Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani m’kachisi wa ku Yerusalemu munkapezeka anthu osintha ndalama?

Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anathetsa zinthu zopanda chilungamo zimene zinkachitika m’kachisi. Baibulo limati: ‘Yesu anathamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”’​—Mateyu 21:12, 13.

Ayuda a m’nthawi ya Yesu komanso anthu amene analowa Chiyuda ankapita kukachisi wa ku Yerusalemu kuchokera kumadera ndi mizinda yosiyanasiyana ndipo popita kumeneko ankatenga ndalama za m’madera amene ankachokerawo. Komabe ankafunika kukhala ndi ndalama zovomerezeka kuti athe kupereka msonkho wapachaka wapakachisi, kugula nyama zopereka nsembe komanso kuti athe kupereka zopereka zina zaufulu. Chifukwa cha zimenezi, panali anthu amene ankasintha ndalama kuti anthu ochokera m’madera ena apeze ndalama zovomerezekazo. Pochita zimenezi, iwo ankalipiritsa anthu ofuna kusinthitsa ndalamawo. Zikondwerero zachiyuda zikamayandikira, anthu osintha ndalamawa ankaika matebulo awo m’Bwalo la Anthu a Mitundu Ina lomwe linali mkati mwa kachisi.

Popeza Yesu anadzudzula osintha ndalamawa kuti anasandutsa kachisi kukhala “phanga la achifwamba,” ndiye kuti iwo ankabera anthu powalipiritsa ndalama zambiri akafuna kusinthitsa ndalama zawo.

Kodi kale mitengo ya maolivi ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri chifukwa chiyani?

Ena mwa madalitso amene Mulungu analonjeza kuti adzapatsa anthu ake akakhala okhulupirika kwa iye, anali mitengo ya maolivi ndi minda ya mpesa. (Deuteronomo 6:10, 11) Mpaka lero, anthu akumadera kumene mitengo ya maolivi imapezeka, amaonabe kuti mitengoyi ndi yofunika kwambiri. Mtengo wa maolivi umatha kubala zipatso zambiri kwa zaka mahandiredi ambiri ngakhale utakhala kuti sukusamalidwa bwino kwenikweni. Mitengoyi imatha kukula bwinobwino ngakhale itabzalidwa pamalo amiyala ndipo ndi yopirira ku chilala. Mtengo wa maolivi akaugwetsa, chitsa chake chimatulutsa mphukira zingapo zimene zimathanso kukula n’kukhala mitengo ikuluikulu.

Kale, makungwa komanso masamba a mtengowu ankawagwiritsa ntchito ngati mankhwala a malungo. Komanso utomoni umene nthambi zakale zimatulutsa, womwe umakhala ndi kafungo kabwino kwambiri, ankaugwiritsa ntchito kupangira perefyumu. Komabe, mtengowu unali wofunika kwambiri chifukwa ankadya zipatso zake komanso makamaka chifukwa cha mafuta amene ankayenga kuchokera ku zipatsozo. Chipatso chokhwima bwino cha mtengowu chimakhala ndi mafuta ambiri.

Mtengo umodzi wosamalidwa bwino, ungatulutse mafuta okwana malita 57 pa chaka. Mafuta a maolivi ankawagwiritsa ntchito ngati mafuta anyali, odzola, atsitsi komanso ngati mankhwala ofewetsera mabala. Ankawagwiritsanso ntchito pa miyambo ya chipembedzo ndi miyambo ina.​—Ekisodo 27:20; Levitiko 2:1-7; 8:1-12; Rute 3:3; Luka 10:33, 34.