Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukhoza ‘Kumudziwadi Mulungu’

Mukhoza ‘Kumudziwadi Mulungu’

Yandikirani Mulungu

Mukhoza ‘Kumudziwadi Mulungu’

YEHOVA MULUNGU ali ndi chuma chamtengo wapatali ndipo akufunitsitsa kuti aliyense achipeze. Sikuti munthu akapeza chuma chimenechi amakhala wolemera mwakuthupi ayi, koma chimamuthandiza kukhala ndi zinthu zimene, ngakhale atakhala ndi ndalama zochuluka chotani, sangathe kugula. Zinthu zimenezi ndi mtendere wamumtima komanso kukhala ndi moyo wokhutira ndi wosangalala. Kodi chuma chimenechi ndi chiyani? Mawu a Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru, opezeka pa Miyambo 2:1-6 amatithandiza kuzindikira chuma chimenechi.

Solomo anatchula kuti chuma chimenechi ndi ‘kumudziwadi Mulungu,’ kapena kuti kudziwa zimene Baibulo limanena zokhudza Mulungu ndiponso zolinga zake. (Vesi 5) Chuma chimenechi chili ndi mbali zosiyanasiyana.

Ziphunzitso zoona. Baibulo lili ndi mayankho a mafunso monga awa: Kodi dzina la Mulungu ndani? (Salimo 83:18) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? (Salimo 146:3, 4) Kodi cholinga cha Mulungu polenga anthu n’chiyani? (Genesis 1:26-28; Salimo 115:16) Tikukhulupirira kuti inunso mukuvomereza kuti mayankho olondola a mafunso amenewa ndi chuma chamtengo wapatali kwambiri.

Malangizo anzeru. Baibulo limatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizikhala ndi moyo wabwino kwambiri. Mwachitsanzo: Kodi mungatani kuti banja lanu likhale lolimba? (Aefeso 5:28, 29, 33) Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti adzakhale anthu odalirika akadzakula? (Deuteronomo 6:5-7; Aefeso 6:4) Kodi mungatani kuti mukhale ndi moyo wosangalala? (Mateyu 5:3; Luka 11:28) Apanso, kodi simukuvomereza kuti malangizo odalirika pa nkhani zimenezi angakhale amtengo wapatali?

Kudziwa Mulungu komanso makhalidwe ake. Baibulo ndi limene limafotokoza zoona zokhudza Mulungu. Limayankha mafunso monga awa: Kodi Mulungu ndi wotani? (Yohane 1:18; 4:24) Kodi amatidera nkhawa? (1 Petulo 5:6, 7) Kodi ena mwa makhalidwe ake apadera ndi ati? (Ekisodo 34:6, 7; 1 Yohane 4:8) Kodi simukuvomereza kuti kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mlengi wathu ndi chinthu chamtengo wapatali?

Kunena zoona, ‘kumudziwadi Mulungu’ ndi chuma chamtengo wapatali. Koma kodi mungatani kuti mupeze chuma chimenechi? Yankho la funso limeneli likupezeka mu vesi 4 la Miyambo chaputala 2. M’vesili Solomo anayerekeza kudziwa Mulungu ndi “chuma chobisika.” Chuma chobisika sichingangochoka chokha pamene chili n’kugwera m’manja mwa munthu woti wangokhala. Munthu amayenera kuchita khama kuti apeze chumacho. Ndi mmenenso zilili ndi kudziwa Mulungu. Tingati chuma chimenechi chabisidwa m’Baibulo ndipo tiyenera kuchita khama kuti tichipeze.

Solomo anafotokoza zimene tiyenera kuchita kuti tithe ‘kumudziwadi Mulungu.’ Mawu akuti “ukamvera mawu anga” ndiponso akuti “ukaika mtima wako” akusonyeza kuti tiyenera kuyesetsa kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira. (Vesi 1, 2) Komanso mawu akuti “ukaitana” ndiponso akuti “ukamazifunafuna . . . ndi kuzifufuza” akusonyeza kuti m’pofunika kuchita khama kwambiri kuti tipeze chumacho. (Vesi 3, 4) Choncho kuti tipeze chuma chimenechi, tiyenera kuphunzira Baibulo mwakhama ndipo tiyenera kuchita zimenezi moona mtima.​—Luka 8:15.

Tikachita zimenezi, Yehova adzatithandiza kupeza chuma chimenechi. Vesi 6 limanena kuti: “Yehova amapereka nzeru.” Tingamvetse mfundo zoona za m’Baibulo pokhapokha ngati Mulungu watithandiza. (Yohane 6:44; Machitidwe 16:14) Mungakhale otsimikiza kuti, mukamafufuza chuma chauzimu chimenechi m’Mawu a Mulungu, muli ndi mtima wofunitsitsa kuphunzira, ‘mudzamudziwadi Mulungu.’ Chimenechi ndi chuma chamtengo wapatali ndipo chingakuthandizeni kwambiri pa moyo wanu.​—Miyambo 2:10-21. *

Mavesi a m’Baibulo amene mungawerenge mu October:

Miyambo chaputala 1 mpaka 21

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Padziko lonse, a Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo panyumba pawo kwaulere ngati anthuwo akufuna kumvetsa bwino Baibulo. Ngati mukufuna kuphunzira Baibulo, uzani a Mboni za Yehova akwanuko kapena lemberani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 4.