zafika poipa chonchi. Kungakuthandizeninso kudziwa chimene chikuchititsa kuti mavutowa azipitirira ngakhale kuti anthu akuyesetsa kuti awathetse. (Salimo 146:3) Komanso mungakhale ndi chiyembekezo choti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino ndipo simungathere nthawi ndiponso mphamvu zanu kuchita zinthu zimene sizingathandize kapena zingangothandiza kwa nthawi yochepa. Mungakhale ndi chiyembekezo chimenechi chifukwa chokhulupirira malonjezo a Mulungu.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Kumvetsa chifukwa chenicheni chimene chimachititsa kuti padzikoli pazichitika zinthu zopanda chilungamo, kungatithandize kwambiri makamaka ngati vutolo latigwera ifeyo. Anthu ena akamatichitira zinthu zopanda chilungamo, tingamve ngati mmene mtumiki wa Mulungu, Habakuku anamvera. Iye anadandaulira Mulungu kuti: “Lamulo latha mphamvu ndipo anthu sakuchitanso chilungamo.” (Habakuku 1:4) Mulungu sanadzudzule Habakuku chifukwa chonena zimenezi. M’malomwake anatsimikizira mtumiki wakeyu kuti waika nthawi yodzakonza zinthu. Anamuthandizanso kukhalabe wosangalala ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ambiri. (Habakuku 2:2-4; 3:17, 18) Mofanana ndi zimenezi, kukhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzathetsa kupanda chilungamo, kungakuthandizeni kuti muzikhala ndi mtendere wamumtima m’dziko lopanda chilungamoli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziwe kumene Mdyerekezi anachokera, werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Kodi n’zoona kuti Mulungu ndi amene amachititsa mavuto komanso zinthu zopanda chilungamo?

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

©Sven Torfinn/​Panos Pictures